Gwiritsirani Ntchito Mwaŵi Wapadera Umenewu!
PETER anali atafika patali ndi maphunziro ake a zamankhwala pamene uthenga wa Baibulo wa chipulumutso unamkopa. Pamene anamaliza maphunziro ake nayamba kugwira ntchito monga dokotala m’chipatala, omuyang’anira ake mosalekeza anali kumlimbikitsa kuti akhale dokotala wa opaleshoni ya minyewa. Unali mwaŵi umene madokotala ambiri atsopano akanaugwiritsira ntchito mosazengereza.
Komabe, Petera anasankha kuukana mwaŵi umenewu. Chifukwa ninji? Kodi anangosoŵa chikhumbo ndi chisonkhezero chofunikira? Ayi, popeza Peter anaulingalirapo mosamala mwaŵiwo. Atakhala Mboni ya Yehova yodzipatulira ndi yobatizidwa, anafuna kuthera nthaŵi yaikulu yomwe akanatha m’mbali zosiyanasiyana za utumiki wachikristu. Atangokhala dokotala wa opaleshoni ya minyewa, analingalira motero, ntchito yake ingatenge nthaŵi ndi nyonga yake yochuluka. Kodi anapusa pokana mwaŵi wapadera umenewu, kapena kodi anali wanzeru?
Kwa ena, chosankha cha Peter mwinamwake chinaoneka ngati chopusa. Komabe, iye analingalira za malemba a m’Baibulo monga Aefeso 5:15, 16. Pamenepo mtumwi Paulo analimbikitsa Akristu anzake kuti: “Penyani bwino umo muyendera, si monga opanda nzeru, koma monga anzeru; akuchita machaŵi, popeza masiku ali oipa.”
Chonde onani liwulo “machaŵi.” Latembenuzidwa kuchokera ku liwu lachigiriki logwiritsiridwa ntchito m’Baibulo kaŵirikaŵiri ponena za nthaŵi kapena nyengo yosonyezedwa ndi zinthu zinazake kapena yoyenerera ntchito yakutiyakuti. Panopa Paulo anagogomezera kuti Akristu ayenera kukhala ndi nthaŵi ya kuchita zinthu zofunika. Indedi, ayenera ‘kutsimikizira zinthu zofunika kwambiri.’ (Afilipi 1:10, NW) Ili nkhani ya kuika zinthu zofunika patsogolo.
Chotero, tsono, kodi chifuno cha Mulungu kaamba ka nthaŵi yathu nchiyani? Kodi chifuniro cha Mulungu kaamba ka awo amene amamkonda nchiyani? Maulosi a Baibulo amasonyeza bwino lomwe kuti nthaŵi yathu ili “nthaŵi ya chimaliziro,” kapena “masiku otsiriza.” (Danieli 12:4; 2 Timoteo 3:1) Kristu Yesu motsimikiza anatchula zimene zidzakhala zofunika kwambiri m’tsiku lathu. Ananena molunjika kuti mapeto a dongosolo loipali la zinthu asanafike, “uthenga uwu wabwino waufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi, ukhale mboni kwa anthu a mitundu yonse.” Ndi pokhapo pamene mapeto adzafika.—Mateyu 24:3, 14.
Chotero, tiyenera kugwiritsira ntchito mwaŵi uliwonse kulalikira uthenga wabwino wa Ufumu ndi kupanga ophunzira. (Mateyu 28:19, 20) Popeza kuti ntchitozi sizidzabwerezedwa, umenewu ndiwo mwaŵi wotsirizira wakuti tipereke zathu zonse pantchito yopulumutsa miyoyo imeneyi. “Tsopano ndiyo nyengo yabwino yolandiridwa.” Inde, “tsopano ndilo tsiku la chipulumutso.”—2 Akorinto 6:2.
Kupanga Chosankha Chanzeru
Peter—mnyamata wotchulidwa pachiyambi—analingalira mosamala za chosankha chake ndi kuchilinganiza ndi zosankha zina. Anazindikira kuti sikungakhale kulakwa kuti iye aphunzire ndi cholinga cha kukhala dokotala wa opaleshoni ya minyewa. Koma kodi nchiyani chimene chinali chofunika koposa kwa iye? Chinali kutengamo mbali kwake mu utumiki wachikristu, polingalira za kufulumira kwa ntchitoyi. Panthaŵi imodzimodziyo, anali ndi mathayo oti akwaniritse. Anali wokwatira ndipo anayenera kusamalira mkazi wake, amene akuchita ntchito yolalikira ya nthaŵi zonse. (1 Timoteo 5:8) Peter anayeneranso kubweza ngongole zimene anatenga kaamba ka maphunziro ake. Chotero, kodi anasankha kuchita chiyani?
Peter anasankha kukhala katswiri wa radiology ndi kupima ndi ultrasound. Imeneyi ndi ntchito imene akanaigwira m’maola ake patsiku. Akanalandiranso maphunziro ake mkati mwa maola a ntchito a nthaŵi zonse. Zoona, ena angaone zimenezi kukhala malo apansi, koma ikanampatsa nthaŵi yochuluka yoti aipereke pa ntchito zauzimu.
Lingaliro linanso linasonkhezera Peter kupanga chosankha chimenecho. Pamene kuli kwakuti sanali kuweruza ena amene mwinamwake anasankha mosiyana, anadziŵa kuti kukhala wotanganitsidwa kwambiri ndi zinthu zakudziko kuli kwangozi kwa Mkristu. Kungamchititse kunyalanyaza mathayo auzimu. Zimenezi zikusonyezedwa ndi chitsanzo china chimene chinakhudza ntchito.
Mlaliki winawake wa Ufumu wa nthaŵi zonse anali wolemba zithunzi wophunzitsidwa. Anali kukwanitsa kudzipezera ndalama mwa kugulitsa zolemba zake. Pamene anali kupereka nthaŵi yake yochuluka ku utumiki wofunika kwambiriwo wachikristu, anali kudzipezera zofunika mosavuta mwanjira imeneyo. Komabe, chikhumbo cha kukulitsa luso lake la kulemba zithunzi chinayamba kukula. Anadziloŵetsa kwambiri m’kulemba zithunzi ndi kugwirizana kwambiri ndi amisiri anzake, nasiya utumiki wa nthaŵi zonse, ndipo m’kupita kwa nthaŵi anakhala wofookeratu pa ntchito ya kulalikira Ufumu. M’kupita kwa nthaŵi, analoŵa m’khalidwe lotsutsana ndi Malemba, zimene zinamchititsa kuti asakhalenso mbali ya mpingo wachikristu.—1 Akorinto 5:11-13.
Nthaŵi Yathu Njapadera
Monga awo amene akutumikira Yehova tsopano, tikufunadi kukhalabe okhulupirika kwa iye. Tikudziŵa kuti tikukhala m’nthaŵi yapadera koposa m’mbiri ya munthu. Kuti tipitirize kutumikira Mulungu ndi kulimbana ndi mikhalidwe ya masiku ano mwachipambano, tingafunikire kusintha zinthu zambiri. Tingayerekezere zimenezi ndi nthaŵi ya mlimi ya kututa. Imeneyi ndi nthaŵi ya ntchito yapadera, pamene antchito a m’munda amayembekezeredwa kukangalika kuposa masiku onse ndi kugwira ntchito maola ochulukirapo masiku ambiri. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti mbewuzo ziyenera kututidwa m’nthaŵi yoikika.
Dongosolo la zinthu loipa lilipoli langotsala ndi kanthaŵi kakang’ono kwambiri. Tsopano kuposa ndi kale lonse, Mkristu woona afunikira kukangalika potsatira chitsanzo cha Yesu ndi kuyenda m’mapazi ake. Moyo wake wa padziko lapansi unasonyeza moonekeratu chimene chinali chofunika kwambiri kwa iye. Anati: “Tiyenera kugwira ntchito za iye wondituma ine, pokhala pali msana; ukudza usiku pamene palibe munthu angakhoze kugwira ntchito.” (Yohane 9:4) Mwa kunena kuti unali kudza usiku, Yesu anali kunena za nthaŵi ya kuyesedwa kwake, kupachikidwa, ndi imfa, pamene utumiki wake wa padziko lapansi udzatha ndipo sadzakhozanso kuchita ntchito ya Atate wake wakumwamba.
Zoonadi, mkati mwa utumiki wake wa zaka zitatu ndi theka, Yesu anathera ina ya nthaŵi yake akumachita zozizwitsa ndi kuchiritsa odwala. Komabe, anagwiritsira ntchito nthaŵi yake yochuluka pa kulalikira uthenga wa Ufumu ndi “kulalikira amsinga mamasulidwe” ku chipembedzo chonyenga. (Luka 4:18; Mateyu 4:17) Yesu anachita utumiki wake mwakhama ndipo anapatulanso nthaŵi ya kuphunzitsa ophunzira ake kotero kuti amange pamaziko amene iye anayala ndi kupitiriza ntchito ya kulalikira mwachipambano. Yesu anagwiritsira ntchito mwaŵi uliwonse kuchirikiza zinthu za Ufumu ndipo anafuna kuti ophunzira ake achite chimodzimodzi.—Mateyu 5:14-16; Yohane 8:12.
Monga Yesu, ife amene tili omtsatira ake amakono tiyenera kuona mkhalidwe wa anthu monga momwe Yehova Mulungu amauonera. Nthaŵi ya dongosolo lino la zinthu ili kutha, ndipo mwachifundo Mulungu akufuna kuti onse akhale ndi mwaŵi wa kupeza chipulumutso. (2 Petro 3:9) Chotero, kodi sikungakhale kwanzeru kuika ntchito zina zonse pambuyo pa kuchita chifuniro cha Yehova? (Mateyu 6:25-33) Makamaka m’nthaŵi yapadera imeneyi monga ino, chinthu chimene mwachibadwa chingaoneke kukhala chofunika chingakhaledi chosafunika kwenikweni m’moyo wathu monga Akristu.
Kodi aliyense wa ife adzachita chisoni chifukwa cha kuika chifuniro cha Mulungu patsogolo m’moyo wathu? Ndithudi ayi, popeza njira yachikristu ya kudzimana njofupadi. Mwachitsanzo, Yesu anauza ophunzira ake kuti: “Ndinena ndi inu ndithu, Palibe munthu anasiya nyumba, kapena abale, kapena alongo, kapena amayi, kapena atate, kapena ana, kapena minda, chifukwa cha ine, ndi chifukwa cha uthenga wabwinowo, amene sadzalandira makumi khumi tsopano nthaŵi ino, nyumba, ndi abale, ndi alongo, ndi amayi, ndi ana, ndi minda, pamodzi ndi mazunzo; ndipo nthaŵi ilinkudza, moyo wosatha.”—Marko 10:29, 30.
Palibe amene angaike mtengo wandalama pa mfupo zimene zili ndi awo amene amagwiritsira ntchito nthaŵi yawo kutamanda Yehova ndi kulengeza uthenga wa Ufumu. Iwo ali ndi madalitso ambirimbiri! Ameneŵa amaphatikizapo mabwenzi oona, chikhutiro cha kuchita chifuniro cha Mulungu, chiyanjo cha Mulungu, ndi chiyembekezo cha moyo wosatha. (Chivumbulutso 21:3, 4) Ndipo ndi dalitso lalikulu chotani nanga kuthandiza anthu mwauzimu ndi kudzetsa ulemu pa dzina loyera la Yehova monga Mboni zake! Mosakayikira, ‘kuchita machaŵi’ kulidi njira yanzeru ndi yofupa. Tsopano ndiyo nthaŵi ya kugaŵanamo kulengeza uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu kuposa ndi kale lonse. Kodi mudzagwiritsira ntchito mwaŵi wapadera umenewu ndi kusautaya?
[Mawu a M’munsi]
a Dzina lobwerekera.