Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w96 1/1 tsamba 29-31
  • ‘Kulunjika Nawo Bwino Mawu a Choonadi’

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • ‘Kulunjika Nawo Bwino Mawu a Choonadi’
  • Nsanja ya Olonda—1996
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kupereka Mkaka wa Mawu a Mulungu
  • Kusamalira Chakudya Chotafuna cha Mawu a Mulungu
  • Madzi Amene Amatsitsimula ndi Kuyeretsa
  • Gwiritsirani Ntchito Mawu a Mulungu Monga Kalirole
  • Mawu a Mulungu Monga Lupanga
  • Kodi Mumadya Bwino Mwauzimu?
    Nsanja ya Olonda—1997
  • ‘Lolani Kupita Patsogolo Kwanu Kuwonekera’
    Nsanja ya Olonda—1992
  • Chakudya Chimene Chiri Chofunika Kaamba ka Moyo Wosatha
    Kusankha Njira Yabwino Koposa ya Moyo
  • ‘Lunjikani Nawo Bwino Mawu a Mulungu’
    Nsanja ya Olonda—2003
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1996
w96 1/1 tsamba 29-31

‘Kulunjika Nawo Bwino Mawu a Choonadi’

MAWU a Mulungu ndiwo nkhokwe ya makhalidwe ofunika pa moyo wabwino. Angathe kuthandiza mtumiki kuphunzitsa, kudzudzula, ndi kuwongolera. (2 Timoteo 3:16, 17) Komabe, kuti tipindule mokwanira ndi chitsogozo choperekedwa ndi Mulungu chimenechi, tiyenera kutsatira uphungu wa mtumwi Paulo kwa Timoteo wakuti: “Uchite changu kudzionetsera kwa Mulungu wovomerezeka, wantchito wopanda chifukwa cha kuchita manyazi, wolunjika nawo bwino mawu a choonadi.”​—2 Timoteo 2:15.

Mawu a Mulungu, pakati pa zinthu zina amafanizidwa ndi mkaka wopatsa thanzi, chakudya chotafuna, madzi otsitsimula ndi oyeretsa, kalirole, ndi lupanga lakuthwa. Kuzindikira tanthauzo la mawu ameneŵa kumathandiza mtumiki kugwiritsira ntchito Baibulo mwaluso.

Kupereka Mkaka wa Mawu a Mulungu

Mkaka ndi chakudya chimene makanda amafuna. Pamene khanda likukula, limapatsidwa chakudya chotafuna pang’onopang’ono, koma choyamba, mimba yake imatha kupukusa mkaka wokha. M’zochitika zambiri, awo amene amadziŵa zochepa pa Mawu a Mulungu ali ngati makanda. Kaya munthu akhale wokondwerera Mawu a Mulungu chatsopano kapena wakhala akuwadziŵa kwa nthaŵi yotalikirapo, ngati akudziŵa zoyamba zokha pa zimene Baibulo limanena, iyeyo ndi khanda lauzimu ndipo afunikira chakudya chofeŵa chopatsa thanzi​—“mkaka” wauzimu. Iye sakhoza kupukusa m’mimba “chakudya chotafuna” panthaŵiyo, zinthu zakuya za Mawu a Mulungu.​—Ahebri 5:12.

Umenewu ndiwo unali mkhalidwe wa mpingo umene unali utangopangidwa kumene ku Korinto pamene Paulo anaulembera kuti: “Ndinadyetsa inu mkaka, si chakudya cholimba ayi; pakuti simunachikhoza.” (1 Akorinto 3:2) Akorinto choyamba anafunikira kuphunzira “zoyamba za chiyambidwe cha maneno a Mulungu.” (Ahebri 5:12) Pamlingo wa kukula umene analipo, sakanatha kupukusa “zakuya za Mulungu.”​—1 Akorinto 2:10.

Monga Paulo, atumiki achikristu lerolino amasonyeza nkhaŵa yawo pamakanda auzimu mwa kuwapatsa “mkaka” ndiko kuti, kuwathandiza kukhala ozikika molimba pa chiphunzitso choyambirira chachikristu. Amalimbikitsa atsopano amenewo kapena osakula msinkhu ‘kulirira mkaka wosaipitsidwa wa mawuwo.’ (1 Petro 2:2, NW) Mtumwi Paulo anasonyeza kuti anazindikira za chisamaliro chapadera chimene atsopano anafuna pamene analemba kuti: “Yense wakudya mkaka alibe chizoloŵezi cha mawu a chilungamo; pakuti ali khanda.” (Ahebri 5:13) Chipiriro, kuganizira ena, kuzindikira, ndi kudekha nzofunika kwa atumiki a Mulungu pamene akugaŵira ena mkaka wabwino wa Mawuwo kwa atsopano ndi osadziŵa zinthu kwambiri mwa maphunziro a Baibulo apanyumba ndi mumpingo.

Kusamalira Chakudya Chotafuna cha Mawu a Mulungu

Kuti afikire chipulumutso, Mkristu amafunikira zoposa “mkaka.” Pamene amvetsa ndi kulandira choonadi choyambirira cha Baibulo amakhala wokonzekera kusunthira ku ‘chakudya chotafuna cha anthu aakulu misinkhu.’ (Ahebri 5:14) Kodi amachita motani zimenezi? Choyamba, mwa chizoloŵezi chokhazikika cha phunziro laumwini ndi kuyanjana ndi ena pamisonkhano yachikristu. Zizoloŵezi zimenezo zidzathandiza Mkristuyo kukhala wolimba mwauzimu, wokhwima, ndi wogwira mtima mu utumiki. (2 Petro 1:8) Kuwonjezera pa chidziŵitso, sitiyenera kuiŵala kuti kuchita chifuniro cha Yehova kulinso mbali ya chakudya chauzimu.​—Yohane 4:34.

Lerolino, “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” waikidwa kuti azipereka chakudya kwa atumiki a Mulungu panthaŵi yake ndi kuwathandiza kumvetsa “nzeru yamitundumitundu ya Mulungu.” Yehova, ndi mzimu wake, amavumbula choonadi chakuya cha m’Malemba kupyolera mwa kapolo wodalirika ameneyu, amene amafalitsa mokhulupirika ‘chakudya chauzimu panthaŵi yake.’ (Mateyu 24:45-47; Aefeso 3:10, 11; yerekezerani ndi Chivumbulutso 1:1, 2.) Mkristu aliyense ali ndi thayo la kugwiritsira ntchito mokwanira makonzedwe ameneŵa.​—Chivumbulutso 1:3.

Zoonadi, zinthu zina m’Baibulo zili “zovuta kuzizindikira,” ngakhale kwa Akristu okula misinkhu. (2 Petro 3:16) Muli mawu ovuta kuwamva, maulosi, ndi mafanizo amene amafuna kufufuza kwakukulu ndi kusinkhasinkha. Nchifukwa chake, phunziro laumwini limaphatikizapo kukumba mozama m’Mawu a Mulungu. (Miyambo 1:5, 6; 2:1-5) Makamaka akulu ndiwo amene ali ndi thayo pambaliyi pophunzitsa mpingo. Kaya akuchititsa Phunziro la Buku la Mpingo, kapena Phunziro la Nsanja ya Olonda, kupereka nkhani zapoyera, kapena kutumikira mu udindo wina uliwonse wa kuphunzitsa, akulu ayenera kudziŵa bwino kwambiri nkhani zawo ndi kukhala okonzekera kupereka chisamaliro pa ‘luso lawo la kuphunzitsa’ pamene akupereka chakudya chotafuna mumpingo.​—2 Timoteo 4:2, NW.

Madzi Amene Amatsitsimula ndi Kuyeretsa

Yesu anauza mkazi Msamariya pachitsime kuti adzampatsa kanthu kena kakumwa kamene kadzakhala mwa iye “kasupe wa madzi otumphukira ku moyo wosatha.” (Yohane 4:13, 14; 17:3) Madzi opatsa moyo ameneŵa amaphatikizapo makonzedwe onse a Mulungu opezera moyo kupyolera mwa Mwanawankhosa wa Mulungu, ndipo makonzedwe ameneŵa amafotokozedwa m’Baibulo. Monga anthu amene tili ndi ludzu la “madzi” amenewo, timavomera chiitano choperekedwa ndi mzimu ndi mkwatibwi wa Kristu cha ‘kutenga madzi a moyo kwaulere.’ (Chivumbulutso 22:17) Kumwa madzi ameneŵa kungatanthauze moyo wosatha.

Ndiponso, Baibulo limapereka miyezo ya makhalidwe ndi yauzimu kwa Akristu oona. Pamene tigwiritsira ntchito miyezo yopangidwa ndi Mulungu imeneyi, timayeretsedwa ndi Mawu a Yehova, ‘kusambitsidwa’ pamachitachita onse amene Yehova Mulungu amada. (1 Akorinto 6:9-11) Kaamba ka chifukwa chimenechi, choonadi chimene chili m’Mawu ouziridwa chimatchedwa ‘madzi osambitsa.’ (Aefeso 5:26, NW) Ngati sitilola choonadi cha Mulungu kutiyeretsa mu njira imeneyi, kulambira kwathu sikudzalandiridwa ndi iye.

Mokondweretsa, akulu amene ‘amalunjika nawo bwino mawu a choonadi’ amafanizidwanso ndi madzi. Yesaya akunena kuti iwo ali “monga mitsinje ya madzi m’malo ouma.” (Yesaya 32:1, 2) Akulu achikondi amayenerera mafotokozedwe ameneŵa pamene achezera abale awo monga abusa auzimu, akumagwiritsira ntchito Mawu a Mulungu otsitsimula kuti apereke chidziŵitso chauzimu chomangirira ndi chotonthoza chimene chimalimbitsa ndi kuchirikiza ena.​—Yerekezerani ndi Mateyu 11:28, 29.a

Ziŵalo zampingo zimayembekezera mwachidwi kuchezeredwa ndi akulu. “Ndikudziŵa mmene akulu angakhalire otonthoza, ndipo ndili wachimwemwe kuti Yehova wapanga makonzedwe ameneŵa,” akutero Bonnie. Lynda, nakubala wolera yekha ana, akulemba kuti: “Akulu anandithandiza ndi chilimbikitso cha m’Malemba kulimbana ndi vuto. Anamvetsera ndi kundichitira chifundo.” Michael akuti: “Anandichititsa kumva kukhala mbali ya gulu limene limasamala za ena.” Wina akunena kuti: “Kundichezera kwa akulu kunandithandiza kugonjetsa nyengo zakupsinjika kwakukulu.” Kuchezeredwa ndi mkulu kotsitsimula mtima mwauzimu kuli ngati chakumwa chozizira ndi chotsitsimula. Anthu onga nkhosa amatonthozedwa pamene akulu achikondi akuwathandiza kuona mmene malamulo amkhalidwe a Malemba angagwirire ntchito mu mkhalidwe wawo.​—Aroma 1:11, 12; Yakobo 5:14.

Gwiritsirani Ntchito Mawu a Mulungu Monga Kalirole

Pamene munthu adya chakudya chotafuna, cholinga chake sichimangokhala kuti amve kukoma. M’malo mwake, amayembekezera kupezamo zomanga thanzi zimene zidzamkhozetsa kuchita zinthu. Ngati ali mwana, amayembekezera kuti chakudyacho chidzamthandiza kukula kukhala wachikulire. Zili chimodzimodzinso ndi chakudya chauzimu. Phunziro laumwini la Baibulo lingakhale losangalatsa, koma chimenecho sindicho chifukwa chokha cholichitira. Chakudya chauzimu chiyenera kutisintha. Chimatithandiza kudziŵa ndi kutulutsa zipatso za mzimu ndi kutithandiza kuvala “[munthu] watsopano, kuti akhale nacho chizindikiritso, monga mwa chifaniziro cha Iye amene anamlenga iye.” (Akolose 3:10; Agalatiya 5:22-24) Chakudya chauzimu chimatithandizanso kukula msinkhu, chikumatipanga kukhala okhoza kugwiritsira ntchito malamulo a mkhalidwe a m’Malemba polimbana ndi mavuto athu ndi pothandiza ena kulimbana ndi awo.

Kodi tingadziŵe bwanji kaya ngati Baibulo likutiyambukira motero? Timagwiritsira ntchito Baibulo monga kalirole. Yakobo anati: “Khalani akuchita mawu, osati akumva okha, . . . Pakuti ngati munthu ali wakumva mawu, wosati wakuchita, iyeyu afanana ndi munthu wakuyang’anira nkhope yake ya chibadwidwe chake m’kalirole; pakuti wadziyang’anira yekha, nachoka, naiŵala pompaja [a]nali wotani. Koma iye wakupenyerera m’lamulo langwiro, ndilo laufulu, natero chipenyerere, ameneyo, posakhala wakumva wakuiŵala, komatu wakuchita ntchito, adzakhala wodala m’kuchita kwake.”​—Yakobo 1:22-25.

‘Timapenyerera’ m’Mawu a Mulungu pamene tiwapenda mosamalitsa ndi kuyerekezera zimene tili ndi zimene tiyenera kukhala mogwirizana ndi miyezo ya Mulungu. Ngati tichita zimenezi, tidzakhala “akuchita mawu, osati akumva okha.” Baibulo lidzakhala ndi chiyambukiro chabwino kwambiri pa ife.

Mawu a Mulungu Monga Lupanga

Potsiriza, mtumwi Paulo akutithandiza kuona mmene tingagwiritsirire ntchito Mawu a Mulungu monga lupanga. Potichenjeza za “maukulu, ndi maulamuliro, ndi akuchita zolimbika a dziko lapansi a mdima uno, ndi auzimu a choipa m’zakumwamba,” amatifulumiza “[kutenganso] . . . lupanga la [m]zimu, ndilo mawu a Mulungu.” (Aefeso 6:12, 17) Mawu a Mulungu ndiwo chida chofunika koposa chimene tiyenera kugwiritsira ntchito kudulira malingaliro alionse amene ali “chokwezeka chonse chimene chidzikweza pokana chidziŵitso cha Mulungu.”​—2 Akorinto 10:3-5.

Mosakayikira, “mawu a Mulungu ali amoyo, ndi ochitachita.” (Ahebri 4:12) Yehova amalankhula kwa anthu kupyolera m’masamba a Mawu ake ouziridwa. Agwiritsireni ntchito bwino pophunzitsa ena ndi povumbula ziphunzitso zonyenga. Agwiritsireni ntchito kulimbikitsira, kumangirira, kutsitsimulira, kutonthozera, kusonkhezera, ndi kulimbitsira ena mwauzimu. Ndipo Yehova “akuyeseni inu opanda chilema m’chinthu chilichonse chabwino, kuti muchite chifuniro chake,” kuti nthaŵi zonse muchite “chomkondweretsa pamaso pake.”​—Ahebri 13:21.

[Mawu a M’munsi]

a Onani nkhani ya mu Nsanja ya Olonda ya September 15, 1993, pamutu wakuti “Amaŵeta Nkhosa Mwachifundo,” masamba 20-3.

[Chithunzi patsamba 31]

Akulu limbikitsani ena, ‘mukumalunjika nawo bwino mawu a choonadi’

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena