Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • ws mutu 20 tsamba 161-169
  • Banja Laumunthu Lachimwemwe mu Ulamuliro wa Atate Watsopano

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Banja Laumunthu Lachimwemwe mu Ulamuliro wa Atate Watsopano
  • Chisungiko cha Padziko Lonse mu Ulamuliro wa “Kalonga wa Mtendere”
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Amene Ali Woyenerera Kukhala Atate
  • Zolengedwa Zoyamba Zaumunthu Kukhala ndi Atate
  • Chiyembekezo Chachimwemwe cha Akufa
  • Chisungiko cha Dziko Lonse Pansi pa “Kalonga wa Mtendere”
    Nsanja ya Olonda—1987
  • Chifukwa Chake Iye Ali Wofunika Kwambiri
    Galamukani!—2006
  • Mdani Wathu Womalizira Adzawonongedwa
    Nsanja ya Olonda—2014
  • Yesu Kristu, kupyolera mwa Amene Mulungu Adzawadalitsa Anthu
    Coonadi Cimene Cimatsogolera ku Moyo Wamuyaya
Onani Zambiri
Chisungiko cha Padziko Lonse mu Ulamuliro wa “Kalonga wa Mtendere”
ws mutu 20 tsamba 161-169

Chaputala 20

Banja Laumunthu Lachimwemwe mu Ulamuliro wa Atate Watsopano

1. Kodi nchifukwa ninji nkhani ya atate watsopano iri mbiri yabwino motero kubanja laumunthu?

PAMBUYO pa Armagedo, anthu onse adzayembekezera atate wachiŵiri. Ndithudi imeneyo iri mbiri yabwino! Atate watsopano amatheketsa moyo wamuyaya mu ungwiro waumunthu m’paradaiso wa padziko lonse lapansi, chifukwa chakuti Atate watsopano wa banja laumunthu mwiniyo ngwosafa. Iye ali ndi mphamvu ya kuperekera moyo wamuyaya kwa onse amene akuŵalandira kukhala ana ake padziko lapansi.

2. Kodi nchifukwa ninji atate watsopano ali wofunika?

2 Atate watsopano ngwofunika chifukwa chakuti anthu anataya atate wawo woyamba, atate amene ali Mlengi. Mzera wakubadwa umene uchokera pa Yesu kubwerera m’mbuyo kwa munthu woyamba, Adamu, umamaliza mwa kutipatsa mpambo uwu: “Kainane, mwana wa Enosi, mwana wa Seti, mwana wa Adamu, mwana wa Mulungu.”—Luka 3:37, 38.

3. Kodi kutayikiridwa kwa anthu onse ndi atateyo Yehova Mulungu kunali kwakukulu motani?

3 Kutayikiridwa kwawo ndi atate amene ali Yehova Mulungu kunatsimikizira kukhala tsoka kwa anthu onse. Mbadwa za Adamu zinalandira choloŵa cha chitsutso cha imfa. Nkhaniyo yalongosoledwa momvekera bwino pa Aroma 5:12: “Uchimo unaloŵa m’dziko lapansi mwa munthu mmodzi, ndi imfa mwa uchimo; chotero imfa inafikira anthu onse, chifukwa kuti onse anachimwa.” “Munthu mmodzi” ameneyu anali Adamu, ndipo chifukwa cha tchimo lake ladala, anatayikiridwa ndi atate ndi Mlengi wake, Yehova.

4. Kodi ndani amene anadzakhala atate wa Adamu ndi wa anthu?

4 Pamenepa kodi Adamu anakhala atate wayani? Kodi iye anabweretsa anthu kwa Atate uti? Akakhala atate amene anapeza chipambano pa iye kuti apanduke m’banja la ana onse a Mulungu omvera kumwamba ndi padziko lapansi. Akakhala atate amene analankhula bodza loyamba, Satana Mdyerekezi. Kodi ndimotani mmene Wotsutsa Yehova ameneyo anachitira zimenezi?

5. (a) Kodi ndichamoyo chiti chimene Satana Mdyerekezi anagwiritsira ntchito kunyenga mkazi wa Adamu kuloŵa m’kusamvera Mulungu? (b) Kodi nchifukwa ninji ndipo ndimotani mmene Adamu anakhalira ndi liwongo mwa chochita chake?

5 Pa 2 Akorinto 11:3 mtumwi Paulo akuulula nkhaniyo, mwa kulemba kuti: “Njoka inanyenga Heva ndi kuchenjera kwake.” Mwa machenjera, Satana anagwiritsira ntchito njoka m’Edene kulankhula bodza loyamba kwa Hava wosanyumwayo, amene monama anaimba Yehova Mulungu mlandu wa kunama. (Genesis 3:1-7; Yohane 8:44) Adamu sanalungamitse mkazi wake. Iye sanakane kudya naye ndipo sanakonze mkhalidwewo. Tchimo lake ladala linachititsa Njoka kupeza chipambano. Akumaika liwongo pamene linayenerera, 1 Timoteo 2:14 amalongosola kuti: “Adamu sananyengedwa, koma mkaziyo ponyengedwa analoŵa m’kulakwa.”

Amene Ali Woyenerera Kukhala Atate

6, 7. Kodi ndimtundu wa atate wotani umene Yesu anadzisonyeza kukhala woyenerera, ndipo ulosi Wabaibulo unasonyeza motani zimenezo?

6 Pokana kulambira “Mulungu wa nthaŵi ino ya pansi pano,” Yesu anatsimikizira kuti anali Iye amene anayenera kukhala atate wachiŵiri wa banja laumunthu. (2 Akorinto 4:4; Mateyu 4:1-11; Luka 4:1-13) Kuyambira pa kubadwa kwake kwaumunthu mu 2 B.C.E., anali Iye amene ulosi wa Yesaya 9:6 unagwirako ntchito wakuti:

7 “Kwa ife mwana wakhanda wabadwa, kwa ife mwana wamwamuna wapatsidwa; ndipo ulamuliro udzakhala papheŵa lake, ndipo adzamutcha dzina lake Wodabwitsa, Wauphungu, Mulungu wamphamvu, Atate Wosatha, Kalonga wa Mtendere.” Motero “Kalonga wa Mtendere” ali ndi mbali ina yofunika ya kuchitira anthu—ya kukhala ‘Atate wawo Wosatha.’

8. Kodi nchifukwa ninji Yesu anachititsidwa kuchitapo kanthu kuti akhale “Atate Wosatha” kwa anthu, ndipo kodi zimenezi zinatsimikiziridwa motani ndi mtumwi Paulo?

8 Mwana wa Mulungu akakhala “Atate Wosatha” kubanja laumunthu limeneli, limene anaperekera nsembe moyo wake waumunthu. Kuli monga momwe mtumwi Paulo analembera kuti: “Pakuti ngati ambiriwo anafa chifukwa cha kulakwa kwa mmodziyo, makamaka ndithu chisomo cha Mulungu, ndi mphatso yaulere zakuchokera ndi munthu mmodziyo Yesu Kristu, zinachulukira anthu ambiri. Chifukwa chake, monga mwa kulakwa kumodzi kutsutsa kunafikira anthu onse; chomwechonso mwa chilungamitso chimodzi chilungamo cha moyo chinafikira anthu onse.”—Aroma 5:15, 18.

9. Kodi ndimotani mmene Yesu anafikira kukhala Adamu wachiŵiri kwa anthu, koma ali Atate wa anthu kuchokera kumalo ati?

9 Motero, pali kuyenerana ndendende kwa nkhani zofunika zimenezi. Iye wochita “tchimo limodzi” anali munthu woyamba padziko lapansi, Adamu. “Chochitika chimodzi cha chilungamo” chinachitidwa ndi munthu wina wangwiro yekha, Yesu. Zimenezi zinamtheketsa kukhala “Atate Wosatha” wa mbadwa za Adamu wochimwayo. Mwanjira imeneyi akukhala Adamu wachiŵiri kubanja laumunthu. Nsembe ya moyo waumunthu wangwiro ndi kuperekedwa kwa kuyenera kwa moyo waumunthu umenewo kwa Woweruza Wamkulu kumwamba zimakupangitsa kukhala kosatheka kwa iye kutumikira pano padziko lapansi monga atate wosatha wa anthu. Pamene anaukitsidwa kwa akufa, anabwezeretsedwera kumalo auzimu ndipo anakwezedwera kudzanja lamanja la Womuukitsayo. Motero kwalongosoledwa kuti: “Munthu woyamba, Adamu, anakhala mzimu wamoyo. Adamu wotsirizayo anakhala mzimu wakulenga moyo.” (1 Akorinto 15:45) Wolandira anthu kukhala Atate wawo watsopano, adzawapatsa chiyambi chabwino koposa chothekera m’moyo.”

Zolengedwa Zoyamba Zaumunthu Kukhala ndi Atate

10. Kodi ndani amene ali zolengedwa zoyamba zaumunthu zimene zikakhala ndi Atate watsopano ameneyo?

10 “Atate Wosatha,” Yesu Kristu Mfumuyo, adzasonyeza oyamba amene adzakhala atate wawo. Motani? Mwa kupulumutsa “m’chisautso chachikulu” anthu odzipatulira mamiliyoni ambiri amene tsopano ali ndi moyo. Iwo ndiwo “khamu lalikulu” la “nkhosa zina.”—Chivumbulutso 7:9, 14.

11. Kodi ndimwaŵi wa padziko lapansi wotani umene uli pamaso pa onga nkhosa opulumuka “chisautso chachikulu”?

11 Wosayerekezeredwa udzakhala mwaŵi wa padziko lapansi woikidwa pamaso pa “khamu lalikulu” pambuyo pa “chisautso chachikulu.” Zikumalongosoledwa monga mbali ya “chizindikiro” cha ‘mapeto a dongosolo limeneli la zinthu,’ mbuzi zophiphiritsira za fanizo la Yesu zidzadulidwa padziko lino lapansi, chimene chidzatanthauza chiwonongeko chake chosatha. Koma sikudzatero kwa “khamu lalikulu” la onga nkhosa amene mwachikondi ndi mokhulupirika anachitira zabwino otsalira a “abale” auzimu a Kristu amene akali padziko lapansi. (Mateyu 25:31-46) Kupulumutsidwa kwa “nkhosa” zimenezo kumka kumbali ina ya “chisautso chachikulu” ndi kuloŵa m’Kulamulira kwa Zaka Chikwi konenedweratuko kwa “Kalonga wa Mtendere” kudzatheketsa opulumuka ameneŵa kuloŵa m’madalitso a gawo la Ufumu. Iwo adzakhala nzika za padziko lapansi za “Kalonga wa Mtendere.”

12. Kodi ndimawu ati a Yesu onena za chiukiriro amene amasonyeza kuti moyo wamuyaya waikidwa pamaso pa awo olandira malo a padziko lapansi Aufumu?

12 Panthaŵi imeneyo mawu amene Yesu analankhula asanaukitse Lazaro kwa akufa adzakwaniritsidwa kwa awo oloŵa m’gawo la padziko lapansi Laufumu. Iye anati: “Ine ndine kuuka ndi moyo: wokhulupirira ine, angakhale amwalira, adzakhala ndi moyo; ndipo yense wa kukhala ndi moyo, nakhulupirira ine, sadzamwalira nthaŵi yonse.” (Yohane 11:25, 26) Kaamba ka kumvera kwawo kwa iye, iwo adzafikira moyo wangwiro waumunthu m’gawo la padziko lapansi Laufumu. Ngakhale wochita zoipa womvera chifundo amene anafa pambali pa Yesu pa Golgota adzapatsidwa mwaŵi wa kuloŵa m’Paradaiso. (Luka 23:43) Yesu adzachita mogwirizana ndi zonse zimene dzina lake lakuti “Atate Wosatha” limatanthauza.

Chiyembekezo Chachimwemwe cha Akufa

13. Kodi chiukiriro cha anthu akufa chidzatheketsa anthu odziŵika ati akale kuwonedwa pagawo la Ufumu la padziko lapansi?

13 Yesu mbadwa yapadera ya Abrahamu, ananena kuti kholo limeneli, mwana wake Isake, ndi mdzukulu wake Yakobo akawonedwa m’gawo la padziko lapansi la Ufumu wa Mulungu. (Mateyu 22:31, 32) Zimenezi zikakhala zotheka mwa chiukiriro. Monga momwe Yesu adanenera, anthu onse akufa amene ali m’manda achikumbukiro adzamva liwu la Mwana wa Mulungu ndi kutuluka. Mtsogolo mwawo pambuyo panthaŵiyo mudzadalira pamkhalidwe umene adzatenga.—Yohane 5:28, 29; Chivumbulutso 20:12-15.

14. Kodi nchiyani chimene chidzafunikira kuchitidwa pasadakhale kaamba ka awo amene adzalandira chiukiriro cha padziko lapansi, ndipo ndani amene adzakhala oyamba kukhala ndi mbali m’zikonzekero zimenezi?

14 Kudzafunikira kuchitidwa makonzedwe aakulu ponena za anthu amene adzaukitsidwa kumanda kupeza moyo padziko lapansi mu Ufumu wa “Atate Wosatha.” Choyamba makonzedwe amenewa adzachitidwa ndi opulumuka “nkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu Wamphamvuyonse” pa Armagedo. (Chivumbulutso 16:14, 16) Kuti ndi chiŵerengero chokulira motani cha “khamu lalikulu” la “nkhosa zina” za “Kalonga wa Mtendere” chimene chidzakhalapo panthaŵiyo sitidziŵa, koma padzakhala okwanira kuchita ntchitoyo.

15. Kodi ambiri adzatumikira m’malo antchito apadera ati kwa Atate watsopano wa anthu?

15 Salmo 45 limalankhula za “Kalonga wa Mtendere” ameneyu kukhala Mfumu, ndipo popeza kuti iye adzakhala “Atate Wosatha,” wa anthu salmo limeneli limati kwa iye: “Mmalo mwa makolo ako iwo adzakhala ana ako, udzaŵaika akhale akalonga m’dziko lonse lapansi.” (Salmo 45:16, NW) Koma ngakhale chiukiriro cha “makolo” okhulupirika amenewo chisanachitike, mamembala aamuna a “khamu lalikulu” la opulumuka Armagedo adzakhala ataikidwa kumalo antchito amenewo aukalonga. Zikwi zambiri za oyembekezera kupulumuka Armagedo zimenezo zikutumikira kale monga akulu m’mipingo yoposa 49-000 ya Mboni za Yehova, kuyang’anira zofunika zauzimu m’mipingo yosiyanasiyana imene amayang’anira.

16. (a) Mwa uyang’aniro wa akalonga, kodi opulumuka Armagedo adzatumikira m’ntchito iti? (b) Kodi ndimafunso otani amene amabuka ponena za dongosolo m’limene akufawo adzaukitsidwa?

16 Mwa uyang’aniro waukalonga, opulumuka Armagedo adzatumikira mwachangu chogwirizanika. Kuti ndimalangizo otani amene “akalonga padziko lonse lapansi” adzalandira kuchokera kwa “Kalonga wa Mtendere” wakumwamba sitidziŵa, adzapereka chochitika chochititsa chidwi kwa anzawo onse opulumuka Armagedo. Talingalirani za zovala zonse zimene zidzafunikira kusokedwa kuveka moyenerera akufa oukitsidwa! Talingalirani zakudya zonse zimene zidzafunikira kugaŵiridwa, kapena kuikidwa m’nkhokwe! Malo okhala adzafunikiranso kulinganizidwa. Idzakhala nthaŵi yochititsa chidwi chotani nanga kwa onse amene adzakhala ndi phande m’ntchito yokonzekera imeneyi! Kodi ndani amene adzaukitsidwa choyamba? Kodi iwo adzaukitsidwa m’dongosolo la kubwerera m’mbuyo mogwirizana ndi njira imene anapitira nayo m’manda achikumbukiro? Kodi wophedwera chikhulupiriro Abele, ndi Enoke, amene anatengedwa ndi Mulungu, limodzi ndi Nowa, Abrahamu, Isake, Yakobo, ndi aneneri onse okhulupirika, adzafupidwa mwapadera mwa kuukitsidwa choyamba?

17. Kodi ndani amene adzapanga chosankha ponena za dongosolo m’limene akufa adzaukitsidwira kumoyo padziko lapansi, ndipo ndidzina laulemu liti lonenedweratu ponena za iye limene limasonyeza kukhoza kwake kusenza mathayo ake?

17 “Kalonga wa Mtendere” amadziŵa ndipo adzapanga chosankha cha zimenezi. Ndipo iye adzakhala woyeneretsedwa mokwanira kaamba ka mathayo ake monga Atate watsopano wa anthu owomboledwa. Lina la maina ake aulemu onenedweratu linali “Mulungu Wamphamvu.” Limenelo limasonyeza kuti iye akakhala Munthu wamkulu, ndi Wamphamvu. Chisonyezero cha umulungu wake chidzakhala champhamvu m’chakuti iye adzaukitsa anthu onse olipiridwira dipo, akumakumbukira maina awo ndi maumunthu awo. (Yohane 5:28, 29; Machitidwe 10:42) Iye ali wokhoza kotheratu kuchotsa chivulazo chonse chimene Satana Mdyerekezi wachita mkati mwa zaka 6 000 zapitazo za kukhalapo kwa anthu.

18. (a) Kodi ndimotani mmene kufunika kwakuti Adamu akhale kholo la Yesu Kristu kunapeŵedwera? (b) Kodi ndimotani mmene Yesu anachititsidwira kukhala atate wachiŵiri wa mbadwa za Adamu?

18 Adamu woyamba anapitirizira chiweruzo cha imfa kwa mbadwa zake zonse. Kodi Adamu anakhala kholo laumunthu la Yesu Kristu? Ayi, Yesu analibe atate waumunthu koma anabadwa mwa namwali amene anakhala ndi pakati mwa mphamvu ya moyo imene Mulungu anasamutsa kuchokera kumalo auzimu. Chotero Adamu wochimwa sanakhale kholo la Mwana wa Mulungu wa padziko lapansi ameneyo. Komabe, Adamu wachiŵiri, wafikira kukhala mzimu wopatsa moyo. Ali ndi mphamvu imeneyi angakwaniritse ulosi wa Yesaya ndi kukhala “Atate Wosatha” kwa mbadwa za Adamu woyamba, zimene amaombola ndi kuzilandira ndi chifuno cha kubwezeretsa moyo waumunthu wangwiro padziko lapansi la paradaiso.

19. Kodi ndiunansi watsopano wotani kulinga kwa anthu umene Yehova Mulungu adzakhala nawo, ndipo motero ndichiwembu chotani cha Satana Mdyerekezi chimene adzalepheretsa?

19 Mwanjira yotero Atate wakumwamba wa Yesu Kristu adzafikira kukhala Gogo wakumwamba wa banja laumunthu lobwezeretsedwa. Chifukwa cha chimenechi banja laumunthu lidzaloŵa muunansi watsopano ndi Mlengi wakumwamba ndi dziko lapansi. Ndi kalelonse sikunatheke ndi pang’ono pomwe kuti Yehova alephere chifuno chake choyambirira. Motero Yehova adzakhala atalepheretsa chiwembu cha Satana Mdyerekezi chankhalwe, chopanda umulungu. Banja lonse laumunthu lowomboledwa lidzazindikira chowonadi chimenechi. Lidzakhala tsiku lokondweretsa chotani nanga pamene Yesu Kristu akhala atate wabanja laumunthu kuti alere anthu m’Paradaiso wobwezeretsedwa padziko lapansi!

[Chithunzi pamasamba 164, 165]

Kristu, m’mphamvu yaufumu, akhala “Atate Wosatha” kwa onse amene awalandira

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena