Kukonda Yehova Kumasonkhezera Kulambira Kowona
‘Pakuti ichi ndi chikondi cha Mulungu, kuti tisunge malamulo ake.’—1 YOHANE 5:3.
1, 2. Kodi tiyenera kutumikira Yehova ndi cholinga chotani?
GULU la alendo 80 ochokera ku Japani linalikuchezera Holo Yosonkhanira ya Mboni za Yehova ku California, U.S.A. Malo ozungulira okongola, kuphatikizapo munda wodzala ndi mbalame zotchedwa blue jay, njiŵa, ndi hummingbird, zinawapangitsa kumva oyandikira kwa Mlengi wawo Wamkulu, Yehova Mulungu. Posapita nthaŵi, wowachezetsa anazindikira kuti pafupifupi aliyense m’gululo anali muutumiki wanthaŵi zonse monga mpainiya. Chotero, pambuyo pake, anafunsa gululo funso limene limafunsidwa kaŵirikaŵiri kuti: “Kodi nchifukwa ninji m’Japani muli apainiya ambiri choncho?” Onse anakhala chete kwakamphindi. Ndiyeno mkazi wina wachichepere anayankha kuti: “Chifukwa chakuti timamkonda Yehova.”
2 Chikondi pa Yehova—ha, chimatikangalitsa chotani nanga muutumiki wake! Zowona, sialiyense amene angakhoze kuchita upainiya. Ndithudi, ochuluka a ofalitsa athu Aufumu oposa pa mamiliyoni anayi sanakhoze kupeza mpata wakuti atenge mwaŵi umenewu. Koma ambiri amene mikhalidwe imawalola amakalimira mwaŵi umenewu. Tonsefe tikhoza ‘kukhulupirira Yehova ndi kuchita chokoma,’ kusonyeza chikondi chathu mwakukhala ndi phande m’ntchito yakupanga ophunzira. (Salmo 37:3, 4) Ndipo olambira odzipereka a Yehova onse akhoza kukhala ndi mbali m’kusonkhezera mzimu waupainiya, kupereka chichirikizo chachikondi kwa amene akuchita upainiya.—Mateyu 24:14; 28:19.
3. Kodi nkusiyana kotani kumene kuyenera kuzindikiridwa pakati pa ambiri odzinenera kukhala Akristu ndi Mboni za Yehova?
3 Mosiyana ndi ochuluka odzinenera kukhala Akristu, amene amawona chipembedzo kungokhala mbali wamba ya miyoyo yawo, Mboni za Yehova zimasonyeza chikondi chachikulu kwa Mulungu chimene chimazisonkhezera kupitirizabe ‘kuthanga zafuna ufumu ndi chilungamo chake.’ Kuchita zimenezi kwafunikiritsa kudzimana, koma kudzimana kumeneko kwakhala koyenerera chotani nanga! (Mateyu 6:33; 16:24) Kwakhala kogwirizana ndi lamulo loyamba lalikulu, lonenedwa choyamba ndi Mose ndipo lobwerezedwa ndi Yesu Kristu lakuti: ‘[Yehova, NW], Mulungu wathu ndiye mmodzi; ndipo uzikonda [Yehova] Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi nzeru zako zonse, ndi mphamvu yako yonse.’—Marko 12:29, 30; Deuteronomo 6:4, 5.
4, 5. Kodi ndani amene ayenera kuwonedwa kukhala okhulupirika, ndipo ndimotani mmene kukhulupirika kungasonyezedwere?
4 Mmodzi wa ogwira ntchito pamalikulu a Mboni za Yehova posachedwapa anati kwa F. W. Franz, prezidenti wa Watch Tower Society wazaka zakubadwa 98 yemwe wathera zaka zoposa 70 muutumiki wanthaŵi zonse: “Mwakhala chitsanzo chabwino cha kukhulupirika, Mbale Franz.” Ndipo Mbale Franz anayankha kuti: “Inde! Uyenera kukhala wokhulupirika.” Yankholi limakwaniritsa zonse. M’mbali iriyonse ya ntchito ya Ufumu imene tingatumikiremo, tikhoza kukhala okhulupirika.—1 Akorinto 4:2; Agalatiya 3:9.
5 Zowona, ambiri angakonde kuchita zoposapo muutumiki wa Yehova, koma mathayo Amalemba kapena mavuto athanzi akhoza kuwalepheretsa mwanjira inayake. Komabe, awo osakhoza kuchita upainiya, sayenera kuwonedwa kukhala osakhulupirika kwambiri. Ena akhalabe okhulupirika pansi pa mikhalidwe yovuta kwenikweni ndipo kaŵirikaŵiri kwa zaka zambiri. Inde, iwo akhalabe okhulupirika! Asonyeza chikondi kwa Yehova ndipo atumikira mwakhama m’kuchirikiza ndi mtima wonse makonzedwe ake ateokratiki. Iwo apereka chisamaliro chachikulu ku ntchito ya apainiya ndipo apereka chilimbikitso kwa othekera kukhala apainiya, kaŵirikaŵiri ana awo enieniwo, kukalimirira upainiya monga ntchito yopambana zina zonse m’moyo wawo.—Yerekezerani ndi Deuteronomo 30:19, 20.
6, 7. Kodi ndimotani mmene chitsanzo choperekedwa pa 1 Samueli 30:16-25 chimagwirira ntchito lerolino?
6 Kugwirizana kwachikondi m’ntchito kwa anthu a Mulungu onse lerolino kungachitiridwe fanizo ndi nkhani ya pa 1 Samueli 30:16-25. M’nkhondo yomenyana ndi Amaleki, ‘Davide anawakantha kuyambira madzulo kufikira usiku wa maŵa wake’ ndipo anatenga zofunkha zambiri. Atabwerera kumsasa, ena a amuna ankhondo a Davide anapempha kuti chofunkha chirichonse chisapatsidwe kwa awo omwe sanaloŵe nawo pakati pakumenyana kwa nkhondoyo. Koma Davide anayankha kuti: ‘Ndani adzavomerezana nanu mlandu uwu? Pakuti monga gawo lake la iye wakumuka kunkhondoko, momwemo lidzakhala gawo lake la iye wakukhala ndi akatundu, adzagaŵana chimodzimodzi.’
7 Lamulo lamakhalidwe abwino lofananalo limagwiranso ntchito lerolino. Apainiya ali kutsogolo kwa nkhondo yathu yauzimu. Koma ena onse mumpingo amapereka chichirikizo chamtima wonse, ndi chokhulupirika. Ndipo chotulukapo chachikulu cha ntchito yawo yogwirizana ya mu 1991 chasonyezedwa pa tchati chosonyezedwacho.
Lipoti Losangalatsa
8. (a) Kodi lipoti ladziko lonse limasonyezanji ponena za chiwonkhetso cha ofalitsa ndi maola amene anawathera muutumiki wa Yehova? (b) Kodi ndimfundo zosangalatsa zotani zimene mukuwona m’maiko owonekera chatsopano palipotilo?
8 Inde, masamba anayi apitawo a magazini ano amasonyeza mmene zoyesayesa zogwirizana za olambira Yehova onse achangu zapangitsa chiwonjezeko chosangalatsa mu 1991. Pakhala chiŵerengero chapamwamba chatsopano cha ofalitsa Ufumu cha 4,278,820—chiwonjezeko cha 6.5 peresenti. Aŵa anapereka maola 951,870,021 (pafupifupi biliyoni imodzi!) ku utumiki. Ndipo onani kuyesayesa kwakukulu kumene abale athu anakuchita m’maiko amene kale munali chiletso koma tsopano akuwonekera pa lipoti la dziko lonse—Bulgaria, Cameroon, Chekosolovakiya, Ethiopia, Mozambique, Nicaragua, Rwanda, ndi U.S.S.R.
9, 10. (a) Kodi apainiya achita motani ndi chitokoso cha nthaŵi zovuta? (b) Kodi nchilimbikitso chotani chimene chikuperekedwa chakuloŵera utumiki waupainiya?
9 M’zaka zaposachedwapa mzimu waupainiya wafalikira padziko lonse. Ngakhale m’maiko kumene ufulu wakulambira wangoperekedwa posachedwapa, apainiya akuwonjezereka. Mavuto aakulu azachuma sakulepheretsa Mboni zolimba zimenezi kulambira Yehova ndi zonse zimene ziri nazo. (Yerekezerani ndi 2 Akorinto 11:23, 27.) Pa avareji yapamwezi, 14 peresenti ya olengeza Ufumu onse akhala akuchita upainiya. Chiŵerengero chapamwamba cha apainiya ndi 780,202, chimene chiri 18 peresenti yabwino koposa ya ofalitsa onse.
10 Powona chisangalalo chimene apainiya akukhala nacho, enanso akulimbikitsidwa kuyamba utumiki umenewu. Ngati simunachitebe upainiya, kodi chikondi chanu pa Yehova chidzakufulumizani kunena, monga momwe timaŵerengera pa Yesaya 6:8 kuti, “Ndine pano; munditumize ine”? Kapena kupyolera m’phunziro lanu lakhama Labaibulo, kodi Mawu a Mulungu angadzutse chikhumbo cha changu mumtima mwanu, kwakuti mungofunikira kutenga sitepe lina kuti muloŵe utumiki waupainiya? Ngakhale m’nthaŵi ya chiyeso, mawu a Yehova anamsonkhezera Yeremiya, kotero kuti sanaleke.—Yeremiya 20:9.
Utumiki Wachikondi kwa Anthu
11. Kodi ndimotani mmene ntchito ya maphunziro Abaibulo apanyumba yapitira patsogolo?
11 Chimodzi cha zinthu zapadera m’lipoti lachaka ndicho kuwonjezeka kwa chiŵerengero cha maphunziro Abaibulo apanyumba aulere, okwanira 3,947,261, ochititsidwa mokhazikika mwezi uliwonse padziko lonse. Aŵa ndimakonzedwe achikondi mwa amene Mboni za Yehova zimathandizira anthu okondwerera amene zimapeza m’ntchito yawo ya kunyumba ndi nyumba. Timakondwa kuchititsa maphunziro Abaibulo kwa anthu a mitundu yonse ndi mafuko osiyanasiyana, tikumagwira ntchito ndi khama limene mtumwi Paulo analisonyeza. Mosakaikira, ‘kuchitira umboni [kwake] Ayuda ndi Ahelene’ kunalira maola ambiri akuphunzitsa chowonadi. (Machitidwe 20:20, 21) Nzofanana ndi lerolino. Mboni za Yehova zimathandiza ‘anthu onse [kuti] apulumuke, nafike pozindikira chowonadi.’—1 Timoteo 2:4.
12-14. Kodi ndimalipoti osangalatsa otani amene akuchokera ku Yuropu?
12 Ngosangalatsa chotani nanga malipoti a ntchito ya maphunziro Abaibulo owonjezereka Kum’maŵa kwa Yuropu! Kwa zaka makumi ambiri abale athu kumeneko ankangokumana m’timagulu tating’ono, mwina ndi kope lojambulidwa limodzi lokha lokumbudzuka la Nsanja ya Olonda pa onse m’kaguluko. Koma tsopano Mabaibulo ndi mabuku ofotokoza Baibulo ambirimbiri akutumizidwa m’maikowo. Zimakumbutsa Nyimbo ya Solomo 2:4, King James Version yakuti: “Iye [Kristu Yesu] anandibweretsa ku nyumba [yauzimu] ya madyerero, ndipo mbendera yake pamwamba panga inali chikondi.” Pokhala ndi makope awo a magazini, ambiri akukhala okonzekeretsedwa bwino ‘kulunjika nawo bwino mawu a chowonadi.’—2 Timoteo 2:15.
13 Mpingo wa ofalitsa 103 mu St. Petersburg, Russia, posachedwapa anachitira lipoti maphunziro Abaibulo apanyumba oposa 300. Monga chotulukapo cha kuyesayesa kwa maphunziro Abaibulo kumeneku, Mboni zatsopano 53 zinabatizidwa m’miyezi isanu ndi itatu yokha. Oposa theka la mpingo akhala m’chowonadi kwa miyezi isanu ndi itatu kapena yocheperapo! Ndipo alibe akulu—mtumiki wotumikira mmodzi yekha ndiye akusamalira kupita patsogolo kwawo kwauzimu.
14 Wofalitsa Ufumu ku Estonia anafunsidwa ndi wophunzira Baibulo ngati angaloledwe kuitana ena a mabwenzi ake kubwera ku phunzirolo. Pamene Mboniyo inafika panyumbapo mlungu wotsatira, inapeza anthu oposa 50 atasonkhana! Ndithudi, panafunikira makonzedwe apadera akusamalira okondwerera onsewo.
15. Kodi tinganenenji pa chiŵerengero cha opezeka pa Chikhumbutso ndi cha obatizidwa?
15 Ambiri amene akuphunzira amalaŵa mayanjano Achikristu kwanthaŵi yoyamba mwakupezeka pa Chikumbutso cha imfa ya Yesu. Chaka chapitachi, opezekapo anaposa 10,000,000 kwanthaŵi yoyamba, 10,650,158 anasonkhana padziko lonse m’mipingo 66,207 kaamba ka chochitika chosangalatsa chimenechi. M’maiko ambiri a ku Latin-America, Afirika, ndi Kum’maŵa kwa Yuropu, panali opezekapo ochuluka kuŵirikiza katatu kapena kanayi kuposa pachiŵerengero cha ofalitsa Ufumu. Tsopano tiyenera kuyamba kukonzekera Chikumbutso cha chaka chino pa Lachisanu, April 17. Tikhulupirira kuti chiŵerengero chachikulu cha ophunzira Baibulo atsopano amene adzapezeka pa Chikumbutso adzapitabe patsogolo kulinga ku ubatizo. Ponena za maubatizo, mu 1991 tinawona kachiŵirinso oposa 300,000 akuphiphiritsa kudzipereka kwawo kwa Yehova Mulungu mwakumizidwa m’madzi.
Okonda Ufulu Waumulungu
16. Kodi ndimalipoti osangalatsa otani omwe akuchokera ku Misonkhano Yachigawo ya “Okonda Ufulu”?
16 Chinthu chapadera m’chaka chautumiki cha 1991 chakhala mpambo wa Misonkhano Yachigawo ya “Okonda Ufulu,” tsopano yomalizidwa ku Chigawo Chadziko Chakumpoto koma ikupitirizabe mpaka mu 1992 ku Chigawo Chadziko Chakum’mwera. Kwanthaŵi yoyamba, programu yonse yamsonkhano inaperekedwa m’maiko ochulukirapo a Kum’maŵa kwa Yuropu, kumene abale athu ali achimwemwe kugwiritsira ntchito ufulu wawo wopezedwa chatsopano kutamanda Yehova. Mu October 1991 chiŵerengero chonse cha opezekapo choperekedwa pa misonkhano 705 yoyambirira m’maiko 54 chinali 4,774,937.
17, 18. (a) Kodi ndiufulu wotani umene olambira a Yehova ali nawo ndi umene akuuyembekezera? (b) Kodi ndimotani mmene ufulu waumulungu umasiyanirana ndi ufulu wakudziko?
17 Yesu anauza ophunzira ake kuti: ‘Chowonadi chidzakumasulani.’ (Yohane 8:32) Lerolino, chowonadi cha Baibulo chamasula mamiliyoni ambiri ku ziphunzitso zatchalitchi za Chikristu Chadziko. Mamiliyoni ameneŵa aphunzira kuti makonzedwe a Yehova a nsembe yadipo ya Yesu adzatheketsa anthu ‘kumasulidwa ku ukapolo wa chivundi, ndi kuloŵa ufulu wa ulemerero wa ana a Mulungu.’ (Aroma 8:19-22) Ha, udzakhala ufulu wodabwitsa chotani nanga—kukhala ndi moyo kosatha padziko lapansi laparadaiso mkati mwa miyezo yoikidwa mwachikondi ndi Yehova!—Yesaya 25:6-8; yerekezerani ndi Machitidwe 17:24-26.
18 Ufulu umene Mboni za Yehova ziri nawo tsopano, ndi umene zikuyembekezera kusangalala nawo mokulira m’dongosolo lazinthu latsopano la Mulungu, ngwochokera kwa Mulungu wathu, Yehova. (2 Akorinto 3:17) Sumadalira pa gulu lirilonse la ndale zadziko kapena lopandukira boma. (Yakobo 1:17) Kuti pasakhale kulingalira molakwa pamfundo imeneyi, mabaji a msonkhano wa 1991 ovalidwa ndi Mboni za Yehova m’maiko ena a Kum’maŵa kwa Yuropu analembedwa kuti “Okonda Ufulu Waumulungu” mmalo mwakungoti “Okonda Ufulu.”
Chikondi Chachikulu pa Yehova
19. Kodi ndimotani mmene kuyandikirana ndi Yehova m’pemphero kungatichirikizire?
19 Chikondi chathu ndi chidaliro pa Yehova zidzatipangitsa kuyandikira kwa iye m’pemphero. Kuli kuyandikirana ndi Yehova kumeneku komwe kwathandiza abale athu kupirira mavuto ambiri ndi mazunzo. (Salmo 25:14, 15) Panthaŵi yake ya chiyeso chachikulu koposa, Yesu anayandikanabe ndi Atate wake kupyolera m’pemphero. (Luka 22:39-46) Kuyandikana ndi Yehova kwa m’pemphero koteroko kunachirikiza Stefano m’kusautsika kwake kwakukulu pa imfa yake yophedwera chikhulupiriro. Akuyang’ana kumwamba, apo ali pafupi kuphedwa mwakuponyedwa miyala, iye anati: ‘Tawonani, ndipenya m’mwamba motseguka, ndi Mwana wa munthu [Yesu] alikuimirira pa dzanja lamanja la Mulungu.’—Machitidwe 7:56.
20-22. Kodi ndimotani mmene chokumana nacho chimasonyezera kuti Mulungu amamva mapemphero?
20 Monga momwe zachitikira kaŵirikaŵiri kwa olambira a Yehova, Yehova amayankha mapemphero ogwirizana ndi chifuniro chake. Mwachitsanzo, m’dziko lina la mu Afirika kumene ntchito ya Mboni iri yoletsedwa, mpainiya wapadera ali paulendo wopita kumpoto pabasi anali ndi thumba lalikulu la mabuku a Ufumu ndi maimvulupu okawapereka. Kondakita yemwe ankakwezeka katundu anafunsa mbaleyo kuti: “Kodi thumbali liri nchiyani?” Mbaleyo ananena chinthu choyamba chimene chinabwera m’maganizo mwake nati: “Makalata.”
21 Ali mkati mwaulendo, basiyo inapitirira pa lodibuloko yanthaŵi zonse, ndipo apolisi anaitsatira naiimika, akuganizira kuti inanyamula katundu wozembetsa. Iwo analamula kuti okweramo onse atsike ndikuti katundu yense afufuzidwe. Iritu lidali vuto! Mbaleyo anayenda kamtunda pang’ono kuchoka pa gulu long’ung’udzalo, pansi gwade, napemphera kwa Yehova. Pamene anabwerera pa gululo, anapeza kuti katundu aliyense wa apaulendowo akutsegulidwa ndi kufufuzidwa mosamalitsa zedi. Pamene thumba la mbaleyo linati litsegulidwe, iye anapempha chithandizo kwa Yehova mwakachetechete.
22 “Kodi thumba ili nlayani, ndipo muli chiyani m’menemu?” anafuula tero wapolisi. Mbaleyo asanatsegule pakamwa, kondakita anayankha nati: “Ndimakalata ochokera ku positi ofesi ya ku———— ndipo akupita ku positi ofesi ya ku————.” “Chabwino,” anatero wapolisiyo. Ananyamula thumbalo nalipereka kwa kondakitayo. “Lisungeni pamalo abwino kwambiri paulendowu,” iye anatero. Mpainiya wapaderayo anagwadanso kuthokoza Wakumva pemphero.—Salmo 65:2; Miyambo 15:29.
23. Kodi nchiyani chimene Yehova wasonyeza, ndipo kodi nchifukwa ninji iye nthaŵi zina amalola chizunzo kuchitika kotheratu?
23 Komabe, izi sizikutanthauza kuti olambira a Yehova ali omasukiratu ku zochitika zatsoka. M’mikhalidwe ina, ponse paŵiri m’nthaŵi za Baibulo ndi lerolino, Yehova wasonyeza kuti akhoza kulanditsa anthu ake. Koma mogwirizana ndi njira yothetsera mkangano wa umphumphu, nthaŵi zina amalola chizunzo kuchitika kotheratu. (Yerekezerani ndi Mateyu 26:39.) Ndiponso, Yehova samangotetezera anthu ake ku ngozi, kulimbana kwachiŵeniŵeni, kapena upandu, ngakhale kuti kugwiritsira ntchito nzeru yothandiza yozikidwa m’Baibulo kungakhale kwaphindu. (Miyambo 22:3; Mlaliki 9:11) Komabe, tikhoza kukhala ndi chidaliro chakuti, kaya ngati tilanditsidwa ku mikhalidwe yovuta kapena ayi, kukhulupirika kwathu kudzafupidwa, ngakhale mwachiukiriro ngati kuli kofunika.—Mateyu 10:21, 22; 24:13.
24. Kodi ndimphatso zachikondi zotani zimene Yehova wapereka, ndipo kodi tiyenera kulabadira motani ku chikondi chake?
24 Ha, mphatso za Yehova zachikondi nzodabwitsa chotani nanga! Mphatso yake kwa anthu ya dziko lapansili ndi zonse zokhalapo iri chisonyezero chapadera cha chikondi chake. (Salmo 104:1, 13-16; 115:16) Ndipo mphatso yachifundo ya Mulungu ya Mwana wake, Yesu Kristu, yakuwombola anthu ku uchimo ndi imfa ndiyo mphatso yachikondi yoposa zonse zoperekedwapo. ‘Umo chidawoneka chikondi cha Mulungu mwa ife, kuti Mulungu anamtuma Mwana wake wobadwa yekha, aloŵe m’dziko lapansi, kuti tikhale ndi moyo mwa iye. Umo muli chikondi, sikuti ife tinakonda Mulungu, koma kuti iye anatikonda ife, ndipo anatuma Mwana wake akhale chiwombolo chifukwa cha machimo athu.’ (1 Yohane 4:9, 10) Kuti tilabadire chikondi chimenecho, tiyenera kukhala okhutiritsidwa kuti ‘ngakhale imfa, ngakhale moyo, ngakhale angelo, ngakhale maufumu, ngakhale zinthu ziripo, ngakhale zinthu zirinkudza, ngakhale zimphamvu, ngakhale utali, ngakhale kuya, ngakhale cholengedwa china chirichonse, sichingadzakhoze kutisiyanitsa ife ndi chikondi cha Mulungu, chimene chiri mwa Kristu Yesu Ambuye wathu.’—Aroma 8:38, 39.
Kupenda Nkhani Ino
◻ Kodi kukhulupirika kumatanthauzanji?
◻ Kodi ndim’mbali ziti za ntchito mmene tingasonyeze chikondi chathu pa Yehova?
◻ Kodi ndimbali ziti za lipoti la chaka chautumiki zimene zinakusangalatsani koposa?
◻ Kodi tingasonyeze motani chiyamikiro kaamba ka mphatso zachikondi za Yehova?
[Bokosi patsamba 15]
KODI NCHIFUKWA NINJI KULI APAINIYA AMBIRI CHONCHO?
Zikusimbidwa kuti, kwa zaka 2,600 Ajapani anali olambira okhulupirika a olamulira awo. M’nkhondo za m’zaka za zana lino la 20 mokha, Ajapani omenya nkhondo oposa mamiliyoni atatu anapereka nsembe miyoyo yawo, popeza kuti kwa iwo kunalibe ulemu umene unaposa kufera wolamulira wawo yemwe adali mulungu kwa iwo. Koma asirikali a Chishinto ndi Chibuda analephera m’Nkhondo Yadziko ya II, ndipo kuchokera pamenepo wolamulira wawo anaukana umulungu wake. Kodi nchiyani chimene chikaloŵa m’malo chikhulupiriro chachipembedzo chimenechi? Mosangalatsa, maphunziro Abaibulo apanyumba ochititsidwa ndi amishonale a Mboni za Yehova ndipo pambuyo pake ndi Mboni zakumaloko anathandiza ambiri kupeza Mulungu wowona, Yehova, ndi kupereka miyoyo yawo kwa iye. Kudzipereka kumeneku kumatanthauza zambiri kwa Mboni Zachijapani zimenezo. Ngati m’nthaŵi zakale iwo anapereka miyoyo yawo kwa wolamulira-mulungu, ndichangu chachikulu motani nanga chimene tsopano akupereka nacho nyonga zawo monga apainiya m’kulambiridwa kwa Mulungu wamoyo ndi Mlengi wa chilengedwe chonse—Mfumu Ambuye Yehova!
[Tchati pamasamba 10-13]
LIPOTI LA CHAKA CHAUTUMIKI CHA 1991 LA MBONI ZA YEHOVA DZIKO LONSE
(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)
[Chithunzi patsamba 16]
Okonda ufulu waumulungu—olambira a Yehova pamsonkhano m’Prague, August 9-11, 1991