‘Valani Umunthu Watsopano’
1 Akristu amayamikira kuti anazindikira choonadi! Taphunzira mmene tiyenera kukhalira ndi moyo kuti tipeŵe zimene amachita anthu amene ali m’dziko. Pokhala ‘anafulatira moyo umene Mulungu amapereka,’ iwo “nzeru zawo zili mumdima.” (Aef. 4:18, Chipangano Chatsopano Cholembedwa m’Chicheŵa Chamakono) Taphunzitsidwa kukonzanso maganizo athu kuti tisiye kuganiza kwa anthu adziko mwa kuvula umunthu wakale ndi kuvala umunthu watsopano.—Aef. 4:22-24.
2 Umunthu wakale umawononga makhalidwe abwino mosalekeza, zimene zimachititsa anthu kukhala oipa ndi kufa. Motero, tikupempha onse amene adzamvetsera uthenga wa Ufumu kuti asiye mkwiyo, kupsa mtima, dumbo, mwano ndi kulankhula zonyansa. Amene akufuna kukhala ndi chiyanjo cha Mulungu ayenera kuvula umunthu wakale wonse motsimikizadi—mofanana ndi mmene angavulire chovala chakuda.—Akol. 3:8, 9.
3 Mphamvu Yatsopano Yosonkhezera Maganizo: Kuvala umunthu watsopano kumaphatikizapo kusandulika atsopano m’mphamvu yosonkhezera maganizo athu. (Aef. 4:23, NW) Kodi munthu amachititsa mphamvu imeneyo, kapena m’khalidwe wa maganizo, kukhala yatsopano motani kotero kuti azilingalira m’njira yoyenera? Zimenezi zimachitika mwa kuphunzira Mawu a Mulungu mokhazikika ndi mwakhama, ndi kumasinkhasinkha pa tanthauzo la zimene akuphunzirazo. Ndiyeno, amayamba kukhala ndi kaganiziridwe katsopano, ndipo amaona zinthu monga momwe Mulungu ndi Kristu amazionera. Moyo wa munthu umasintha pamene iye avala mikhalidwe yambiri yonga ya Kristu, kuphatikizapo chifundo, kukoma mtima, kudzichepetsa, kufatsa, kuleza mtima, ndi chikondi.—Akol. 3:10, 12-14.
4 Mwa kuvala umunthu watsopano, timadzisiyanitsa ndi dziko. Moyo wathu umatipangitsa kukhala osiyana ndi ena. Timalankhula choonadi ndipo timagwiritsa ntchito mawu abwino kuti timangirire ena. Timateteza mkwiyo wathu ndipo m’malo mokhala aukali, ozaza, olankhula zonyansa, ndi a dumbo, timakhala ndi mikhalidwe yaumulungu yolungama. Timachita zambiri kuposa zimene timafunika kuchita pokhululukira ena. Zonsezi zimachitikadi mochokera pansi pa mtima.—Aef. 4:25-32.
5 Musavule umunthu watsopano. Sitingatumikire Yehova movomerezeka ngati tilibe umunthu umenewu. Lolani kuti uthandize kukopera anthu m’choonadi, ndipo uloleni kuti ulemekeze Yehova, Mlengi wa umunthu wathu watsopano wokometsetsa.—Aef. 4:24.