Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Chipulumutso Chiri Pafupi kwa Anthu Odzipereka Mwaumulungu!
    Nsanja ya Olonda—1990 | April 15
    • 2, 3. (a) Kodi nchifukwa ninji lerolino tikupeza zimene zanenedwa pa 2 Petro 2:9 kukhala zolimbikitsa? (b) Kodi ndi machitidwe achipulumutso achindunji otani amene Baibulo limasonyako monga maziko a chilimbikitso?

      2 Zimene zikuchitika m’tsiku lathu zimatikumbutsa za nthaŵi zina zotchuka m’mbiri ya munthu. Mtumwi Petro akukokera chisamaliro chathu ku machitidwe a chipulumutso amene Mulungu anachita pa zochitika zimenezo ndipo akufika ku mapeto otsimikizira awa: “Yehova amadziŵa kulanditsa anthu odzipereka mwaumulungu ku chiyeso.” (2 Petro 2:9, NW) Onani mawu ozungulira lemba a ndemanga imeneyo, pa 2 Petro 2:4-10 (NW):

      3 “Ndithudi ngati Mulungu sanaleka kulanga angelo amene anachimwa, koma, mwa kumawaponya iwo mu Dzenje, anawapereka iwo ku maenje a mdima waukulu kuti akasungidwe kaamba ka chiweruzo; ndipo iye sanaleka kulanga dziko lakale, koma anamsunga Nowa, mlaliki wa chilungamo, bwino lomwe limodzi ndi ena asanu ndi aŵiri pamene iye anadzetsa chigumula pa dziko la anthu opanda umulungu; ndipo mwa kumaisandutsa mizinda ya Sodomu ndi Gomora kukhala phulusa iye anaitsutsa iyo, akumapereka chitsanzo kaamba ka anthu opanda umulungu a zinthu zirinkudza; ndipo iye anamlanditsa Loti wolungamayo, amene anasautsidwa kwakukulu ndi kumwerekera kwa anthu onyoza lamulo mu mkhalidwe wachisembwere​—pakuti munthu wolungama ameneyo mwa zimene iye anaziwona ndi kuzimva pamene anali kukhala pakati pawo tsiku ndi tsiku zinali kumauzunza moyo wake wolungama chifukwa cha zochita zawo zosaweruzika​—Yehova amadziŵa kulanditsa anthu odzipereka mwaumulungu ku chiyeso, koma kuwasunga anthu osalungama kaamba ka tsiku la chiweruzo kuti akadulidwe, komabe, makamaka, awo amene amatsatira thupi limodzi ndi chikhumbo chakuliipitsa ndi amene amanyozetsa umbuye.” Monga mmene malemba amenewo akusonyezera, zimene zinachitika m’tsiku la Nowa ndi m’nthaŵi ya Loti ziri ndi tanthauzo kwa ife.

  • Chipulumutso Chiri Pafupi kwa Anthu Odzipereka Mwaumulungu!
    Nsanja ya Olonda—1990 | April 15
    • 4. M’tsiku la Nowa, kodi nchifukwa ninji Mulungu anawona dziko lapansi kukhala lovunda? (Salmo 11:5)

      4 Cholembedwa cha mbiri mu Genesis mutu 6 chimatiuza kuti m’tsiku la Nowa dziko lapansi linavunda pamaso pa Mulungu. Chifukwa ninji? Chifukwa cha chiwawa. Iyo sinali nkhani ya upandu wachiwawa cha apa ndi apo. Genesis 6:11 akusimba kuti “dziko lapansi . . . linadzala ndi chiwawa.”

      5. (a) Kodi ndi mkhalidwe wotani kumbali ya anthu umene unathandizira ku chiwawa cha tsiku la Nowa? (b) Kodi Enoke adali atachenjezanji ponena za kupanda umulungu?

      5 Kodi nchiyani chimene chinali chochititsa? Lemba logwidwa mawu pa 2 Petro likulozera kwa anthu opanda umulungu. Inde, mzimu wa kupanda umulungu unaipitsa machitachita a anthu. Zimenezi zinaloŵetsamo osati kokha kusasamala malamulo aumulungu kwachisawawa koma mkhalidwe wamwano kulinga kwa Mulungu iyemwini.a Ndipo pamene anthu ali amwano kulinga kwa Mulungu, kodi zingayembekezeredwe motani kuti iwo akachitira mwachifundo anthu anzawo? Kalekale Nowa asanabadwe, kupanda umulungu kumeneku kunali kochuluka kotero kuti Yehova anapangitsa Enoke kulosera ponena za zotulukapo zake. (Yuda 14, 15) Kuchitira kwawo Mulungu mwano kunali kotsimikiza kuwabweretsera chiweruzo chaumulungu.

  • Chipulumutso Chiri Pafupi kwa Anthu Odzipereka Mwaumulungu!
    Nsanja ya Olonda—1990 | April 15
    • a “Anomia kuli kunyalanyaza, kapena kuchitira mwano, malamulo a Mulungu; asebeia [mpangidwe wa nauni wa liwu lotembenuzidwa ‘anthu opanda umulungu’] uli mkhalidwe umodzimodziwo kulinga ku Munthu wa Mulungu.”​—Vine’s Expository Dictionary of Old and New Testament Words, Volyumu 4, tsamba 170.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena