Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • rs tsamba 190-tsamba 195
  • Kulambira Mizimu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kulambira Mizimu
  • Kukambitsirana za m’Malemba
  • Nkhani Yofanana
  • Mizimu Yoipa Njamphamvu
    Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi
  • Chifukwa Chimene Muyenera Kupeŵera Kukhulupirira Mizimu
    Galamukani!—2000
  • Kodi Amalankhuladi Ndi Akufa?
    Nsanja ya Olonda—1988
  • Mmene Zochita za Angelo Komanso Ziwanda Zimakhudzira Moyo Wathu
    Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?
Onani Zambiri
Kukambitsirana za m’Malemba
rs tsamba 190-tsamba 195

Kulambira Mizimu

Tanthauzo: Chikhulupiriro chakuti mbali ya mzimu ya anthu imapulumuka imfa yathupi laumunthu ndipo ingakhoze kulankhulana ndi amoyo, kaŵirikaŵiri kupyolera mwa munthu amene amatumikira monga wobwebweta. Anthu ena amakhulupirira kuti zinthu zonse zakuthupi ndi zochitika zonse za chilengedwe ziri ndi mizimu yokhalamo. Kupenduza ndiko kugwiritsiridwa ntchito kwa mphamvu imene imavomerezedwa kukhala yochokera kwa mizimu yoipa. Mipangidwe yonse ya kukhulupirira mizimu imatsutsidwa mwamphamvu m’Baibulo.

Kodi kulidi kotheka kwa munthu kulankhulana ndi “mzimu” wa wokondedwa wakufa?

Mlal. 9:5, 6, 10: “Amoyo adziŵa kuti tidzafa; koma akufa sadziŵa kanthu bi . . . Chikondi chawo ndi mdano wawo ndi dumbo lawo lomwe zatha tsopano; ndipo nthaŵi yamuyaya sagaŵa konse kanthu kalikonse kachitidwa pansi pano. Chirichonse dzanja lako lichipeza kuchichita, uchichite ndi mphamvu yako; pakuti mulibe ntchito ngakhale kulingirira ngakhale kudziŵa, ngakhale nzeru, [ku Sheoli] kumanda uli kupitako.”

Ezek. 18:4, 20: “Moyo wochimwawo ndiwo udzafa.” (Motero moyo sindiwo kanthu kena kamene kamapulumuka imfa yathupi ndi kamene pambuyo pake anthu amoyo angalankhulane nako.)

Sal. 146:4: “Mpweya [mzimu (NW)] wake uchoka, abwerera kumka kunthaka yake; tsiku lomwelo zotsimikiza mtima zake zitayika.” (Pamene mzimu unenedwa kuti ‘uchoka’ m’thupi, imeneyi iri kokha njira ina ya kunena kuti mphamvu ya moyo yaleka kugwira ntchito. Motero, munthu atafa, mzimu wake sumakhalako monga chinthu chapadera chimene chingalingalire ndi kukwaniritsa zolinganiza popanda thupi. Uwo sindiwo kanthu kena kamene amoyo angalankhulane nako pambuyo pa imfa ya munthuyo.)

Wonaninso tsamba 153-155, pamutu wakuti “Imfa.”

Kodi Baibulo silimasonyeza kuti Mfumu Sauli analankhulana ndi mneneri Samueli pambuyo pa imfa ya Samueli?

Cholembedwacho chikupezeka pa 1 Samueli 28:3-20. Vesi 13, 14 imasonyeza kuti Sauli sanawone Samueli koma anangoyerekezera kokha mwa malongosoledwe operekedwa ndi wowombedzayo akuti iye anawona Samueli. Mothedwa nzeru Sauli anafuna kukhulupirira kuti anali Samueli ndipo motero anadzichititsa kuti anyengedwe. Vesi 3 limanena kuti Samueli anali wakufa ndi woikidwa m’manda. Malemba ogwidwa mawu m’mutu wankhani waung’ono wapitawo amamveketsa bwino kuti panalibe mbali ya Samueli imene inali moyo m’dziko lina ndi imene inali yokhoza kulankhulana ndi Sauli. Liwu limene linayeserera kukhala la Samueli linali la wonyenga.

Kodi ndani amene awo oyesayesa kulankhula ndi akufa kwenikweni amalankhulana nawo?

Chowonadi cha mkhalidwe wa akufa chalongosoledwa momvekera bwino m’Baibulo. Koma kodi ndani amene anayesa kunyenga anthu aŵiri oyamba ponena za imfa? Satana anatsutsa chenjezo la Mulungu lakuti kusamvera kukadzetsa imfa. (Gen. 3:4; Chiv. 12:9) Ndithudi, m’nthaŵi yokwanira, kunafikira kukhala kwachiwonekere kuti anthu anafa monga momwe Mulungu ananenera kuti akatero. Pamenepo, moyenerera, kodi ndani amene anali ndi thayo la kupeka lingaliro lakuti anthu samafadi koma kuti mbali ina ya munthu imapulumuka imfa yathupi? Chinyengo chotero chimayenera Satana Mdyerekezi, amene Yesu analongosola kukhala “atate wake wabodza.” (Yoh. 8:44; wonaninso 2 Atesalonika 2:9, 10.) Chikhulupiriro chakuti akufa alidi amoyo m’chigawo china ndi kuti tingathe kulankhulana nawo sichinapindulitse anthu. Mmalo mwake, Chivumbulutso 18:23 chimanena kuti, kupyolera mwa machitachita a kukhulupirira mizimu a Babulo Wamkulu, “mitundu yonse inasokeretsedwa.” Machitachita a kukhulupirira mizimu a ‘kulankhula ndi akufa’ alidi chinyengo cha machenjera chimene chingaike anthu m’chigwirizano ndi ziŵanda (angelo amene anakhala adyera napandukira Mulungu) ndipo kaŵirikaŵiri amatsogolera ku kumva mawu osafunika ndi kuukiridwa ndi mizimu yoipa imeneyo kwa munthuyo.

Kodi pali chivulazo m’kufunafuna mankhwala kapena chitetezo mwanjira ya kukhulupirira mizimu?

Agal. 5:19-21: “Ntchito zathupi ziwonekera, ndizo dama, chodetsa, kukhumba zonyansa, kupembedza mafano, nyanga . . . zimene ndikuchenjezani nazo, monga ndachita, kuti iwo akuchitachita zotere sadzaloŵa Ufumu wa Mulungu.” (Kutembenukira ku kukhulupirira mizimu kaamba ka chithandizo kumatanthauza kuti munthuyo akukhulupirira mabodza a Satana ponena za imfa; iye akufunafuna uphungu kwa anthu amene amayesayesa kupeza mphamvu kuchokera kwa Satana ndi ziŵanda zake. Motero munthu woteroyo amadzigwirizanitsa ndi awo amene ali adani odziŵika a Yehova Mulungu. Mmalo mwa kuthandizidwadi, yense wa kupitirizabe m’njira yotero amakhala ndi chivulazo chosatha.)

Luka 9:24: “Amene aliyense akafuna kupulumutsa moyo wake [kapena, umoyo], iye adzautaya; koma amene aliyense akataya moyo wake chifukwa cha ine [chifukwa chakuti ali wotsatira wa Yesu Kristu], iye adzaupulumutsa uwu.” (Ngati mwadala munthu aswa malamulo olongosoledwa momvekera bwino a Mawu a Mulungu m’kuyesayesa kutetezera kapena kusunga moyo wake wamakono, adzatayikiridwa ndi chiyembekezo cha moyo wamuyaya. Ha nkupusa kotani nanga!)

2 Akor. 11:14, 15: “Satana yemwe adziwonetsa ngati mngelo wa kuunika. Chifukwa chake sikuli kanthu kwakukulu ngatinso atumiki ake adziwonetsa monga atumiki achilungamo.” (Chotero sitiyenera kusokeretsedwa pamene zina za zinthu zochitidwa mwanjira yolankhula ndi mizimu zingawonekere kukhala zopindulitsa kwakanthaŵi.)

Wonaninso tsamba 166-170, pamutu wakuti “Kuchiritsa.”

Kodi kuli kwanzeru kutembenukira kunjira ya kukhulupirira mizimu kuphunzira chimene mtsogolo muli nacho kapena kudzitsimikizira chipambano m’ntchito ina?

Yes. 8:19: “Pamene iwo adzati kwa iwe, Funa kwa olaula, ndi obwebweta, amene alira pyepye, nang’ungu’udza; kodi anthu sadzafuna kwa Mulungu wawo?”

Lev. 19:31: “Musamatembenukira kwa obwebweta, kapena anyanga; musawafuna; ndi kudetsedwa nawo; ine ndine Yehova Mulungu wanu.”

2 Maf. 21:6: “[Mfumu Manase] nawombeza maula, nachita zanyanga, naika obwebweta ndi openda; anachita zoipa zambiri pamaso pa Yehova kuutsa mkwiyo wake.” (Machitachita okhulupirira mizimu otero anaphatikizadi kutembenukira kwa Satana ndi ziwanda zake kaamba ka chithandizo. Nposadabwitsa kuti zinali “zoipa m’maso mwa Yehova,” ndipo anadzetsa chilango chachikulu pa Manase kaamba ka chochitikacho. Koma pamene analapa nasiya machitachita oipa amenewa, anadalitsidwa ndi Yehova.)

Kodi nchivulazo chotani chimene chingakhalepo m’kuseŵera maseŵero oloŵetsamo mpangidwe wa kuwombedza kapena kufunafuna tanthauzo la kanthu kena kamene kamawonekera kukhala malodza abwino?

Deut. 18:10-12: “Asapezeke mwa inu munthu . . . wosamalira mitambo, kapena wosamalira kulira kwa mbalame, kapena wanyanga. Kapena wotsirika, kapena wobwebweta, kapena wopenduza, kapena wofunsira akufa. Popeza aliyense wa kuchita izi Yehova anyansidwa naye.” (Kuwombeza kumafunafuna kuulula chidziŵitso chobisika kapena kuneneratu zochitika, osati monga chotulukapo cha kufufuza, koma mwa kutanthauzira malodza kapena mwachithandizo cha mphamvu zoposa zaumunthu. Yehova analetsa machitachita otero pakati pa atumiki ake. Chifukwa ninji? Machitachita onsewa amachititsa kulankhula kapena kukhala ndi mizimu yonyansa, kapena ziŵanda. Kuphatikizidwa m’zinthu zotero kukakhala kusakhulupirika kwakukulu kulinga kwa Yehova.)

Mac. 16:16-18: “Namwali wina amene anali ndi mzimu wambwembwe, amene anapindulira ambuye ŵake zambiri pakubwebweta kwake.” (Mwachiwonekere, palibe aliyense wokonda chilungamo amene akanafunsira kumagwero otero a chidziŵitso, kaya ndi cholinga chenicheni kapena monga maseŵera. Paulo atatopa ndi kufuula kwake, ndipo analamula mzimuwo kutuluka mwa iye.)

Kodi mizimu yoipa njokhoza kutenga mpangidwe waumunthu?

M’masiku a Nowa, angelo osamvera anavala thupi la munthu. Kwenikweni iwo anakwatira, ndipo anabala ana. (Gen. 6:1-4) Komabe, pamene Chigumula chinadza, angelo amenewo anakakamizika kubwerera m’chigawo chauzimu. Ponena za iwo, Yuda 6 amati: “Angelonso amene sanasunga chikhalidwe chawo choyamba, komatu anasiya pokhala pawopawo, adawasunga m’ndende zosatha pansi pa mdima, kufikira chiweruziro cha tsiku lalikulu.” Sikokha kuti Mulungu anawatsitsa pamwaŵi wawo woyambirira wakumwamba ndi kuwapereka mu mdima waukulu ponena za zifuno za Yehova, koma mawu akutiwo ndende amasonyeza kuti wawaikira malire. Ku kusachita chiyani? Mwachiwonekere, kusavalanso matupi aumunthu kotero kuti akhale ndi maunansi a kugonana ndi akazi, monga momwe adachitira kale Chigumula chisanakhale. Baibulo limasimba kuti angelo okhulupirika, monga amithenga a Mulungu, anavala matupi pochita ntchito zawo kufikira m’zaka za zana loyamba C.E. Koma pambuyo pa chigumula, angelo amene adagwiritsira ntchito molakwa mphatso zawo anamanidwa mphamvu za kuvala thupi la munthu.

Koma, nkokondweretsa, kuti mwachiwonekere ziŵanda zingathe kuchititsa anthu kuwona masomphenya, ndipo zimene amawona zingawonekere kukhala zenizeni. Pamene Mdyerekezi anayesa Yesu, mwachiwonekere anagwiritsira ntchito njira zimenezo kuti asonyeze Yesu “maufumu onse adziko ndi ulemerero wawo.”—Mat. 4:8.

Kodi ndimotani mmene munthu angakhalire womasuka ku chisonkhezero cha kukhulupirira mizimu?

Miy. 18:10: “Dzina la Yehova ndilo linga lolimba; wolungama athamangiramo napulumuka.” (Izi sizitanthauza kuti kugwiritsira ntchito dzina la Mulungu mwini kumatumikira monga chiŵindo chothamangitsira zoipa. “Dzina” la Yehova limaimira Munthu mwiniyo. Timatetezeredwa pamene tifikira pakumdziŵa ndi kuika chidaliro chathu chonse mwa iye, tikumagonjera kuulamuliro wake ndi kumvera malamulo ake. Ngati tichita izi, pamenepo pamene tipempha chithandizo, tikumagwiritsira ntchito dzina lakelo, amatipatsa chitetezo chimene walonjeza m’Mawu ake.)

Mat. 6:9-13: “Pempherani inu chomwechi: . . . musatitengere kokatiyesa, koma mutipulumutse kwa woipayo.” Muyeneranso ‘kuchita khama m’pemphero.’ (Aroma 12:12) (Mulungu amamva mapemphero otero ochokera kwa amene ali ndi chikhumbo cha kudziŵa chowonadi ndi kumlambira iye mwanjira imene imamkondweretsa.)

1 Akor. 10:21: “Simungathe kumwera chikho cha Ambuye, ndi chikho cha ziŵanda.” (Awo amene amafuna unansi wa Yehova ndi chitetezo chake ayenera kusiya kutenga mbali kulikonse m’misonkhano ya kulankhula ndi mizimu. Mogwirizana ndi chitsanzo cholembedwa pa Machitidwe 19:19, kulinso kofunika kuwononga kapena kutaya bwino lomwe zinthu zonse zimene munthuyo angakhale nazo zogwirizanitsidwa ndi kukhulupirira mizimu.)

Yak. 4:7: “Potero mverani Mulungu; koma kanizani Mdyerekezi, ndipo adzakuthaŵani inu.” (Kuti muchite zimenezi, khalani waphamphu m’kuphunzira chifuniro cha Mulungu ndi kuchigwiritsira ntchito m’moyo wanu. Mwa kukonda Mulungu kukulimbikitsani motsutsana ndi kuwopa munthu, kanani mwamphamvu kutenga mbali m’madzoma alionse ogwirizanitsidwa ndi kulankhula kapena kumvera malangizo alionse oikidwa ndi munthu wokhulupirira mizimu.)

Valani “zida zonse za Mulungu” zolongosoledwa mu Aefeso 6:10-18 ndipo khalani wachangu mwa kusunga mbali zake zonse m’mkhalidwe wabwino.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena