Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w98 8/15 tsamba 30
  • Kodi Mukukumbukira?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Mukukumbukira?
  • Nsanja ya Olonda—1998
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Tsiku la Chiweruzo N’chiyani?
    Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?
  • Tsiku Lopereka Chiweruzo la Mulungu Lidzabweretsa Madalitso Osangalatsa Kwambiri
    Mapeto Osangalatsa a Masomphenya a M’buku la Chivumbulutso
  • Tsanzirani Yehova—Chitani Chilungamo
    Nsanja ya Olonda—1998
  • Kodi Ndimotani Mmene Munthu Angakhalire m’Chifanizo cha Mulungu?
    Nsanja ya Olonda—1994
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1998
w98 8/15 tsamba 30

Kodi Mukukumbukira?

Kodi mwawaphunzira mosamalitsa makope aposachedwapa a Nsanja ya Olonda? Ngati zili motero, mudzasangalala kukumbukira zotsatirazi:

◻ Kodi nchifukwa chiyani chiphunzitso cha tsogolo lolembedweratu chili chopanda nzeru?

Chikhala Mulungu anadziŵiratu ndi kulinganiziratu za kuchimwa kwa Adamu, ndiye kuti akanakhala mlengi wa uchimo pamene analenga munthu ndiponso akanakhala kuti ndiye akuchititsa mwadala makhalidwe onse oipa a anthu ndi mavuto awo. Zimenezi sizikugwirizana ndi choonadi chakuti Yehova ndi Mulungu wachikondi amene amadana ndi zoipa. (Salmo 33:5; Miyambo 15:9; 1 Yohane 4:8)​—4/15, masamba 7, 8.

◻ Pokwaniritsa Yesaya 2:2-4, kodi anthu ochokera m’mitundu yambiri akuchitanji?

Pamene akusonkhana kunyumba ya Yehova yolambiriramo, iwo akupeŵanso ‘kuphunzira nkhondo’ chifukwa chakuti akudalira chitetezo cha magulu ankhondo akumwamba a Mulungu, amene ali okonzekera kuwononga adani onse a mtendere.​—4/15, tsamba 30.

◻ Kodi amphamvu a Mulungu amene akunenedwa pa Yoweli 3:10, 11 ndiwo ayani?

Pafupifupi nthaŵi 280 m’Baibulo, Mulungu woona akutchedwa kuti “Yehova wa makamu.” (2 Mafumu 3:14) Makamu ameneŵa ndiwo magulu amphamvu a angelo akumwamba, okonzeka kuchita zimene Yehova awauza.​—5/1, tsamba 23.

◻ Kodi tingaphunzirepo phunziro lotani pamene Yehova anafuna kuti Yobu apempherere awo amene anamlakwira? (Yobu 42:8)

Yobu asanachiritsidwe, Yehova anamuuza kuti apempherere awo amene anamlakwira. Zimenezi zikusonyeza kuti Yehova amafuna kuti tikhululukire kaye awo amene amatichimwira, machimo athu asanakhululukidwe. (Mateyu 6:12; Aefeso 4:32)​—5/1, tsamba 31.

◻ Kodi Yakobo anatanthauzanji pamene ananena kuti: “Chipiriro chikhale nayo ntchito yake yangwiro”? (Yakobo 1:4)

Chipiriro chili ndi “ntchito” yoichita. Ntchito yake ndiyo kutipangitsa kuti tikhale okwanira m’mbali zonse. Choncho mwa kulola mayesero kuchita ntchito yake, ndi kusayesa kugwiritsira ntchito njira zosemphana ndi Malemba kuti tithetse mayeserowo msanga, chikhulupiriro chathu chimayesedwa ndi kuyengedwa.​—5/15, tsamba 16.

◻ Kodi nchifukwa chiyani Mulungu wayembekezerera nthaŵi yaitali chonchi osathetsa mavuto a anthu?

Yehova amaŵerenga nthaŵi mosiyana ndi mmene ifeyo timaiŵerengera. Kwa Mulungu wamuyaya, nthaŵi yonse kuchokera pa kulengedwa kwa Adamu mpaka lero sikwana ngakhale mlungu umodzi. (2 Petro 3:8) Koma kaya timaiŵerenga motani nthaŵi, tsiku lililonse limene limapita limatiyandikizitsa ku tsiku la Yehova la kukwezedwa kwake.​—6/1, masamba 5, 6.

◻ Kodi nchiyani chimasonkhezera Mboni za Yehova?

Chiphunzitso cha Yehova chadzetsa anthu apadera, ophunzitsidwa kukondana wina ndi mnzake ndi kukonda mnansi wawo monga momwe adzikondera iwo eni. (Yesaya 54:13) Chikondi ndicho chimasonkhezera Mboni za Yehova kuti zipitirizebe kulalikira mosasamala kanthu kuti pali ena amene safuna kumvetsera kapena amene amawazunza. (Mateyu 22:36-40; 1 Akorinto 13:1-8)​—6/15, tsamba 20.

◻ Kodi mawu a Yesu akuti: “Yesetsani kuloŵa pakhomo lopapatiza” akutanthauzanji? (Luka 13:24)

Mawu a Yesu amatanthauza kulimbikira, kuyesetsa. Mawu ake amatanthauzanso kuti ena angafune ‘kuloŵa pakhomopo’ monga mmene angafunire, angayende mosatekeseka monga momwe akufunira. Choncho aliyense wa ife angadzifunse kuti, ‘Kodi ndikuyesetsa mwakhama ndi mokangalika?’​—6/15, tsamba 31.

◻ Kodi ndi motani mmene anthu oukitsidwa ‘adzaweruzidwira mwa zolembedwa m’mabuku, monga mwa ntchito zawo’? (Chivumbulutso 20:12)

Mabuku ameneŵa si kaundula wa zochita zawo zakale; pamene anafa, iwo anamasulidwa kumachimo amene anachita ali ndi moyo. (Aroma 6:7, 23) Komabe, anthu oukitsidwawo adzakhalabe ndi uchimo wa Adamu. Ndiye kuti mabuku ameneŵa ayenera kuti adzakhala ndi malangizo aumulungu akuti onse azitsatira kuti apindule ndi nsembe ya Yesu Kristu mokwanira.​—7/1, tsamba 22.

◻ Kodi fanizo la Yesu la Msamariya wabwino lili ndi maphunziro otani kwa ife? (Luka 10:30-37)

Fanizo la Yesu likusonyeza kuti munthu wolungamadi ndiye amene samangomvera malamulo a Mulungu koma amatsanziranso mikhalidwe yake. (Aefeso 5:1) Likusonyezanso kuti tiyenera kuona aliyense monga mnansi wathu mosasamala kanthu za mtundu wake, mwambo wake, kapena chipembedzo chake. (Agalatiya 6:10)​—7/1, tsamba 31.

◻ Kodi ndi m’njira zitatu ziti zimene mungadziŵire ana anu ndi kuwapatsa chitsogozo chaukholo?

(1) Thandizani ana anu kusankha ntchito yabwino yakuthupi; (2) akonzekeretseni kupirira zovuta za kusukulu ndi za kuntchito; (3) asonyezeni mmene angasamalirire zosoŵa zawo zauzimu.​—7/15, tsamba 4.

◻ Kodi nchifukwa ninji Mulungu anapumula pa “tsiku lachisanu ndi chiŵiri”? (Genesis 2:1-3)

Mulungu sanapumule chifukwa cha kutopa ayi. M’malo mwake, analekeza ntchito ya padziko lapansi pofuna kulola ntchito ya manja ake kuti ikule kufika paulemerero wake wonse wodzetsa chitamando ndi ulemu kwa iye.​—7/15, tsamba 18.

◻ Kodi tingachite chilungamo m’njira zitatu ziti?

Choyamba, tiyenera kutsatira malamulo a Mulungu a makhalidwe abwino. (Yesaya 1:17) Chachiŵiri, timachita chilungamo pamene tichitira ena zimene tikufuna kuti Yehova atichitire. (Salmo 130:3, 4) Chachitatu, timasonyeza chilungamo cha Mulungu pamene tichita ntchito yolalikira mwakhama. (Miyambo 3:27)​—8/1, masamba 14, 15.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena