Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w91 7/15 tsamba 4-7
  • Dziko Latsopano Layandikira!

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Dziko Latsopano Layandikira!
  • Nsanja ya Olonda—1991
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Dziko Latsopano Linalonjezedwa
  • Dziko Latsopano Liri Pafupi Kwenikweni!
  • Madalitso Amene Anthu Sakhoza Kuwabweretsa
  • Zosoŵa Zazikulu Zikwaniritsidwa Kotheratu
  • Kodi Inu Mudzakhalako?
  • Kodi Chiwonongeko cha Dziko Chonenedweratucho Chidzadza Liti?
    Mtendere Weniweni ndi Chisungiko—Kodi Mungazipeze Motani?
  • “Mapeto a Dziko” Ayandikira!
    Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi
  • Ufumu wa Mulungu Uyamba Kulamulira Pakati pa Adani Ace
    Coonadi Cimene Cimatsogolera ku Moyo Wamuyaya
  • Kodi Tilidi ‘M’masiku Otsiriza’?
    Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1991
w91 7/15 tsamba 4-7

Dziko Latsopano Layandikira!

NDUNA za boma zanena zochuluka ponena za dongosolo ladziko latsopano lopanga zokha. Zimanena za kuchotsa mantha padziko lapansi ndi zopinga za kugwirizana pakati pa anthu ndi maboma. Koma kodi kuli kwa anthu kudzetsa dziko latsopano?

Anthu akhala ndi zaka mazana ambiri zakukhazikitsa dziko lamtendere ndi chisungiko. Mosakaikira, ambiri akhala owona mtima kwambiri m’zoyesayesa zotero. Komabe, mosasamala kanthu za mpangidwe wa maboma olinganizidwa ndi anthu akukwaniritsira zolinga zoterozo, mawu a Baibulo aŵa atsimikizira kukhala owona: ‘Sikuli kwa munthu woyenda kulongosola mapazi ake.’​—Yeremiya 10:23.

Dziko Latsopano Linalonjezedwa

Chikhalirechobe, Mawu ouziridwa a Mulungu amodzimodziwo amapereka chitsimikiziro chakuti kudzakhala dziko latsopano. Pambuyo poneneratu za mapeto a dongosolo la zinthu lakale, mtumwi Wachikristu Petro analengeza kuti: ‘Monga mwa lonjezano lake tiyembekezera miyamba yatsopano, ndi dziko latsopano m’menemo mukhalitsa chilungamo.’​—2 Petro 3:10-13.

Kodi lonjezo limeneli nlandani? Palibe wina walipereka kusiyapo Yehova, “Wam’mwambamwamba padziko lonse lapansi.” (Salmo 83:18) Iye adzakwaniritsa zimene anthu sangathe. Inde, Yehova Mulungu adzadzetsa dziko latsopano. Koma kodi ndiliti?

Dziko Latsopano Liri Pafupi Kwenikweni!

Dziko latsopano lolonjezedwa la Mulungu lisanakhale lenileni kotheratu, “dziko” lamakonoli, kapena “dongosolo la zinthu,” liyenera kutha. Ponena za ichi, ophunzira a Yesu Kristu anafunsa kuti: “Tiuzeni, kodi zinthu zimenezi zidzakhala liti? ndipo kodi nchiyani chimene chidzakhala chizindikiro cha kudza kwanu, ndi cha mapeto a dziko?” (Mateyu 24:3, King James Version) Monga momwe New World Translation yolondola koposa imanenera, otsatira a Yesu anafunsa kuti: “Tiuzeni, Kodi zinthu zimenezi zidzakhala liti, ndipo kodi nchiyani chimene chidzakhala chizindikiro cha kukhalapo kwanu ndi cha mapeto a dongosolo la zinthu?”

Poyankha, Yesu ananeneratu mbali zambiri za chizindikiro cha kukhalapo kwake kosawoneka monga munthu wauzimu muulamuliro Waufumu wakumwamba. (1 Petro 3:18) Mwachitsanzo, iye anati: ‘Mtundu umodzi wa anthu udzaukirana ndi mtundu wina, ndi ufumu ndi ufumu wina; ndipo kudzakhala njala ndi zivomezi m’malo akutiakuti.’ Chiyambire ‘zoŵaŵa zoyamba’ mu 1914, ‘mbadwo uno’ wolozedwako ndi Yesu wakumana ndi nkhondo zomapitirizabe, njala, ndi zivomezi monga mbali ya chizindikiro cha kukhalapo kwake kosawoneka.​—Mateyu 24:7, 8, 34.

Kuyambira 1914 nkhondo zasakaza mbadwo uno mwa njira yopanda ina yofanana nayo. Nkhondo Yadziko ya I inapha chiŵerengero cha miyoyo pafupifupi mamiliyoni 14. Mkati mwa Nkhondo Yadziko ya II, otenga mbali m’nkhondo ndi anthu wamba mamiliyoni 55 anaphedwa. Eya, chiyambire 1914 miyoyo yoposa mamiliyoni 100 yataika m’nkhondo! Ndithudi, chimenechi chimazindikiritsa mbali ya chizindikiro cha kukhalapo kwa Yesu.

Njala, yonenedweratunso ndi Kristu, inasakaza maiko ambiri pambuyo pa iriyonse ya nkhondo za dziko ziŵirizo. Mosasamala kanthu za kupita patsogolo m’zasayansi, pafupifupi chigawo chimodzi mwa zinayi cha dziko chiri ndi njala lerolino. Chaka chirichonse, ana mamiliyoni ambiri ndi ena amafa chifukwa cha kudya kosakwanira. The World Book Encyclopedia ikuti: “Unyinji wa maiko otukuka kumene mu Afirika, Asia, ndi Latin America ali ndi chakudya chosakwanira kaamba ka anthu awo. Anthu mamiliyoni m’maiko ameneŵa ali ndi njala. Pamene kulima chakudya kapena kugula zinthu kunja kutsika kaamba ka chifukwa chirichonse, pamakhala njala ndipo anthu zikwi zambiri kapena mamiliyoni amafa.”

Zivomezi zawononga miyoyo yambiri mkati mwa mbadwo uno kuzindikiritsa ‘nthaŵi ya chimaliziro.’ (Danieli 12:4) Ziŵerengero zongoyerekezera za minkhole ya zivomezi zimasiyana. Koma chiyambire 1914 kuwononga kochitidwa ndi zivomezi kwawonjezereka padziko lonse lapansi, ndipo zimenezi zapha miyoyo zikwi mazana ambiri. Ikuthirira ndemanga pa ziŵiri zokha za zimenezi, Yorkshire Post ya October 19, 1989, inati: “Mu 1920 chivomezi m’chigawo cha ku China cha Jiangsu chinapha anthu 180,000, ndipo pa July 28, 1976, China anakanthidwa ndi chivomezi chowopsa koposa mu mbiri yake yamakono. Osachepera pa anthu 240,000 anamwalira pamene mzinda wa Tangshan wa kumpoto koma chakum’maŵa unasalazidwa pafupifupi kotheratu ndi chivomezi chimene chinapimidwa pa 7.8 pa chipangizo chopimira cha Richter chosalimba kwenikweni.” Nyuzipepalayo inandandalitsa zivomezi zina zazikulu zoposa 30 m’zaka za zana la 20.

Ntchito yolengeza ufumu inanenedweratunso monga mbali ina ya chizindikiro cha kukhalapo kwa Yesu kosawoneka. Iye anauza ophunzira ake ofunsawo kuti: “Ndipo mbiri yabwino imeneyi ya ufumu idzalalikidwa m’dziko lonse lapansi lokhalidwa ndi anthu kaamba ka umboni kwa mitundu yonse; ndipo pomwepo mapeto adzafika.” (Mateyu 24:14, NW) Mongadi momwe Yesu analoserera, ntchito yolalikira imeneyi tsopano ikuchitidwa padziko lonse lapansi m’maiko 212 ndi Mboni za Yehova zoposa 4,000,000.

Kukwaniritsidwa kwamakono kwa maulosi ameneŵa ndi ena kumatsimikizira kuti tikukhaladi mu “masiku otsiriza.” (2 Timoteo 3:1-5) ‘Chisautso chachikulu’ chonenedweratunso ndi Yesu Kristu chiri patsogolo pathupa. Chidzafika pachimake pa ‘nkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu, Wamphamvuyonse’ pa Armagedo, ndi kudzetsa mapeto pa dongosolo la zinthu loipali. (Mateyu 24:21; Chibvumbulutso 16:14-16) Pamenepo dziko latsopano lolonjezedwa la Mulungu lidzakhala lenileni.a

Madalitso Amene Anthu Sakhoza Kuwabweretsa

Nduna za boma zimadzitama ponena za dongosolo ladziko latsopano lopanga zokha. Koma Yehova, Mulungu wa kumwamba ndi dziko lapansi, sanaŵapemphe anthu ndikalelonse kuloŵetsa m’malo dongosolo liripoli ndi dziko latsopano. Iye mwini adzachita chimenecho patsiku ndi nthaŵi yodziŵika kwa iye yekha. (Mateyu 24:34, 36) Mtumwi Yohane wokalambayo anawoneratu zimene Mulungu, osati munthu, adzachita:

‘Ndipo ndinawona m’mwamba mwatsopano ndi dziko latsopano; pakuti m’mwamba moyamba ndi dziko loyamba zidachoka, ndipo kulibenso nyanja. Ndipo ndinawona mzinda woyerawo, Yerusalemu watsopano, ulikutsika Kumwamba kwa Mulungu, wokonzeka ngati mkwatibwi wokometsedwera mwamuna wake. Ndipo ndinamva mawu aakulu ochokera ku mpando wachifumu, ndi kunena Tawonani, chihema cha Mulungu chiri mwa anthu; ndipo adzakhalitsa nawo, ndi iwo adzakhala anthu ake, ndi Mulungu yekha adzakhala nawo, Mulungu wawo; ndipo adzaŵapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pawo; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena chowawitsa; zoyambazo zapita. Ndipo iye wakukhala pa mpando wachifumu anati, Tawonani, ndichita zonse zikhale zatsopano. Ndipo ananena, Talemba; pakuti mawu aŵa ali okhulupirika ndi owona.’​—Chibvumbulutso 21:1-5.

“M’mwamba mwatsopano” ndiwo Ufumu wakumwamba wa Yesu Kristu. “Dziko latsopano” siliri mbulunga ina yadziko koma chitaganya chatsopano cha anthu pa pulaneti lino​—onsewo ndi nzika zomvera za Ufumu wa Kristu, zopanda magaŵano aufuko, autundu, kapena achinenero. (Yerekezerani ndi Salmo 96:1.) M’mwamba ndi dziko zamakono zophiphiritsira​—dongosolo la zinthu la Mdyerekezi lokhala ndi mpangidwe wa maboma osonkhezeredwa ndi Satana ndi ziŵanda zake​—zidzawonongedwa. (1 Yohane 5:19) Ngakhale kuti nyanja zenizeni zidzatsala, nyanja yophiphiritsiridwa ya anthu oipa osakhazikika, idzapita. Olamulira anzake a Yesu akumwamba amapanga Yerusalemu Watsopano ndipo mogwirizana naye amapanga malikulu, gulu limene lidzalamulira chitaganya cholungama cha anthu. Mulungu ‘adzakhala nawo’ anthu omvera moimiriridwa pamene iwo akugwirizanitsidwa naye mokwanira kupyolera mwa Kristu mkati mwa Tsiku Lachiweruzo la zaka chikwi.​—Chibvumbulutso 14:1-4; 20:6.

Pansi pa ulamuliro Waufumu padzakhala zifukwa zambiri zokhalira achimwemwe. Maliro, kulira, ndi zowawitsa zochititsidwa ndi matenda, chisoni, ndi zina zofanana nazo zidzakhala zinthu zakale. Ngakhale imfa imene inafalikira kwa anthu kuchokera kwa kholo lathu loyambirira, Adamu wochimwa, sidzakhalakonso. (Aroma 5:12) Nchimwemwe chotani nanga chimene chidzakhalako pamene chodzetsa misozi cha padziko lonse chimenechi sichidzakhalako kosatha!

Osati anthu okhoza kufa koma Mulungu iyemwini amapereka chitsimikizo ponena za madalitso ameneŵa. Iye Ndiye amati: ‘Tawonani, ndichita zonse zikhale zatsopano.’ Inde, ndipo Yehova Mulungu anauza mtumwi Yohane kuti: ‘Talemba; pakuti mawu aŵa ali okhulupirika ndi owona.’

Zosoŵa Zazikulu Zikwaniritsidwa Kotheratu

M’dziko latsopano lopangidwa ndi Mulungu, dziko lapansi lidzakhala paradaiso kotheratu. Ichi nchotsimikizirika, popeza kuti Yesu analonjeza wochita zoipa wolapa wopachikidwa pambali pake kuti: ‘Indetu ndinena ndi iwe lerolino, udzakhala ndine m’Paradaiso.’ (Luka 23:43) Pakati pa mikhalidwe yaparadaiso, zosoŵa za anthu zonga ngati chakudya ndi nyumba zidzasamaliridwa.

Njala imapha miyoyo mamiliyoni ambiri lerolino. Mosasamala kanthu za mmene zoyesayesa zakudyetsa anjala zingakhalire zowona mtima, umbombo ndi zinthu zina zimalepheretsa anthu kuthetsa mavuto oterowo. Mwachitsanzo, nyuzipepala ya Saturday Star ya ku Johannesburg, mu South Africa, ikusimba kuti: “Mikangano ya ndale zadziko, mitengo yokwera ya mafuta ndi kunyonyotsoka kwachisawawa pamodzi ndi kulimbana kwa mu Afirika kosayembekezeredwa kutha zikugwirizana kuchedwetsa chithandizo . . . Mu Sudan, limodzi la maiko okanthidwa moipitsitsa ndi njala, anthu pakati pa 5 ndi 6 miliyoni ali ndi njala mu 1991.” Koma njala idzaiŵalika m’dziko latsopano la Mulungu. Pansi pa ulamuliro Waufumu ‘m’dziko mudzakhala dzinthu zochuluka pamwamba pa mapiri.’​—Salmo 72:16.

Nyumba ndichosoŵa china cha anthu chimene sichikhoza kupezedwa mokwanira ndi anthu ambiri m’tsiku lathu. Mamiliyoni ambiri amakhala m’timisasa kapena alibiretu nyumba. Mogwirizana ndi The New York Times, m’dziko lina la Kum’maŵa, “pa kampani ina ya zamagetsi . . . , olembedwa ntchito a zaka 20 zakubadwa amakhala pa ndandanda ya zaka 73 yakuyembekezera kupatsidwa nyumba,” ndipo lipoti la boma limasonyeza kuti anthu ena amakhala “m’nyumba zosungira zinthu, maofesi kapena ngakhale m’zimbudzi.” Koma kudzakhala kosiyana chotani nanga m’dziko latsopano! Mu Paradaiso wamtsogolo, ‘iwo adzamanga nyumba ndi kukhalamo; ndipo iwo adzawoka minda yampesa, ndi kudya zipatso zake. Iwo sadzamanga, ndi wina kukhalamo; iwo sadzawoka, ndi wina kudya; pakuti monga masiku a mtengo adzakhala masiku a anthu anga; ndi osankhidwa anga adzasangalala nthaŵi zambiri ndi ntchito za manja awo.’​—Yesaya 65:21, 22.

Mavuto a nthaka ndi zachilengedwe adzazimiririka m’dziko latsopano lolonjezedwa la Mulungu. Kuipitsa mpweya kowopseza thanzi ndi kowononga zomera sikudzakhalakonso. Kuipitsa ndi kuwononga malo okhala tsopano kododometsa mitundu yambiri ya zomera ndi ya zinyama sikudzakhalanso chiwopsezo panthaŵiyo. Ndipo zinthu zonga ngati kuwononga chifunda thambo sizidzaika paupandu moyo padziko lapansi. Tikhoza kukhala otsimikiza kuti Yehova Mulungu adzathetsa mavuto onse ameneŵa, popeza kuti Mawu ake amatitsimikiziritsa kuti posachedwapa iye ‘adzawononga iwo akuwononga dziko.’​—Chibvumbulutso 11:18.

M’dziko latsopano, nkhondo idzakhalanso chinthu chakale koma osati chifukwa chakuti nduna za boma zapambana m’kutulitsa pansi zida mitundu yonse. Mmalomwake, Mulungu adzachita zimene olamulira andale zadziko alephera. Iye adzabweretsa mtendere pa anthu omvera akukwaniritsa mawu aŵa a wamasalmo: ‘Idzani, penyani ntchito za Yehova, amene achita [zozizwitsa, NW] padziko lapansi. Aletsa nkhondo kumalekezero adziko lapansi; athyola uta, nadula nthungo; atentha magareta ndi moto.’ (Salmo 46:8, 9) M’dziko latsopano la Mulungu lolonjezedwa loyandikiralo, anthu sadzachitanso nkhondo koma adzasangalala ndi mtendere weniweni ndi chisungiko.​—Mika 4:2-4.

Kodi Inu Mudzakhalako?

Mukhoza kukhala ndi chidaliro m’dziko latsopano lolonjezedwa ndi Yehova Mulungu. Iye samanama. (Ahebri 6:17, 18) Mawu ake, Baibulo, ali owona, ndipo zimene amalonjeza nthaŵi zonse zimakwaniritsidwa.​—Yohane 17:17.

Mbiri yabwino ya madalitso odabwitsa kaamba ka anthu omvera ndiimene Mboni za Yehova zimayesayesa kugaŵana ndi anthu owona mtima. Inu tsopano muyenera kuyesayesa kupeza chidziŵitso cha chifuno chaumulungu, ndi kuchitapo kanthu pa malonjezo opezeka m’Malemba Opatulika. Njira imeneyi ikhoza kutsogolera ku moyo wosatha, pakuti Yesu anati: ‘Koma moyo wosatha ndi uwu, kuti akadziŵe inu Mulungu wowona yekha, ndi Yesu Kristu amene munamtuma.’ (Yohane 17:3) Ndiyeno mudzakhala ndi mwaŵi wa kusangalala ndi nthaŵi zachimwemwe patsogolopa, popeza kuti dziko latsopano la Mulungu layandikira!

[Mawu a M’munsi]

a Onani mitu 17 ndi 18 m’bukhu la Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi, lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena