Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • re mutu 16 tsamba 89-99
  • Anthu Anayi Okwera Mahatchi Ali pa Liwiro

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Anthu Anayi Okwera Mahatchi Ali pa Liwiro
  • Mapeto Osangalatsa a Masomphenya a M’buku la Chivumbulutso
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Hatchi Yoyera ndi Wokwerapo Wake Waulemerero
  • Anapita Kukagonjetsa Adani Ake
  • Taonani Hatchi Yofiira Ngati Moto
  • Hatchi Yakuda Inatulukira
  • Hatchi Yotuwa ndi Wokwerapo Wake
  • Kodi Anthu 4 Okwera Pamahatchi Akuimira Chiyani?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2017
  • Kodi Ndani Amachititsa Nkhondo Komanso Mavuto Ena Padzikoli?
    Nsanja ya Olonda—2014
  • Zimene Zili Mʼbuku la Chivumbulutso
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
  • Kodi Ulosi wa Anthu 4 Okwera Pamahatchi Umakukhudzani Bwanji Inuyo?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2017
Onani Zambiri
Mapeto Osangalatsa a Masomphenya a M’buku la Chivumbulutso
re mutu 16 tsamba 89-99

Mutu 16

Anthu Anayi Okwera Mahatchi Ali pa Liwiro

Masomphenya 3—Chivumbulutso 6:1-17

Nkhani yake: Mahatchi anayi ndi okwerapo ake, mboni zimene zinaphedwa zikuoneka zili pansi pa guwa lansembe, ndiponso tsiku lalikulu la mkwiyo

Nthawi ya kukwaniritsidwa kwake: Kuyambira mu 1914 mpaka kuwonongedwa kwa dziko loipali

1. Kodi Yehova anaululira bwanji Yohane zimene zinali mumpukutu wochititsa chidwi umene Yesu anatsegula?

M’MASIKU a mavuto ano, n’zosachita kufunsa kuti tikufunitsitsa kudziwa “zinthu zimene ziyenera kuchitika posachedwapa,” chifukwa chakuti zikutikhudza kwambiri. Choncho tiyeni tionere limodzi ndi Yohane pamene Yesu akutsegula mpukutu wochititsa chidwiwo. N’zochititsa chidwi kuti Yohane sakufunikira kuwerenga mpukutuwo. Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti iye anaonetsedwa zinthu zimene zinali mumpukutuwo pogwiritsira ntchito “zizindikiro,” m’masomphenya osiyanasiyana ochititsa chidwi kwambiri.—Chivumbulutso 1:1, 10.

2. (a) Kodi Yohane anaona ndi kumva chiyani, ndipo maonekedwe a kerubi anachititsa Yohane kuganizira mfundo yotani? (b) Kodi kerubi woyamba ankaitana ndani, ndipo n’chifukwa chiyani mukuyankha choncho?

2 Tamvani zimene Yohane anaona ndi kumva pamene Yesu ankamatula chidindo choyamba chomatira mpukutuwo. Iye anati: “Ndinaona Mwanawankhosa atamatula chidindo chimodzi mwa zidindo 7 zija, ndipo ndinamva chamoyo chimodzi mwa zamoyo zinayi zija chikulankhula ndi mawu ngati kugunda kwa bingu kuti: ‘Bwera!’” (Chivumbulutso 6:1) Amenewa ndi mawu a kerubi woyamba. Maonekedwe a kerubiyo okhala ngati mkango anachititsa Yohane kuganizira mfundo yakuti gulu la Yehova lidzachita zinthu molimba mtima popereka chiweruzo chake cholungama. Kodi pamene kerubiyo ananena kuti “Bwera!” ankaitana ndani? Sankaitana Yohane, chifukwa chakuti iye anali ataitanidwa kale kuti adzaone zochitika zaulosizi. (Chivumbulutso 4:1) Choncho mawu omveka “ngati kugunda kwa bingu” amenewa ankaitana ena oti adzachite nawo zinthu zina m’chigawo choyamba cha masomphenya ochititsa chidwi a zigawo zinayi.

Hatchi Yoyera ndi Wokwerapo Wake Waulemerero

3. (a) Kodi kenako Yohane anafotokoza chiyani? (b) Mogwirizana ndi mmene Baibulo limafotokozera zinthu mophiphiritsira, kodi hatchi yoyera ija iyenera kuti imaimira chiyani?

3 Yohane pamodzi ndi Akhristu odzozedwa akhama komanso anzawo masiku ano, ali ndi mwayi woona zinthu zimene zikuchitika mofulumira kwambiri. Yohane anati: “Nditayang’ana, ndinaona hatchi yoyera. Wokwerapo wake ananyamula uta. Iye anapatsidwa chisoti chachifumu, ndi kupita kukagonjetsa adani ake ndipo anapambana pa nkhondo yolimbana nawo.” (Chivumbulutso 6:2) Patamveka mawu omveka ngati bingu akuti “Bwera!” panatulukira hatchi yoyera ili pa liwiro. M’Baibulo, kawirikawiri hatchi imaimira nkhondo. (Salimo 20:7; Miyambo 21:31; Yesaya 31:1) Hatchi yokongola imeneyi, yomwe mwina inali yamphongo, inali yoyera kwambiri ndipo zimenezi zinkaimira kuti inali yosadetsedwa. (Yerekezerani ndi Chivumbulutso 1:14; 4:4; 7:9; 20:11.) Zimenezi n’zoyenera, chifukwa zikuimira nkhondo yoyera komanso yolungama pamaso pa Yehova, yemwe ndi woyera.—Onaninso Chivumbulutso 19:11, 14.

4. Kodi Wokwera pahatchi yoyera ndani? Fotokozani.

4 Kodi Wokwera pahatchi imeneyi ndani? Iye anali ndi uta, womwe ndi chida chomenyera nkhondo, komanso anapatsidwa chisoti chachifumu. Anthu olungama okhawo amene Yohane anawaona atavala zisoti zachifumu m’tsiku la Ambuye ndi Yesu komanso gulu limene likuimiridwa ndi akulu 24. (Danieli 7:13, 14, 27; Luka 1:31-33; Chivumbulutso 4:4, 10; 14:14)a N’zokayikitsa kuti mmodzi wa m’gulu la akulu 24 amenewo angasonyezedwe akulandira yekha chisoti chachifumu. Choncho wokwera pahatchi ameneyu ayenera kuti si winanso ayi koma ndi Yesu Khristu. Apa Yohane anaona m’masomphenya Yesu ali kumwamba mu 1914, pa nthawi yosaiwalika imene Yehova ananena kuti, “Inetu ndakhazika mfumu yanga,” ndi kumuuza Yesu kuti wachita zimenezi kuti ‘amupatse mitundu ya anthu kukhala cholowa chake.’ (Salimo 2:6-8)b Choncho pomatula chidindo choyambacho Yesu anasonyeza mmene iye, monga Mfumu yongoikidwa kumene, adzapitire kukamenya nkhondo pa nthawi yoikidwa ndi Mulungu.

5. Kodi wamasalimo anamufotokoza bwanji Wokwera pahatchi mofanana ndi mmene lemba la Chivumbulutso 6:2 limamufotokozera?

5 Mbali imeneyi ya masomphenyawa ikugwirizana bwino kwambiri ndi lemba la Salimo 45:4-7. Musalimo limeneli, Yehova akulankhula ndi Mfumu yomwe anaiika pampando, kuti: “Ndipo upambane mu ulemerero wako. Kwera pahatchi yako chifukwa cha choonadi, kudzichepetsa ndi chilungamo, ndipo dzanja lako lamanja lidzakulangiza mu zinthu zochititsa mantha. Mivi yako yakuthwa idzalasa mitima ya adani a mfumu, mitundu ya anthu idzagwa pamapazi ako. Mulungu ndiye mpando wako wachifumu mpaka kalekale, ndithu mpaka muyaya. Ndodo yako yachifumu ndiyo ndodo yachilungamo. Umakonda chilungamo ndipo umadana ndi zoipa. N’chifukwa chake Mulungu, Mulungu wako, wakudzoza ndi mafuta achikondwerero chachikulu kuposa cha mafumu ena.” Popeza Yohane ankadziwa bwino mawu aulosi amenewa, iye ayenera kuti anadziwa kuti masomphenya amenewa ankafotokoza za ntchito imene Yesu adzagwire monga Mfumu.—Yerekezerani ndi Aheberi 1:1, 2, 8, 9.

Anapita Kukagonjetsa Adani Ake

6. (a) N’chifukwa chiyani Wokwera pahatchi akuyenera kupita kukagonjetsa adani ake? (b) Kodi Wokwera pahatchiyo wapitirizabe kugonjetsa mpaka kufika nthawi iti?

6 Koma n’chifukwa chiyani zinali zoyenera kuti Mfumu yongoikidwa kumeneyo ipite kukamenya nkhondo pahatchi? N’chifukwa chakuti ufumu wake unakhazikitsidwa pa nthawi imene Satana Mdyerekezi, yemwe ndi mdani wamkulu wa Yehova, ankatsutsana kwambiri ndi Mulungu. Iye ankachita zimenezi mogwirizana ndi anthu ena padziko lapansi, amene modziwa kapena mosadziwa, amachita zofuna za Satanayo. Ndipo kubadwa kwa Ufumuwu kunachititsa kuti kumwamba kumenyedwe nkhondo yoopsa kwambiri. Pa nkhondoyi, Yesu ankadziwika ndi dzina lakuti Mikayeli (kutanthauza “Ndani Angafanane ndi Mulungu?”), ndipo iye anagonjetsa Satana ndi ziwanda zake n’kuwaponya padziko lapansi. (Chivumbulutso 12:7-12) Yesu, yemwe wakwera pahatchi, wakhala akugonjetsa adani ake chiyambire tsiku la Ambuye mpaka pano, pamene anthu ofanana ndi nkhosa akusonkhanitsidwa. Ngakhale kuti dziko lonse lidakali “m’manja mwa woipayo,” Yesu akupitiriza kuweta mwachikondi abale ake odzozedwa komanso anzawo, ndipo akuthandiza aliyense wa iwo kuti apambane pa nkhondo yachikhulupiriro chawo.—1 Yohane 5:19.

7. Kodi Yesu wagonjetsa bwanji adani ake padziko lapansi m’zaka zoposa 90 zoyambirira za m’tsiku la Ambuye, ndipo ifeyo tiyenera kukhala ofunitsitsa kuchita chiyani?

7 Kodi Yesu wagonjetsa adani ake m’njira zinanso ziti pa zaka zoposa 90 zoyambirira za m’tsiku la Ambuye? Padziko lonse, anthu a Yehova, monga mpingo kapena munthu aliyense payekha, akumana ndi mavuto, masautso komanso mazunzo ambiri ofanana ndi amene mtumwi Paulo anafotokoza popereka umboni wotsimikizira kuti iye anali mtumiki wa Mulungu. (2 Akorinto 11:23-28) Mboni za Yehova zimafunikira “mphamvu yoposa yachibadwa” kuti zipirire, makamaka m’malo amene kukuchitika nkhondo ndi ziwawa. (2 Akorinto 4:7) Komabe, ngakhale m’nthawi zovuta kwambiri, Mboni zokhulupirika zatha kunena mawu ofanana ndi amene Paulo ananena, akuti: “Ambuye anaima pafupi ndi ine ndi kundipatsa mphamvu, kuti kudzera mwa ine, ntchito yolalikira ichitidwe mokwanira.” (2 Timoteyo 4:17) Inde, Yesu anawagonjetsera adani awo. Ifenso tikakhala ndi mtima wofunitsitsa kupambana pa nkhondo ya chikhulupiriro chathu, Yesu adzapitiriza kutigonjetsera adani athu.—1 Yohane 5:4.

8, 9. (a) Kodi mpingo wa Mboni za Yehova wapadziko lonse wapambana pa nkhondo ziti? (b) Kodi Mboni za Yehova zawonjezeka mochititsa chidwi m’mayiko ati?

8 Mpingo wapadziko lonse wa Mboni za Yehova wapambana pa nkhondo zosiyanasiyana motsogoleredwa ndi Mfumu yawo yopambana pa nkhondo. Iye anateteza mwapadera kwambiri Ophunzira Baibulo kuti asafafanizidwe mu 1918, pamene ‘anagonjetsedwa’ kwakanthawi ndi gulu landale la Satana. Chotero mu 1919, anawapulumutsa powatulutsa m’ndende ndipo kenako anawapatsanso mphamvu kuti apitirize kulengeza uthenga wabwino “mpaka kumalekezero a dziko lapansi.”—Chivumbulutso 13:7; Machitidwe 1:8.

9 Nkhondo yachiwiri ya padziko lonse isanayambe komanso itatha, maboma amene ankapondereza anthu anayesetsa kuti afafanize Mboni za Yehova. Izi zinkachitika m’mayiko ambiri mmene atsogoleri achipembedzo, makamaka a Katolika, ankathandizira kwambiri olamulira oponderezawo modzionetsera kapena mwakabisira. Pamene nkhondo yachiwiri ya padziko lonse inkayamba mu 1939, Mboni zimene zinkalalikira zinali zokwana 71,509, koma pofika kumapeto kwa nkhondoyi mu 1945 chiwerengerochi chinawonjezeka kufika pa 141,606. Izi zinachitika ngakhale kuti Mboni zoposa 10,000 zinakhala m’ndende zozunzirako anthu ndi m’ndende zina kwa zaka zambiri ndipo zina pafupifupi 2,000 zinaphedwa. Chiwerengero cha Mboni zimene zikulalikira mwakhama padziko lonse chawonjezeka ndipo masiku ano chaposa 7 miliyoni. Mboni zawonjezeka kwambiri makamaka m’mayiko achikatolika komanso m’mayiko amene Mboni za Yehova zinkazunzidwa kwambiri monga ku Germany, Italy ndi Japan. Panopa m’mayiko amenewa muli Mboni zimene zikulalikira mwakhama zoposa 620,000.—Yesaya 54:17; Yeremiya 1:17-19.

10. Kodi Mfumu yopambana pa nkhondo yathandiza bwanji anthu ake “kuteteza uthenga wabwino ndi kukhazikitsa mwalamulo ntchito ya uthenga wabwino”?

10 Mfumu yathu yopambana pa nkhondo yadalitsanso anthu ake akhama potumikira Mulungu, powatsogolera pa nkhondo zambiri zimene anapambana, zofuna “kuteteza uthenga wabwino ndi kukhazikitsa mwalamulo ntchito ya uthenga wabwino” m’makhoti komanso pamaso pa olamulira. (Afilipi 1:7; Mateyu 10:18; 24:9) Zimenezi zachitika m’mayiko osiyanasiyana monga ku Australia, Argentina, Canada, Greece, India, Swaziland, Switzerland, Turkey, ndi m’mayiko ena. Ina mwa milandu 50 imene Mboni za Yehova zinapambana m’Khoti Lalikulu Kwambiri ku United States inali yozipatsa ufulu wolalikira uthenga wabwino “poyera komanso kunyumba ndi nyumba” ndiponso ufulu woti zisamachite nawo miyambo yosonyeza kukonda kwambiri dziko lawo, komwe ndi kulambira mafano. (Machitidwe 5:42; 20:20; 1 Akorinto 10:14) Choncho khomo la mwayi wofutukulira ntchito yolalikira padziko lonse lakhalabe lotseguka.

11. (a) Kodi Wokwera pahatchi ‘adzapambana bwanji pa nkhondo yolimbana ndi adani ake’? (b) Kodi kumatulidwa kwa chidindo chachiwiri, chachitatu ndi chachinayi kuyenera kutikhudza bwanji?

11 Kodi Yesu ‘adzapambana bwanji pa nkhondo yolimbana ndi adani ake’?c Kutsogoloku tiona kuti iye adzachita zimenezi pothetsa chipembedzo chonyenga ndipo kenako adzaponya mbali iliyonse yotsala ya gulu la Satana looneka ndi maso “m’nyanja ya moto” yophiphiritsira ya chiwonongeko. Iye adzachita zonsezi posonyeza kuti Yehova ndiye woyenera kulamulira. Molimba mtima, tikuyembekezera tsiku limeneli pa Aramagedo pamene “Mfumu ya mafumu” idzagonjetse komaliza gulu la Satana landale limene likupondereza anthu. (Chivumbulutso 16:16; 17:14; 19:2, 14-21; Ezekieli 25:17) Koma padakali pano, Wopambana pa nkhondo wosagonjetseka ameneyu, yemwe wakwera pahatchi yoyera, adakali pa liwiro pamene Yehova akupitiriza kubweretsa anthu oona mtima mumtundu wake wolungama padziko lapansi. (Yesaya 26:2; 60:22) Kodi inuyo mukuthandizana ndi Akhristu odzozedwa pogwira ntchito yosangalatsa yomwe ikuthandiza anthu ambiri kudziwa za Ufumu? Ngati mukugwira nawo, ndiye kuti zimene mtumwi Yohane anaona pamene zidindo zitatu zotsatira zinamatulidwa zikulimbikitsani kuti muwonjezere zimene mukuchita pa ntchito ya Yehova masiku ano.

Taonani Hatchi Yofiira Ngati Moto

12. Kodi Yesu ananena kuti n’chiyani chimene chidzakhale chizindikiro cha kukhalapo kwake kosaoneka monga Mfumu?

12 Chakumapeto kwa utumiki wa Yesu padziko lapansi, ophunzira ake anamufunsa payekha kuti: “Kodi . . . chizindikiro cha kukhalapo kwanu ndi cha mapeto a nthawi ino chidzakhala chiyani?” Poyankha, iye ananeneratu za masoka amene adzakhale “chiyambi cha masautso, ngati mmene zimayambira zowawa za pobereka.” Yesu anati: “Mtundu udzaukirana ndi mtundu wina, ndipo ufumu udzaukirana ndi ufumu wina. Kudzachitika zivomezi zamphamvu, ndipo kudzakhala miliri ndi njala m’malo osiyanasiyana. Kudzaoneka zoopsa ndipo kumwamba kudzaoneka zizindikiro zodabwitsa.” (Mateyu 24:3, 7, 8; Luka 21:10, 11) Zinthu zimene Yohane anaona pamene zidindo zotsatira za mpukutuwo zinamatulidwa zikufanana kwambiri ndi ulosi umenewu. Taonani zimene Yohane anaona pamene Yesu, amene ali mu ulemerero wake, anamatula chidindo chachiwiri.

13. Kodi Yohane anali atatsala pang’ono kuona kusiyana kotani pa kagwiritsidwe ntchito ka mphamvu?

13 “Atamatula chidindo chachiwiri, ndinamva chamoyo chachiwiri chikunena kuti: ‘Bwera!’” (Chivumbulutso 6:3) Kerubi wachiwiri, wooneka ngati ng’ombe yamphongo ndi amene ananena mawu akuti “Bwera!” Maonekedwe a kerubiwa akuimira mphamvu za Mulungu, zimene amazigwiritsira ntchito molungama. Mosiyana ndi zimenezi, Yohane anali atatsala pang’ono kuona mmene mphamvu zikugwiritsidwira ntchito mwankhanza pozunza ndi kupha anthu.

14. Kodi kenako Yohane anaona hatchi ndi wokwerapo wake zotani, ndipo masomphenya amenewa akuimira chiyani?

14 Kodi mawu achiwiri oitana kuti “Bwera!” atamveka, chinachitika n’chiyani? Yohane ananena kuti: “Pamenepo, hatchi ina inatulukira. Imeneyi inali yofiira ngati moto. Wokwerapo wake analoledwa kuchotsa mtendere padziko lapansi, kuti anthu aphane. Iye anapatsidwanso lupanga lalikulu.” (Chivumbulutso 6:4) Amenewa ndi masomphenya oipa kwabasi, chifukwa mosakayikira akuimira nkhondo. Imeneyi si nkhondo yolungama ya Mfumu ya Yehova yopambana pa nkhondo, koma ndi nkhondo za anthu za padziko lonse, zomwe ndi zankhanza komanso zimapha ndi kuzunza anthu osalakwa. M’pake kuti munthu ameneyu wakwera pahatchi yofiira ngati moto.

15. N’chifukwa chiyani sitingafune kugwirizana ndi wokwera pahatchi wachiwiri?

15 N’zoonekeratu kuti Yohane sakanafuna kugwirizana ndi wokwera pahatchi ameneyu kapena kugwirizana ndi zochita zake chifukwa ulosi unaneneratu za anthu a Mulungu kuti: “Anthuwo sadzaphunziranso nkhondo.” (Yesaya 2:4) Mofanana ndi Yohane, Akhristu odzozedwa amene “adakali m’dzikoli” komanso a khamu lalikulu masiku ano “sali mbali” ya dzikoli, limene lakhetsa magazi a anthu ambiri. Zida zathu si zophera anthu pa nkhondo, koma ndi zauzimu ndipo ndi “zamphamvu zimene Mulungu watipatsa” kuti tithe kulengeza choonadi mwakhama.—Yohane 17:11, 14; 2 Akorinto 10:3, 4.

16. Kodi wokwera pahatchi yofiira anapatsidwa liti “lupanga lalikulu” ndipo waligwiritsira ntchito bwanji?

16 Chaka cha 1914 chisanafike, pamene Wokwera pahatchi yoyera anapatsidwa chisoti chachifumu, panachitika nkhondo zambiri. Koma tsopano wokwera pahatchi yofiira anapatsidwa “lupanga lalikulu.” Kodi zimenezi zikutanthauza chiyani? Kungoyambira ndi nkhondo yoyamba ya padziko lonse, nkhondo za anthu zinayamba kukhala zoopsa komanso zowononga kwambiri kuposa kale. Pa nthawi ya nkhondo yoyamba yapadziko lonse (1914-1918), yomwe inapha anthu ambiri, akasinja, mpweya wapoizoni, ndege zankhondo, sitima zankhondo za m’madzi, mfuti zikuluzikulu zoponyera mizinga ndiponso zida zina zongotchera zinagwiritsidwa ntchito kwa nthawi yoyamba kapena zinagwiritsidwa ntchito kwambiri kuposa kale. M’mayiko ena 28, anthu onse m’dzikomo osati asilikali okha, anakakamizidwa kumenya nkhondo, ndipo anthu ankhaninkhani anaphedwa. Pamene nkhondoyi imafika kumapeto, asilikali oposa 9 miliyoni ndiponso anthu wamba osawerengeka anali ataphedwa. Ngakhale nkhondoyi itatha, padziko lapansi sipanakhalenso mtendere weniweni. Patapita zaka zoposa 50 chichitikireni nkhondo imeneyi, wandale wina wotchuka wa ku Germany, dzina lake Konrad Adenauer, ananena kuti: “Anthu sakukhalanso mwa bata ndi mtendere kuyambira mu 1914.” Apa zikuonekeratu kuti wokwera pahatchi yofiira ngati moto uja analoledwadi kuchotsa mtendere padziko lapansi.

17. Kodi wokwera pahatchi yofiira wapitiriza bwanji kugwiritsa ntchito “lupanga lalikulu” pambuyo pa nkhondo yoyamba ya padziko lonse?

17 Kenako pofuna kupitiriza kukhetsa magazi ambiri, wokwera pahatchi yofiira uja anayambitsa nkhondo yachiwiri ya padziko lonse. Anthu anayamba kugwiritsa ntchito zida zoopsa kwambiri ndipo ophedwa pa nkhondo imeneyi anachuluka kwambiri kuwirikiza kanayi poyerekezera ndi anthu amene anafa pa nkhondo yoyamba ya padziko lonse. Mu 1945 mabomba awiri oopsa kwambiri anaphulitsidwa m’dziko la Japan, ndipo bomba lililonse linapha anthu masauzande ambirimbiri m’kanthawi kochepa chabe. Pa nkhondo yachiwiri yapadziko lonse, wokwera pahatchi yofiirayu anapha anthu pafupifupi 55 miliyoni, ndipo ngakhale anachita zimenezi iye sanakhutirebe. Pali umboni wodalirika wosonyeza kuti anthu oposa 20 miliyoni aphedwa ndi “lupanga lalikulu” chichitikireni nkhondo yachiwiri ya padziko lonse.

18, 19. (a) Kodi kuphedwa kwa anthu ambirimbiri pambuyo pa nkhondo yachiwiri ya padziko lonse ndi umboni wa chiyani? (b) Kodi anthu ali pa ngozi yotani, ndipo Wokwera pahatchi yoyera adzachita chiyani polepheretsa zimenezo?

18 Kodi zimenezi zikusonyeza kuti luso lopanga zida zankhondo n’lothandiza? Ayi, koma umenewu ndi umboni wosonyeza kuti hatchi yofiira yopanda chifundoyo ili pa liwiro. Kodi liwiro limeneli likathera kuti? Akatswiri ena asayansi amanena kuti nkhondo yoopsa ya zida zanyukiliya ingathe kuyamba mwangozi, komanso amanena kuti n’zotheka kuti iyambe mochita kukonzekera. Koma n’zosangalatsa kuti Wokwera pahatchi yoyera, yemwe ndi wopambana pa nkhondo, ali ndi maganizo ena pa nkhani imeneyi.

19 Anthu akapitiriza kukonda kwambiri dziko lawo komanso kudana, apitirizanso kukhala mwamantha poopa kuti nkhondo ya zida zanyukiliya ikhoza kuyambika nthawi ina iliyonse. Ngakhale mayiko atawononga zida zawo zonse zanyukiliya pofuna kupewa nkhondo yoopsa, iwo adzakhalabe akudziwa njira yopangira zidazo. M’nthawi yochepa, iwo angathe kupanganso zida zina zoopsa zanyukiliya. Choncho nkhondo iliyonse ya zida wamba ingakule kwambiri n’kukhala ya zida zanyukiliya. Anthu a m’mayiko onse akapitiriza kunyada komanso kudana, zingayambitse nkhondo imene ingaphe anthu onse padzikoli, pokhapokha Wokwera pahatchi yoyera uja ataletsa hatchi yofiira ngati moto ija kuti isapitirize liwiro lake lowononga. Tiyeni tikhale otsimikizira kuti Khristu Mfumu yathu adzapitiriza liwiro lake la pahatchi ndipo adzapambana pa nkhondo yolimbana ndi dziko limene likulamuliridwa ndi Satanali, ndiponso adzakhazikitsa dziko lapansi latsopano limene lidzakhale lamtendere. Anthu adzapitiriza kukhala pa mtendere chifukwa chokonda Mulungu komanso anthu anzawo. Chikondi chimenechi n’chomwe chidzachititse anthu kukhala pa mtendere weniweni, osati chifukwa choopa zida zanyukiliya za m’nthawi yathu yovuta ino.—Salimo 37:9-11; Maliko 12:29-31; Chivumbulutso 21:1-5.

Hatchi Yakuda Inatulukira

20. N’chiyani chikutitsimikizira kuti Wokwera pahatchi yoyera adzathetsa mavuto onse?

20 Kenako Yesu anamatula chidindo chachitatu. Kodi Yohane anaona chiyani? Iye anati: “Atamatula chidindo chachitatu, ndinamva chamoyo chachitatu chikunena kuti: ‘Bwera!’” (Chivumbulutso 6:5a) N’zosangalatsa kuti kerubi wachitatuyu ‘anali ndi nkhope ngati ya munthu,’ ndipo zimenezi zinkaimira khalidwe la chikondi. Anthu a m’dziko latsopano la Mulungu adzakhala ndi chikondi chotsatira mfundo zachilungamo, chimenenso chikuoneka m’gulu lonse la Yehova masiku ano. (Chivumbulutso 4:7; 1 Yohane 4:16) Sitikukayikira kuti Wokwera pahatchi yoyera uja, amene “ayenera kulamulira monga mfumu kufikira Mulungu ataika adani onse pansi pa mapazi ake,” mwachikondi adzachotsa mavuto otsatira amene Yohane anaonetsedwa.—1 Akorinto 15:25.

21. (a) Kodi hatchi yakuda ndi wokwerapo wake zikuimira chiyani? (b) N’chiyani chikusonyeza kuti hatchi yakuda idakali pa liwiro?

21 Kodi patamveka mawu achitatu oitana kuti “Bwera!” Yohane anaona chiyani? Iye ananena kuti: “Ndipo nditayang’ana, ndinaona hatchi yakuda. Wokwerapo wake anali ndi sikelo m’dzanja lake.” (Chivumbulutso 6:5b) Njala yoopsa kwambiri. Umenewu ndi uthenga wochititsa mantha womwe uli m’masomphenya aulosi amenewa. Masomphenyawa ankanena za m’tsogolo, kumayambiriro kwa tsiku la Ambuye, pamene anthu ankachita kuwayezera chakudya pasikelo. Kuyambira mu 1914 anthu akupitiriza kuvutika ndi njala padziko lonse. Nkhondo zimene zikuchitika masiku ano zachititsanso kuti anthu azivutika ndi njala, chifukwa chakuti ndalama zimene akanagulira chakudya chothandizira anthu amene akuvutika ndi njala, amazigwiritsa ntchito pogulira zida zankhondo. Nthawi zina anthu sakolola chakudya chokwanira chifukwa chakuti alimi amalembedwa usilikali, nthaka imene inali yachonde imawonongeka chifukwa cha kuphulitsidwa kwa mabomba ndiponso boma limayamba kuyendera mfundo zina zimene zimachititsa kuti chakudya chichepe m’dziko. Umu ndi mmene zinalili pa nkhondo yoyamba ya padziko lonse, pamene anthu mamiliyoni ambiri anafa ndi njala. Komanso wokwera pahatchi yakuda yoimira njala uja sanaleke kuvutitsa anthu ngakhale nkhondoyo itatha. M’zaka za m’ma 1930 anthu 5 miliyoni anafa ndi njala imodzi yokha ku Ukraine. Nkhondo yachiwiri yapadziko lonse nayonso inabweretsa njala yaikulu. Pamene hatchi yakuda ikupitiriza liwiro lake, bungwe la United Nations linanena kuti anthu oposa 863 miliyoni padziko lonse alibe chakudya chokwanira ndipo ana oposa 5 miliyoni amafa chaka chilichonse ndi matenda oyamba chifukwa cha kuperewera kwa zakudya m’thupi.

22. (a) Kodi Yohane anamva mawu otani, ndipo mawuwo ankanena za kufunika kochita chiyani? (b) Kodi mtengo wa kilogalamu imodzi ya tirigu ndi makilogalamu atatu a balere ukutanthauza chiyani?

22 Yohane anapitiriza kuti: “Kenako ndinamva mawu ngati ochokera pakati pa zamoyo zinayi zija. Mawuwo anali akuti: ‘Kilogalamu imodzi ya tirigu, mtengo wake ukhala dinari imodzi, ndipo makilogalamu atatu a balere, mtengo wake ukhala dinari imodzi. Koma musawononge mafuta a maolivi ndi vinyo.’” (Chivumbulutso 6:6) Akerubi onse anayi ananena mogwirizana za kufunika kosamala chakudya ngati mmene zinalili mzinda wa Yerusalemu utatsala pang’ono kuwonongedwa mu 607 B.C.E. Pa nthawi imeneyo, anthu anafunikira ‘kudya chakudya chochita kuyeza ndipo anachidya ali ndi nkhawa.’ (Ezekieli 4:16) M’nthawi ya Yohane, kilogalamu imodzi ya tirigu inali chakudya chimene msilikali aliyense ankalandira pa tsiku. Kodi kilogalamu imodzi ya tirigu munthu akanaigula ndalama zingati? Akanaigula dinari imodzi, yomwe inali malipiro a tsiku lonse. (Mateyu 20:2)d Nanga bwanji munthu amene anali ndi banja? Iye akanatha kugula makilogalamu atatu a balere wosapuntha. Komabe, balere ameneyu anali wongokwanira banja laling’ono. Ndipo anthu ankaona kuti balere si chakudya chabwino ngati tirigu.

23. Kodi mawu akuti “musawononge mafuta a maolivi ndi vinyo” akutanthauza chiyani?

23 Kodi mawu akuti “musawononge mafuta a maolivi ndi vinyo” akutanthauza chiyani? Ena amaganiza kuti mawuwa amatanthauza kuti pa nthawi imene anthu ambiri azidzasowa chakudya, ena n’kumafa ndi njala, anthu olemera adzakhalabe ndi zakudya zabwino. Koma ku Middle East, mafuta ndi vinyo si zakudya za anthu olemera okha. Kale kudera limeneli anthu ankaona kuti mkate, mafuta ndi vinyo zinali zakudya zimene aliyense ankayenera kukhala nazo. (Yerekezerani ndi Genesis 14:18; Salimo 104:14, 15.) Nthawi zina madzi sankakhala abwino kumwa, choncho anthu ankamwa vinyo ndipo nthawi zina ankamugwiritsa ntchito ngati mankhwala. (1 Timoteyo 5:23) Tikanena za mafuta, m’nthawi ya Eliya, ngakhale kuti mkazi wamasiye wa ku Zarefati anali wosauka, anali ndi mafuta ochepa amene akanatha kuphikira chakudya pogwiritsa ntchito ufa umene unatsala. (1 Mafumu 17:12) Choncho mawu akuti “musawononge mafuta a maolivi ndi vinyo” akuoneka kuti ndi malangizo akuti anthu asagwiritse ntchito zinthu zofunikazi mowononga kuti zisathe msanga. Akanapanda kutero, zinthuzi ‘zikanawonongedwa,’ kapena kuti zikanatha msanga njala isanathe.

24. N’chifukwa chiyani hatchi yakuda sidzapitiriza liwiro lake mpaka kalekale?

24 Tiyenera kusangalala chifukwa posachedwapa, Wokwera pahatchi yoyera adzaimitsa hatchi yakuda imeneyi, yomwe ili pa liwiro. Ponena zimene iye adzachitire anthu mwachikondi m’dziko lapansi latsopano, Malemba amati: “M’masiku ake, wolungama adzaphuka, ndipo padzakhala mtendere wochuluka kwa nthawi yonse pamene mwezi udzakhalepo. Padziko lapansi padzakhala tirigu wambiri. Pamwamba pa mapiri padzakhala tirigu wochuluka.”—Salimo 72:7, 16; onaninso Yesaya 25:6-8.

Hatchi Yotuwa ndi Wokwerapo Wake

25. Yesu atamatula chidindo chachinayi, kodi Yohane anamva mawu a ndani, ndipo zimenezi zikuimira chiyani?

25 Yohane anapitiriza kuona masomphenyawo. Iye anaona Yesu akumatula chidindo chachinayi ndipo akutiuza zotsatira zake, kuti: “Atamatula chidindo chachinayi, ndinamva mawu a chamoyo chachinayi chikunena kuti: ‘Bwera!’” (Chivumbulutso 6:7) Mawu amenewa ndi a kerubi wooneka ngati chiwombankhanga chimene chikuuluka. Kerubi ameneyu akuimira nzeru zoona patali, ndipo Yohane, Akhristu odzozedwa komanso atumiki onse a Mulungu padziko lapansi amafunika kuona patali ndi kuchita zinthu mwanzeru mogwirizana ndi zimene kerubiyu akuimira. Tikamachita zimenezi tingatetezeke ku miliri imene ikugwera anthu amene amadziona kuti ndi anzeru m’dzikoli, omwe ndi onyada komanso okonda chiwerewere.—1 Akorinto 1:20, 21.

26. (a) Kodi wokwera pahatchi wachinayi ndani, ndipo n’chifukwa chiyani m’pake kuti hatchi yake ndi yotuwa? (b) N’chiyani chimene chikutsatira wokwera pahatchi wachinayi, ndipo n’chiyani chidzachitikire anthu amene akupita kwa iye?

26 Kodi ndi zinthu zina ziti zochititsa mantha zimene zikuchitika pamene wokwera pahatchi wachinayi akufika? Yohane akutiuza kuti: “Nditayang’ana, ndinaona hatchi yotuwa. Wokwerapo wake dzina lake anali Imfa. Ndipo Manda anali kumutsatira pafupi kwambiri.” (Chivumbulutso 6:8a) Wokwera pahatchi wachinayiyu dzina lake ndi Imfa. Pa okwera pahatchi onse a m’buku la Chivumbulutso, ndi yekhayu amene anachita kuneneratu zimene akuimira. M’pake kuti Imfa wakwera pahatchi yotuwa, chifukwa chakuti mawu akuti kutuwa (Chigiriki, khlo·rosʹ) amagwiritsidwa ntchito m’mabuku achigiriki pofotokoza nkhope ya munthu amene akuoneka kuti akudwala kapena alibe magazi okwanira. Komanso m’pake kuti Imfayu akutsatiridwa pafupi kwambiri ndi Manda, ngakhale kuti sizikudziwika kuti akutsatiridwa bwanji. Izi zili choncho chifukwa chakuti ku Manda kukupita anthu ambirimbiri amene aphedwa ndi wokwera pahatchi wachinayi ameneyu. Chosangalatsa n’chakuti anthu amenewa adzaukitsidwa pamene ‘imfa ndi Manda zidzapereke akufa amene ali mmenemo.’ (Chivumbulutso 20:13) Kodi Imfa ameneyu amapha bwanji anthuwa?

27. (a) Kodi Imfa, amene wakwera pahatchi, akupha bwanji anthu? (b) Kodi mawu akuti “gawo limodzi la magawo anayi a dziko lapansi,” limene likulamuliridwa ndi Imfa, akutanthauza chiyani?

27 Masomphenyawa akufotokoza zina mwa njira zimene iye amaphera anthu, kuti: “Iwo anapatsidwa ulamuliro pa gawo limodzi la magawo anayi a dziko lapansi, kuti aphe anthu ndi lupanga lalitali, njala, mliri wakupha, ndi zilombo za padziko lapansi.” (Chivumbulutso 6:8b) Amene akukhudzidwa ndi wokwera pahatchi ameneyu si anthu okwanadi gawo limodzi la magawo anayi a anthu a padziko lapansi, koma ndi anthu ochokera kumbali yaikulu ya dziko lapansi, kaya kuli anthu ambiri kapena ochepa. Wokwera pahatchi ameneyu akutenga anthu amene aphedwa ndi lupanga lalikulu la wokwera pahatchi wachiwiri, komanso amene aphedwa ndi njala ya wokwera pahatchi wachitatu. Iye akuphanso anthu akeake ndi miliri komanso zivomezi zofotokozedwa pa Luka 21:10, 11.

28. (a) Kodi ulosi wonena za “mliri wakupha” wakwaniritsidwa bwanji? (b) Kodi anthu a Yehova atetezedwa bwanji ku matenda ambiri masiku ano?

28 Chinthu chimodzi chimene chili chatsopano pa masomphenyawa ndi “mliri wakupha.” Nkhondo yoyamba ya padziko lonse itangotha, kunagwa mliri wa chimfine cha ku Spain chimene chinapha anthu oposa 20 miliyoni m’miyezi yochepa yokha ya mu 1918 ndi 1919. Dera lokhalo padziko lonse limene silinakhudzidwe ndi mliri umenewu linali chilumba chaching’ono cha St. Helena. M’madera amene anthu ambiri anafa, mitembo ankangoiunjika milumilu n’kuiwotcha. Ndipo masiku ano anthu ambiri akufa ndi matenda a mtima komanso khansa. Matenda amenewa nthawi zambiri amayamba chifukwa cha kusuta fodya. Zaka za m’ma 1980, zimene anthu amanena kuti “zinali zoipa kwambiri,” pa “mliri wakupha” panawonjezeka mliri wa Edzi chifukwa cha khalidwe la anthu ambiri losemphana ndi mfundo za m’Baibulo. M’chaka cha 2000, dokotala wamkulu wa ku United States akuti ananena kuti n’kutheka kuti Edzi ndi “mliri woopsa kwambiri kuposa mliri wina uliwonse umene unabukapo padzikoli.” Iye ananena kuti anthu 52 miliyoni padziko lonse anali atatenga kachilombo ka HIV koyambitsa Edzi, ndipo anthu 20 miliyoni mwa anthu amenewa anali atamwalira. Anthu a Yehova ali ndi mwayi chifukwa chakuti malangizo anzeru opezeka m’Mawu ake amawathandiza kupewa dama komanso kupewa kugwiritsa ntchito magazi molakwika, zinthu zimene zimafalitsa matenda ambiri masiku ano.—Machitidwe 15:28, 29; yerekezerani ndi 1 Akorinto 6:9-11.

29, 30. (a) Kodi zinthu ‘zinayi zowononga’ zotchulidwa pa Ezekieli 14:21 zikukwaniritsidwa bwanji masiku ano? (b) Kodi “zilombo” zotchulidwa pa Chivumbulutso 6:8 zingatanthauze chiyani? (c) Kodi zikuoneka kuti mfundo yaikulu ya masomphenya aulosiwa ndi yotani?

29 Masomphenya a Yohane akutchulanso zilombo kuti ndi chinthu chachinayi chimene chikuchititsa kuti anthu azifa nthawi yawo isanakwane. N’zoona kuti kalelo, zinthu monga nkhondo, njala, matenda ndi zilombo, zimene zinaonekera atamatula chidindo chachinayi, zinkaoneka kuti n’zimene zinkapha anthu kwambiri nthawi yawo isanakwane. Choncho zingaimire zinthu zonse zimene zikuchititsa kuti anthu azifa nthawi yawo isanakwane masiku ano. Izi zikungogwirizana ndi chenjezo limene Yehova anapereka kwa Aisiraeli kuti: “Zidzateronso ndikadzabweretsa ziweruzo zanga zinayi izi zowononga: lupanga, njala, zilombo zolusa zakutchire ndi mliri. Ndidzatumiza zimenezi mu Yerusalemu kuti zikaphemo anthu ndi ziweto.”—Ezekieli 14:21.

30 Masiku ano ndi anthu ochepa amene amaphedwa ndi zilombo zakutchire ngakhale kuti m’mayiko ena amene muli nkhalango, nyama zakutchire zikupitiriza kupha anthu. M’tsogolomu mwina nyama zimenezi zidzapha anthu ambiri ngati dziko litachita chipululu chifukwa cha nkhondo kapena ngati anthu atafooka kwambiri ndi njala n’kumalephera kuthamangitsa zilombo zanjala. Komanso masiku ano pali anthu ambiri amene amachita zinthu ngati nyama zosaganiza, moti amasonyeza makhalidwe osiyana ndi amene afotokozedwa pa Yesaya 11:6-9. Anthu amenewa ndi omwe achititsa kuti padziko lonse kuphana, uchigawenga, kuphulitsa mabomba, ndiponso milandu yokhudzana ndi kugonana, ziwonjezeke masiku ano. (Yerekezerani ndi Ezekieli 21:31; Aroma 1:28-31; 2 Petulo 2:12.) Wokwera pahatchi wachinayi uja akusonkhanitsanso anthu amene akufa chifukwa cha zinthu zimenezi. Apa zikuoneka kuti mfundo yaikulu ya masomphenya aulosiwa ndi yakuti wokwera pahatchi yotuwayi akuchititsa kuti anthu azifa pa zifukwa zosiyanasiyana nthawi yawo isanakwane.

31. N’chiyani chimene chikutilimbikitsa ngakhale kuti okwera pahatchi yofiira, yakuda ndi yotuwa abweretsa mavuto oopsa?

31 Zinthu zimene taona Yesu atamatula zidindo zinayi zoyambirira za mpukutu uja ziyenera kutilimbikitsa. Zili choncho popeza taona kuti sitiyenera kuda nkhawa chifukwa cha nkhondo, njala, matenda ndi zinthu zina zimene zikupha anthu nthawi yawo isanakwane, zimene zachuluka kwambiri masiku ano. Sitiyeneranso kutaya mtima poona kuti atsogoleri a anthu alephera kuthetsa mavuto amene tikukumana nawo masiku ano. Ngati zochitika za m’dzikoli zikusonyezeratu kuti okwera pahatchi yofiira, yakuda ndi yotuwa ali paliponse, tisaiwale kuti Wokwera pahatchi yoyera ndi amene anayamba liwiro lake. Yesu anakhala kale Mfumu, ndipo anayamba kale kugonjetsa adani ake moti anachotsa Satana kumwamba. Zina zimene wachita posonyeza kuti wagonjetsa adani ake ndi kusonkhanitsa ana a Isiraeli wauzimu amene anatsalira kuti chiwerengero chawo chikwanire. Komanso wasonkhanitsa khamu lalikulu la anthu ochokera m’mayiko osiyanasiyana, omwe panopa aposa 7 miliyoni, ndipo iwo adzapulumuka pa chisautso chachikulu. (Chivumbulutso 7:4, 9, 14) Iye apitiriza liwiro lake la pahatchi mpaka atapambana pa nkhondo yolimbana ndi adani ake onse.

32. Kodi chimachitika n’chiyani Yesu akamatula chidindo chilichonse mwa zidindo zinayi zoyambirira zija?

32 Chidindo chilichonse mwa zidindo zinayi zija chikamatulidwa, pankamveka mawu oitana, akuti: “Bwera!” Zikatero pankatulukira hatchi ndi wokwerapo wake. Kuyambira ndi chidindo chachisanu, mawu oitanawo sakumvekanso. Koma okwera pamahatchiwo adakali pa liwiro ndipo apitiriza kuthamanga m’nyengo yonse ya mapeto a nthawi ino. (Yerekezerani ndi Mateyu 28:20.) Kodi Yesu anavumbula zinthu zinanso ziti zofunika kwambiri pamene anamatula zidindo zitatu zotsalazo? Zina mwa zinthuzo anthu sangathe kuziona. Zina n’zooneka koma zidzachitika m’tsogolo ndipo sitikukayikira kuti zidzakwaniritsidwa. Tsopano tiyeni tione zinthu zimenezi.

[Mawu a M’munsi]

a Komabe onani kuti “mkazi” wotchulidwa pa Chivumbulutso 12:1 wavala mophiphiritsira “chisoti chachifumu chokhala ndi nyenyezi 12.”

b Kuti muone umboni watsatanetsatane wosonyeza kuti Yesu anayamba kulamulira mu Ufumu wake mu 1914, onani buku lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? tsamba 215 mpaka 218. Bukuli n’lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

c Mabaibulo ambiri anamasulira mawu amenewa kuti “kugonjetsa” (Revised Standard, The New English Bible, King James Version) kapena “kutsimikiza kuti agonjetse,” (Phillips, New International Version). Koma mawu achigiriki amene anawagwiritsira ntchito palemba limeneli amasonyeza kuti ntchitoyo yamalizidwa kapena kuti yafika kumapeto. Choncho buku lina lofotokozera mawu a m’Baibulo lolembedwa ndi Robertson limanena kuti: “Mmene mawuwa analembedwera palembali amasonyeza kuti wogonjetsayo anapambana pamapeto pake.”—Word Pictures in the New Testament.

d Kuti mudziwe zambiri zokhudza dinari, onani Matanthauzo a Mawu Ena patsamba 1968 mu Baibulo la Dziko Latsopano.

[Bokosi patsamba 92]

Mfumu Yokwera Pahatchi Inapambana

M’zaka za m’ma 1930 ndi m’ma 1940, adani ouma mtima anayesetsa kuchita zinthu zoipitsa mbiri ya Mboni za Yehova kuti anthu aziona ngati utumiki wawo ndi wosemphana ndi malamulo, woipa komanso wolimbikitsa kuukira boma. (Salimo 94:20) Chiwerengero chodziwika cha atumiki a Yehova amene anamangidwa m’chaka cha 1936 chokha m’dziko la United States, chinali 1,149. Mbonizo zinamenyera ufulu wawo m’makhoti osiyanasiyana mpaka kukafika ku Khoti Lalikulu Kwambiri la ku United States, ndipo m’munsimu muli ina mwa milandu imene anapambana.

Pa May 3, 1943, pa mlandu wa pakati pa Murdock ndi akuluakulu a chigawo cha Pennsylvania, Khoti Lalikulu Kwambiri linagamula kuti Mboni za Yehova sizikufunikira kukhala ndi chikalata chaboma chowaloleza kuomboletsa mabuku awo. Tsiku lomweli, pa mlandu wa pakati pa Martin ndi akuluakulu a mzinda wa Struthers, khoti linagamula kuti a Mboni za Yehova saphwanya malamulo akamagogoda m’makomo a anthu n’kumagawira timapepala towaitanira kumisonkhano yawo kapena timapepala tina.

Pa June 14, 1943, pa mlandu wa pakati pa Taylor ndi akuluakulu a chigawo cha Mississippi, Khoti Lalikulu Kwambiri linaona kuti ntchito yolalikira ya Mboni za Yehova silimbikitsa anthu kuti asamamvere boma. Tsiku lomweli, pa mlandu wa pakati pa Barnette ndi akuluakulu oyang’anira maphunziro m’chigawo cha West Virginia, Khoti Lalikulu Kwambirili linagamula kuti komiti ya sukulu inalibe ufulu wochotsa sukulu ana a Mboni za Yehova amene akana kuchitira sawatcha mbendera. Tsiku lotsatira, oweruza onse a Khoti Lalikulu ku Australia anachotsa lamulo laboma loletsa Mboni za Yehova m’dzikolo. Oweruzawo ananena kuti lamulo limeneli linali “losayenerera, linaikidwa mopupuluma komanso linali lopondereza.”

[Bokosi patsamba 94]

“Analoledwa Kuchotsa Mtendere Padziko Lapansi”

Kodi zotsatira za luso la zopangapanga zidzakhala zotani? Nyuzipepala ina (The Globe and Mail) ya ku Toronto, m’dziko la Canada, ya pa January 22, 1987, inalemba zimene ananena Ivan L. Head, mkulu wa bungwe linalake lochita kafukufuku (International Development Research Centre), kuti:

“Pali umboni wosonyeza kuti pa akatswiri anayi alionse asayansi komanso luso la zopangapanga padziko lonse amene akupanga kafukufuku, mmodzi akupanga kafukufuku wothandiza popanga zida zankhondo. . . . M’chaka cha 1986, mayiko ankagwiritsa ntchito ndalama zoposa madola 1.5 miliyoni pa mphindi iliyonse pa ntchito yokhudzana ndi zidazo. . . . Kodi luso la zopangapanga limeneli likuthandiza kuti tikhale otetezeka kwambiri? Zida za nyukiliya zimene mayiko amphamvu kwambiri ali nazo n’zochuluka kwambiri kuwirikiza nthawi 6,000 poyerekezera ndi zida zonse zimene zinagwiritsidwa ntchito pa nkhondo yachiwiri yapadziko lonse. Zimenezi zikutanthauza kuti mayikowa angamenye nkhondo zokwana 6,000 zofanana ndi nkhondo yachiwiri yapadziko lonse. Kuyambira mu 1945, milungu 7 sinathepo popanda kuchitika nkhondo m’dera linalake padziko lapansili. Kuchokera pa nthawiyi, pachitika nkhondo zoposa 150 za pakati pa mayiko kapena za pachiweniweni zimene mwina zapha anthu 19.3 miliyoni. Zambiri mwa nkhondo zimenezi zachitika chifukwa cha luso la zopangapanga limene lapita patsogolo kwambiri m’nthawi ino imene pali bungwe la United Nations.”

Pofika m’chaka cha 2005, anthu oposa 20 miliyoni anali ataphedwa pa nkhondo.

[Bokosi patsamba 98]

Mmene Buku la Chivumbulutso Lilili

Popeza takambirana zambiri m’buku la Chivumbulutso, tsopano tikuyamba kuona bwinobwino mmene bukuli lilili. Pambuyo pa mavesi ake oyambirira, omwe ali ndi nkhani zochititsa chidwi (Chivumbulutso 1:1-9), tingagawe masomphenya a m’buku la Chivumbulutso m’zigawo 16 zotsatirazi:

MASOMPHENYA OYAMBA (1:10–3:22): Mothandizidwa ndi mzimu woyera, Yohane anaona Yesu ali mu ulemerero wake. Yesuyo anatumiza mauthenga olimbikitsa okhala ndi malangizo ku mipingo 7.

MASOMPHENYA ACHIWIRI (4:1–5:14): Yohane anaona mpando wachifumu wa Yehova Mulungu kumwamba, womwe ndi waulemerero kwambiri. Wokhala pampando wachifumuyo anapereka mpukutu kwa Mwanawankhosa.

MASOMPHENYA ACHITATU (6:1-17): Mwanawankhosayo anamatula zidindo zoyambirira 6 zomatira mpukutuwo, ndipo pang’onopang’ono anaonetsa Yohane masomphenya a zinthu zosiyanasiyana zimene zikuchitika m’tsiku la Ambuye. Yohane anaona anthu anayi atakwera pamahatchi komanso akapolo a Mulungu amene anaphedwa chifukwa cha chikhulupiriro chawo akupatsidwa mikanjo yoyera. Iye anamvanso zimene zidzachitike pa tsiku lalikulu la mkwiyo.

MASOMPHENYA ACHINAYI (7:1-17): Angelo agwira mphepo zowononga kufikira a 144,000, omwe ndi Isiraeli wauzimu, atadindidwa zidindo. Khamu lalikulu la anthu ochokera m’dziko lililonse akuvomereza kuti Mulungu komanso Khristu ndi amene angawapulumutse ndipo akusonkhanitsidwa kuti apulumuke chisautso chachikulu.

MASOMPHENYA ACHISANU (8:1–9:21): Pamene anamatula chidindo cha 7 panamveka kulira kwa malipenga 7. Malipenga 6 oyambirirawo analira mkati mwa masomphenya achisanu. Kulira kwa malipenga 6 amenewa kunasonyeza kulengezedwa kwa chiweruzo chimene Yehova akupereka kwa anthu. Lipenga lachisanu linalengeza za tsoka loyamba ndipo lipenga la 6 linalengeza za tsoka lachiwiri.

MASOMPHENYA A 6 (10:1–11:19): M’masomphenya amenewa Yohane anapatsidwa mpukutu waung’ono ndi mngelo wamphamvu. Mulinso nkhani yokhudza kuyezedwa kwa kachisi komanso mboni ziwiri. Masomphenyawa anafika pachimake pamene kunamveka kulira kwa lipenga la 7. Lipenga limeneli linalengeza kubwera kwa Ufumu wa Yehova ndi Khristu wake. Kubwera kwa Ufumu umenewu ndi tsoka lachitatu limene lidzagwere adani a Mulungu.

MASOMPHENYA A 7 (12:1-17): Masomphenya amenewa akufotokoza za kubadwa kwa Ufumu, zimene zinachititsa kuti Mikayeli aponye Satana, yemwe ndi njoka, kudziko lapansi.

MASOMPHENYA A 8 (13:1-18): Chilombo champhamvu chinatuluka m’nyanja, ndipo chilombo china cha nyanga ziwiri ngati mwana wa nkhosa chinalimbikitsa anthu kuti alambire chilombo choyambacho.

MASOMPHENYA A 9 (14:1-20): Yohane anaona masomphenya ochititsa chidwi a 144,000 ali paphiri la Ziyoni. Mauthenga osiyanasiyana ochokera kwa angelo anamveka padziko lonse lapansi, mpesa wa padziko lapansi unamwetedwa ndipo anaupondaponda m’choponderamo mphesa cha mkwiyo wa Mulungu.

MASOMPHENYA A 10 (15:1–16:21): Yonane anaonanso bwalo lakumwamba, kenako anaona mbale 7 za mkwiyo wa Yehova zikuthiridwa padziko lapansi. Masomphenya amenewanso anamaliza ndi kufotokoza mophiphiritsira kutha kwa dziko la Satanali.

MASOMPHENYA A 11 (17:1-18): Babulo Wamkulu, amene ndi hule lalikulu, anakwera pachilombo chofiira kwambiri chimene chinaponyedwa kuphompho kwa kanthawi koma kenako chinatulukako n’kuwononga hule lija.

MASOMPHENYA A 12 (18:1–19:10): Chilengezo chokhudza kugwa ndi kuwonongedwa komaliza kwa Babulo Wamkulu chinamveka. Pamene Babulo Wamkulu anawonongedwa, ena anamulirira koma ena anatamanda Yehova. Panamvekanso chilengezo cha ukwati wa Mwanawankhosa.

MASOMPHENYA A 13 (19:11-21): Yesu anatsogolera magulu ankhondo akumwamba kukapereka chiweruzo cha mkwiyo wa Mulungu kudziko la Satana, ku magulu ankhondo a m’dziko la Satanali ndiponso kwa anthu onse amene ali kumbali ya Satana. Ndipo mbalame zodya nyama zinadya mitembo yawo.

MASOMPHENYA A 14 (20:1-10): Masomphenya amenewa akunena za kuponyedwa kuphompho kwa Satana Mdyerekezi, Ulamuliro wa Zaka 1,000 wa Khristu ndi mafumu anzake, kuyesedwa komaliza kwa anthu komanso za kuwonongedwa kwa Satana ndi ziwanda zake.

MASOMPHENYA A 15 (20:11–21:8): Masomphenyawa akunena za kuukitsidwa kwa anthu komanso za Tsiku la Chiweruzo lalikulu. Yohane anaonanso kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano zimene zidzabweretse madalitso osatha kwa anthu olungama.

MASOMPHENYA A 16 (21:9–22:5): Mapeto osangalatsa a buku la Chivumbulutso anali masomphenya a ulemerero a Yerusalemu Watsopano, amene ndi mkazi wa Mwanawankhosa. Mumzinda umenewu munatuluka madalitso a Mulungu omwe anachiritsa anthu ndi kuwapatsa moyo.

Kumapeto kwa buku la Chivumbulutso kuli moni komanso malangizo ochokera kwa Yehova, Yesu, mngelo ndi Yohane. Munthu aliyense akuitanidwa kuti, “Bwera!”—Chivumbulutso 22:6-21.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena