Kodi Yehova Amandiona Kuti Ndine Munthu Wotani?
1. Kodi Baibulo limafanana bwanji ndi galasi?
1 Kodi inuyo mumakonda kudziyang’anira pagalasi? Ambirife timadziyang’anira tsiku lililonse chifukwa zimatithandiza kuona pofunika kukonza. Baibulo limayerekezeredwa ndi galasi. Kuwerenga Mawu a Mulungu, kumatithandiza kudziwa kuti ndife munthu wotani. Zimenezi n’zofunika chifukwa Yehova amaona munthu wamkati. (1 Sam. 16:7; Yak. 1:22-24) Mawu a Mulungu amathanso “kuzindikira zimene munthu akuganiza komanso zolinga za mtima wake.” (Aheb. 4:12) Kodi kuwerenga Baibulo tsiku ndi tsiku komanso kusinkhasinkha zimene tawerengazo kungatithandize bwanji kuona zimene tikufunika kusintha komanso kuti tizilalikira mwaluso?—Sal. 1:1-3.
2. Kodi Baibulo lingatithandize bwanji kudzifufuza?
2 Muzigwiritsa Ntchito Baibulo Ngati Galasi: Nkhani za m’Baibulo zonena za atumiki okhulupirika a Yehova zimatithandiza kudziwa makhalidwe amene iye amasangalala nawo. Mwachitsanzo, Davide anasonyeza kuti anali wachangu potumikira Yehova ndipo sankafuna kuti dzina la Mulungu lizinyozedwa. (1 Sam. 17:45, 46) Yesaya anadzipereka kulalikira kwa anthu ovuta. (Yes. 6:8, 9) Yesu ankakonda kwambiri atate wake wakumwamba. Zimenezi zinapangitsa kuti aziona kuti kutumikira Mulungu n’kosangalatsa osati kolemetsa. (Yoh. 4:34) Akhristu a m’nthawi ya atumwi ankalalikira mwakhama, ankadalira Yehova ndiponso sanalole kuti chilichonse chilepheretse utumiki wawo. (Mac. 5:41, 42; 2 Akor. 4:1; 2 Tim. 4:17) Kuganizira zitsanzo zimenezi kungatithandize kudzifufuza n’cholinga choti tione zofunika kukonza kuti tizitumikira bwino Yehova.
3. N’chifukwa chiyani sitiyenera kuzengereza ngati taona kuti pali zinazake zolakwika zimene tikufunika kusintha?
3 Tizichita Zimene Taphunzira: Munthu sangapindule chilichonse ngati atadziyang’anira pa galasi n’kuona kuti akufunika kukonza penapake, koma osakonza. Tiyenera kupempha Yehova kuti atithandize kudzifufuza moona mtima komanso kusintha ngati pakufunika kutero. (Sal. 139:23, 24; Luka 11:13) Nthawi imene yatsala yafupika komanso tikufunika kuthandiza anthu ambiri kuti adzapulumuke. Choncho ngati tikuona kuti tikufunika kusintha zinazake, sitiyenera kuzengereza.—1 Akor. 7:29; 1 Tim. 4:16.
4. Kodi chimachitika n’chiyani munthu akamaphunzira Mawu a Mulungu n’kumatsatira zimene waphunzirazo?
4 Yehova amayang’ana munthu wamkati yemwe ndi wofunika kwambiri kuposa mmene timaonekera. (1 Pet. 3:3, 4) Kodi chimachitika n’chiyani munthu akamaphunzira Mawu a Mulungu n’kumatsatira zimene waphunzirazo? Munthu wotereyu ‘amakhala wosangalala chifukwa chakuti sali wongomva n’kuiwala, koma wochita.’ (Yak. 1:25) Kuchita zimenezi kungatithandize kuti tizilalikira mogwira mtima chifukwa tingakhale “ngati magalasi oonera amene amaonetsa ulemerero wa Yehova.”—2 Akor. 3:18.