Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g94 11/8 tsamba 18-20
  • Kodi Ndachita Tchimo Losakhululukidwa?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Ndachita Tchimo Losakhululukidwa?
  • Galamukani!—1994
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Chifukwa Chake Chikumbumtima Chathu Chimatipweteka
  • Chisoni Chaumulungu
  • Kudzimva Waliwongo pa Machimo Aang’ono
  • Magwero a Chithandizo ndi Chitonthozo
  • Yehova Amakhululukira Koposa
    Nsanja ya Olonda—1992
  • Kodi Ndi Tchimo Liti Limene Munthu Sangakhululukidwe?
    Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
  • Yehova, Mulungu “Wokhululukira”
    Nsanja ya Olonda—1997
  • Kodi Pali Tchimo Limene Silingakhululukidwe?
    Galamukani!—2003
Onani Zambiri
Galamukani!—1994
g94 11/8 tsamba 18-20

Achichepere Akufunsa Kuti . . .

Kodi Ndachita Tchimo Losakhululukidwa?

“SINDINAPSINJIKEPO mtima motero. Ndinalibenso ulemu waumwini, ndipo ndinalingalira kuti Mulungu sakandikhululukira konse.”—Marco.a

“Zinandilefula kwambiri. Liwongo linadzaza mumtima mwanga. Ndinalingalira kuti ndinachita machimo osakhululukidwa.”—Alberto.

“Palibe munthu wosachimwa,” limatero Baibulo. (1 Mafumu 8:46) Koma nthaŵi zina wachichepere angalingalire kuti wachita tchimo lalikulu kwambiri. Mofanana ndi Marco ndi Alberto, iye angavutitsidwe ndi maganizo a liwongo osatha. Angalingalire kuti chimene wachita nchonyansa kwenikweni, choipitsitsa, kwakuti Mulungu sangamkhululukire konse.

Bwanji ngati malingaliro otero akukuvutitsani? Limbani mtima. Mkhalidwe wanu suli konse wothetseratu nzeru.

Chifukwa Chake Chikumbumtima Chathu Chimatipweteka

Kuli kwachibadwa kuipidwa pamene muchita cholakwa chopusa. Tonse timabadwa ndi mkhalidwe umene Baibulo limautcha “chikumbumtima.” Ndicho nzeru ya kudziŵa chabwino ndi choipa, belu lamkati limene nthaŵi zonse limalira tikachita chinthu choipa. (Aroma 2:14, 15) Mwachitsanzo, talingalirani za Mfumu Davide. Iye anachita chigololo ndi mkazi wa munthu wina. Pambuyo pake, anatumiza mwamuna wa mkaziyo, Uriya, ku imfa yotsimikizirika. (2 Samueli 11:2-17) Kodi Davide anakhudzidwa motani?

“Usana ndi usiku dzanja [la Mulungu] linandilemera ine,” anavomereza motero Davide. Inde, anamva kulemera kwa kusakondwa kwa Mulungu. Davide anatinso: “M’mafupa anga simuzizira, chifukwa cha cholakwa changa. Pakuti mphulupulu zanga zapitirira pamutu panga: Ndathodwa nazo monga ndi katundu wolemera. . . . Ndimayenda woliralira tsiku lonse.” (Salmo 32:4; 38:3-6) Chikumbumtima cha Davide chinamsautsa nthaŵi zonse kufikira anakakamizika kuchitapo kanthu ndi kulapa tchimo lake.

Mofananamo, ngati mwaphunzitsidwa ndi makolo Achikristu koma mwapambuka pa miyezo ya Baibulo, mudzaipidwa. Kuipidwa kumeneku kuli kwachibadwa ndi koyenera. Kungachititse munthuyo kudziwongolera kapena kufuna thandizo tchimolo lisanakhale chizoloŵezi chozika mizu. Komanso munthu amene aumirira pa tchimo amawononga chikumbumtima chake. M’kupita kwa nthaŵi chimakhala chakufa, monga khungu lokakala. (1 Timoteo 4:2) Chotsatirapo chotsimikizirika chimakhala kuwonongeka kwa makhalidwe.—Agalatiya 6:7, 8.

Chisoni Chaumulungu

Chotero, nzosadabwitsa pamene Baibulo limanena za “tchimo la kuimfa.” (1 Yohane 5:16; yerekezerani ndi Mateyu 12:31.) Tchimo loterolo sindilo kufooka chabe kwa thupi. Limachitidwa mwadala, mwamwano, mouma khosi. Si tchimolo mwa ilo lokha limene limalichititsa kukhala losakhululukidwa, koma mkhalidwe wa mtima wa wochimwayo ndiwo.

Komabe, kupwetekedwa mtima ndi kupsinjika kwanuko kumasonyeza kuti simunachite tchimo losakhululukidwa. Baibulo limanena kuti “chisoni cha kwa Mulungu chitembenuzira mtima kuchipulumutso.” (2 Akorinto 7:10) Indedi, taonani chilangizo choperekedwa pa Yakobo 4:8-10 chakuti: “Sambani m’manja, ochimwa inu; yeretsani mitima, a mitima iŵiri inu. Khalani osautsidwa, lirani, lirani misozi; kuseka kwanu kusanduke kulira, ndi chimwemwe chanu chisanduke chisoni. Dzichepetseni pamaso pa Ambuye, ndipo adzakukwezani.”

Zoona, cholakwacho chingakhale chachikulu kwambiri. Mwachitsanzo, Julie wachichepere anayamba kupsompsonana ndi kugwiranagwirana ndi bwenzi lachimuna. “Poyamba ndinamva kukhala waliwongo kwambiri,” iye akuvomereza motero, “koma m’kupita kwa nthaŵi, ndinazoloŵera zimenezo. Sizinavutitsenso kwambiri chikumbumtima changa.” M’kupita kwa nthaŵi, machitidwe osayenerawo anafika pa kugonana. “Ndinamva kukhala wothedwa nzeru,” akutero Julie. “Chikumbumtima changa chinafooka kwambiri kufika pamlingo wakuti tchimolo linachitidwa kangapo konse.”

Kodi mkhalidwe woterowo uli wothetseratu nzeru? Osati kwenikweni. Bwanji ponena za Manase, mmodzi wa mafumu a Yuda? Iye anachita machimo oipitsitsa, kuphatikizapo kulambira mizimu ndi kupereka nsembe ana. Komabe, Mulungu anamkhululukira chifukwa cha kulapa kwake koona mtima. (2 Mbiri 33:10-13) Bwanji nanga za Mfumu Davide? Pokhala atalapa machitidwe ake oipa, anapeza Yehova kukhala Mulungu “wabwino, ndi wokhululukira.”—Salmo 86:5.

Akristu lerolino ali ndi chitsimikizo ichi: “Ngati tivomereza machimo athu, ali wokhulupirika ndi wolungama iye, kuti atikhululukire machimo athu, ndi kutisambitsa kutichotsera chosalungama chilichonse.” (1 Yohane 1:9) Kodi nkwayani kumene munthu ayenera kuvomereza machimo ake? Choyamba, kwa Yehova Mulungu. “Tsanulirani mitima yanu pamaso pake.” (Salmo 32:5; 62:8) Mungakuone kukhala kokuthandizani kuŵerenga za kuvomereza machimo kwa Davide kwa kulapa mu Salmo 51.

Ndiponso, Baibulo limalimbikitsa Akristu omwe agwera m’tchimo lalikulu kuti alankhule kwa akulu a mpingo. (Yakobo 5:14, 15) Uphungu wawo woona mtima ndi mapemphero awo angakuthandizeni kukhazikitsanso unansi wanu ndi Mulungu ndi kupezanso chikumbumtima choyera. Iwo akhoza kuona kusiyana pakati pa kufooka ndi kuipa. Ayeneranso kutsimikizira kuti mwapatsidwa chithandizo chimene mufunikira kotero kuti musadzabwerezenso cholakwa chanu. Julie atatenga sitepe lolimba mtima limeneli, akulangiza kuti: “Ndinayesa ‘kudzidzudzula ndekha’ ndipo ndinaganizadi kuti zinandithandiza pamlingo winawake. Koma pambuyo pa chaka chimodzi ndinadziŵa kuti ndinali wolakwa. Simungathe kuthetsa mavuto aakulu popanda chithandizo cha akulu.”

Kudzimva Waliwongo pa Machimo Aang’ono

Komabe, nthaŵi zina wachichepere ‘angagwidwe nako kulakwa.’ (Agalatiya 6:1) Kapena angalole chilakolako cha thupi kumgonjetsa. Wachichepere wokhala mumkhalidwe umenewu angavutike kwambiri ndi malingaliro a liwongo—mwinamwake kukhala ndi liwongo lalikulu kuposa loyenera cholakwacho. Zotulukapo zimakhala nsautso yosafunikira. Malingaliro aliwongo lalikulu otero angachititsidwe ndi chikumbumtima chabwino komabe chatcheru mopambanitsa. (Aroma 14:1, 2) Kumbukirani, pamene tichimwa “nkhoswe tili naye kwa Atate, ndiye Yesu Kristu wolungama.”—1 Yohane 2:1, 2.

Talingaliraninso nkhani ya Marco wachichepereyo, wogwidwa mawu m’mawu athu oyamba. Mkristu wachichepere ameneyu anali wotsimikiza kuti anali atachita tchimo losakhululukidwa. Iye ankanena kuti: ‘Ndimadziŵa bwino lomwe malamulo a mkhalidwe a Baibulo, komabe sindileka kuchita tchimo!’ Tchimo lotani? Vuto la psotopsoto. ‘Angandikhululukire bwanji Mulungu ngati sindileka chizoloŵezicho?’ Marco analingalira motero. Alberto, yemwe nayenso anali ndi vuto la kudziipsa anati: “Ndinadzimva waliwongo mumtima mwanga chifukwa chakuti sindinathe kudzimasula ku tchimolo.”

Psotopsoto ndi chizoloŵezi chonyansa. (2 Akorinto 7:1) Komabe, Baibulo silimaika mchitidwewo m’gulu la machimo aakulu onga dama. Ndipo ilo silimautchula nkomwe. Motero, kugwera mumchitidwe wa psotopsoto sikungakhale kosakhululukika iyayi. Kukuona monga kuti kunali kosakhululukika kungakhaledi kwangozi; wachichepere angalingalire kuti kuli kosaphula kanthu kuyesayesa kugonjetsa vutolo. Koma malamulo a mkhalidwe a Baibulo amasonyeza kuti Mkristu ayenera kuyesayesa zolimba kulimbana ndi chizoloŵezi chimenechi.b (Akolose 3:5) Yehova amadziŵa kuti “timakhumudwa tonse pa zinthu zambiri.” (Yakobo 3:2) Ngati agweranso m’chimenecho, wachichepere sayenera kumva kukhala wokanidwa.

Zilinso motero ponena za zophophonya ndi zolakwa zina. Yehova samafuna kuti tidzilange tokha ndi liwongo lopambanitsa. Mmalomwake, iye amakondwera pamene tichitapo kanthu kuwongolera vutolo.—2 Akorinto 7:11; 1 Yohane 3:19, 20.

Magwero a Chithandizo ndi Chitonthozo

Komabe, mwachionekere mudzafunikira chithandizo chaumwini kuti muchite zimenezo. Kaŵirikaŵiri, makolo owopa Mulungu amathandiza kwambiri ndi kuchirikiza ana awo. Ndipo mpingo Wachikristu umapereka njira zina zochirikiza. Marco akukumbukira kuti: “Chinthu chimene chinandithandiza kwenikweni chinali kukambitsirana ndi mkulu. Ndinafunikira kulimba mtima kuti ndilankhule momasuka ndi kumuuza zakukhosi kwanga. Koma iye anandilimbikitsa kwambiri, motero ndinapempha uphungu wake.” Alberto nayenso, anapempha uphungu kwa mkulu. “Sindingaiŵale uphungu wake wolimbikitsa,” akutero Alberto. “Iye anandiuza kuti pamene anali wamng’ono, nayenso anali ndi vuto limodzimodzilo. Sindikanakhulupirira konse zimenezo. Ndinatchera khutu kwa iye ndi chiyamikiro chachikulu kaamba ka kuona mtima kwake.” Ndi chithandizo limodzi ndi chilimbikitso choterocho, Marco ndi Alberto anagonjetsa mavuto awo. Onse aŵiriwo tsopano akutumikira pamalo athayo m’mipingo yawo.

Pemphero lakhama ndilo thandizo lina. Mofanana ndi Davide, mukhoza kupempherera “mtima woyera” ndi “mzimu wokhazikika.” (Salmo 51:10) Kuŵerenga Mawu a Mulungu ndiko magwero ena a chitonthozo. Mwachitsanzo, kungakhale kokuthandizani kudziŵa kuti mtumwi Paulo nayenso anali ndi nkhondo mkati mwake. Iye anavomereza kuti: “Pamene ndifuna chabwino, choipa chiliko.” (Aroma 7:21) Paulo anakhala wokhoza kuletsa zizoloŵezi zake zolakwa. Inunso mukhoza kutero. Mungakuone kukhala kokutonthozani kwambiri kuŵerenga masalmo, makamaka onena za kukhululukira kwa Mulungu, onga ngati Masalmo 25, 86, ndi 103.

Mulimonse mmene zingakhalire, peŵani kudzipatula ndi kusumika maganizo pa kuipa kwa chinthucho. (Miyambo 18:1) Pindulani mokwanira ndi chifundo cha Yehova. Kumbukirani kuti, iye ‘amakhululukira kwambiri’ pa maziko a nsembe ya dipo ya Yesu. (Yesaya 55:7; Mateyu 20:28) Musapeputse zolakwa zanu, komanso musagamule kuti Mulungu sangakukhululukireni. Limbitsani chikhulupiriro chanu ndi kutsimikiza mtima kwanu kwa kumtumikira iye. (Afilipi 4:13) M’kupita kwa nthaŵi mudzakhala ndi mtendere wa maganizo ndi chisangalalo cha mumtima cha kudziŵa kuti mwakhululukiridwa.—Yerekezerani ndi Salmo 32:1.

[Mawu a M’munsi]

a Maina ena asinthidwa.

b Malingaliro othandiza aperekedwa m’mitu 25 ndi 26 ya buku lakuti Mafunso Achichepere Akufunsa—Mayankho Amene Amathandiza, lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.

[Chithunzi patsamba 19]

Kukambitsirana zinthu ndi Mkristu wachidziŵitso kungakupatseni kaonedwe ka zinthu katsopano

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena