Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 5/96 tsamba 3
  • Kutamanda Yehova m’Kuimba Kogwirizana!

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kutamanda Yehova m’Kuimba Kogwirizana!
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—1996
Utumiki Wathu wa Ufumu—1996
km 5/96 tsamba 3

Kutamanda Yehova m’Kuimba Kogwirizana!

Kuimba kuli mbali ya mwambo wa m’Afirika. M’mudzi weniweni wa m’Afirika, sikumakhala kwachilendo kuona akazi akulima molingana ndi kamvekedwe ka nyimbo zamwambo, achichepere akung’ung’udza nyimbo zawo zapamtima pamene akukama ng’ombe, ndipo amuna akuimba nyimbo mobwerezabwereza ngati kuti akufuna kulimbikitsa ng’ombe zawo kukoka katundu wawo wolemera. M’mudzi mumakhala pafupifupi nyimbo ya chochitika chilichonse. Koposa zimenezo, kuimba kuli mbali ya kulambira kwathu. Chifukwa cha zimenezi, Sosaite imagogomezera kwambiri kuimba nyimbo za Ufumu. Ngakhale zili choncho, kwaonedwa kuti m’mipingo ina, nyimbo zolinganizidwira programu zasinthidwa. Nyimbo pamisonkhano yathu zimasankhidwa mosamala kuti zigwirizane ndi programu. Nyimbo za Phunziro la Nsanja ya Olonda, Msonkhano Wautumiki, ndi Sukulu Yautumiki Wateokratiki zimasankhidwa mosamala. Ndiyeno pamene akulu akupereka nkhani za Baibulo, amasankha nyimbo imene imayenerera mutu wa nkhani yawo.

Kuti tithandizidwe kusonyeza chiyamikiro cha nyimbo zabwino pamisonkhano yathu, tikulimbikitsidwa kuphunzira pasadakhale nyimbo zimene zalinganizidwa, kotero kuti mwaŵi wathu ndi thayo lathu la kuziimba tilitenge mosamala. Monga mmene timadziŵira za mkupiti wa utumiki wakumunda miyezi itatu pasadakhale kotero kuti tiode ndi kulandira mabuku ofunika panthaŵi yabwino, timauzidwanso za nyimbo zenizeni zogwiritsira ntchito pamisonkhano kukali nthaŵi yabwino.

Pulezidenti wakale wa Watch Tower Society, Nathan H. Knorr, pambuyo pa kupezeka pamsonkhano wa Mboni za Yehova mu Zambia, anafotokoza bwino za mazana a mawu osonkhezera okwezedwa m’kuimba kogwirizana. Iye anati: ‘Kayimbidweko kanatsitsimula moyo ndi kudzetsa misozi—kanali kabwino koposa. Palibe ziŵiya zoimbira zomwe zinafunikira, ndipo komwe kunaonekera ngati kuimba mbali zosiyanasiyana kovuta kunachitidwa mosavuta koposa. Kugwirizanako kunali kokongola.’ Monga mpingo ndi aliyense payekha, tisakhale ndi chizoloŵezi chomasintha nyimbo zimene Sosaite yasankha. Chonde gwiritsirani ntchito matepi a Sosaite kuti muphunzire nyimbo zimenezi. Oyang’anira madera adzachita bwino kufufuza ndi kuona kuti makonzedwe ameneŵa apambana, kuti tonsefe titamande Yehova m’kuimba kogwirizana!

Posachedwapa tidzakhala pa Misonkhano Yachigawo ya “Amithenga a Mtendere Waumulungu.” Kuti itithandize kukonzekera ndi kutengamo mbali mokwanira m’kuimba, Sosaite yasankha nyimbo zotsatirazi zodzagwiritsira ntchito: 8, 15, 16, 26, 38, 42, 59, 111, 123, 127, 159, 170, 174, 187, 207, 211, 215 ndi 212. Akulu akulimbikitsidwa kupanga makonzedwe enieni akuti mpingo uyambe kuyeseza nyimbo zimenezi. Monga mmene tikuyamikirira makonzedwe a Yehova a msonkhano wa chaka chino, tidzaimbanso zitamando kwa iye ndi mtima wonse.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena