-
Sayansi: Kodi Yatsimikiziritsa Baibulo Kukhala Lolakwa?Baibulo—Kodi Ndilo Mawu a Mulungu Kapena a Munthu?
-
-
Mutu 8
Sayansi: Kodi Yatsimikiziritsa Baibulo Kukhala Lolakwa?
Mu 1613 wasayansi Wachitaliyana Galileo anafalitsa bukhu lotchedwa “Letters on Sunspots.” Mmenemo, iye anaperekamo umboni wakuti dziko lapansi limazungulira dzuŵa, koposa dzuŵa kuzungulira dziko lapansi. Mwakutero, iye anayambitsa kuyenda kwa mpambo wa zochitika zimene potsirizira pake zinamchititsa kukawonekera pamaso pa Bwalo Lachiweruzo Lachiroma pamlandu wa “kukaikiridwa kukhala akufalitsa manong’onong’o.” Potsirizira pake, iye anakakamizidwa “kusintha.” Kodi nchifukwa ninji lingaliro lakuti dziko lapansi limayenda mozugulira dzuŵa linawonedwa kukhala manong’onong’o? Chifukwa chakuti otsutsa a Galileowo ananena kuti kunali kosemphana ndi zimene Baibulo limanena.
1. (Phatikizamoni mawu oyamba.) (a) Kodi nchiyani chimene chinachitika pamene Galileo anapereka lingaliro lakuti dziko lapansi limayenda kuzungulira dzuŵa? (b) Ngakhale kuli kwakuti Baibulo siliri bukhu lophunzirira sayansi, kodi timapezanji pamene tiliyerekezera ndi sayansi yamakono?
KUMANENEDWA mofalala lerolino kuti Baibulo liri losagwirizana ndi sayansi, ndipo ena amaloza kuzokumana nazo za Galileo kukutsimikizira. Koma kodi ziri choncho? Poyankha funso limenelo, tiyenera kukumbukira kuti Baibulo liri bukhu laulosi, mbiri, pemphero, lamulo, uphungu, ndi chidziŵitso chonena za Mulungu. Silimadzinenera kukhala bukhu lophunzirira sayansi. Komabe, pamene Baibulo likhudza nkhani zonena za sayansi, zimene iro limanena ziri zolondola kotheratu.
Planeti Lathuli Dziko Lapansi
2. Kodi Baibulo limafotokoza motani malo a dziko lapansi m’mlengalenga?
2 Mwachitsanzo, talingalirani zimene Baibulo limanena ponena za planeti lathuli, dziko lapansi. M’bukhu la Yobu, timaŵerenga kuti: “[Mulungu] ayala kumpoto popanda kanthu, nalenjeka dziko pachabe.” (Yobu 26:7) Yerekezerani zimenezi ndi mawu a Yesaya, pamene iye akunena kuti: “Iye amene akhala pamwamba pamalekezero a dziko lapansi.” (Yesaya 40:22) Chithunzithunzi choperekedwa chonena za dziko lapansi lobulungira ‘lolenjekeka pachabe mmalo opanda kanthu’ chimatikumbutsa mwamphamvu za zithunzithuzi zojambulidwa ndi akatsiwiri opita kutali m’mlengalenga za mpira wathuwu dziko lapansi likuyandama m’mlengalenga mopanda kanthu.
3, 4. Kodi madzi a padziko lapansi amayenda motani, ndipo kodi Baibulo limanenanji ponena za zimenezi?
3 Lingaliraninso, zungulirezungulire wodabwitsayo wa madzi a dziko lapansi. Compton’s Encyclopedia imafotokoza zimene zimachitika motere: “Madzi . . . amasanduka nthunzi kuchokera pamwamba panyanja zazikulu kumka m’mlengalenga . . . Mphepo yomayenda mosalekezayo m’mlengalenga mwa dziko lapansi imanyamula madzi okhala ndi chinyonthowo kumka nawo kumtunda. Pamene mpweyawo uzizira, nthunziyo imagwirana kupanga timadontho tachipale. Ameneŵa mofala amawoneka kukhala mitambo. Kaŵirikaŵiri timadonthoto timagwirizana pamodzi kupanga madontho amvula. Ngati m’mlengalenga muli mozizira mokwanira, timiyala tamadzi oundana timapangika mmalo mwa madontho amvula. M’chochitika chirichonse, madzi amene ayenda kuchokera kunyanja makilomitala mazanamazana kapena ngakhale zikwizikwi amagwera pankhope ya dziko lapansi. Kumeneku amasonkhana pamodzi kukhala mitsinje kapena amakhathamira m’nthaka ndi kuyamba ulendo wake wobwerera kunyanja.”1
4 Njira yapadera imeneyi, imene imatheketsa moyo pamtunda wouma kukhala wothekera, inafotokozedwa bwino lomwe pafupifupi zaka 3 000 zapitazo m’mawu osavuta, ndi olunjika m’Baibulo: “Mitsinje yonse imayenda kumka kunyanja, komabe nyanja sizimasefukira; amabwereranso kumene mitsinjeyo inachokera kuti akayendenso.”—Mlaliki 1:7, The New English Bible.
5. Kodi mawu a wamasalmo ali amakono mwapadera motani ponena za mbiri ya mapiri a padziko lapansi ndi nthaŵi?
5 Mwinamwake chapaderanso kwambiri ndicho chidziŵitso cha Baibulo m’mbiri yamapiri. Nazi zimene bukhu lophunzirira za miyala limanena: “Kuyambira panthaŵi ya kuphunzira za miyala isanakwane kudzafika m’nthaŵi yamakono, njira yosalekeza ya kupanga ndi kuwononga mapiri yapitirizabe. . . . Sikokha kuti mapiri apangika kuyambira pansi pa nyanja zofafanizika, koma iwo kaŵirikaŵiri amizika asanapangike, ndiyeno atumphukanso.”2 Yerekezerani zimenezi ndi kanenedwe ka ndakatulo ka wamasalmo: “Mudalikuta [dziko lapansi] ndi nyanja ngati ndi chovala; madzi anafikira pamwamba pamapiri. Anakwera m’mapiri, anatsika m’zigwa, kufikira malo mudawakonzeratu.”—Salmo 104:6, 8.
“Pachiyambi”
6. Kodi ndimawu otani a Baibulo amene ali ogwirizana ndi nthanthi zamakono za sayansi ponena za chiyambi cha chilengedwe?
6 Vesi loyambirira lenilenilo la Baibulo limati: “Pachiyambi Mulungu analenga kumwamba ndi dziko lapansi.” (Genesis 1:1) Mafufuzidwe achititsa asayansi kupereka lingaliro lakuti chilengedwe chakuthupichi chinalidi ndi chiyambi. Sichinakhaleko kwa nthaŵi yonse. Katswiri wa zakuthambo Robert Jastrow, wosakhulupirira m’nkhani zachipembedzo, analemba kuti: “Mfundozo zimasiyana, koma mbali zofunika m’zolembedwa zakuthambo ndi za Baibulo za Genesis ziri zofanana: mtandadza wa zochitika kukafika kwa munthu unayamba mwadzidzidzi ndi mofulumira panyengo ya nthaŵi yotsimikizirika, m’kuthwanima kwa kuunika ndi nyonga.”3
7, 8. Ngakhale kuli kwakuti sakuvomereza mbali ya Mulungu m’nkhaniyo, kodi nchiyani chimene asayansi ambiri akakamizika kuvomereza ponena za chiyambi cha chilengedwe chonse?
7 Zowona, asayansi ambiri, pamene kuli kwakuti amakhulupirira kuti chilengedwe chinali ndi chiyambi, samavomereza mawu akuti “Mulungu analenga.” Komabe, ena tsopano amavomereza kuti nkovuta kunyalanyaza umboni wanzeru kutseri kwa chirichonse. Profesala wa sayansi ya chilengedwe Freeman Dyson akunena kuti: “Pamene ndikupenda chilengedwe ndi kuphunzira mfundo zake zatsatanetsatane za kaumbidwe, npamene ndikupeza umboni wakuti chilengedwe m’lingaliro lina chiyenera kukhala chitadziŵa kuti ife tinalinkudza.”
8 Dyson akupitirizabe kuvomereza kuti: “Pokhala wasayansi, wophunzitsidwa zizoloŵezi za kuganiza ndi chinenero za m’zaka za zana lamakumi aŵiri osati za m’zaka za zana la khumi ndi chisanu ndi chitatu, sindikunena kuti kaumbidwe kachilengedwe kamatsimikizira kukhalapo kwa Mulungu. Ndikungonena chabe kuti kaumbidwe ka chilengedwe kali kogwirizana ndi nthanthi yakuti luntha limachita mbali yofunika m’kugwira kwake ntchito.”4 Mawu ake ndithudi amasonyeza kaimidwe ka maganizo kokaikira ka m’nthaŵi yathu. Koma atakankhira pambali kukaikira kumeneku, munthuyo amawona kuti pali kugwirizana kwapadera pakati pa sayansi yamakono ndi mawu a Baibulo akuti “pachiyambi Mulungu analenga kumwamba ndi dziko lapansi.”—Genesis 1:1.
Thanzi ndi Ukhondo
9. Kodi ndimotani mmene lamulo la Baibulo lonena za nthenda yoyambukira ya khungu limasonyezera nzeru? (Yobu 12:9, 16a)
9 Talingalirani mmene Baibulo limagwirira ntchito kumbali ina: thanzi ndi ukhondo. Mwachitsanzo, ngati Mwisrayeli anali ndi mathothomathotho pakhungu okaikiridwa kukhala khate, iye anali kubindikiritsidwa. “Masiku onse amene mliriwo uli mwa iye iye adzakhala wodetsedwa. Iye ali wodetsedwa. Iye ayenera kukhala kwayekha. Kunja kwa msasa ndiwo malo ake okhala.” (Levitiko 13:46) Ngakhale malaya oyambukiridwa anali kuwotchedwa. (Levitiko 13:52) M’masikuwo, imeneyi inali njira yogwira mtima yotetezerera kufalikira kwa nthenda zopatsana.
10. Kodi ndim’njira yotani mmene ambiri m’maiko ena akapindulira ndi kutsatira uphungu wa Baibulo wonena za ukhondo?
10 Lamulo lina lofunika linali lonena za kutayidwa kwa matudzi a anthu, amene anafunikira kukwiriridwa kunja kwa msasa. (Deuteronomo 23:12, 13) Mosakaikira lamulo limeneli linatchinjirizira Israyeli kumatenda ambiri. Ngakhalenso lerolino, mavuto aakulu a zathanzi mmalo ena amachititsidwa ndi kutayidwa mosayenera kwa zoipa zotuluka mwa anthu. Ngati anthu m’maiko amenewo akadangotsatira lamulo lolembedwa zaka zikwi zochuluka zapitazo m’Baibulo, iwo akanakhala athanzi kwambiri.
11. Kodi ndiuphungu wa Baibulo wotani wonena za thanzi la maganizo umene wapezedwa kukhala wogwira ntchito?
11 Muyezo wapamwamba wa Baibulo wa kasungidwe kathupi unaphatikizapo ngakhale thanzi la malingaliro. Mwambi wa Baibulo umati: “Mtima wabwino ndimoyo wathupi; koma nsanje ivunditsa mafupa.” (Miyambo 14:30) M’zaka zaposachedwapa, kufufuza kwa a zachipatala kwasonyeza kuti thanzi lathu lakuthupi limayambukiridwadi ndi kaimidwe kathu kamaganizo. Mwachitsanzo, dokotala C. B. Thomas wa pa Yunivesite ya Johns Hopkins anapenda ophunzira omaliza maphunziro oposa chikwi mkati mwa nyengo ya zaka 16, akumayerekezera mkhalidwe wawo wakuthupi ndi kukhala kwawo osachedwa kugwidwa ndi matenda. Chinthu chimodzi chimene iye anawona nchakuti: Omaliza maphunziro osachedwa kwambiri kugwidwa ndi matenda anali awo amene anali opsa mtima kwambiri ndi odera nkhaŵa mopambanitsa pamene apsinjika.5
Kodi Baibulo Limanenanji?
12. Kodi nchifukwa ninji Tchalitchi cha Katolika chinaumirira kuti nthanthi ya Galileo yonena za dziko lapansi inali manong’onong’o?
12 Ngati Baibulo liri lolondola motero pankhani za sayansi, nangano, kodi nchifukwa ninji, Tchalitchi cha Katolika chinanena kuti chiphunzitso cha Galileo chakuti dziko limazungulira dzuŵa chinali chosagwirizana ndi Malemba? Chifukwa cha mmene akuluakulu anatanthauzirira mavesi ena a Baibulo.6 Kodi iwo anali olondola? Tiyeni tiŵerenge ziŵiri za ndime zimene iwo anagwira mawu ndi kuwona.
13, 14. Kodi ndimavesi a Baibulo ati amene Tchalitchi cha Katolika chinagwiritsira ntchito molakwa? Fotokozani.
13 Ndime imodzi imati: “Dzuŵa limatuluka, dzuŵa limaloŵa; ndiyeno limathamanga kumka kumalo ake ndipo kumeneko limatuluka.” (Mlaliki 1:5, The Jerusalem Bible) Malinga ndi kunena kwa chigomeko cha Tchalitchicho, mawu akutiwo “dzuŵa limatuluka” ndi “dzuŵa limaloŵa,” amatanthauza kuti dzuŵa, osati dziko lapansi, likuyenda. Komatu ngakhale lerolino timanena kuti dzuŵa limatuluka ndi kuloŵa, ndipo ochuluka a ife timadziŵa kuti ndilo dziko lapansi limene limayenda, osati dzuŵa. Pamene tigwiritsira ntchito mawu onga ngati ameneŵa, tikungofotokoza kokha kayendedwe kowonekera kadzuŵa monga momwe kamawonekerera kwa wopenyerera waumunthu. Ndipo wolemba Baibuloyo anali kungochita kwenikweni motero.
14 Ndime ina imati: “Inu munakhazika dziko lapansi pamaziko ake, losagwedezeka kosatha.” (Salmo 104:5, The Jerusalem Bible) Ameneŵa anatanthauziridwa kukhala akutanthauza kuti pambuyo pa kulengedwa kwake dziko lapansi silikanathanso kusunthika. Komabe, kunena zowona, vesilo likugogomezera kukhalitsa kwa dziko lapansi, osati kusasunthika kwake. Dziko lapansi ‘silidzagwedezedwa’ kulifafaniza, kapena kuwonongedwa, monga momwe mavesi ena amatsimikizira. (Salmo 37:29; Mlaliki 1:4) Ndiponso, lemba iri, liribenso chochita chirichonse ndi kuyenda kwenikweni kwa dziko lapansi ndi dzuŵa. Chidali Tchalitchi m’nthaŵi ya Galileo, chimene chinadodometsa kukambitsirana komasuka kwasayansi, osati Baibulo.
Chisinthiko ndi Chilengedwe
15. Kodi nchiyani chimene chiri nthanthi ya chisinthiko, ndipo kodi ndimotani mmene imatsutsanira ndi Baibulo?
15 Komabe, pali mbali imene ambiri akanena kuti sayansi yamakono ndi Baibulo ziri zosemphana motayitsa mtima. Asayansi ochuluka amakhulupirira nthanthi yachisinthiko, imene imaphunzitsa kuti zinthu zonse zamoyo zinasinthika kuchokera kumpangidwe wa moyo waung’ono umene unakhalako zaka mamiliyoni ochuluka zapitazo. Kumbali ina, Baibulo, limaphunzitsa kuti kagulu kalikonse kakakulu ka zamoyo kanalengedwa mwapadera ndipo kamabalana kokha “monga mwa mtundu wake.” Iri limanena kuti, munthu analengedwa “kuchokera m’dothi lapansi.” (Genesis 1:21; 2:7) Kodi chimenechi chiri cholakwa chachikulu chasayansi m’Baibulo? Tisanagamule, tiyeni tiyang’ane mosamalitsa pa zimene sayansi imadziŵa, mosiyana ndi zimene limaphunzitsa monga nthanthi.
16-18. (a) Kodi ndikupenda kotani kumene Charles Darwin anapanga kumene kunamtsogolera ku kukhulupirira m’chisinthiko? (b) Kodi tingatsutse motani kuti zimene Darwin anawona mu Zisumbu za Galápagos sizimatsutsana ndi zimene Baibulo limanena?
16 Nthanthi ya chisinthiko inachititsidwa kukhala yofala mkati mwa zaka za zana lathali ndi Charles Darwin. Pamene iye anali pa Zisumbu za Galápagos mu Pacific, Darwin anagwidwa mtima kwambiri ndi mitundu yosiyanasiyana ya mapingo a zisumbu zosiyanasiyana, imene, iye anayiganizira kuti yonseyo iyenera kukhala itatuluka kuchokera mumtundu umodzi wa kholo. Mwapang’ono chifukwa cha lingaliro limeneli, iye anapititsa patsogolo nthanthi yakuti zamoyo zonse zimachokera kumagwero amodzi a mpangidwe waung’ono. Iye anatsimikizira kuti, mphamvu yosonkhezera kutseri kwa chisinthiko cha zolengedwa zapamwamba kwambiri kuchokera m’zotsika, inali kusankha kwa chilengedwe, kupulumuka kwa zamphamvu kopambana. Chithokozo chimke kuchisinthiko, iye anatero, zinyama zapamtunda zinachokera kunsomba, mbalame zinachokera kwa abuluzi, ndi zina zotero.
17 Kunena zowona, zimene Darwin anawona m’zisumbu zakutali zimenezi sizinali zosagwirizana ndi Baibulo, limene limavomereza kukhalapo kwa kusiyanasiyana mkati mwa mtundu waukulu wa zamoyo. Mwachitsanzo, mafuko onse a anthu, anachokera kwa anthu aŵiri chabe oyambirira. (Genesis 2:7, 22-24) Chotero sichiri chinthu chachilendo kuti mitundu yosiyanasiyana imeneyo ya mapingo ikachokera kwa mtundu umodzi wa kholo. Koma iwo anakhalabe mapingo. Iwo sanasanduke kukhala akabaŵi kapena ziombankhanga.
18 Mitundu yosiyanasiyana ya mapingo kapena china chirichonse chimene Darwin anawona sizimatsimikizira kuti zinthu zonse zamoyo, kaya ndi anamngumi kapena akakoŵa, njovu kapena nyongolotsi, ziri ndi kholo limodzi. Komabe, asayansi ambiri amanena kuti chisinthiko sichirinso nthanthi chabe koma kuti nchenicheni. Ena, pamene kuli kwakuti akuzindikira zovuta za nthanthiyo, amanena kuti amangoikhulupirirabe. Nkofala kuchita motero. Komabe, tifunikira kudziŵa kaya ngati chisinthiko chatsimikiziridwa kufika pamlingo wakuti Baibulo liyenera kukhala lolakwa.
Kodi Chatsimikiziridwa?
19. Kodi cholembedwa cha mafupa ofukulidwa chimachirikiza chisinthiko kapena chilengedwe?
19 Kodi ndimotani mmene nthanthi ya chisinthiko ingapendedwere? Njira yowonekera bwino kopambana ndiyo kupenda cholembedwa cha mafupa ofukulidwa kuti tiwone ngati kusintha kwapang’onopang’ono kuchoka kumtundu umodzi kumka ku wina kunachitikadi. Kodi kunachitika? Ayi, monga mmene asayansi angapo mowona mtima amavomerezera. Mmodzi, Francis Hitching, akulemba kuti: “Pamene ufunafuna milumikizo pakati pa timagulu tatikulu tazinyama, iyo kulibeko.”7 Kusoŵeka kwa umboni kumeneku kuli kowonekera bwino kwambiri m’cholembedwa cha mafupa ofukulidwa kwakuti okhulupirira chisinthiko adza ndi njira zina zosiyana ndi nthanthi ya Darwin ya kusintha kwapang’onopang’ono. Komabe, chowonadi nchakuti, kuwoneka kwamwadzidzidzi kwa mitundu ya zinyama mu cholembedwa chamafupa ofukulidwa kumachirikiza kulengedwa kwapadera koposa mmene chimachitira chisinthiko.
20. Kodi nchifukwa ninji mmene maselo a moyo amadzichulukitsira samalolera chisinthiko kuchitika?
20 Ndiponso, Hitching akusonyeza kuti zolengedwa za moyo zinalinganizidwa kubala zamtundu wawo ndendende koposa ndi kusinthika kukhala kanthu kenanso. Iye akunena kuti: “Maselo amoyo amadzichulukitsa pafupifupi mokhulupirika kotheratu. Mlingo wa cholakwa uli waung’ono kopambana kwakuti palibe makina opangidwa ndi munthu amene angathe kuyandikirapo. Mulinso zoletsa zoumbiridwa mkati. Zomera zimafika paukulu wakutiwakuti ndipo zimakana kukula koposa pamenepo. Ntchentche za m’zipatso zimakana kukhala kanthu kena kalikonse koma ntchentche za m’zipatso pansi pa mikhalidwe iriyonse imene iri yodziŵika.”8 Pamene asayansi anakakamiza kuika kusinthika muntchentche za m’zipatso kwa zaka makumi ambiri, analephera kuzikakamiza kuti zikhale kanthu kananso.
Magwero a Moyo
21. Kodi ndilingaliro lotani lotsimikizidwa ndi Louis Pasteur limene limapanga vuto lalikulu kwa okhulupirira chisinthiko?
21 Funso lina lovuta kwambiri limene achisinthiko alephera kuliyankha nlakuti: “Kodi nchiyani chimene chinali magwero a moyo? Kodi ndimotani mmene mpangidwe woyambirira wosavutawo wa cholengedwa wa moyo—kumene ife tonse timayerekezeredwa kukhala titachokerako—unakhalirako? Zaka mazana ambiri zapitazo, zimenezi sizikanawonekera kukhala vuto. Anthu ochuluka panthaŵi imeneyo anaganiza kuti ntchentche zikatha kuchokera m’nyama yomavunda ndi kuti mulu wa ziguduli zakale ukatha potsirizira pake kutulutsa makoswe. Koma, zaka zoposa zana limodzi zapitazo, wosanganiza mankhwala Wachifrenchi Louis Pasteur anasonyeza kuti moyo ungathe kokha kuchokera kumoyo umene unalipo kale.
22, 23. Malinga ndi kunena kwa okhulupirira chisinthiko, kodi moyo unayamba motani, koma kodi zenizeni zikusonyezanji?
22 Chotero kodi ndimotani mmene achisinthiko amafotokozera magwero a moyo? Malinga ndi kunena kwa nthanthi yotchuka kopambana, kusanganikira kwa mwamwaŵi kwa makhemikolo ndi mphamvu kunayambitsa kukhalako kwa panthaŵi yomweyo kwa moyo zaka mamiliyoni ochuluka zapitazo. Bwanji nanga ponena za njira yochitira zinthu imene Pasteur anatumba? The World Book Encyclopedia inafotokoza kuti: “Pasteur anasonyeza kuti moyo sungathe kungobuka mwapanthaŵi yomweyo pansi pa mikhalidwe ya makhemikolo ndi ya zachilengedwe imene iripo padziko lapansi lerolino. Komabe, zaka mabiliyoni ambiri zapitazo, mkhalidwe wa makhemikolo ndi wa zachilengedwe padziko lapansi unali wosiyana kwambiri”!9
23 Komabe, ngakhale pansi pa mikhalidwe yosiyana kotheratu, pali kusiyana kwakukulu pakati pa zinthu zosakhala za moyo ndi chamoyo chaching’ono kopambana. M’bukhu lake lakuti Evolution: A Theory in Crisis, Michael Denton, akuti: “Pakati pa selo la moyo ndi dongosolo lolinganizidwa mwapamwamba kopambana losakhala la zamoyo, longa ngati kunyezimira kapena kachipanthi ka chipale, pali phompho lalikulu kwambiri ndi lotheratu losati nkukhoza kulizindikira.”10 Lingaliro lakuti zinthu zosakhala zamoyo zikatha kukhala ndi moyo mwamwaŵi wongochitika zokha liri lapatali kwambiri kwakuti nlosatheka. Kufotokoza kwa Baibulo, kwakuti ‘moyo unachokera m’moyo’ m’chakuti moyo unalengedwa ndi Mulungu, kuli kogwirizana mokhutiritsa maganizo ndi zenizeni.
Kulekeranji Chilengedwe
24. Mosasamala kanthu za mavuto a nthanthiyo, kodi nchifukwa ninji asayansi ambiri akuumirirabe kunthanthi yachisinthiko?
24 Mosasamala kanthu za zovuta zopezeka m’nthanthi yachisinthiko, kukhulupirira m’chilengedwe kukuwonedwa lerolino monga kosagwirizana ndi sayansi, ngakhale kwachilendo. Kodi nchifukwa ninji izi ziri choncho? Kodi nchifukwa ninji ngakhale akuluakulu onga ngati Francis Hitching, amene mowona mtima amasonya ku zofooka za chisinthiko, amakana lingaliro la chilengedwe?11 Michael Denton akufotokoza kuti chisinthiko, ndi zolephera zake zonse, chidzapitirizabe kuphunzitsidwa chifukwa chakuti nthanthi zogwirizana ndi chilengedwe “zimatembenuzira mowona mtima ku zoyambitsa zoposa zaumunthu.”12 M’kunena kwina, chenicheni chakuti chilengedwe chimaloŵetsamo Mlengi chimachipangitsa kukhala chosalandirika. Ndithudi, limeneli ndiro mtundu umodzimodziwo wa kulingalira kodziŵika kumene tinakumana nako m’chochitika cha zozizwitsa: Zozizwitsa nzosatheka chifukwa chakuti izo ziri zozizwitsa!
25. Kodi nchofooka chotani chachisinthiko, chimene malinga ndi kunena kwasayansi, chimasonyeza kuti icho sichiri choloŵa mmalo chogwira ntchito chachilengedwe m’kufotokoza chiyambi cha moyo?
25 Ndiponso, nthanthi yachisinthiko yeniyeniyo iri yokaikitsa kwambiri m’lingaliro la sayansi. Michael Denton akupitirizabe kunena kuti: “Pokhala kwenikweni nthanthi ya kuumbidwanso kwa m’mbiri, [nthanthi yachisinthiko ya Darwin] njosatheka kuyesa kuitsimikizira mwa kupenda kwa kuyesa kapena kupenda mwachindunji monga momwe kuli kozoloŵereka m’sayansi. . . . Ndi iko komwe, nthanthi yachisinthiko imaphatikizapo mpambo wa zochitika zapadera, chiyambi cha moyo, chiyambi cha luntha ndi zina zotero. Zochitika zapadera ziri zosabwerezedwanso ndipo sizingathe kuchititsidwa kukhala ndi mtundu uliwonse wa kupenda mwa kuyesa.”13 Chowonadi nchakuti, mosasamala kanthu za kukhala kwake yotchuka, nthanthi ya chisinthiko iri ndi zokaikitsa zambiri ndi zovuta kwakuti siimapereka chifukwa chabwino chokanira cholembedwa cha Baibulo cha chiyambi cha moyo. Mutu woyamba wa Genesis umapereka cholembedwa chomvekera bwino kotheratu cha mmene “zochitika zapadera” “zosabwerezedwanso” zimenezi zinachitikira mkati mwa ‘masiku’ a kulenga amene anali autali wa zaka zikwi zochuluka zanthaŵi.a
Bwanji Nanga Ponena za Chigumula?
26, 27. (a) Kodi Baibulo limanenanji ponena za Chigumula? (b) Kodi m’mbali ina, madzi a chigumula, ayenera kukhala atachokera kuti?
26 Ambiri amasonya ku chowonekera kukhala kusemphana kwina pakati pa Baibulo ndi sayansi yamakono. M’bukhu la Genesis, timaŵerenga kuti zaka zikwi zambiri zapitazo kuipa kwa anthu kunali kwakukulu kwambiri kwakuti Mulungu anatsimikizira kuwawononga. Komabe, iye analangiza munthu wolungama Nowa kumanga chingalaŵa chachikulu cha matabwa, chombo. Ndiyeno Mulungu anadzetsa chigumula pamtundu wonse wa anthu. Nowa yekha ndi banja lake anapulumuka, pamodzi ndi zoimira za mitundu yonse ya zinyama. Chigumulacho chinali chachikulu kwambiri kwakuti “mapiri onse aatali amene anali pansi pa thambo lonse anamira.”—Genesis 7:19, NW.
27 Kodi madzi onsewo anachokera kuti amene anakuta dziko lonse lapansi? Baibulo lenilenilo limayankha. Kuchiyambiyambiko m’kuchitika kwa chilengedwe, pamene mum’lengalenga mwamphepo munayamba kupangika, panakhala “madzi . . . pansi pa mlengalengamo” ndipo “madzi . . . pamwamba pa mlengalenga.” (Genesis 1:7, NW; 2 Petro 3:5) Pamene Chigumula chinadza, Baibulo limanena kuti: “Mazenera a chigumula akumwamba anatsegulidwa.” (Genesis 7:11, NW) Mwachiwonekere, “madzi . . . pamwamba pa mlengalenga” anagwa ndipo anapereka ochuluka a madzi amene anamizawo.
28. Kodi ndimotani mmene atumiki amakedzana a Mulungu, kuphatikizapo Yesu, anawonera Chigumula?
28 Mabukhu amakono ali oyedzamira kukutsutsa chigumula cha dziko lonse. Chotero tiyenera kufunsa kuti: Kodi Chigumulacho chiri nthano yongopeka chabe, kapena kodi icho chinachitikadi? Tisanaliyankhe, tiyenera kudziŵa kuti olambira akale a Yehova anavomereza Chigumula kukhala mbiri yeniyeni; iwo sanachilingalire kukhala nthano yongopeka. Yesaya, Yesu, Paulo, ndi Petro anali pakati pa awo amene anachitchula monga ngati kanthu kena kamene kanachitikadi. (Yesaya 54:9; Mateyu 24:37-39; Ahebri 11:7; 1 Petro 3:20, 21; 2 Petro 2:5; 3:5-7) Koma pali mafunso amene ayenera kuyankhidwa ponena za Chigumula cha dziko lonse.
Madzi a Chigumula
29, 30. Kodi nzenizeni zotani ponena za kuchuluka kwa madzi a padziko lapansi zimene zimasonyeza kuti chigumula chinalikodi?
29 Choyamba, kodi lingaliro la kumizidwa kwa dziko lonse lapansi siliri longoyerekezera mopambanitsa? Osati kwenikweni. Zowonadi, kumlingo wakutiwakuti dziko lapansi likali lokutidwabe ndi madzi. Maperesenti ake makumi asanu ndi aŵiri ali okutidwa ndi madzi ndipo 30 peresenti yokha ndiyo imene iri mtunda wouma. Ndiiko komwe, 75 peresenti ya madzi opanda mchere a dziko lapansi atsekeredwa m’miyala ya madzi oundana ndi kumathero a malo ozizira kopambana okhala m’chipale. Ngati chipale chonsechi chikadati chisungunuke, madzi a m’nyanja akachuluka kwambiri. Mizinda yonga ngati New York ndi Tokyo ikazimiririka.
30 Ndiponso, The New Encyclopædia Britannica imati: “Avareji ya kuzama kwa nyanja zonse zazikulu yayerekezeredwa kukhala mamitala 3 790 (mapazi 12 430), chiŵerengero chachikulu kopambana poyerekezera ndi cha avareji ya kutukuka kwa mtunda pamwamba pa moyambira nyanja, mmene muli mamitala 840 (mapazi 2 760). Ngati avareji ya kuzamayo ichulukitsidwa ndi malo ake enieni a mtundawo, kuchuluka kwa malo a Nyanja za Mchere za Padziko Lonse kuli kuwirikiza nthaŵi 11 kuposa mtunda wa pamwamba pa molekezera nyanjawo.”14 Chotero, ngati chirichonse chikanachititsidwa kukhala cha thyathyathya—ngati mapiri anachititsidwa kukhala athyathyathya ndipo pansi pa nyanjapo paadzazidwa—nyanja ikanakuta dziko lonse lapansi ndi kuzama kwa mamitala zikwi zambiri.
31. (a) Kuti Chigumula chikhale chitachitika, kodi mkhalidwe uyenera kukhala unali wotani padziko lapansi la Chigumula chisanakhale? (b) Kodi nchiyani chimene chimasonyeza kuti nkoyenerera kuti mapiri ayenera kukhala anali aafupi ndi kuti pansi pa nyanja panali posazama kwambiri Chigumula chisanadze?
31 Kuti Chigumulacho chichitike, pansi pa nyanja za Chigumula chisanachitike payenera kukhala panali posazama, ndipo mapiri anali aafupi koposa mmene aliri patsopano lino. Kodi zimenezi nzothekera? Eya, bukhu lina limanena kuti: “Kumene mapiri a dziko lonse tsopano ali aatali mochititsa chizumbazumba, nyanja zamchere ndi zigwa panthaŵi ina, zaka mamiliyoni ochuluka zapitazo, zinali tantha zathyathyathya zonse. . . . Mayendedwe a malo athyathyathya pansi pa makontinenti amachititsa mtunda ponse paŵiri kukwera kufika pautali kumene zinyama zolimba kopambana ndi zomera zingathe kukhala ndi moyo ndipo, kumbali inayo, kutsika ndi kukhala obisika mozama muulemerero pansi pa nyanja.”15 Popeza kuti mapiri ndi pansi pa nyanja pamakwera ndi kutsika, kuli kwachiwonekere kuti panthaŵi ina mapiri sanali aatali monga momwe aliri patsopano lino ndipo pansi pa nyanja sipanali pozama motere.
32. Kodi nchiyani chimene chiyenera kukhala chitachitikira madzi a Chigumula? Fotokozani.
32 Kodi chinachitika nchiyani kumadzi a chigumula pambuyo pa Chigumulacho? Iwo ayenera akukhala atatsikira pansi pa nyanja. Motani? Asayansi amakhulupirira kuti makontinenti ali pamwamba pamalo athyathyathya aakulu. Kuyenda kwa malo kwathyathyathya ameneŵa kungathe kuchititsa masinthidwe m’malo amtunda wa dziko lapansi. Mmalo ena lerolino, muli maphompho apansi pa madzi a makilomitala oposa 10 kuzama kuchoka pamene payambira malo athyathyathya.16 Kuli kothekera kuti—mwinamwake moyambitsidwa ndi Chigumula chenichenicho—malo athyathyathyawo anayenda, pansi panyanja paatsika, ndipo mayenje aakulu anatseguka, kulola madziwo kutsikira pansi pa mtunda.b
Zizindikiro za Chigumula
33, 34. (a) Kodi ndiumboni wotani umene asayansi ali nawo kale umene mwinamwake ungakhale umboni wa Chigumula? (b) Kodi nkoyenera kunena kuti asayansi angakhale akuŵerenga molakwa umboniwo?
33 Ngati tivomereza kuti chigumula chachikulu chiyenera kukhala chitachitika, kodi nchifukwa ninji asayansi sanapeze zizindikiro zake? Mwinamwake iwo atero, koma iwo amatanthauzira umboniwo mwanjira ina. Mwachitsanzo, sayansi yachikale imaphunzitsa kuti nkhope ya dziko lapansi yaumbidwa m’malo ambiri ndi malo achipale amphamvu mkati mwa mpambo wa nyengo ya kupangika kwa chipale. Koma nthaŵi zina umboni wowonekera wa kugwira ntchito kwa chipale ungathe kukhala wochititsidwa ndi kugwira ntchito kwa madzi. Pamenepo, mwinamwake, wina wa umboni wa Chigumula ukupendedwa molakwa monga umboni wa nyengo ya kupangika kwa chipale.
34 Zolakwa zofananazo zapangidwa. Ponena za nthaŵi pamene asayansi analinkupanga nthanthi yawo ya nyengo ya kupangika kwa chipale, timaŵerenga kuti: “Iwo anali kupeza nyengo za kupangika kwa chipale pasiteji iriyonse ya mbiri ya sayansi yophunzira miyala, mogwirizana ndi nthanthi ya kulingana. Komabe, kupendanso mosamalitsa umboniwo m’zaka zaposachedwapa, kwakana zochuluka zanyengo za kupangika kwa chipale zimenezi; zoumbika zimene panthaŵi ina zinasonyezedwa kukhala miyala yachipale zatanthauziridwanso kukhala miyulu younjikidwa ndi kuyenda kwa matope, zigumukire zapansi pa nyanja, kuŵinduka kwa mafunde: zigumukire zamadzi oŵinduka amene amanyamula timiyala, mchenga ndi nsalangabwi kuzichotsa pansi pa nyanja.”18
35, 36. Kodi ndiumboni wotani m’cholembedwa cha mafupa ofukulidwa ndi m’miyala umene ungakhale wogwirizana ndi Chigumula? Fotokozani.
35 Umboni wina wonena za Chigumula ukuwonekera kukhala cholembedwa cha m’mafupa ofukulidwa pansi. Panthaŵi ina, malinga ndi cholembedwa chimenechi, akambuku aakulu a mano akuthwa anali kuŵendera nyama zawo mu Ulaya, akavalo aakulu koposa alionse amene ali ndi moyo patsopano lino anali kuyendayenda mu North America, ndipo zinyama zikuluzikulu zinali kumayendayenda mu Siberia. Ndiyeno, padziko lonse, mitundu ya zinyama zoyamwitsa inangozimiririka. Panthaŵi imodzimodziyo panali kusintha kwadzidzidzi kwa mkhalidwe wakunja. Zikwi makumi ochuluka za zinyama zazikulu zinaphedwa ndi kukutidwa mwamsanga ndi chipale mu Siberia.c Alfred Wallace, munthu wotchuka wa panthaŵi imodzimodzi ndi Charles Darwin, analingalira kuti kuwonongedwa kofalikira koteroko kuyenera kukhala kutachititsidwa ndi chochitika china chosawonekawoneka cha padziko lonse.19 Ochuluka anena kuti chochitika chimenechi chinali Chigumula.
36 Mawu olembedwa ndi mkonzi m’magazine otchedwa Biblical Archaeologist anati: “Nkofunika kukumbukira kuti nthano yonena za chigumula chachikulu iri umodzi wa miyambo yosiiranasiirana yofalikira kopambana m’mkhalidwe wa anthu . . . Komabe kutseri kwa miyambo yakale kopambana yopezedwa m’magwero a maiko Akummaŵa, pangakhalenso kugwa kwa chimvula chenicheni chachikulu kopambana chimene chinachitika nyengo za chigumula zisanakhalepo . . . zaka zikwi zambiri zapitazo.”20 Nyengo za kugwa kwa mvula zinali nthaŵi pamene nkhope ya dziko lapansi inali yachinyontho kwambiri koposa mmene iriri tsopano. Nyanja zamadzi opanda mchere padziko lonse zinali zazikulu kwambiri. Kukulingaliridwa kuti chinyonthocho chinali kuchititsidwa ndi pwatapwata wa mvula wogwirizanitsidwa ndi kutha kwa nyengo ya chipale. Koma ena apereka lingaliro lakuti panthaŵi ina, chinyontho chopambanitsa cha nkhope ya dziko lapansi chinachititsidwa ndi Chigumula.
Anthu Sanaiŵale
37, 38. Kodi ndimotani mmene wasayansi wina akusonyezera kuti, malinga ndi kunena kwa umboni, Chigumula chiyenera kukhala chitachitika, ndipo kodi timadziŵa bwanji kuti chinachitika?
37 Profesala wa sayansi yophunzira zamiyala John McCampbell panthaŵi ina alemba kuti: “Kusiyana kofunika pakati pa chipolowe cha Baibulo [Chigumula] ndi kufanana kwa a zachisinthiko sikuli pazenizeni zopezedwa za ophunzira miyala koma pamatanthauziridwe a zenizeni zimenezo. Kutanthauzira koyanjidwa kudzadalira kwakukulukulu pachiyambi ndi zoyerekezeredwa pasadakhale za wophunzira weniweniyo.”21
38 Chakuti Chigumula chinachitika chikuwonedwa m’chenicheni chakuti mtundu wa anthu suunachiiŵale. Padziko lonse lapansi, mmalo otalikirana monga ngati Alaska ndi ku Zisumbu za Nyanja Yakummwera, kuli nthano zamakedzana zonena za icho. Mitundu ya eni nthaka, ndi ya pambuyo pa Columbus ku America, kudzanso ku Aborigine a ku Australia, onse adakali ndi nthano zonena za Chigumula. Pamene kuli kwakuti zina za zolembedwazo zimasiyana m’kalogosoledwe, chenicheni chachikulu chakuti dziko lapansi linamizidwa ndi madzi ndipo anthu oŵerengeka chabe anapulumutsidwa ali m’chingalaŵa chopangidwa ndi munthu zimadza pafupifupi m’zolembedwa zonse. Malongosoledwe okha onena za kulandiridwa kofala kumeneko ngakuti Chigumula chinali chochitika cha m’mbiri.d
39. Kodi ndiumboni wowonjezereka wotani umene ife tauwona wa chenicheni chakuti Baibulo liri mawu a Mulungu, osati amunthu?
39 Chotero, m’mbali zofunika Baibulo liri logwirizana ndi sayansi yamakono. Kumene pali kuwombana pakati pa ziŵirizo, umboni wa sayansi ngwokaikitsa. Kumene pali kugwirizana, Baibulo kaŵirikaŵiri liri lolondola kwambiri kwakuti ife tiyenera kulikhulupirira kuti linapeza chidziŵitso chake kuchokera kwa munthu wanzeru zoposa zamunthu. Zowonadi, kugwirizana kwa Baibulo ndi sayansi yotsimikizirika kumapereka umboni wina wakuti iro liri mawu a Mulungu, osati a munthu.
-
-
Maulosi Amene AnakwaniritsidwaBaibulo—Kodi Ndilo Mawu a Mulungu Kapena a Munthu?
-
-
Mutu 9
Maulosi Amene Anakwaniritsidwa
Anthu sangathe kuneneratu zamtsogolo motsimikizira kwenikweni. Kaŵirikaŵiri zoyesayesa zawo pakuneneratu zalephera momvetsa chisoni. Chotero bukhu la maulosi amene anakwaniritsidwa liyenera kukopa maganizo athu. Baibulo ndilo bukhu loterolo.
1. (Phatikizamoni mawu oyamba.) Kodi nchiyani chimene chikutsimikiziridwa ndi chenicheni chakuti Baibulo limalemba maulosi amene amakwaniritsidwa?
MAULOSI ambiri a Baibulo akwaniritsidwa mwatsatanetsatane kwambiri kwakuti osuliza amanena kuti iwo analembedwa pambuyo pa kukwaniritsidwa kwawo. Koma kunena koteroko sikowona. Mulungu, pokhala wamphamvu yonse, ali wokhoza kotheratu kulosera. (Yesaya 41:21-26; 42:8, 9; 46:8-10) Maulosi a Baibulo amene anakwaniritsidwa ali umboni wa kuuziridwa ndi Mulungu, osati wa kulemba kwapambuyo pake. Tsopano tidzayang’ana pa ena a maulosi amene anakwaniritsidwa—kupereka umboni wowonjezereka wakuti Baibulo liri mawu a Mulungu, osati a munthu.
Andende m’Babulo
2, 3. Kodi nchiyani chimene chinachititsa Mfumu Hezekiya kusonyeza chuma chonse cha m’nyumba mwake ndi ufumu wake kwa nthumwi zochekera ku Babulo?
2 Hezekiya anali mfumu m’Yerusalemu kwa pafupifupi zaka 30. Mu 740 B.C.E. iye anawona kuwonongedwa kwa Israyeli wakumpoto, woyandikirana nayeyo, mowonongedwa ndi Asuri. Mu 732 B.C.E., iye anawona mphamvu yopulumutsa ya Mulungu, pamene kuyesayesa kwa Asuri kugonjetsa Yerusalemu kunalephera, nzotulukapo za tsoka kwa woukirayo.—Yesaya 37:33-38.
3 Tsopano, Hezekiya akulandira nthumwi zochokera kwa Merodakibaladani, mfumu ya ku Babulo. Kunja chabe, nthumwizo zadza ndi mafuno abwino kwa Hezekiya pa kuchira kwake matenda aakulu. Komabe, mwinamwake, Merodakibaladani akuwona Hezekiya monga wothekera kugwirizana naye motsutsana ndi ulamuliro wa dziko wa Asuri. Hezekiya sakuchita chirichonse kulingaliro loterolo pamene iye akuwonetsa alendo Achibabulowo chuma chonse cha nyumba yake ndi ufumu wake. Mwinamwake iyenso, akufuna ogwirizana nawo motsutsana ndi kubwereranso kothekera kwa Asuri.—Yesaya 39:1, 2.
4. Kodi nchotulukapo cha tsoka chotani cha cholakwa cha Hezekiya chimene Yesaya anachilosera?
4 Yesaya ndiye mneneri wapadera wapanthaŵi imeneyo, ndipo iye mofulumira akuzindikira kuchita mopanda nzeru kwa Hezekiya. Iye akudziŵa kuti chitetezo chotsimikizirika cha Hezekiya ndiye Yehova, osati Ababulo, ndipo akumuuza kuti kachitidwe kake ka kusonyeza Ababulo chuma chake kadzatsogolera kutsoka. “Masiku afika,” akutero Yesaya, “kuti zonse za m’nyumba mwako, ndi zimene atate wako anazikundika kufikira lerolino, zidzatengedwa kumka ku Babulo.” Yehova analengeza kuti: “Sipadzatsala kanthu.”—Yesaya 39:5, 6.
5, 6. (a) Kodi nchiyani chimene Yeremiya ananena kutsimikizira ulosi wa Yesaya? (b) Kodi ndim’njira yotani imene ulosi wa Yesaya ndi Yeremiya unakwaniritsidwira?
5 Kalero m’zaka za zana lachisanu ndi chitatu B.C.E., kungakhale kutawonekera kukhala kosatheka kuti ulosi umenewo ukwaniritsidwe. Komabe, zaka zana limodzi pambuyo pake, mkhalidwewo unasintha. Babulo analoŵa mmalo mwa Asuri monga ulamuliro wa dziko wolamulira, pamene Yuda anakhala woluluzika kopambana, pankhani ya chipembedzo, kwakuti Mulungu anachotsa dalitso lake. Tsopano, mneneri wina, Yeremiya, anauziridwa kubwereza chenjezo la Yesaya. Yeremiya analengeza kuti: “Ndidzatengera [Babulo] padziko lino, okhala ake onse . . . Ndipo dziko lonse lidzakhala labwinja, ndi chizizwitso, ndipo mitundu iyi idzatumikira mfumu ya ku Babulo zaka makumi asanu ndi aŵiri.”—Yeremiya 25:9, 11.
6 Pafupifupi zaka zinayi Yeremiya atapereka ulosi umenewu, Ababulo anapanga Yuda kukhala mbali ya ufumu wawo. Zaka zitatu pambuyo pake, iwo anatengera muukapolo Ayuda ena, limodzi ndi chuma china cha pakachisi pa Yerusalemu, kumka nacho ku Babulo. Zaka zisanu ndi zitatu pambuyo pake, Yuda anapandukira ndipo kachiŵirinso anaukiridwa ndi mfumu ya Babulo, Nebukadnezara. Panthaŵi ino, mzindawo ndi kachisi wake zinawonongedwa. Chuma chake chonse, ndi Ayuda iwo eniwo, anatengedwa ndi kumka nawo kutali ku Babulo, monga momwedi Yesaya ndi Yeremiya anali atateneneratu.—2 Mbiri 36:6, 7, 12, 13, 17-21.
7. Kodi ndimotani mmene zofukula za m’mabwinja zimachitira umboni kukukwaniritsidwa kwa ulosi wa Yesaya ndi Yeremiya ponena za Yerusalemu?
7 The Archaeological Encyclopedia of the Holy Land imanena kuti pamene chiukiriro cha Ababulo chinatha, “kuwonongedwa kwa mzindawo [Yerusalemu] kunali kotheratu.”1 Wofukula za m’mabwinja W. F. Albright akuti: “Kufufuza kwa zofukulidwa m’mabwinja ndi zapamwamba mu Yuda kwatsimikizira kuti sikokha kuti matauni a Yuda anawonongedweratu ndi Akaladayo m’ziukiriro zawo ziŵirizo, koma sanakhalidwenso kwa mibadwomibadwo—kaŵirikaŵiri osakhalidwanso m’mbiri.”2 Motero, zofukulidwa m’mabwinja zikutsimikizira kukwaniritsidwa kovutitsa maganizo kwa ulosi umenewu.
Choikidwiratu cha Turo
8, 9. Kodi ndiulosi wotani umene Ezekieli ananena motsutsana ndi Turo?
8 Ezekieli anali wolemba wina wamakedzana amene analemba maulosi ouziridwa mwaumulungu. Iye analosera kuyambira kumapeto kwa zaka za zana lachisanu ndi chiŵiri B.C.E. mpaka kukafika m’zaka za zana lachisanu ndi chimodzi—ndiko kuti, mkati mwa zaka zotsogolera kuchiwonongeko cha Yerusalemu ndiyeno mkati mwa zaka makumi angapo oyambirira za undende wa Ayuda mu Babulo. Ngakhale otsutsa amakono amavomereza kuti bukhulo linalembedwa pafupifupi panthaŵi imeneyi.
9 Ezekieli analemba ulosi wogwira mtima wonena za chiwonongeko cha mnansi wapafupi wakumpoto wa Israyeli, Turo, amene anachoka pamkhalidwe waumbwenzi ndi anthu a Mulungu kumka kuudani. (1 Mafumu 5:1-9; Salmo 83:2-8) Iye analemba kuti: “Atero [mfumu] Ambuye Yehova, ndikutsutsa iwe, Turo, ndidzakukweretsera amitundu, monga nyanja iutsa mafunde ake. Ndipo adzagamula malinga a Turo, ndi kugwetsa nsanja zake; inde ndidzausesa fumbi lake, ndi kuuyesa pathanthwe poyera. . . . Nadzaponya miyala yako, ndi mitengo yako, ndi fumbi lako, mmadzi.”—Ezekieli 26:3, 4, 12.
10-12. Kodi ndiliti pamene ulosi wa Ezekieli potsirizira pake unakwaniritsidwa, ndipo motani?
10 Kodi zimenezi zinachitikadi? Eya, zaka zoŵerengeka Ezekieli atapereka ulosiwo, mfumu ya Babulo Nebukadnezara, anazinga Turo. (Ezekieli 29:17, 18) Komabe, sikunali kuzinga kosavuta. Mbali ina ya Turo inali chamkati pang’ono mwa dzikolo (mbali yotchedwa Turo Wakale). Koma mbali ina ya mzindawo inali pachisumbu chokhala pafupifupi pamtunda wa mamitala 800 mphepete mwa nyanja. Nebukadnezara anazinga chisumbucho kwa zaka 13 chisanagonjere potsirizira pake kwa iye.
11 Komabe, munali mu 332 B.C.E. pamene ulosi wa Ezekieli unakwaniritsidwa m’chirichonse cha tsatanetsatane wake. Panthaŵi imeneyo, Alesandro Wamkulu, wogonjetsa wochokera ku Makedonia, anali kuukira Asiya. Turo, atakhazikika mtima pansi pamalo ake achisumbuwo, analimbana naye. Alesandro sanafune kusiya wothekera kukhala mdani kumbuyo kwake, koma sanafune kuwononga zaka zambiri atazinga Turo, monga momwe anachitira Nebukadnezara.
12 Kodi iye anathetsa bwanji vuto lankhondo limeneli? Iye anamanga ulalo wapamtunda, kapena chiunda, kudutsa kumka kuchisumbucho, kotero kuti asilikali ake ankhondo akadatha kuguba kudutsa ndi kukaukira mzinda wa pachisumbuwo. Komabe, wonani chimene anagwiritsira ntchito kumangira mtumbirawo. The Encyclopedia Americana ikusimba kuti: “Ndi zogumuka za zigawo za mzinda wa m’dzikowo, umene iye anali ataugwetsa, iye anamanga mtumbira wakulu mu 332 kukagwirizanitsa chisumbucho ndi dzikolo.” Pambuyo pa kuzingidwa kwa nthaŵi yaifupi chabe, mzinda wachisumbuwo unawonongedwa. Komabe, ulosi wa Ezekieli unakwaniritsidwa m’mbali zake zonse. Ngakhale ‘miyala ndi mitengo ndi dothi’ za Turo Wakale ‘zinaikidwa mkati mwa madzi.’
13. Kodi ndimotani mmene wapaulendo wa m’zaka za zana la 19 anafotokozera malo a Turo wamakedzana?
13 Wapaulendo wa m’zaka za zana la 19 ananenapo mawu onena za zimene zinatsala za mzinda wamakedzana wa Turo m’nthaŵi yake, akumati: “Mwa Turo woyambirira amene anali wodziŵika kwa Solomo ndi aneneri a Isarayeli, palibe zotsalira zowoneka kusiyapo m’manda ake ozokotedwa pamiyala mphepete mwa phiri, ndi makoma a maziko . . . Ngakhale chisumbucho, chimene Alesandro Wamkulu, m’kuzinga kwake mzindawo, anachisandutsa ndomo mwa kudzaza madzi pakati pake ndi dziko lakumtundalo, ulibe zotsalira zodziŵika bwino za nyengo yachikale kwambiri koposa ya m’nthaŵi Zankhondo Zamtanda. Tauni yamakono, imene yonse yathunthu iri yatsopano, iri kutheka lakumpoto la chimene kalero chinali chisumbucho, pamene pamwamba ponse potsalirapo pali pokutidwa ndi mabwinja osazindikirika.”3
Kutembenukiridwa kwa Babulo
14, 15. Kodi ndimaulosi otani amene Yesaya ndi Yeremiya analemba motsutsa Babulo?
14 Kalero m’zaka za zana lachisanu ndi chitatu B.C.E., Yesaya, mneneri amene anachenjeza Ayuda za kugonjetsedwa kwawo kumene kunalinkudza kochitidwa ndi Ababulo, ananeneratunso kanthu kena kodabwitsa: kufafanizidwa kotheratu kwa Babulo iye mwiniyo. Iye ananeneratu zimenezi m’kafotokozedwe katsatanetsatane kuti: “Tawonani, ndidzawautsira Amedi . . . Ndipo Babulo, ulemerero wa maufumu, mudzi wokongolawo Akasidi anaunyadira, adzakhala monga momwe Mulungu anapasula Sodomu ndi Gomora. Anthu sadzakhalamo konse, sadzakhalamo mbadwo ndi mbadwo.”—Yesaya 13:17-20.
15 Mneneri Yeremiya nayenso ananeneratu za kugwa kwa Babulo, kumene kukachitika zaka zambiri pambuyo pake. Ndipo iye anaphatikizamo tsatanetsatane wokondweretsa: “Chirala chiri pamadzi ake ndipo adzaphwa; . . . Olimba a ku Babulo akana kumenyana, akhala m’malinga awo; mphamvu yawo yalephera.”—Yeremiya 50:38; 51:30.
16. Kodi Babulo anagonjetsedwa liti, ndipo ndi yani?
16 Mu 539 B.C.E., nthaŵi ya ulamuliro wa Babulo monga ulamuliro womalamulira wa padziko lonse inatha pamene wolamulira wakhama Wachiperisi Koresi, motsagana ndi gulu lankhondo la Amedi, anaguba motsutsana ndi mzindawo. Komabe, chimene Koresi anapeza, chinali champhamvu. Babulo anakwetezedwa ndi malinga aakulu kwambiri ndipo anawonekera kukhala wosaloŵeka. Mtsinje waukulu Firate, nawonso, unayenda kudutsa mzindawo ndipo unathandizira kwambiri chitetezo chake.
17, 18. (a) Kodi ndim’njira yotani kuti panakhala “kuwonongedwa kwa madzi [a Babulo]”? (b) Kodi nchifukwa ninji ‘amuna amphamvu a Babulo analeka kumenya nkhondo’?
17 Wolemba mbiri Wachigriki Herodotus akufotokoza mmene Koresi anathetsera vutolo: “Iye anakhazika mbali ina ya gulu lake lankhondo pamalo amene mtsinjewo umaloŵera mumzindawo, ndiyeno gulu lina kumbuyo kumene umatulukira, atalamula kuguba kukaloŵa m’tauniyo moyenda pansi pouma pa mtsinjewo, mwansanga pamene madziwo anakhala ochepa mokwanira . . . Iye anapambutsa Firate mwa ngalande yonkera mphepete [nyanja yopanga yokumbidwa ndi wolamulira wapapitapo wa Babulo], chimene panthaŵiyo chinali thaŵale, palimene mtsinjewo unazama kufika pamlingo wakuti mpangidwe wa pansi pamtsinjewo sipanakhale pakuya. Panopo Aperisi amene anasiyidwa kaamba ka chifuno chimenecho pa Babulo mphepete mwa mtsinjewo, analoŵa mumtsinjewo, umene tsopano unaphwa kotero kuti ukafike pakatikati pa ntchafu za munthu, ndipo motero anakafika m’tauniyo.”4
18 Mwanjira imeneyi mzindawo unagwa, monga momwe Yeremiya ndi Yesaya anali atachenjezera. Koma wonani kukwaniritsidwa kwatsatanetsatane kwa ulosi. Panali ‘chiwonongeko chotheratu pamadzi ake, ndipo anaumitsidwa.’ Kunali kuphwetsedwa kwa madzi a Firate kumene kunatheketsa Koresi kukafika kumzindawo. Kodi ‘amuna amphamvu a Babulo analeka kumenya nkhondo,’ monga momwe Yeremiya anali atachenjezera? Baibulo—kudzanso olemba mbiri Achigriki Herodotus ndi Xenophon—akusimba kuti Ababulo anali kwenikweni kuchita phwando pamene chiukiro cha Aperesi chinachitika.5 Mbiri ya Nabonidasi, cholembedwa chozokota chaukumu, chimanena kuti magulu ankhondo a Koresi analoŵa m’Babulo “popanda nkhondo,” mwachiwonekere kutanthauza kuti popanda nkhondo yaikulu ya kulimbana.6 Mwachiwonekere, ngwazi Zachibabulo sizinachite zochuluka kumtetezera.
19. Kodi ulosi wakuti Babulo “sakakhalidwanso ndi anthu” unakwaniritsidwa? Fotokozani.
19 Bwanji nanga ponena za kuneneratu kuti Babulo ‘sakakhalidwanso ndi anthu’ kachiŵiri? Kumeneko sikunakwaniritsidwe panthaŵi yomweyo mu 539 B.C.E. Koma mosaphonyetsa ulosiwo unakwaniritsidwa. Pambuyo pa kugwa kwake, Babulo anakhala malo apakati a zipanduko zingapo, kufikira mu 478 B.C.E. pamene iye anawonongedwa ndi Aritasasta. Chakumapeto kwa zaka zana lachinayi, Alesandro Wamkulu analinganiza kumbwezeretsanso, koma iye anafa ntchitoyo isanapite patali kwambiri. Kuyambira panthaŵi imeneyo kumkabe mtsogolo, mzindawo unali kumangonyonyosoka. Munali mudakali ŵanthu okhalamo m’zaka za zana Loyamba la Nyengo Yathu ino, koma lerolino chokha chimene chatsala ponena za mzinda wamakedzana wa Babulo ndiwo mulu wamabwinja mu Iraq. Ngakhale ngati mabwinja ake angabwezeretsedwe pang’ono, Babulo akangokhala malo okayang’anako odzacheza, osati mzinda wokhalamo, wokongola. Malo ake opasukawo amachitira umboni kukukwaniritsidwa kotsirizira kwa maulosi ouziridwa otsutsana naye.
Kuguba kwa Maulamuliro a Dziko
20, 21. Kodi ndiulosi wotani umene Danieli anawona wa kuguba kwa maulamuliro a dziko, ndipo kodi ndimotani mmene umenewu unakwaniritsidwira?
20 M’zaka za zana lachisanu ndi chimodzi B.C.E., mkati mwa kukhala undende kwa Ayuda m’Babulo, mneneri wina, Danieli, anauziridwa kulemba masomphenya ena apadera omaneneratu dongosolo lamtsogolo la zochitika za dziko. Mu amodzi, Danieli akufotokoza nyama zingapo zophiphiritsira zimene zimachotsana pamalo antchito china ndi chinzake pankhope yadziko. Mngelo akufotokoza kuti zinyama zimenezi zinaphiphiritsira kuguba kwa maulamuliro a dziko kuyambira panthaŵi imeneyi kumkabe mtsogolo. Pokamba za zirombo ziŵiri zotsirizira, iye akuti: “Nkhosa yamphongo waiwona ya nyanga ziŵiri ndizo mafumu a Mediya ndi Perisiya. Ndi tonde wamanyenje ndiye mfumu ya Helene, ndi nyanga yaikulu iri pakati pa maso ake ndiyo mfumu yoyamba. Ndi kuti zinaphuka zinayi mmalo mwake mwa iyo itathyoka, adzauka maufumu anayi ochokera mumtunduwu wa anthu, koma osakhala nayo mphamvu ya uja.”—Danieli 8:20-22.
21 Kuwoneratu kolosera kumeneku kunakwaniritsidwa ndendende. Ufumu wa Babulo unagubuduzidwa ndi Amedi ndi Aperisi, umene, zaka 200 pambuyo pake, unagonjera kuulamuliro wa dziko wa Grisi. Ufumu wa Grisi unatsogozedwa ndi Alesandro Wamkulu, “nyanga yaikulu.” Komabe, atafa Alesandro, akazembe ake anamenyanira ulamuliro, ndipo potsirizira pake ufumu wokhala ndi malo aakuluwo unagaŵika kukhala maufumu aang’onoang’ono anayi, “maufumu anayi.”
22. Muulosi wofanana nawo wa kuguba kwa maulamuliro a dziko, kodi ndiulamuliro wadziko wowonjezereka wotani umene unaloseredwa?
22 Mu Danieli mutu 7, masomphenya ochita ngati ofananirapo anayang’ananso mowonjezereka mtsogolo. Ulamuliro wa dziko lonse wa Babulo unaphiphiritsiridwa ndi mkango, Aperisi ndi chimbalangondo, ndipo Agriki ndi nyalugwe wokhala ndi mapiko anayi pamsana pake ndi mitu inayi. Kenako, Danieli akuwona chirombo china, “chowopsa ndi chochititsa mantha, ndi champhamvu . . . , ndipo chinali ndi nyanga khumi.” (Danieli 7:2-7) Chirombo chachinayi chimenechi chinaphiphiritsira Ufumu wamphamvu Wachiroma, umene unayamba kubuka pafupifupi zaka mazana atatu pambuyo pa kulembedwa kwa ulosi wa Danieli umenewu.
23. Kodi ndim’njira yotani mmene chirombo chachinayi cha ulosi wa Danieli chinaliri “chosiyana ndi maufumu ena onse”?
23 Mngeloyo analosera ponena za Roma kuti: “Chirombo chachinayi ndicho ufumu wachinayi padziko lapansi, umene udzasiyana nawo maufumu onse, nudzalusira dziko lonse lapansi, nudzalipondereza ndi kuliphwanya.” (Danieli 7:23) H. G. Wells m’bukhu lake, A Pocket History of the World, akunena kuti: “Ulamuliro wa Roma watsopano umenewo umene unabuka kulamulira dziko lakumadzulo m’zaka za zana lachiŵiri ndi loyamba B.C. unali m’mbali zingapo chinthu chosiyana ndi alionse a maufumu aakulu amene analamulirapo m’dziko lonse lathunthu lotsungula.”7 Uwo unayamba monga lipabuliki ndipo unapitirizabe monga ulamuliro wokhala ndi mfumu. Mosafanana ndi maufumu apapitapo, suunali ndi wogonjetsa mmodzi aliyense koma unakula mosalekeza m’kupita kwa zaka mazana ochuluka. Uwo unakhalapo kwanthaŵi yaitali kwambiri ndipo unalamulira chigawo chachikulu kopambana koposa ufumu uliwonse wapapitapo.
24, 25. (a) Kodi ndimotani mmene nyanga khumi za chirombo zinapangira kuwonekera kwake? (b) Kodi ndikulimbana kotani pakati pa nyanga za chirombocho kumene Danieli anawoneratu?
24 Komabe, bwanji ponena za nyanga khumi za chirombo chachikulucho? Mngeloyo anati: “Kunena za nyanga khumi, muufumu uwu adzauka mafumu khumi, ndi pambuyo pawo idzauka ina; iyo idzasiyana ndi oyamba aja, nidzachepetsa mafumu atatu.” (Danieli 7:24) Kodi zimenezi zinadzayenda motani?
25 Eya, pamene Ulamuliro Wachiroma unayamba kunyonyosoka m’zaka za zana lachisanu C.E., suunaloŵedwe mmalo panthaŵi yomweyo ndi ulamuliro wina wadziko. Mmalo mwake, uwo unagaŵanika kukhala maufumu angapo, “maufumu khumi.” Potsirizira pake, Ufumu wa Briteni unagonjetsa maufumu atatu opikisanawo wa Spanya, Falansa, ndi Netherlands kuti ukhale ulamuliro wadziko waukulu. Motero ‘nyanga’ yodza chatsopanoyo ikuchititsa manyazi “mafumu atatu.”
Maulosi a Danieli—Pambuyo pa Chenicheni?
26. Kodi osuliza amanena kuti Danieli analembedwa liti, ndipo chifukwa ninji?
26 Baibulo limasonyeza kuti bukhu la Danieli linalembedwa mkati mwa zaka za zana lachisanu ndi chimodzi B.C.E. Komabe, kukwaniritsidwa kwa maulosi ake kuli kwandendende kwambiri kotero kuti osuliza amanena kuti liyenera kukhala litalembedwa pafupifupi mu 165 B.C.E. pamene angapo a maulosiwo anali atakwaniritsidwa kale.8 Mosasamala kanthu za chenicheni chakuti chifukwa chokha chenicheni chonenera zimenezi ndicho chakuti maulosi a Danieli anakwaniritsidwa, deti la pambuyo pake la bukhu la Danieli limeneli likusonyezedwa kukhala chenicheni chotsimikizirika m’mabukhu ambiri a maumboni.
27, 28. Kodi ndiati amene ali ena a maumboni otsimikizira kuti Danieli sanalembedwe mu 165 B.C.E.?
27 Komabe, motsutsana ndi nthanthi imeneyo, tiyenera kupenda zenizeni zotsatirapozi. Choyamba, bukhulo linagwidwa mawu m’mabukhu Achiyuda otulutsidwa mkati mwa zaka za zana lachiŵiri B.C.E., monga ngati bukhu loyamba la Amakabeo. Ndiponso, linaphatikizidwa m’bukhu la Septuagint Yachigriki, limene kutembenuzidwa kwake kunayamba m’zaka za zana lachitatu B.C.E.9 Chachitatu, zidutswa za makope a Danieli zinali pakati pa zopezedwa kaŵirikaŵiri m’Mipukutu ya Nyanja Yakufa—ndipo zidutswa zimenezi zikukhulupiriridwa kukhala ziri za madeti apafupifupi 100 B.C.E.10 Mowonekera bwino, pamene Danieli atanenedwa kukhala atalembedwa, linali litadziŵidwa kale mofala ndi kulemekezedwa: umboni wamphamvu wakuti iro linatulutsidwa kalekale koposa pamene otsutsawo akunena kuti iro linatulutsidwa.
28 Ndiponso, Danieli ali ndi mfundo zatsatanetsatane za m’mbiri zimene zikanakhala zosadziŵidwa kwa wolemba wa m’zaka za zana lachiŵiri. Chapadera ndicho chochitika cha Belisazara, wolamulira wa Babulo amene anaphedwa pamene Babulo anagwa mu 539 B.C.E. Magwero aakulu osakhala a Baibulo a chidziŵitso cha kugwa kwa Babulo ndiwo Herodotus (zaka za zana lachisanu), Xenophon (zaka za zana lachisanu ndi zana lachinayi), ndi Berossus (zaka za zana lachitatu). Palibe aliyense wa ameneŵa anadziŵa za Belisazara.11 Nkokaikitsa chotani nanga mmene kuliri kuti wolemba wa m’zaka za zana lachiŵiri akanakhala ndi chidziŵitso chimene chinali chosapezeka kwa olemba oyambirira ameneŵa! Chidziŵitso cha mu Danieli mutu 5 chonena za Belisazara ndicho chigomeko champhamvu chakuti Danieli analemba bukhu lakelo olemba enawo asanalembe awo.a
29. Kodi nchifukwa ninji kuli kosatheka kuti bukhu la Danieli linalembedwa pambuyo pa kukwaniritsidwa kwa maulosi amene ali mmenemo?
29 Potsirizira pake, pali maulosi angapo mu Danieli amene anakwaniritsidwa kale kwambiri 165 B.C.E. isanakwane. Umodzi wa ameneŵa unali ulosi wonena za Ufumu Wachiroma, wotchulidwa poyambirirapo. Wina ndiwo ulosi wapadera woneneratu kudza kwa Yesu, Mesiya.
Kudza kwa Wodzozedwayo
30, 31. (a) Kodi ndiulosi wotani wa Danieli umene unaneneratu kuwonekera kwa Mesiya? (b) Kodi ndimotani mmene tingaŵerengerere, kuchokera paulosi wa Danieli, chaka chimene Mesiya anali woyenera kuwonekera?
30 Ulosi umenewu walembedwa mu Danieli, mutu 9, ndipo umati: “Masabata makumi asanu ndi aŵiri [a zaka, kapena zaka mazana anayi ndi makumi asanu ndi anayi] alamulidwa anthu a mtundu wako ndi pamzinda wako woyera.”b (Danieli 9:24, The Amplified Bible) Kodi nchiyani chimene chikayenera kuchitika mkati mwa zaka 490 zimenezi? Timaŵerenga kuti: “Kuyambira kutuluka lamulolo la kukonzanso, ndi kumanga Yerusalemu [kudza kwa] kufikira wodzozedwayo, ndiye kalonga, kudzakhala masabata asanu ndi aŵiri [a zaka]; ndi masabata makumi asanu ndi limodzi mphambu aŵiri [a zaka].” (Danieli 9:25) Chotero uwu uli ulosi wonena za nthaŵi ya kudza kwa “wodzozedwayo,” Mesiya. Kodi unakwaniritsidwa motani?
31 Lamulo la kubwezeretsa ndi kumanga Yerusalemu ‘linatuluka’ mu “chaka cha makumi aŵiri cha Artasasta mfumu” wa Peresiya, ndiko kuti, mu 455 B.C.E. (Nehemiya 2:1-9) Pakutha kwa zaka 49 (masabata 7 a zaka), wochuluka wa ulemerero wa Yerusalemu unali utabwezeretsedwa. Ndiyeno pamenepo kuŵerenga zaka zokwanira 483 (masabata 7 kuphatikiza ndi 62 a zaka) kuyambira mu 455 B.C.E., tikufika pa 29 C.E. Kunena zowona, chimenechi, chinali “chaka cha khumi ndi chisanu cha ulamuliro wa Tiberiyo Kaisara,” chaka chimene Yesu anabatizidwa ndi Yohane Mbatizi. (Luka 3:1) Panthaŵi imeneyo, Yesu anadziŵika poyera kukhala mwana wa Mulungu ndipo anayamba utumiki wake wa kulalikira mbiri yabwino kumtundu Wachiyuda. (Mateyu 3:13-17; 4:23) Iye anakhala, “wodzozedwayo,” kapena Mesiya.
32. Malinga ndi kunena kwa ulosi wa Danieli, kodi utumiki wapadziko lapansi wa Yesu ukakhala wautali motani, ndipo kodi nchiyani chimene chikachitika pamapeto pake?
32 Ulosiwo ukuwonjezera kuti: “Ndipo pakutha kwa masabata makumi asanu ndi limodzi mphambu aŵiri [a zaka] wodzozedwayo adzadulidwa.” Uwo ukunenanso kuti: “Ndipo adzaloŵa m’pangano lamphamvu ndi lokhazikika ndi ambiri kwa sabata limodzi [zaka zisanu ndi ziŵiri]; ndipo pakatikati pa mlunguwo iye adzachititsa nsembe ndi zopereka kulekeka.” (Danieli 9:26, 27, AB) Mogwirizana ndi zimenezi, Yesu anamka mwapadera kwa “ambiri,” Ayuda akuthupi. Pachochitika china, iye analalikiranso kwa Asamariya, amene anakhulupirira ena a Malemba koma amene anapanga kagulu kawo kachipembedzo kosiyana ndi Chiyuda chodziŵika. Ndiyeno, “pakatikati pa mlunguwo,” pambuyo pa zaka zitatu ndi theka za kulalikira, iye anapereka moyo wake monga nsembe ndipo motero ‘anadulidwa.’ Kumeneku kunasonyeza mapeto a Chilamulo cha Mose limodzi ndi nsembe zake ndi zopereka za mphatso. (Agalatiya 3:13, 24, 25) Chotero, mwa imfa yake, Yesu anachititsa “nsembe ndi zopereka kulekeka.”
33. Kodi Yehova akachita ndi Ayuda okha akuthupi kwautali wotani, ndipo kodi ndichochitika chotani chimene chinasonyeza mapeto a nyengo imeneyi?
33 Komabe, kwa zaka zina zitatu ndi theka mpingo Wachikristu wobadwa chatsopanowo unachitira umboni kwa Ayuda okha ndipo, pambuyo pake, kwa Asamariya achibale awowo. Komabe, mu 36 C.E., pamapeto a masabata 70 a zakawo, mtumwi Petro anatsogozedwa kulalikira kwa Wamitundu, Korneliyo. (Machitidwe 10:1-48) Tsopano, ‘pangano ndi ambiri’ silinalinso lolekezera kwa Ayuda. Chipulumutso chinalalikidwanso kwa Amitundu osadulidwa.
34. Mogwirizana ndi ulosi wa Danieli, kodi nchiyani chimene chinachitikira Israyeli wakuthupi chifukwa chakuti iwo anakana Mesiya?
34 Chifukwa chakuti mtundu Wachiyuda unakana Yesu ndi kulinganiza chiwembu chakuti iye aphedwe, Yehova sanawatetezere pamene Aroma anadzawononga Yerusalemu mu 70 C.E. Motero, mawu owonjezereka a Danieli anakwaniritsidwa: “Ndipo anthu a kalonga winayo amene adzadza adzawononga mzindawo ndi malo ake opatulika. Mapeto ake adzadza ndi liyambwe, ndipo ngakhale mpaka kumapeto padzakhala nkhondo.” (Danieli 9:26b, AB) “Kalonga” wachiŵiri ameneyu anali Tito, kazembe wankhondo Wachiroma amene anawonga Yerusalemu mu 70 C.E.
Ulosi Umene Unauziridwa
35. Kodi ndimaulosi ena owonjezereka otani onena za Yesu amene anakwaniritsidwa?
35 Mwanjira imeneyi, ulosi wa Danieli wa masabata 70 unakwaniritsidwa ndendende m’mkhalidwe wapadera. Ndithudi, ochuluka a maulosiwo olembedwa m’Malemba Achihebri anakwaniritsidwa mkati mwa zaka zana loyamba, ndipo angapo a ameneŵa anali onena za Yesu. Malo obadwira Yesu, changu chake kaamba ka nyumba ya Mulungu, ntchito yake yolalikira, kuperekedwa kwake ndi ndalama zasiliva 30, mkhalidwe wa imfa yake, chenicheni chakuti maere anachitidwa kaamba ka zovala zake—mfundo zatsatanetsatane zonsezi zinaloseredwa m’Malemba Achihebri. Kukwaniritsidwa kwawo kunatsimikizira popanda chikaikiro kuti Yesu anali Mesiya, ndipo kunasonyezanso kuti maulosiwo anali ouziridwa.—Mika 5:2; Luka 2:1-7; Zekariya 11:12; 12:10; Mateyu 26:15; 27:35; Salmo 22:18; 34:20; Yohane 19:33-37.
36, 37. Kodi tikuphunziranji kuchokera ku chenicheni chakuti maulosi a Baibulo akwaniritsidwa, ndipo kodi ndichidaliro chotani chimene chidziŵitso chimenechi chimatipatsa?
36 Kunena zowona, maulosi onse a Baibulo amene anayera kukwaniritsidwa akwaniritsidwa. Zinthu zachitika ndendende monga momwe Baibulo linanenera kuti zikachitikira. Zimenezi ziri umboni wamphamvu wakuti Baibulo liri Mawu a Mulungu. Payenera kukhala panali nzeru yoposa yaumunthu kutseri kwa mawu olosera amenewo kuti iwo akhale olondola kwambiri motero.
37 Koma muli maulosi ena m’Baibulo amene sanakwaniritsidwe m’masiku amenewo. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti iwo anayenera kukwaniritsidwa m’nthaŵi yathu, ndipo ngakhale mtsogolo mwathu. Kudalirika kwa maulosi amakedzana amenewo kumatipangitsa ife kukhala ndi chidaliro chakuti maulosi ena ameneŵa adzakwaniritsidwa mosalephera. Monga momwe tidzawonera m’mutu wotsatirapo, izi ziridi choncho.
[Mawu a M’munsi]
a Wonani Mutu 4, “Kodi ‘Chipangano Chakale’ Nchokhulupirika Motani?” ndime 16 ndi 17.
b M’matembenuzidwe ano, mawu m’bokosiwo awonjezeredwa ndi wotembenuza kumveketsa tanthauzo.
[Mawu otsindika patsamba 133]
Maulosi onse amene anayenera kukwaniritsidwa akwaniritsidwa. Zinthu zinachitika ndendende monga momwe Baibulo linanenera kuti zikatero
[Chithunzi patsamba 118]
Ofukula za m’mabwinja atumba kuti kuwonongedwa kwa Yerusalemu kochitidwa ndi Nebukadnezara kunali kotheratu
[Chithunzi patsamba 121]
Chithunzithunzi cha Turo wamakono. Palibiretu zotsalira zowonekera za Turo amene aneneri a Israyeli anamdziŵa
[Chithunzi patsamba 123]
Odzacheza amene amakafika pamalowo a Babulo wamakedzana ali mboni za kukwaniritsidwa kwa maulosi otsutsa mzindawo
[Zithunzi patsamba 126]
Maulosi a Danieli a kuguba kwa maulamuliro a dziko anakwaniritsidwa mwandendende kwambiri kotero kuti osuliza amakono amaganiza kuti iwo analembedwa pambuyo pa kukwaniritsidwa kwawo
BABULO
PERISIYA
GRISI
ROMA
BRITENI
[Chithunzi patsamba 130]
Danieli analosera nthaŵi yeniyeni pamene Mesiya akawonekera m’Israyeli
-
-
Ulosi wa Baibulo Umene Mwawona UkukwaniritsidwaBaibulo—Kodi Ndilo Mawu a Mulungu Kapena a Munthu?
-
-
Mutu 10
Ulosi wa Baibulo Umene Mwawona Ukukwaniritsidwa
Kodi munayamba mwadabwa chifukwa chake zinthu ziri zosiyana kwambiri lerolino poyerekezera ndi mmene zinaliri zaka zana limodzi zapitazo? Zinthu zina, ziri bwinopo kwambiri. M’maiko ambiri, matenda amene anali kupha kale tsopano akuchiritsidwa mosavuta, ndipo anthu wamba akusangalala ndi muyezo wokhalira moyo umene sunalingaliridwe ndi makolo awo. Kumbali ina, zaka za zana lathu lino zawona nkhondo zoipa koposa ndi nkhanza zina zoipa kopambana m’mbiri yonse. Kulemerera kwa anthu—ngakhale kupitirizabe kukhalapo kwawo—kukuwopsezedwa ndi kuchulukitsitsa kwa chiŵerengero cha anthu, vuto la kuipitsa, ndi kuunjikidwa kwa m’mitundu yonse kwa miyulu ya zida zankhondo za nyukliya, zovunditsa ziŵalo, ndi zamakhemikolo. Kodi nchifukwa ninji zaka za zana la 20 ziri zosiyana kwambiri ndi zaka za mazana apapitapo?
1. (Phatikizamoni mawu oyamba.) (a) Kodi zaka za zana la 20 zasiyana bwanji ndi mazana apapitapo? (b) Kodi chidzatithandiza nchiyani kumvetsetsa chifukwa chake nthaŵi zathuzi ziri zosiyana kwambiri?
YANKHO la funso limeneli liyenera kuphatikizapo ulosi wapadera wa Baibulo umene inu mwawuwona ukukwaniritsidwa. Ndiwo ulosi umene Yesu iye mwiniyo anapereka ndi kuti, kuphatikiza pa kupereka umboni wa kuuziridwa kwa Baibulo, umasonyeza kuti ife tikukhala ndi moyo pafupi kwambiri ndi masinthidwe aakulu m’zochitika za padziko. Kodi ulosi umenewu ndiuti? Ndipo kodi tidziŵa bwanji kuti ukukwaniritsidwa?
Ulosi Waukulu wa Yesu
2, 3. Kodi ndifunso lotani limene ophunzira a Yesu adamfunsa, ndipo kodi yankho lake tikulipeza kuti?
2 Baibulo limatiuza kuti mwamsanga imfa ya Yesu isanachitike, ophunzira ake anali kukambitsirana za nyumba zazikulu za pakachisi m’Yerusalemu; iwo anachita chidwi ndi ukulu wake ndipo mwachiwonekere kulimba kwake. Koma Yesu anati kwa iwo: “Simuwona izi zonse kodi? indetu ndinena kwa inu, sipadzakhala pano mwala umodzi paunzake, umene suudzagwetsedwa.”—Mateyu 24:1, 2.
3 Ophunzira a Yesu ayenera kukhala atadabwa ndi mawu ake. Pambuyo pake iwo anadza kwa iye kaamba ka chidziŵitso chowonjezereka, akumati: “Tiuzeni, Kodi zinthu zimenezi zidzakhala liti, ndipo kodi nchiyani chimene chidzakhala chizindikiro cha kukhala pafupi kwanu ndi cha mapeto a dongosolo lino la zinthu?” (Mateyu 24:3, NW) Yankho la Yesu likupezeka m’mbali yotsalira ya Mateyu mutu 24 ndi 25. Mawu ake alembedwanso, m’Marko mutu 13 ndi Luka mutu 21. Umenewu mwachiwonekere unali ulosi wofunika kopambana umene Yesu anapereka pamene anali padziko lapansi.
4. Kodi ophunzira a Yesu anali kufunsa ponena za zinthu zosiyana ziti?
4 Kunena zowona, atumwi a Yesu anali kufunsa za zinthu ziŵiri zosiyana. Choyamba, iwo anadzutsa funso lakuti: “Zija zidzawoneka liti?” ndiko kuti, Kodi ndiliti pamene Yerusalemu ndi kachisi wake adzawonongedwa? Chachiŵiri, iwo anafuna kudziŵa chizindikiro chimene chikasonyeza kuti kukhalapo kwa Yesu monga Mfumu ya Ufumu wakumwamba wa Mulungu kunali kutayamba ndi kuti mapeto a dongosolo iri la zinthu anali pafupi.
5. (a) Kodi ndikukwaniritsidwa koyamba kotani kumene kunalipo kwa ulosi wa Yesu, koma kodi ndiliti pamene mawu ake akakhala ndi kukwaniritsidwa kwake kotheratu? (b) Kodi ndimotani mmene Yesu anayambira yankho lake kufunso la ophunzirawo?
5 Poyankha, Yesu analingalira mfundo ziŵiri zonsezo. Ochuluka a mawu ake anakwaniritsidwadi kalero m’zaka za zana loyamba, mkati mwa zaka zimene zinatsogolera ku chiwonongeko chowopsa cha Yerusalemu mu 70 C.E. (Mateyu 24:4-22) Koma kunena zowona ulosi wake unayenera kukhala ndi kufunika kokulirapo kwambiri pambuyo pake, m’masiku athu ano. Ndiyeno, kodi nchiyani chimene Yesu ananena? Iye anayamba mwa kunena mawu olembedwera m’vesi 7 ndi 8 kuti: “Mtundu umodzi wa anthu udzaukirana ndi mtundu wina, ndi ufumu ndi ufumu wina; ndipo kudzakhala njala ndi zivomezi m’malo akutiakuti. Koma ndizo zonsezi zowawa zoyamba.”
6. Kodi mawu a Yesu m’Mateyu 24:7, 8 amatikumbutsa ife za ulosi uti wofanana nawo?
6 Mwachiwonekere, kukhalapo kwa Yesu monga Mfumu yakumwamba kukasonyezedwa ndi chipwirikiti chachikulu padziko lapansi. Zimenezi zikutsimikiziridwa ndi ulosi wofanana nawo umene uli m’bukhu la Chivumbulutso: masomphenya a okwera paakavalo anayi a Chivumbulutso. (Chivumbulutso 6:1-8) Woyambirira wa wokwera pakavalo ameneyu amaphiphiritsira Yesu iye mwini monga Mfumu yogonjetsa. Okwera enawo limodzi ndi akavalo awo amaphiphiritsira zochitika padziko lapansi zimene zinasonyeza chiyambi cha kulamulira kwa Yesu: nkhondo, njala, ndi imfa zosakhala zapanthaŵi yake kupyolera mwa zochititsa zosiyanasiyana. Kodi tikuwona maulosi aŵiri ameneŵa akukwaniritsidwa lerolino?
Nkhondo!
7. Kodi chiyani chimene molosera chikuphiphiritsiridwa ndi kukwera kwa wapakavalo wachiŵiri wa Chivumbulutso?
7 Tiyeni tiziyang’ane mosamalitsa kwambiri. Choyamba, Yesu anati: “Mtundu umodzi wa anthu udzaukirana ndi mtundu wina, ndi ufumu ndi ufumu wina.” Umenewu unali ulosi wa nkhondo. Mofananamo, wachiŵiri wa okwera paakavalo anayi a m’Chivumbulutso anaphiphiritsira nkhondo. Timaŵerenga motere: “Anatuluka kavalo wina, wofiira: ndipo anampatsa iye womkwera mphamvu ya kuchotsa mtendere padziko ndi kuti aphane; ndipo anampatsa iye lupanga lalikulu.” (Chivumbulutso 6:4) Tsopano, mtundu wa anthu wakhala ukumenya nkhondo kwazaka zikwi zochuluka. Nangano, nchifukwa ninji, mawu ameneŵa ayenera kukhala ndi kufunika kwapadera kaamba ka tsiku lathu?
8. Kodi nchifukwa ninji tikayembekezera nkhondo kukhala mbali yapadera ya chizindikiro?
8 Kumbukirani kuti nkhondo mwa iyo yokha sindiyo chizindikiro cha kukhalapo kwa Yesu. Chizindikirocho chikupangidwa ndi zinthu zonse za muulosi wa Yesu zochitika m’nyengo yanthaŵi yodziŵika imodzimodzi. Koma nkhondo ndiyo mbali yoyambirira yotchulidwa, chotero tingathe kuyembekezera kuti mbali imeneyi ikakwaniritsidwa mwanjira yapadera imene ikachitika kuti ife tiiwone, kunena kwake titero. Ndipo aliyense ayenera kuvomereza kuti nkhondo za m’zaka za zana lino la 20 ziri zosiyana ndi za m’mbiri yonse yapapitapo.
9, 10. Kodi ndimotani mmene maulosi onena zankhondo anayambira kukwaniritsidwa?
9 Mwachitsanzo, palibe nkhondo zakale—zankhanza ndi zosakaza monga momwe zochuluka zinaliri—zimene zinafika ngakhale pafupi chabe kuukulu wake wa nkhondo ziŵiri zadziko za m’zaka za zana la 20 m’kusakaza. Eya, nkhondo yoyamba yadziko potsirizira pake inachititsa pafupifupi imfa ya mamiliyoni 14, kuposa chiŵerengero chathunthu cha maiko ambiri. Zowonadi, “anampatsa . . . mphamvu ya kuchotsa mtendere padziko ndi kuti aphane.”
10 Malinga ndi kunena kwa ulosiwo, ‘lupanga lalikulu linapatsidwa’ wokwera pakavalo wachiŵiri wonga nkhondoyo wa m’Chivumbulutso. Kodi umenewo ukugwira ntchito motani? Motere: Zida zankhondo zinakhala zakupha kopambana. Pokhala ndi akasinja, ndege, mpweya wokhala ndi poizoni yakupha, sitima zoyenda pansi pa madzi, ndi mizinga imene ikatha kuponya mpholopolo zophulika pamtunda wa makilomitala ochuluka, munthu anafikira kukhala waluso kwambiri m’kupha mnansi wake. Ndipo chiyambire pankhondo yoyamba yadziko, “lupanga lalikulu” lafikira kukhala lowonongadi kwambiri—chifukwa cha kugwiritsiridwa ntchito kwa zinthu zonga kulankhulirana kwa pawailesi, makina owonera ndege, mfuti zachimakono, zida zankhondo zowononga minyeŵa ndi za makhemikolo, mabomba oponya malaŵi amoto, mabomba a petulo, mitundu yatsopano ya mabomba, mabomba oponyedwa kukaphulikira kumaiko ena, sitima zapansi zokhala ndi zida za nyukliya, ndege zopititsidwa patsogolo, ndi ngalaŵa zazikulu zankhondo.
“Zoŵaŵa Zoyamba”
11, 12. Kodi nkhondo yoyamba yadziko inali kokha “zoŵaŵa zoyamba” m’njira yotani?
11 Mavesi oyambirira a ulosi wa Yesu akumaliza ndi mawu akuti: “Ndizo zonsezi zoŵaŵa zoyamba.” Ndithudi zimenezi zinali zowona ponena za nkhondo yoyamba yadziko. Kutha kwake mu 1918 sikunadzetse mtendere wa nthaŵi yaitali. Iyo posapita nthaŵi inatsatiridwa ndi zochitika zankhondo zochepa koma zowopsa mu Itiyopiya, Libya, Spanya, Rasha, Indiya, ndi maiko ena. Ndiyeno panadza nkhondo yowopsa yachiŵiri ya dziko lonse, imene inapha asilikali ndi alaiya okwanira 50 miliyoni.
12 Ndiponso, mosasamala kanthu za mapangano amtendere a apa ndi apo ndi kuima kaye m’kumenyana, mtundu wa anthu ukali pankhondobe. Mu 1987 kunasimbidwa kuti nkhondo zazikulu 81 zinamenyedwa chiyambire 1960, zikumapha amuna, akazi, ndi ana 12 555-000. Chaka cha 1987 chinakhala ndi nkhondo zochuluka zomamenyedwa koposa chaka china chirichonse chapapitapo m’mbiri yolembedwa.1 Ndiponso, kukonzekera nkhondo ndi ndalama zowonongeredwa pankhondo, tsopano zimafika pachionkhetso chapafupifupi $1 000 000 000 000 pachaka, kusokoneza chuma cha padziko lonse.2 Ulosi wa Yesu wonena za ‘mtundu wa anthu kuukirana ndi mtundu wina ndi ufumu ndi ufumu wina’ ukukwaniritsidwadi. Kavalo wofiira wankhondo akupitirizabe kuthamanga kochititsa mantha kudutsa padziko lonse lapansi. Koma bwanji ponena za mbali yachiŵiri ya chizindikiro?
Njala!
13. Kodi Yesu ananeneratu zochitika zatsoka zotani, ndipo kodi ndimotani mmene masomphenya a wokwera pakavalo wachitatu wa m’Chivumbulutso amachirikizira ulosi wake?
13 Yesu aneneratu kuti: “Ndipo kudzakhala njala . . . m’malo akutiakuti.” Wonani mmene umenewu ukugwirizanira ndi kukwera kwa wachitatu wa okwera apaakavalo anayi a Chivumbulutso. Ponena za iye timaŵerenga kuti: “Ndipo ndinapenya, tawonani, kavalo wakuda; ndipo iye womkwera anali nawo muyeso m’dzanja lake. Ndipo ndinamva ngati mawu pakati pa zamoyo zinayi, nanena, Muyeso wa tirigu wogula lupiya, ndi miyeso itatu ya barele zogula lupiya; ndi mafuta ndi vinyo musadziipse.” (Chivumbulutso 6:5, 6) Inde, njala zazikulu kwambiri!
14. Kodi ndinjala zazikulu zotani chiyambire 1914 zimene zakwaniritsa ulosi wa Yesu?
14 Kodi nkothekera kuti ulosi umenewu ukukwaniritsidwa lerolino, pamene maiko ambiri afikira pamuyezo wapamwamba kwambiri wokhalira ndi moyo? Kuyang’ana mofulumira padziko lonse lathunthu sikukusiya chikaikiro chirichonse ponena za yankho. Mogwirizana ndi mbiri, njala zachititsidwa ndi nkhondo ndi masoka achilengedwe. Pamenepo, nkosadabwitsa, kuti, zaka za zana lathu lino, zimene zakhala ndi masoka ndi nkhondo zokulira, zakanthidwa mobwerezabwereza ndi njala. Mbali zambiri za dziko lapansi zakanthidwa ndi masoka motere chiyambire 1914. Lipoti lina likundandalika njala zazikulu zoposa 60 chiyambire 1914, m’maiko okhala motalikirana kwambiri monga ngati Grisi, Netherlands, U.S.S.R., Nigeria, Chad, Chile, Peru, Bangladesh, Bengal, Kampuchea, Itiopiya, ndi Japan.3 Zina za njala zimenezi zakhala kwazaka zingapo ndipo zachititsa imfa za mamiliyoni ochuluka.
15, 16. Kodi ndinjala zina zotani zimene ziri zowonongadi lerolino?
15 Ngakhale kuli kwakuti njala zazikulu kaŵirikaŵiri zimafalitsidwa kwambiri, pambuyo pakanthaŵi zimatha ndipo opulumuka mwapang’onopang’ono amabwerera kumoyo wamasiku onse bwino lomwe. Komabe, mtundu wina wowopsa kwambiri wa njala wabuka mkati mwa zaka za zana la 20. Umenewu uli wosakulirapo kwambiri ndipo chifukwa cha chimenecho kaŵirikaŵiri umanyalanyazidwa. Koma umakhalapo chaka ndi chaka. Umenewu ndiwo mliri wadzawoneni wa kudya mosakhuta umene umayambukira kufikira mbali imodzi mwa zisanu ya anthu a pachiunda chathu chino ndipo umapha pakati pa anthu mamiliyoni 13 ndi 18 chaka chirichonse.4
16 M’kunena kwina, kaŵirikaŵiri mtundu umenewu wa njala umapha pafupifupi anthu ochuluka kwambiri m’masiku aŵiri koposa amene anaphedwa pa Hiroshima ndi bomba la atomu. Zowonadi, zaka ziŵiri zirizonse, pali anthu ochuluka amene amafa chifukwa cha ziyambukiro za njala koposa asilikali ankhondo amene anaphedwa m’Nkhondo Yadziko I ndi Nkhondo Yadziko II zitaphatikidwa pamodzi. Kodi pakhala “njala . . . m’malo akutiakuti” chiyambire 1914? Ndithudi, inde!
Zivomezi
17. Kodi ndichivomezi chosakaza chotani chimene chinachitika mwamsanga pambuyo pa 1914?
17 Pa January 13, 1915, pamene nkhondo yoyamba yadziko inali ndi miyezi yoŵerengeka chabe, chivomezi chinagwedeza Abruzzi, Italiya, ndipo chinatenga miyoyo ya anthu 32 610. Tsoka lalikulu limeneli likutikumbutsa kuti nkhondo ndi njala mkati mwa kukhalapo kwa Yesu zikatsagana ndi kanthu kenanso: “Kudzakhala . . . zivomezi m’malo akutiakuti.” Monga momwe kunaliri ndi nkhondo ndi njala, chivomezi cha pa Abruzzi chinali kokha “zowawa zoyamba.”a
18. Kodi ndimotani mmene ulosi wa Yesu wonena za zivomezi wakwaniritsidwira?
18 Zaka za zana la 20 zakhala zaka za zana la zivomezi, ndipo tithokoze kutulukiridwa kwa njira zofalitsira nyuzi, mtundu wonse wa anthu uli wozindikira bwino kwambiri kusakaza kumene izo zachititsa. Kungotchula zoŵerengeka chabe, 1920 anakhala ndi 200 000 akufa m’chivomezi cha m’China; mu 1923, okwanira 99 300 anafa m’chivomezi cha m’Japan; mu 1935, chivomezi china chinapha 25 000 m’chimene tsopano chikutchedwa Pakistan, pamene 32 700 anafa mu Turkey mu 1939. Panali akufa 66 800 m’chivomezi cha mu Peru mu 1970. Ndipo mu 1976, okwanira 240 000 (kapena, malinga ndi magwero ena, 800 000) anafa m’Tangshan, China. Posachedwa pompa, mu 1988, panali 25 000 amene anafa m’chivomezi chachikulu m’Armenia.b Ndithudi, “zivomezi m’malo akutiakuti”!6
“Mliri Wakupha”
19. Kodi ndimfundo ina yotani yonena za chizindikiro imene inanenedweratu ndi Yesu ndi kuphiphiritsiridwa ndi wokwera pakavalo wachinayi wa m’Chivumbulutso?
19 Mfundo ina ya ulosi wa Yesu njonena za matenda. Mlaliki Luka, m’cholembedwa chake, akulemba kuti Yesu ananeneratu za “miliri mmalo akutiakuti.” (Luka 21:11) Izinso ziri zogwirizana ndi masomphenya olosera a okwera paakavalo anayi a m’Chivumbulutso. Wokwera pakavalo wachinayi akutchedwa Imfa. Iye akuphiphiritsira imfa yosakhala ya panthaŵi yake yochokera m’zochititsa zosiyanasiyana, kuphatikizapo ‘mliri wakupha ndi . . . zirombo zapadziko.’—Chivumbulutso 6:8, NW.
20. Kodi ndichaola chapadera chotani chimene chinali mbali ya kukwaniritsidwa kwa ulosi wa Yesu wonena za miliri?
20 Kalero mu 1918 ndi 1919, oposa anthu 1 000 000 000 anadwala fuluwenza ya Spanya, ndipo anthu oposa 20 000 000 anafa. Nthendayo inapha anthu oposa ambiri koposa nkhondo yeniyeniyo.7 Ndipo “mliri wakupha,” kapena ‘chaola,’ ukupitirizabe kukantha mbadwo uno, mosasamala kanthu za kupita patsogolo kwapadera kwa zamankhwala. Kodi nchifukwa ninji izi ziri choncho? Choyamba, nthaŵi zonse maiko osauka kwambiri samakhala ndi mapindu a kupita patsogolo kwa sayansi. Anthu osauka amavutika ndi kufa ndi matenda amene akanatha kuchiritsidwa ngati ndalama zochuluka zikanapangitsidwa kukhala zopezeka.
21, 22. Kodi ndimotani mmene maiko olemera ndi maiko osauka omwe avutikira ndi “mliri wakupha”?
21 Motero, anthu okwanira mamiliyoni 150 padziko lonse akuvutika ndi malungo. Anthu ena okwanira mamiliyoni 200 akugwidwa ndi likodzo. Nthenda ya Chaga ikukantha anthu pafupifupi mamiliyoni khumi. Pafupifupi mamiliyoni 40 akuvutika ndi nthenda ya khungu lochititsidwa ndi madzi oipa. Matenda a kusanza ndi kutseguka m’mimba amapha ana mamiliyoni ochuluka chaka chirichonse.8 Kholozi ndi khate akali chikhalirebe vuto lalikulu lathanzi. Mwapadera, osauka onse apansi pano amavutika ndi ‘mliri mmalo akutiakuti.’
22 Koma nchimodzimodzinso olemera. Mwachitsanzo, fuluwenza, imakantha olemera ndi osauka omwe. Mu 1957 kugwira kumodzi kwa fuluwenza kunachititsa imfa 70 000 mu United States mokha. Mu Jeremani kukuyerekezeredwa kuti munthu mmodzi mwa asanu ndi mmodzi potsirizira pake adzavutika ndi kensa.9 Matenda opatsirana mwa kugonana nawonso akukantha olemera ndi osauka omwe. Chindoko, nthenda yopatsana mwa kugonana yochitiridwa lipoti mwakaŵirikaŵiri koposa mu United States, imakantha ochuluka okwanira 18,9 peresenti ya chiŵerengero cha anthu m’mbali zina za Afrika.10 Chinzonono, chikhuthula, ndi matuza ku ziŵalo zogonanira ziri zina za “miliri” yofalitsidwa mofala mwa kugonana.
23. Kodi ndi“mliri wakupha” wotani umene posachedwapa wakhala wofala m’mitu ya nkhani?
23 M’zaka zaposachedwapa, “mliri wakupha” wa AIDS waloŵanso pampambo wa “miliri.” AIDS iri nthenda yowopsa kwambiri chifukwa chakuti, pofika panopo pamene tikulemba, palibe mankhwala amene apezeka, ndipo chiŵerengero cha akufa nayo chikupitirizabe kuwonjezereka. Dr. Jonathan Mann, dairekitala wa WHO (Gulu la Padziko Lonse Lazaumoyo) Programu Yapadera yonena za AIDS, anati: “Tikuyerekezeranso kuti pali anthu mamiliyoni asanu kufikira pa 10 padziko lonse lapansi lerolino amene agwidwa ndi kachirombo kopha mphamvu yolimbanira ndi matenda mwa munthu (HIV).”11 Malinga ndi kunena kwa kuyerekezera kumodzi kofalitsidwa, kachirombo ka AIDS kamakantha mkhole watsopano mphindi iriyonse. Ndithudi ndiwo “mliri wakupha”! Koma bwanji ponena za ulosi wonena za imfa yochititsidwa ndi zirombo?
“Zirombo za Padziko”
24, 25. (a) Kodi mneneri Ezekieli anali kunena za mtundu wanji wa ‘chirombo’? (b) Kodi Yesu ananenanji ponena za “zirombo” kukhala ziri zotanganitsidwa padziko lapansi mkati mwa kukhalapo kwake?
24 Chenicheni nchakuti, pamene zirombo zitchulidwa masiku ŵano m’manyuzipepala, kuli chifukwa chakuti mitundu ina iri paupandu kapena kuti yatsala pang’ono kusoloka. “Zirombo za padziko” ziri zowopsezedwa kwambiri ndi anthu koposa mmene anthu aliri owopsezedwera nazo. Mosasamala kanthu za zimenezi, m’maiko ena zirombo monga akambuku ku Indiya akutengabe miyoyo ya anthu mokhazikika.
25 Komabe, Baibulo likutisonyeza mtundu wina wa chirombo chimene chachititsa mantha enieni m’zaka zaposachedwapa. Mneneri Ezekieli anayerekezera anthu achiwawa ndi zirombo pamene iye anati: “Akalonga ake mkati mwake akunga afisi akumwetula nyama, kukhetsa mwazi, kuwononga miyoyo, kuti awone phindu lonyenga.” (Ezekieli 22:27) Pamene iye analosera za “kuchuluka kwa kusayeruzika,” Yesu, kwenikweni, anali kunena kuti “zirombo” zoterozo zikakhala zokangalika padziko lapansi mkati mwa kukhalapo kwake. (Mateyu 24:12) Wolemba Baibulo Paulo akuwonjeza kuti mkati mwa kukhalapo kwa Yesu anthu adzakhala “okonda ndalama . . . osadziletsa, owopsa, osakonda zabwino.” (2 Timoteo 3:1-3, NW) Kodi zakhala choncho chiyambire 1914?
26-28. Kodi ndimalipoti otani ochokera kumbali zosiyanasiyana zadziko amene akusonyeza kuti “zirombo” zaupandu zikulusira dziko lapansi?
26 Zakhaladi choncho. Ngati mukhala mu pafupifupi mzinda uliwonse waukulu padziko lapansi, inu mukudziŵa kale zimenezo. Koma ngati mukukaikira, tangolingalirani mawu ogwidwa m’manyuzipepala aposachedwapa otsatirapoŵa. Kuchokera ku Colombia: “Chaka chathachi apolisi analemba m’mabukhu mwawo . . . pafupifupi mbanda 10 000 ndi kuba mowopseza ndi mfuti 25 000.” Kuchokera ku Victoria, Australia: “Kukwera Kwakukulu Muupandu Waukulu.” Kuchokera ku United States: “Kupha mu New York Kukufika Pachiŵerengero Chapamwamba Koposa China Chirichonse.” “Detroit anaposa Gary, Ind., chaka chathachi monga mzinda waukulu wokhala ndi chiŵerengero chapamwamba kopambana cha mbanda mumtunduwo—58 mwa anthu okhalamo 100 000 alionse.”
27 Kuchokera ku Zimbabwe: “Kuphedwa kwa makanda kwafika pamlingo wa kukhala vuto.” Kuchokera ku Brazil: “Kuli upandu wochuluka kwambiri kuno, ndi kuseŵera kwambiri ndi zida zankhondo, kwakuti mbiri za chiwawa sizirinso zodabwitsa konse.” Kuchokera ku New Zealand: “Ziukiro za kugonana ndi upandu wa chiwawa zikupitirizabe kukhala nkhaŵa yaikulu kwa apolisi.” “Ukulu wa chiwawa cha anthu a mu New Zealand kwa wina ndi mnzake ungangofotokozedwe kokha kukhala wauchinyama.” Kuchokera ku Spanya: “Spanya akuvutika ndi vuto laupandu womawonjezereka.” Kuchokera ku Italiya: “Gulu la Mafia lakupha la ku Sicily, pambuyo pa kudodometsedwa, likuyambiranso funde lake lakumka liipha.”
28 Izi ziri zitsanzo zazing’ono chabe za malipoti a m’manyuzipepala owonekera posachedwapa bukhu lino lisanafalitsidwe. Ndithudi, “zirombo” zikulusira dziko lapansi, zikumachititsa anthu kuwopera chisungiko chawo.
Kulalikira Mbiri Yabwino
29, 30. Kodi mkhalidwe wachipembedzo uli wotani m’Chikristu cha Dziko, mokwaniritsa ulosi wa Yesu?
29 Kodi chipembedzo chikakhala bwanji mkati mwa nthaŵi zovuta za kukhalapo kwa Yesu? Kumbali ina, Yesu analosera kuti pakakhala kuwonjezereka kwa ntchito ya chipembedzo: “Aneneri ambiri onyenga adzabuka ndi kusokeretsa ambiri.” (Mateyu 24:11, NW) Kumbali ina, iye ananeneratu kuti m’Chikristu cha Dziko monse, chikondwerero mwa Mulungu chikakhala chotsika kwambiri. “Chikondi cha aunyinji chidzazirala.”—Mateyu 24:12, NW.
30 Uwu ndithudi ukufotokoza zimene zikuchitika lerolino m’Chikristu cha Dziko. Kumbali ina, matchalitchi aakulu kulikonse akulephera chifukwa cha kusoŵa chichirikizo. Mu amene panthaŵi ina anali maiko Achiprotestante amphamvu akumpoto kwa Ulaya ndi Mangalande, chipembedzo sichirinso chamoyo koma chakufa. Panthaŵi imodzimodziyo, Tchalitchi cha Katolika chiri ndi vuto la kusoŵa ansembe ndi kuchepachepa kwa chichirikizo. Kumbali ina, pakhala kubuka kwa timagulu tachipembedzo tochuluka. Timipatuko tozikidwa pa zipembedzo Zakummaŵa tikufalikira, pamene alaliki aumbombo a pawailesi yakanema akudzikundikira madola mamiliyoni ochuluka.
31. Kodi nchiyani chimene Yesu ananeneratu chimene chikuthandiza kudziŵikitsa Akristu owona lerolino?
31 Komabe, bwanji ponena za Chikristu chowona, chipembedzo choyambitsidwa ndi Yesu ndi kulalikidwa ndi atumwi ake? Ichi chikakhalapobe mkati mwa kukhalapo kwa Yesu, koma kodi icho chikazindikiridwa motani? Pali zinthu zingapo zimene zimadziŵikitsa Chikristu chowona, ndipo chimodzi chikutchulidwa muulosi waukulu wa Yesu. Akristu owona akakhala otanganitsidwa m’ntchito ya kulalikira ya padziko lonse. Yesu analosera kuti: “Ndipo mbiri yabwino imeneyi yaufumu idzalalikidwa mu dziko lonse lapansi lokhalidwa ndi anthu kaamba ka umboni kumitundu yonse; ndipo pomwepo mapeto adzafika.”—Mateyu 24:14, NW.
32. Kodi ndigulu limodzi lokha liti limene lakwaniritsa ulosi wa Yesu wolembedwa m’Mateyu 24:14?
32 Kulalikira kumeneku tsopano kukuchitika pamlingo wa padziko lonse lapansi! Lerolino, gulu lachipembedzo lotchedwa Mboni za Yehova liri lotanganitsidwa m’ntchito yaikulu kwambiri ya kulalikira m’mbiri ya Chikristu. (Yesaya 43:10, 12) Kalero mu 1919, pamene zipembedzo zazikulu Zachikristu cha Dziko zokhala ndi maganizo a andale zadzikozo zinali kuchirikiza Chigwirizano cha Mitundu choikidwiratu ku kuwonongedwacho, Mboni za Yehova zinali kukonzekera mkupiti wa kulalikira kwapadziko lonse umenewu.
33, 34. Kodi mbiri yabwino ya Ufumu yalakikidwa padziko lonse lapansi kumlingo waukulu motani?
33 Panthaŵiyo panali Mboni zokwanira pafupifupi 10 000 chabe, koma izo zinadziŵa ntchito imene inayenera kuchitidwa. Molimba mtima, izo zinayamba ntchito ya kulalikira. Izo zinazindikira kuti kugaŵanika kukhala kagulu ka atsogoleri achipembedzo ndi ka anthu wamba kunali kosemphana ndi zonse ziŵiri malamulo a Baibulo ndi chitsanzo cha atumwi. Chotero izo zonse, mosasiyapo munthu aliyense, zinaphunzira mmene zingalankhulire ndi anansi awo ponena za Ufumu wa Mulungu. Izo zinakhala gulu la alaliki.
34 M’kupita kwa nthaŵi, alaliki ameneŵa anapirira chitsutso chachikulu. Mu Ulaya, izo zinatsutsidwa ndi mitundu yosiyanasiyana ya maboma olamulira motsendereza ufulu. Mu United States, ndi Canada, izo zinayang’anizana ndi zitokoso za lamulo ndi kachitidwe ka magulu achipolowe. M’maiko ena, izo zinafunikira kulaka kuderedwa kukhosi ndi otengeka ndi chipembedzo ndi chizunzo chankhanza chochitidwa ndi olamulira ankhanza otsendereza ufulu. M’zaka zaposachedwapa, izo zinafunikiranso kulimbana ndi mzimu wa kukaikira ndi wakukonda zosangalatsa umene wabuka. Koma izo zapirira kufikira pamlingo wakuti, lerolino, ziripo zoposa mamiliyoni atatu ndi theka m’maiko 212. Ndi kale lonse mmbuyomu mbiri yabwino ya Ufumu sinalalikidwepo mofala kwambiri chotere—kukwaniritsidwa kwamphamvu kwa mbali ya chizindikiro imeneyi!
Kodi Zonsezi Zikutanthauzanji?
35. (a) Kodi ndimotani mmene kukwaniritsidwa kwa ulosiwo lerolino kumathandizira kusonyeza kuuziridwa kwa Baibulo? (b) Kodi kukwaniritsidwa kwa chizindikiro chimene Yesu anapereka kumatanthauzanji kaamba ka tsiku lathu?
35 Mosakaikira ife tikuwona kukwaniritsidwa kwa chizindikiro chachikulu chimene Yesu anapereka. Chenicheni chimenechi chikuwonjezera kuumboni wakuti Baibulo liridi louziridwa ndi Mulungu. Palibe munthu amene akanatha kuneneratu kwanthaŵi yaitali pasadakhale chotero zochitika zimene zikachitika mkati mwa zaka zino za zana la 20. Ndiponso, kukwaniritsidwa kwa chizindikiro kukutanthauza kuti ife tikukhala ndi moyo m’nthaŵi ya kukhalapo kwa Yesu ndi yamapeto a dongosolo la zinthu. (Mateyu 24:3) Kodi zimenezi zitanthauzanji? Kodi nchiyani chimene chikuphatikizidwa m’kukhalapo kwa Yesu? Ndipo kodi nchiyani chimene chiri dongosolo la zinthu limene likupita kumapeto? Kuti tiyankhe mafunso ameneŵa, tifunikira kupenda umboni wina wamphamvu wa kuuziridwa kwa Baibulo: kugwirizana kwake kwa mkati kwapadera. M’mutu wotsatirapo, tidzafotokoza zimenezi ndi kuwona mmene mutu waukulu wa Baibulo ukufikira ngakhale patsopano lino pa chimake chochititsa mantha.
[Mawu a M’munsi]
a Panali zivomezi zokwanira zisanu pakati pa 1914 ndi 1918 zimene kulemera kwake kunafika 8 kapena kuposerapo pa sikelo yopimira zivomezi ya Richter—zamphamvu kwambiri koposa chivomezi cha pa Abruzzi. Komabe, zivomezi zimenezi zinachitikira kumalo akutali kwambiri a dziko lapansi, ndipo motero sizinadziŵidwe kwambiri mofanana ndi chivomezi cha mu Italiya.5
b Ziwonkhetso zosiyana zaperekedwa kaamba ka ziŵerengero za akufa mu ena a masoka ameneŵa. Komabe, zonse zinali zosakaza kopambanitsa.
-
-
Kugwirizana kwa Baibulo LonseBaibulo—Kodi Ndilo Mawu a Mulungu Kapena a Munthu?
-
-
Mutu 11
Kugwirizana kwa Baibulo Lonse
Tayekezerani nkhokwe ya mabukhu 66 olembedwa ndi pafupifupi anthu osiyanasiyana 40 mkati mwa nyengo yanthaŵi ya zaka 1 600. Zinenero zitatu zinagwiritsiridwa ntchito ndi olemba amene anakhala ndi moyo m’maiko angapo. Olemba onse anali ndi maumunthu osiyana, maluso, ndi ziyambi. Koma pamene mabukhu amene anawalembera potsirizira pake anasonkhanitsidwa pamodzi, zinachitika kuti, kwenikweni, iwo anapanga bukhu limodzi lokha lalikulu lomatsatira mutu umodzi waukulu kuyambira pachiyambi kufikira kumapeto. Zimenezo nzovuta kuziyerekezera, kodi sichoncho? Komabe, Baibulo ndilo nkhokwe ya mabukhu yoteroyo.
1. (Phatikizamoni mawu oyamba.) Kodi ndikugwirizana kwapadera kotani kumene kumatsimikizira chenicheni chakuti Baibulo liridi louziridwa ndi Mulungu?
PALIBE wophunzira wowona mtima amene angalephere kugwidwa mtima ndi chenicheni chakuti Baibulo, ngakhale kuli kwakuti ndiro kusonkhanitsidwa pamodzi kwa mabukhu osiyanasiyana, liri chinthu chimodzi chogwirizanitsidwa. Iro liri logwirizanitsidwa m’chakuti, kuyambira pachiyambi kukafikira kumapeto, limapititsa patsogolo kulambiridwa kwa Mulungu mmodzi yekha amene mikhalidwe yake siimasintha konse, ndipo mabukhu ake onse amafotokoza mutu umodzi waukulu. Kugwirizana kwa lonse lathunthu kumeneku ndiko umboni wamphamvu wakuti Baibulo liri, ndithudi, Mawu a Mulungu.
2, 3. Kodi ndiulosi wotani wonenedwa mu Edene umene unapereka maziko a chiyembekezo, ndipo kodi ndimikhalidwe yotani imene inatsogolera kukunenedwa kwa ulosiwo?
2 Mutu waukulu wa Baibulo ukusonyezedwa m’mitu yoyambirira ya bukhu lake loyambirira lenilenilo, Genesis. Mmenemo, timaŵerenga kuti makolo athu oyambirira, Adamu ndi Hava, analengedwa ali angwiro naikidwa m’munda wa paradaiso, Edene. Komabe, Hava, anafikiridwa ndi njoka, imene inatsutsa kuyenerera kwa malamulo a Mulungu nimnyenga ndi mabodza a machenjera kuloŵa m’njira yauchimo. Adamu anamtsatira ndipo nayenso sanamvere Mulungu. Nchotulukapo chotani? Onse aŵiri anathamangitsidwa m’Edene ndipo anatsutsidwira kuimfa. Ife lerolino tikuvutika ndi zotulukapo za chipanduko choyambirira chimenecho. Ife tonse timalandira uchimo ndi imfa kuchokera kwa makolo athu oyambirira.—Genesis 3:1-7, 19, 24; Aroma 5:12.
3 Komabe, panthaŵi yovuta imeneyo, Mulungu anapereka ulosi umene unapereka maziko a chiyembekezo. Ulosiwo unanenedwa kwa chinjoka, koma unaperekedwa Adamu ndi Hava akumva kotero kuti iwo akanatha kuusimbira kwa ana awo. Nazi zimene Mulungu ananena: “Ndipo ndidzaika udani pakati pa iwe ndi mkaziyo ndi pakati pa mbewu yako ndi mbewu yake. Iye adzakuzunzunda iwe mutu ndi iwe udzamzunzunda chitende.”—Genesis 3:15, NW; Aroma 8:20, 21.
4. Kodi ndianthu ati amene anatchulidwa muulosi wa Yehova mu Edene, ndipo kodi ndimotani mmene iwo akachitira mkati mwa zaka mazana ochuluka?
4 Wonani zinthu zinayi zimene zikutchulidwa m’vesi la mutu wa nkhani limeneli: chinjoka ndi mbewu yake kudzanso mkazi ndi mbewu yake. Zinthu zimenezi zikakhala zochitika zofunika m’zochitika kwa zaka zikwi zochuluka zirinkudza. Udani wosalekeza unayenera kukhalapo pakati pa mkazi ndi mbewu yake kumbali imodzi ndi chinjoka ndi mbewu yake kumbali ina. Udani umenewu ukaphatikizapo kulimbana kosalekeza pakati pa kulambira kowona ndi konyenga, khalidwe loyenera ndi kuipa. Panthaŵi ina, chinjoka chikapeza chowonekera kukhala phindu pamene chikazunzunda chitende cha mbewu ya mkazi. Komabe, potsirizira pake, mbewu yamkazi ikaphwanya mutu wa chinjoka, ndipo Mulungu iye mwini akatamandidwa pamene zodziŵikitsa zonse za chipanduko choyambirira chimenecho zikachotsedwa.
5. Kodi tikudziŵa motani kuti Hava sanali mkazi wa muulosi umenewo?
5 Kodi ndani amene ali mkaziyo ndi chinjoka? Ndipo kodi ndani amene ali mbewu zawo? Pamene Hava anabala mwana wake wamwamuna wachisamba, Kaini, iye ananena kuti: “Ndabala munthu mwa chithandizo cha Yehova.” (Genesis 4:1, NW) Mwinamwake iye analingalira kuti iye anali mkazi wa muulosi uja ndi kuti mwana wawo wamwamuna ameneyu akatsimikizira kukhala mbewu. Komabe, Kaini, anali ndi mzimu woipa wofanana ndi wa chinjoka. Iye anasanduka wambanda, akumapha m’ngono wake wa iye mwini Abele. (Genesis 4:8) Mwachiwonekere, ulosiwo unali ndi tanthauzo lozama, lophiphiritsira limene Mulungu yekha akanatha kulifotokoza. Ndipo zimenezi iye anazichita, mwapang’ono panthaŵi imodzi. Mabukhu onse 66 a Baibulo amathandizira mwanjira zosiyanasiyana kuvumbulutsidwa kwa tanthauzo la umenewu, ulosi woyambirira m’Baibulo.
Kodi Ndani Amene Ali Chinjoka?
6-8. Kodi ndimawu otani a Yesu amene amatithandiza kudziŵa mphamvu kutseri kwa chinjoka? Fotokozani.
6 Choyamba, kodi ndani amene ali chinjoka chotchulidwa m’Genesis 3:15? Cholembedwacho chikunena kuti njoka yeniyeni inafikira Hava mu Edene, koma njoka zenizeni sizingathe kulankhula. Payenera kukhala panali mphamvu ina kutseri kwa njokayo yomaichititsa kuchita monga mmene inachitiramo. Kodi mphamvu imeneyo inali chiyani? Mphamvuyo siinadziŵike bwino lomwe kufikira m’zaka za zana loyamba la Nyengo ya Onse, pamene Yesu anali kuchita utumiki wake padziko lapansi pano.
7 Pachochitika china, Yesu anali kulankhula ndi atsogoleri achipembedzo Achiyuda odzilunganitsa amene monyada ananena kuti iwo anali ana a Abrahamu. Komabe, iwo anatsutsa kwantu wagalu chowonadi cholalikidwa ndi Yesu. Chotero Yesu anati kwa iwo: “Inu muli ochokera kwa atate wanu Mdyerekezi, ndipo mufuna kuchita zolakalaka za atate wanu. Ameneyo anali wakupha munthu pamene iye anayamba, ndipo sanaima mwamphamvu m’chowonadi, chifukwa chakuti chowonadi sichiri mwa iye. Pamene iye alankhula bodza, iye amalankhula mogwirizana ndi chifuniro chake cha iye mwini, chifukwa chakuti iye ali wabodza ndi atate wabodza.”—Yohane 8:44, NW.
8 Mawu a Yesu anali amphamvu koma olunjikadi. Iye anafotokoza Mdyerekezi monga “wakupha munthu” ndi “atate wabodza.” Tsopano, mabodza oyambirira kulembedwa anali awo onenedwa ndi njoka mu Edene. Aliyense amene ananena mabodza amenewo analidi “atate wabodza.” Ndiponso, mabodza amenewo anachititsa imfa ya Adamu ndi Hava, akumapangitsa kuti wabodza wamakedzanayo akhale wambanda. Chotero mwachiwonekere, mphamvu imene inali kutseri kwa chinjoka mu Edene inali Satana Mdyerekezi, ndipo Yehova analidi kulankhula kwenikweni ndi Satana mu ulosi wamakedzana umenewo.
9. Kodi Satana anakhalako motani?
9 Ena afunsa kuti: Ngati Mulungu ali wabwino, kodi nchifukwa ninji iye analenga cholengedwa choterocho chonga Mdyerekezi? Mawu a Yesu amatithandiza kuyankha funso limenelo. Ponena za Satana Yesu anati: “[Iye] anali wakupha munthu kuyambira pachiyambi.” Chotero pamene Satana ananamiza Hava, ndipo pamene iye anayamba kukhala Satana—kuchokera ku liwu Lachihebri limene limatanthauza “wotsutsa.” Mulungu sanalenge Satana. Mngelo wokhulupirika papitapoyo analola chikhumbo cholakwa kukula mumtima mwake kotero kuti anakhala Satana.—Deuteronomo 32:4; yerekezerani ndi Yobu 1:6-12; 2:1-10; Yakobo 1:13-15.
Mbewu ya Chinjoka
10, 11. Kodi ndimotani mmene Yesu ndi mtumwi Yohane akutithandizira kudziŵa mbewu ya Chinjoka?
10 Komabe, bwanji ponena za ‘mbewu [kapena mbadwa] ya chinjoka’? Mawu a Yesu amatithandizanso kuthetsa mbali imeneyi ya vutolo. Iye kwa atsogoleri achipembedzo Achiyuda anati: “Inu muli ochokera kwa atate wanu Mdyerekezi, ndipo inu mufuna kuchita zikhumbo za atate wanu.” Ayuda ameneŵa anali mbadwa za Abrahamu, monga momwedi monyada ananenera. Koma khalidwe lawo loipa linawapanga iwo kukhala ana auzimu a Satana, woyambitsa uchimo.
11 Mtumwi Yohane, akulemba chakumapeto kwa zaka za zana loyamba, akufotokoza momvekera bwino amene anali a mbewu ya Chinjoka, Satana. Iye akulemba kuti: “Iye wochita tchimo ali wochokera mwa Mdyerekezi, chifukwa Mdyerekezi amachimwa kuyambira pachiyambi. . . . Mmenemo awoneka ana a Mulungu, ndi ana a Mdyerekezi: yense wosachita chilungamo siali wochokera mwa Mulungu; ndi iye wosakonda mbale wake.” (1 Yohane 3:8, 10) Mwachiwonekere, a mbewu ya Chinjoka akhala okangalika kwambiri m’mbiri yonse ya anthu!
Kodi Ndani Amene Ali Mbewu ya Mkazi?
12, 13. (a) Kodi ndimotani mmene Yehova anavumbulira kwa Abrahamu kuti mbewu ya mkazi ikawonekera pakati pa mbadwa zake? (b) Kodi ndani amene analandira mwacholoŵa lonjezo lonena za Mbewu?
12 Pamenepa, kodi ndani amene ali ‘mbewu [kapena mbadwa] ya mkazi’? Limeneli liri limodzi la mafunso ofunika kopambana amene anafunsidwapo, pakuti ndiyo mbewu ya mkaziyo imene potsirizira pake idzaphwanya mutu wa Satana ndi kuthetsa ziyambukiro zoipa za chipanduko choyambiriracho. Kalero m’zaka za zana la 20 B.C.E., Mulungu anavumbula chisonyezero chachikulu chodziŵira ponena za kudziŵika kwa ameneyu kwa munthu wokhulupirika Abrahamu. Chifukwa cha chikhulupiriro chachikulu cha Abrahamu, Mulungu anapanga mpambo wa malonjezo kwa iye wonena za mbadwa imene ikabadwa kwa iye. Limodzi la ameneŵa linakupangitsa kukhala kowonekera bwino kuti ‘mbewu ya mkazi’ imene ‘ikaphwanya mutu wachinjoka’ ikawonekera pakati pa ana a Abrahamu. Mulungu anamuuza kuti: “Mbewu zako zidzagonjetsa chipata cha adani awo. M’mbewu zako mitundu yonse yadziko idzadalitsidwa chifukwa wamvera mawu anga.”—Genesis 22:17, 18.
13 Pamene zaka zinali kupita, lonjezo la Yehova kwa Abrahamu linabwerezedwa kwa mwana wamwamuna wa Abrahamu Isake ndi kwa mdzukulu wake Yakobo. (Genesis 26:3-5; 28:10-15) Potsirizira pake, mbadwa za Yakobo zinakhala mafuko 12, ndipo limodzi la mafuko amenewo, Yuda, linalandira lonjezo lapadera: “Ndodo yachifumu siidzachoka mwa Yuda, kapena wolamulira pakati pa mapazi ake, kufikira atadza Silo; ndipo anthu adzamvera iye.” (Genesis 49:10) Mwachiwonekere, Mbewu inayenera kuwoneka m’fuko la Yuda.
14. Kodi ndimtundu wotani umene unalinganizidwa kuti ukonzekere kaamba ka kudza kwa Mbewu?
14 Pamapeto a zaka za zana la 16 B.C.E., mafuko 12 a Israyeli analinganizidwa kukhala mtundu monga anthu apadera a Mulungu. Ndi cholinga chimenechi, Mulungu anapanga pangano la lumbiro ndi iwo nawapatsa mpambo wa malamulo. Chifukwa chachikulu chochitira zimenezi chinali kukonzekeretsa mtundu kaamba ka kudza kwa Mbewu. (Eksodo 19:5, 6; Agalatiya 3:24) Kuyambira panthaŵi imeneyo kumkabe mtsogolo, udani wa Satana kwa Mbewu ya mkazi unawonekera mu udani wamitundu ku anthu osankhidwa a Mulungu.
15. Kodi nchisonyezero chotsirizira chotani chimene chinaperekedwa ponena za kuti ndi banja liti pakati pa mbadwa za Abrahamu limene likatulutsa Mbewu?
15 Chisonyezero chotsirizira chonena za kuti ndibanja liti limene likatulutsa Mbewu chinaperekedwa m’zaka za zana la 11 B.C.E. Panthaŵi imeneyo, Mulungu analankhula ndi mfumu yachiŵiri ya Israyeli, Davide, namlonjeza kuti Mbewu ikachokerapo pakati pa mbadwa zake ndi kuti mpando wachifumu wa ameneyu “ukakhazikitsidwa mwamphamvu kunthaŵi yonse.” (2 Samueli 7:11-16, NW) Kuyambira pamenepopo kumkabe mtsogolo, Mbewuyo moyenerera imasonyezedwa kukhala mwana wa Davide.—Mateyu 22:42-45.
16, 17. Kodi ndimotani mmene Yesaya anafotokozera madalitso amene Mbewu ikadzetsa?
16 M’zaka zotsatirapo, Mulungu anadzutsa aneneri kupereka chidziŵitso chouziridwa chowonjezereka chonena za Mbewu irinkudza. Mwachitsanzo, m’zaka za zana lachisanu ndi chitatu B.C.E., Yesaya analemba kuti: “Kwa ife kwabadwa mwana, mwana wamwamuna waperekedwa kwa ife; ndipo ulamuliro waukalonga udzakhala pamapeŵa pake. Ndipo dzina lake lidzatchedwa Phungu Wodabwitsa, Mulungu Wamphamvu, Atate Wosatha, Kalonga wa Mtendere. Kuchuluka kwa ulamuliro wake waukalonga ndi mtendere sikudzatha, pampando wachifumu wa Davide ndi paufumu wake.”—Yesaya 9:6, 7, NW.
17 Yesaya kenako analosera ponena za Mbewu imeneyi kuti: “Ndi chilungamo iye ayenera kulamula ofatsa, ndipo ndi chilungamo iye ayenera kupereka chidzudzulo mmalo mwa ofatsa a dziko lapansi. . . . Ndipo mbulu udzakhala pamodzi kwakanthaŵi ndi nkhosa yamphongo, ndipo nyalugwe adzagona pansi ndi mwana wa mbuzi, ndipo mwana wang’ombe ndi mwana wa mkango ndi choŵeta chonenepa pamodzi . . . Sizidzachititsa chivulazo chirichonse kapena kuchititsa kuipitsa kulikonse m’phiri langa lopatulika; chifukwa chakuti dziko lapansi lizadzadzadi ndi kudziŵa Yehova monga momwe madzi amadzadzira nyanja.” (Yesaya 11:4-9, NW) Ha ndimadalitso aakulu chotani nanga amene mbewu imeneyi inali kuzadzetsa!
18. Kodi ndichidziŵitso chowonjezereka chotani chonena za Mbewu chimene Danieli analemba?
18 M’zaka za zana lachisanu ndi chimodzi Nyengo Yathu Yofala ino isanakhale, Danieli analemba umboni wina wowonjezereka ponena za Mbewu. Iye ananeneratu za nthaŵi pamene wina wonga mwana wamunthu akawonekera kumwamba, nanena kuti “ndipo kwa iye kunapatsidwa ulamuliro ndi ulemu ndi ufumu, kuti mitundu ya anthu, timagulu ta anthu ndi a zinenero ayenera onse kumtumikira iye.” (Danieli 7:13, 14, NW) Chotero Mbewu inalinkudzayo ikalandira choloŵa cha ufumu wakumwamba, ndipo ulamuliro wake wachifumu ukafutukukira padziko lonse lapansi.
Chovutacho Chathetsedwa
19. Kodi ndimbali yotani, monga momwe yavumbulutsidwira ndi mngelo, imene Mariya anayenera kuchita m’Mbewu imene inali nkudza?
19 Kudziŵika kwa Mbewu potsirizira pake kunavumbulidwa pa kuyambika kwa Nyengo Yathu Yofala ino. M’chaka cha 2 B.C.E., mngelo anawonekera kwa namwali Wachiyuda wotchedwa Mariya, amene anali mbadwa ya Davide. Mngeloyo anamuuza kuti akabala mwana wapadera kwambiri ndipo anati: “Ameneyo adzakhala wamkulu kwambiri ndipo adzatchedwa Mwana wa Wam’mwambamwambayo; ndipo Yehova Mulungu adzampatsa iye mpando wachifumu wa Davide atate wake, ndipo adzalamulira monga mfumu panyumba yonse ya Yakobo kosatha, ndipo ufumu wake suudzatha.” (Luka 1:32, 33, NW) Chotero kuyembekezeredwa kwanthaŵi yaitali kwa “mbewu” potsirizira pake kunalinkufika kumapeto.
20. Kodi ndani amene ali Mbewu yolonjezedwayo, ndipo kodi ndiuthenga wotani umene iye analalikira mu Israyeli?
20 M’chaka cha 29 C.E. (chaka chonenedweratu kalekale pasadakhale ndi Danieli), Yesu anabatizidwa. Pamenepo mzimu woyera unatsikira pa iye, ndipo Mulungu anamvomereza iye kukhala Mwana wake. (Danieli 9:24-27; Mateyu 3:16, 17) Kwazaka zitatu ndi theka pambuyo pake, Yesu anachitira umboni kwa Ayuda, akumalengeza kuti: “Ufumu wakumwamba wasendera pafupi.” (Mateyu 4:17, NW) Mkati mwa nthaŵi imeneyo, iye anakwaniritsa maulosi ochuluka kwambiri ochokera m’Malemba Achihebri kwakuti panalibenso mpata wa chikaikiro ponena zakuti iye analidi Mbewu yolonjezedwayo.
21. Kodi nchiyani chimene Akristu oyambirira anamvetsa ponena za kudziŵika kwa Mbewu?
21 Akristu oyambirira anamvetsetsa zimenezi bwino lomwe. Paulo anafotokoza kwa Akristu m’Galatiya kuti: “Tsopano malonjezowo anaperekedwa kwa Abrahamu ndi kumbewu yake. Likunena, osati: ‘Ndi kwa mbewu zake,’ monga ngati akunena zambiri, koma ndi kunena imodzi: ‘Ndi kwa mbewu yako,’ imene iri Kristu.” (Agalatiya 3:16, NW) Chotero Yesu anali kudzakhala “Kalonga wa Mtendere” padziko lonse lapansi wonenedweratu ndi Yesaya. Pamene iye potsirizira pake akaloŵa Muufumu wake, chiweruzo cholungama ndi chilungamo zikakhazikitsidwa padziko lonse.
Nangano, Ndani Amene, Ali Mkaziyo?
22. Kodi ndani amene ali mkazi wotchulidwa muulosi wa Yehova mu Edene?
22 Ngati Yesu ali Mbewu, ndani amene ali mkazi amene anatchulidwa kalero mu Edene? Popeza kuti mphamvu imene inali kutseri kwa chinjoka inali cholengedwa cha mzimu, sitiyenera kudabwa kuti mkaziyo nayenso ayenera kukhala mzimu ndipo osati munthu. Mtumwi Paulo analankhula za “mkazi” wakumwamba pamene iye anati: “Koma Yerusalemu wakumwamba ali waufulu, ndipo iye ndiye amayi ŵathu.” (Agalatiya 4:26, NW) Malemba ena amasonyeza kuti “Yerusalemu wakumwamba” ameneyu wakhalapo kale kwa zaka zikwi zochuluka. Iye ndiye gulu lakumwamba la Yehova la zolengedwa zauzimu, kuchokera m’limene Yesu anatsika kudzakwaniritsa ntchito ya ‘mbewu ya mkazi.’ Kokha mtundu wa “mkazi” ameneyu ukanatha kupirira udani wa “chinjoka chakalecho” kwa zaka zikwizikwi.—Chivumbulutso 12:9; Yesaya 54:1, 13; 62:2-6.
23. Kodi nchifukwa ninji kuvumbulutsidwa kopita patsogolo kwa tanthauzo la ulosi wa Yehova wa pa Edene kuli kwapadera kwambiri?
23 Kupenda kwachidule kwa chochitika cha ulosi wamakedzana umenewo mu Genesis 3:15 kuli umboni wamphamvu wa kugwirizana kwakukulu kwa Baibulo. Kuli kwapadera kwenikweni kuti ulosi ungathe kumvedwa kokha pamene tisonkhanitsa pamodzi zochitika ndi zonenedwa zochokera m’zaka za zana la 20, la 11, la 8, ndi la 6 B.C.E. limodzi ndi zonena ndi zochitika zochokera m’zaka za zana loyamba la Nyengo Yathu ya Onse ino. Zimenezi sizingakhale zitangochitika mwamwaŵi. Payenera kukhala panali dzanja lotsogoza kutseri kwa zonsezi.—Yesaya 46:9, 10.
Tanthuzo Lake kwa Ife
24. Kodi kudziŵika kwa Mbewu kumatanthauzanji kwa ife?
24 Kodi zonsezi zikutanthauzanji kwa ife? Eya, Yesu ali wamkulu wa ‘mbewu ya mkaziyo.’ Ulosi wamakedzana umenewo mu Genesis 3:15 udaneneratu kuti chitende chake ‘chikazunzundidwa’ ndi Chinjoka, ndipo zimenezi zinachitika pamene Yesu anafa pamtengo wozunzirapo. Kuzunzundidwa sikumakhala kosatha. Chotero, chowonekera ngati chipambano cha Chinjoka mwamsanga chinachititsidwa kukhala kugonja pamene Yesu anaukitsidwa. (Monga momwe tinawonera m’Mutu 6, pali umboni wamphamvu wakuti zimenezi zinachitikadi.) Imfa ya Yesu inakhala maziko kaamba ka chipulumutso cha mtundu wa anthu owongoka mtima, chotero Mbewu inayamba kukhala dalitso, monga momwe Mulungu anali atalonjezera Abrahamu. Koma bwanji ponena za maulosi akuti Yesu akayenera kulamulira kuchokera Muufumu wakumwamba pachigawo chake chonse cholamulidwa cha padziko lapansi?
25, 26. Kodi ndi nkhani yotani imene inali yophatikizidwa ponena za udani umene uli pakati pa mbewu ya mkazi ndi Chinjoka, umene walongosoledwa m’Chivumbulutso?
25 M’masomphenya olongosola molosera m’Chivumbulutso mutu 12, chiyambi cha Ufumu umenewo chikuphiphiritsiridwa ndi kubadwa kwa mwana wamwamuna kumwamba. Mu Ufumu umenewu, Mbewu yolonjezedwayo ikutenga ulamuliro pansi pa dzina la ulemu lakuti Mikaeli, kutanthauza “Ndani Afanana ndi Mulungu?” Iye akusonyeza kuti palibe aliyense amene moyenera angathe kutsutsa ulamuliro wa Yehova, pamene iye athamangitsa “chinjoka choyambiriracho” kumwamba kwanthaŵi yonse. Timaŵerenga kuti: “Chotero chinaponyedwa pansi chinjoka chachikulucho, chinjoka chakalecho, iye wotchedwa Mdyerekezi ndi Satana, amene akusokeretsa dziko lonse lapansi lokhalidwa ndi anthu; anaponyeredwa pansi kudziko lapansi.”—Chivumbulutso 12:7-9, NW.
26 Chotulukapo ndicho mpumulo kaamba ka miyamba koma nsautso padziko lapansi. “Tsopano zafika chipulumutso ndi mphamvu ndi ufumu za Mulungu wathu ndi ulamuliro wa Kristu wake,” inadza motero mfuu yachipambano. Ndiponso timaŵerenga kuti: “Chifukwa chake kondwerani, miyamba inu ndi inu amene mumakhalamo! Tsoka dziko lapansi ndi nyanja, chifukwa Mdyerekezi watsikira kwa inu, wokhala nawo mkwiyo waukulu, podziŵa kuti ali ndi nyengo ya nthaŵi yaifupi.”—Chivumbulutso 12:10, 12, NW.
27. Kodi ndiliti pamene ulosi wonena za kuthamangitsidwa kwa Satana kuchokera kumwamba unakwaniritsidwa? Kodi tidziŵa bwanji?
27 Kodi tingathe kunena kuti ndiliti pamene ulosi umenewu ukakwaniritsidwa? Kwenikweni, limeneli linali funso limene linadzutsidwa ndi ophunzira pamene iwo anafunsa Yesu ponena za ‘chizindikiro cha kukhalapo kwake ndi cha mathedwe a dongosolo la zinthu’—monga momwe tafotokozera m’Mutu 10. (Mateyu 24:3) Monga momwe tinawonera, umboni ulipo wochuluka wakuti kukhalapo kwa Yesu m’mphamvu ya Ufumu wakumwamba kunayamba mu 1914. Kuyambira panthaŵi imeneyo, tawonadi “tsoka padziko lapansi”!
28, 29. Kodi ndimasinthidwe aakulu otani pa zochitika za padziko lapansi amene akali mtsogolo, ndipo kodi tikudziŵa motani kuti iwo adzachitika msanga?
28 Koma tawonani: Kuti mfuu yakumwamba imeneyo inalengeza kuti Satana ali ndi “nyengo yanthaŵi yaifupi” chabe. Chotero ulosi woyambirira umenewo m’Genesis 3:15 ukuyenda kumka kuchimake chosalakwika. Chinjoka, mbewu yake, mkazi, ndi mbewu yake zonsezo zadziŵikitsidwa. Mbewuyo ‘inazunzundidwa chitende,’ koma inachira. Posachedwapa, kuphwanyidwa kwa Satana (ndi mbewu yake) kudzayamba pansi pa Mfumu ya Mulungu imene iri tsopano linoyo pampando wachifumu, Kristu Yesu.
29 Kumeneku kudzaloŵetsamo masinthidwe aakulu pa zochitika za padziko lapansi. Limodzi ndi Satana, awo amene adzitsimikizira iwo eni kukhala mbewu yake adzachotsedwa. Monga momwe wamasalmo analoserera: “Katsala kanthaŵi, ndipo oipa sadzakhalakonso; ndipo iwe ndithudi udzayang’ana pamalo ake, ndipo iye adzakhala palibe.” (Salmo 37:10, NW) Ha ndikusintha kwakukulu chotani nanga mmene kumeneko kudzakhalira! Pamenepo, mawu owonjezerapo a wamasalmo adzakwaniritsidwa akuti: “Koma ofatsa iwo eniwo adzalandira dziko lapansi, ndipo ndithudi adzapeza chikondwerero chawo chochuluka m’kuchuluka kwa mtendere.”—Salmo 37:11, NW.
30. Kodi nchifukwa ninji okaikira amene amaika chikaikiro pa kuuziridwa kwa Baibulo ndipo ngakhale pakukhalapo kwa Mulungu iwo eniwo ali okaikitsa?
30 Mwanjira imeneyi, “Kalonga wa Mtendere” potsirizira pake azadzetsa mtendere kwa mtundu wa anthu. Iritu ndilo lonjezo la Baibulo monga momwe tinawonera pa Yesaya 9:6, 7. M’nyengo ino yokaikira, ambiri amapeza lonjezo loterolo kukhala lokaikiritsa. Koma kodi ndichinthu china chotani chimene munthu amapereka? Palibe! Kumbali ina, lonjezo limeneli lalongosoledwa momvekera bwino m’Baibulo, ndipo Baibulo ndilo Mawu osalephera a Mulungu. Kwenikweni ndiwo okaikirawo amene ali okaikiritsa. (Yesaya 55:8, 11) Iwo amanyalanyaza Mulungu, amene anauzira Baibulo ndi amene ali weniweni wamkulu koposa onse.
-