Misonkhano Yautumiki ya February
Mlungu Woyambira February 1
Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Zilengezo zosankhidwa mu Utumiki Wathu wa Ufumu. Kumbutsani onse kuti apereke malipoti a utumiki wakumunda a January.
Mph. 17: “Gaŵirani Buku la Chimwemwe cha Banja kwa Anthu a Misinkhu Yonse.” Mkulu akambirane nkhaniyo ndi ofalitsa okhoza aŵiri kapena atatu. Sumikani malingaliro pa kuthandiza ena kuzindikira kuti chinsinsi cha chimwemwe cha banja chagona pa kutsatira uphungu wa Baibulo. (Onani buku la Chimwemwe cha Banja, masamba 9-12.) Chitirani chitsanzo umodzi mwa maulaliki amene aperekedwawo. Sonyezani mmene tingatsegulire mpata wa ulendo wobwereza.
Mph. 18: “Valani Umunthu Watsopano.” Nkhani, longosolani Aefeso 4:20-24. (Onani Nsanja ya Olonda ya March 1, 1993, masamba 14-18, ndime 4-17.) Fotokozani mmene timavulira umunthu wakale ndi kuvala watsopano.
Nyimbo Na. 4 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira February 8
Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Lipoti la maakaunti.
Mph. 15: Zosoŵa za pampingo.
Mph. 20: “Chitirani Umboni Choonadi.” Kambiranani nkhaniyo mwa mafunso ndi mayankho. Funsani ofalitsa amene akonza ndandanda zawo kotero kuti achite ntchito ya upainiya wothandiza.
Nyimbo Na. 173 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira February 15
Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Mbiri Yateokalase.
Mph. 18: Kodi N’chiyani Chimene Timapindula mwa Kulembetsa Sukulu ya Utumiki Wateokalase? Woyang’anira sukulu akambirane ndi omvetsera. Kuphunzira kulankhula pagulu si cholinga chokhacho cha sukuluyi. Timapindulanso m’njira zina. (Onani Buku Lolangiza la Sukulu, masamba 12-13.) Timaphunzira mmene tingalankhulirane bwino ndi anthu ena. Timaphunzira kulankhula momveka bwino, mosadodoma, ndi mwachidaliro. Timayankha mwaluso anthu akamatifunsa zokhudza zikhulupiriro zathu, ndiponso timawalongosolera bwino kuti timasankha zochita malinga ndi mmene Baibulo limatitsogozera. Chidziŵitso chathu cha Baibulo chimawonjezeka, kutithandiza kukhala ogwira mtima kwambiri pochita umboni kwa ena. Timaphunzira kuvomereza zophophonya zathu ndi kulandira uphungu, zimene zimatipangitsa kuchita zinthu mwamtendere ndi anthu ena. Maphunziro amene sukuluyi imapereka onse pamodzi amatithandiza kukhalabe atumiki a Mulungu “okwanira.”—2 Akor. 3:5, 6.
Mph. 17: “Mmene Banja Limachitira Zinthu Kuti Onse Azitengamo Mbali Mokwanira—Pa Phunziro la Baibulo.” Banja likambirane. Afotokoze mmene akugwiritsira ntchito malingaliro a kuŵerenga ndi kuphunzira Baibulo kwa banja lonse omwe ali mu Nsanja ya Olonda ya May 15, 1996, masamba 14-15, ndiponso ya October 15, 1992, masamba 16-17.
Nyimbo Na. 57 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira February 22
Mph. 10: Zilengezo za pampingo.
Mph. 15: Bokosi la Mafunso. Phatikizanipo bokosi lakuti: “Mumtsimikizire Ameneyo Chikondi Chanu” kuchokera mu Nsanja ya Olonda ya October 1, 1998, tsamba 17.
Mph. 20: Mmene Mungapezere Chimwemwe Popanga Ophunzira. Nkhani yochokera mu Nsanja ya Olonda ya February 15, 1996, masamba 19-22.
Nyimbo Na. 91 ndi pemphero lomaliza.