Nthaŵi Zabwinopo Mtsogolo
“IFE timachita wani-ziro-wani,” akutero mkazi wina.
“Kwa ine nzovutiratu,” akuyankha motero bwenzi lake. “Ndili pa ziro-ziro-wani.”
M’mbali zina za West Africa, kukambitsirana kwachidule koteroko nkodziŵika bwino. M’malo mwa kudya chakudya katatu patsiku (wani-wani-wani), munthu amene ali pa wani-ziro-wani amangodya kaŵiri patsiku—kamodzi mmaŵa ndi kamodzi madzulo. Mnyamata amene ali pa ziro-ziro-wani akulongosola za mkhalidwe wake kuti: “Ndimadya kamodzi patsiku. M’firiji ndimangoikamo madzi basi. Ndimangodya gari [chinangwa] pogona usiku. Ndiwo wakhala umoyo wanga umenewo.”
Umenewo ndiwo mkhalidwe wa anthu omawonjezereka lerolino. Mitengo imakwera, ndipo mphamvu ya ndalama yogulira imachepa.
Kupereŵera kwa Chakudya Kunanenedweratu
Mu mpambo wa masomphenya osonyezedwa kwa mtumwi Yohane, Mulungu ananeneratu za mikhalidwe yovuta imene ambiri akuyang’anizana nayo lerolino. Pakati pa imeneyo pali kupereŵera kwa chakudya. Yohane akuti: “Ndipo ndinapenya, taonani, kavalo wakuda; ndipo iye womkwera anali nawo muyeso m’dzanja lake.” (Chivumbulutso 6:5) Kavalo watsoka ameneyu ndi womkwera wake akuchitira chithunzi njala—chakudya chidzasoŵa kwakuti chidzapimidwa pa muyeso.
Kenako mtumwi Yohane akuti: “Ndipo ndinamva . . . nanena, Muyeso wa tirigu wogula lupiya, ndi miyeso itatu ya barele yogula lupiya.” M’tsiku la Yohane, muyeso umodzi wa tirigu unali malipiro a tsiku ndi tsiku a msilikali, ndipo lupiya limodzi ndilo linali malipiro operekedwa pa ntchito ya tsiku limodzi. Motero, matembenuzidwe a Richard Weymouth amatembenuza vesilo motere: “Malipiro a tsiku lonse a mtanda wa buledi, malipiro a tsiku lonse pa makeke atatu a barele.”—Chivumbulutso 6:6.
Kodi lerolino malipiro a tsiku lonse ndi otani? Lipoti la State of World Population, 1994 limati: “Anthu pafupifupi [1,100 miliyoni], pafupifupi 30 peresenti ya anthu okhala m’maiko osatukuka amakhalira moyo pafupifupi $1 patsiku.” Motero, kwa osauka a padziko lonse, malipiro a tsiku limodzi amaguladi mtanda wa buledi chabe.
Ndithudi, zimenezi si zodabwitsa kwa osauka kwambiri. “Buledi!” anadzuma motero mwamuna wina. “Ndani amene amadya buledi? Masiku ano buledi ngwakudya panthaŵi yake!”
Modabwitsa, chakudya sichili chopereŵera. Malinga ndi kunena kwa a United Nations, pazaka khumi zapitazo, chakudya chotulutsidwa padziko chawonjezeka ndi 24 peresenti, chimene chinali chambiri kuposa kuwonjezeka kwa chiŵerengero cha anthu. Komabe, kuwonjezeka kwa chakudya kumeneku sikunapindulitse onse. Mwachitsanzo, mu Afirika, chakudya chotulutsidwa chinatsika ndi 5 peresenti, pamene chiŵerengero cha anthu chinakwera ndi 34 peresenti. Chotero mosasamala kanthu za kuchuluka kwa chakudya kwa dziko lonse, kupereŵera kwa chakudya kukupitiriza m’maiko ena ambiri.
Kupereŵera kwa chakudya kumachititsa kukwera kwa mitengo. Kusoŵa kwa ntchito, malipiro ochepa, ndi kukwera kwa mitengo ya zinthu kumachititsa kupeza ndalama zogulira zinthu zimene zilipo kukhala kovuta kwambiri. Human Development Report 1994 ikunena kuti: “Anthu amakhala ndi njala osati chifukwa chakuti chakudya palibe—koma chifukwa chakuti sakhoza kuchigula.”
Pali kusoŵa chochita komakulakula, kuthedwa nzeru, ndi kutaya mtima. “Anthu ali ndi lingaliro lakuti lero zinthu nzoipa, koma maŵa zidzaipiratu,” anatero Glory, amene akukhala ku West Africa. Mkazi wina anati: “Anthu akuona kuti akuyandikira tsoka. Amalingalira kuti tsiku lidzafika pamene msika udzakhala ulibe kalikonse.”
Yehova Anasamalira Atumiki Ake m’Nthaŵi Zakale
Atumiki a Mulungu amadziŵa kuti Yehova amadalitsa okhulupirika ake mwa kuwagaŵira zosoŵa ndi mwa kuwapatsa nyonga yopiririra mikhalidwe yovuta. Chidaliro choterocho pa mphamvu ya Mulungu ya kugaŵira zinthu, chilidi mbali yofunika ya chikhulupiriro chawo. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Iye wakudza kwa Mulungu ayenera kukhulupirira kuti alipo, ndi kuti ali wobwezera mphotho iwo akumfuna iye.”—Ahebri 11:6.
Yehova nthaŵi zonse wasamalira atumiki ake okhulupirika. Panthaŵi ina ya chilala cha zaka zitatu ndi theka, Yehova anapereka chakudya kwa mneneri Eliya. Poyamba, Mulungu analamulira makungubwi kubweretsera Eliya mkate ndi nyama. (1 Mafumu 17:2-6) Pambuyo pake, Yehova mwachozizwitsa anachulukitsa ufa wa tirigu ndi mafuta a mkazi wamasiye amene anapatsa chakudya Eliya. (1 Mafumu 17:8-16) M’nthaŵi ya chilala chimodzimodzicho, mosasamala kanthu za chizunzo chachikulu chachipembedzo choperekedwa kwa iwo ndi Mfumukazi yoipayo Yezebeli, Yehova anatsimikiziranso kuti aneneri ake anagaŵiridwa mkate ndi madzi.—1 Mafumu 18:13.
Pambuyo pake, pamene mfumu ya Babulo inalalira Yerusalemu wopandukayo, anthu ‘anadya chakudya mwa muyeso ndi mosamalira.’ (Ezekieli 4:16) Mkhalidwewo unakhala woipa kwambiri kwakuti akazi ena anadya mnofu wa ana awoawo. (Maliro 2:20) Komabe, ngakhale kuti mneneri Yeremiya anali m’ndende chifukwa cha kulalikira kwake, Yehova anachititsa kuti ‘mkate uzipatsidwa [kwa Yeremiya] wofuma ku msewu wa oumba mikate, mpaka unatha mkate wonse wa m’mudzi.’—Yeremiya 37:21.
Kodi Yehova anaiŵala Yeremiya pamene mkate unatha? Mwachionekere sanatero, chifukwa chakuti pamene mzindawo unatengedwa ndi Ababulo, Yeremiya anapatsidwa “phoso ndi mtulo, namleka amuke.”—Yeremiya 40:5, 6; onaninso Salmo 37:25.
Yehova Amachirikiza Atumiki Ake Lerolino
Monga momwe Yehova anachirikizira atumiki ake m’mibadwo yakale, amateronso lerolino, kuwasamalira pa zinthu zakuthupi ndi zauzimu. Mwachitsanzo, talingalirani chochitika cha Lamitunde, amene akukhala ku West Africa. Iye akusimba kuti: “Ndinali ndi famu yaikulu ya nkhuku. Tsiku lina, mbala zonyamula mfuti zinabwera pafamu ndi kuba nkhuku zochuluka, makina apambali a generator ndi ndalama zimene tinali nazo. Posapita nthaŵi, nkhuku zoŵerengeka zotsalazo zinafa ndi nthenda. Zimenezo zinawononga bizinesi yanga ya nkhuku. Kwa zaka ziŵiri ndinayesa kupeza ntchito koma ndinalephera. Zinthu zinali zovutadi, koma Yehova anatichirikiza.
“Chimene chinandithandiza kwambiri kupirira nthaŵi zovutazo chinali kuzindikira kuti Yehova amalola zinthu kuchitika kwa ife kuti tiyengeke. Ine ndi mkazi wanga tinapitiriza kuphunzira Baibulo, ndipo zimenezi zinatithandizadi. Pemphero linatipatsanso nyonga. Nthaŵi zina kunali kovuta kuti ndipemphere, koma pamene ndinapemphera, ndinamva bwinopo.
“Mkati mwa nyengo yovuta imeneyo, ndinaphunzira phindu la kusinkhasinkha pa Malemba. Ndinkalingalira kwambiri za Salmo 23, limene limanena za Yehova monga Mbusa wathu. Lemba lina limene linandilimbikitsa linali Afilipi 4:6, 7, limene limanena za ‘mtendere wa Mulungu wakupambana chidziŵitso chonse.’ Lemba lina limene linandilimbitsa linali 1 Petro 5:6, 7, limene limati: ‘Dzichepetseni pansi pa dzanja la mphamvu la Mulungu, kuti panthaŵi yake akakukwezeni; ndi kutaya pa iye nkhaŵa yanu yonse pakuti iye asamalira inu.’ Mavesi onseŵa anandithandiza m’nthaŵi zovutazo. Pamene musinkhasinkha, malingaliro abwino amatenga malo a zinthu zimene zimakuchititsani kupsinjika maganizo.
“Tsopano ndinaloŵanso ntchito, koma kunena zoona, zinthu nzovutabe. Monga momwe Baibulo linaneneratu pa 2 Timoteo 3:1-5, tikukhala mu ‘masiku otsiriza,’ odziŵika ndi ‘nthaŵi zoŵaŵitsa.’ Sitingasinthe zimene malemba amanena. Motero sindikuyembekezera kuti moyo ungakhale wofeŵa. Komabe, ndikuona kuti mzimu wa Yehova ukundithandiza kupirira.”
Mosasamala kanthu za nthaŵi zovuta zimene tikukhalamo, awo amene amakhulupirira Yehova ndi Mwana wake Mfumu, Kristu Yesu, sadzagwiritsidwa mwala. (Aroma 10:11) Yesu mwiniyo anatitsimikizira kuti: “Chifukwa chake ndinena kwa inu, Musadere nkhaŵa moyo wanu, chimene mudzadya ndi chimene mudzamwa; kapena thupi lanu, chimene mudzavala. Kodi moyo suli woposa chakudya, ndi thupi loposa chovala? Yang’anirani mbalame za kumwamba, kuti sizimafesa ayi, kapena sizimatema ayi, kapena sizimatutira m’nkhokwe; ndipo Atate wanu wa kumwamba azidyetsa. Nanga inu mulibe kusiyana nazo kuziposa kodi? Ndipo ndani wa inu ndi kudera nkhaŵa angathe kuwonjezera pa msinkhu wake mkono umodzi? Ndipo muderanji nkhaŵa ndi chovala?”—Mateyu 6:25-28.
Mafunso amenewo alidi ofufuza mtima m’masiku ano oŵaŵitsa. Koma Yesu anapitiriza ndi mawu olimbikitsa aŵa: “Tapenyetsani maluŵa a kuthengo, makulidwe awo; sagwiritsa ntchito, kapena sapota: koma ndinena kwa inu, kuti angakhale Solomo mu ulemerero wake wonse sanavala monga limodzi la ameneŵa. Koma ngati Mulungu aveka chotero maudzu a kuthengo, akhala lero, ndi maŵa oponyedwa pamoto, nanga si inu kopambana ndithu, inu akukhulupirira pang’ono? Chifukwa chake musadere nkhaŵa, ndi kuti, Tidzadya chiyani? kapena, Tidzamwa chiyani? kapena, Tidzavala chiyani? Pakuti anthu akunja azifunitsa zonse zimenezo; pakuti Atate wanu wa kumwamba adziŵa kuti musoŵa zonse zimenezo. Koma muthange mwafuna Ufumu wake ndi chilungamo chake, ndipo zonse zimenezo zidzawonjezedwa kwa inu.”—Mateyu 6:28-33.
Nthaŵi Zabwinopo Mtsogolo
Pali umboni woonekeratu wakuti m’mbali zambiri za dziko, mikhalidwe yomanyonyosoka ya zachuma ndi kakhalidwe idzapitiriza kuipiraipira. Komabe, anthu a Mulungu amazindikira kuti mikhalidwe imeneyi ili yakanthaŵi. Ulamuliro waulemerero wa Mfumu Solomo unachitira chithunzi ulamuliro wolungama wa Mfumu yokulirapo kuposa Solomo imene idzalamulira dziko lonse lapansi. (Mateyu 12:42) Mfumu imeneyo ndiyo Kristu Yesu, “Mfumu ya mafumu, ndi Mbuye wa ambuye.”—Chivumbulutso 19:16.
Salmo 72, limene linali ndi kukwaniritsidwa koyamba kokhudza Mfumu Solomo, limalongosola ulamuliro waulemerero wa Yesu Kristu. Talingalirani zinthu zina zodabwitsa zimene limaneneratu za mtsogolo mwa dziko lapansi pansi pa Kristu monga Mfumu.
Mikhalidwe Yamtendere Padziko Lonse: Mu “masiku ake wolungama adzakhazikika; ndi mtendere wochuluka, kufikira sipadzakhala mwezi. Ndipo adzachita ufumu kuchokera kunyanja kufikira kunyanja. Ndi kuchokera ku Mtsinje kufikira malekezero a dziko lapansi.”—Salmo 72:7, 8.
Kusamalira Aumphaŵi: “Adzapulumutsa waumphaŵi wofuulayo; ndi wozunzika amene alibe mthandizi. Adzachitira nsoni wosauka ndi waumphaŵi, nadzapulumutsa moyo wa aumphaŵi. Adzawombola moyo wawo ku chinyengo ndi chiwawa; ndipo mwazi wawo udzakhala wa mtengo pamaso pake.”—Salmo 72:12-14.
Chakudya cha Mwana Alirenji: “M’dzikomo mudzakhala dzinthu dzochuluka pamwamba pa mapiri.”—Salmo 72:16.
Dziko Lapansi Lidzala ndi Ulemerero wa Yehova: “Wolemekezeka Yehova Mulungu, Mulungu wa Israyeli, amene achita zodabwiza yekhayo: ndipo dzina lake la ulemerero lidalitsike kosatha; ndipo dziko lonse lapansi lidzale nawo ulemerero wake.”—Salmo 72:18, 19.
Motero mtsogolomu mulidi nthaŵi zabwinopo.