Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 3/99 tsamba 3-6
  • Pologalamu Yatsopano Yomanga Nyumba za Ufumu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Pologalamu Yatsopano Yomanga Nyumba za Ufumu
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—1999
  • Timitu
  • THUMBA LA SOSAITE LA NDALAMA ZA NYUMBA ZA UFUMU —MMENE LIGWIRIRE NTCHITO
Utumiki Wathu wa Ufumu—1999
km 3/99 tsamba 3-6

Pologalamu Yatsopano Yomanga Nyumba za Ufumu

1 Mosakayikira Yehova akukwaniritsa lonjezo lake lophunzitsa am’nyumba yake ndi kuwatsogolera m’njira zake. (Yes. 54:13) Kuyambira m’nthaŵi zakale iye wakhala akupanga makonzedwe abwino akulambira mogwirizana komwe kumaphatikizapo kuwapatsa malangizo ofunika. (Deut. 31:12, 13; Neh. 8:1-8; Sal. 122:1) Zimenezi zakhala zopindulitsa kwambiri kwa anthu ake okhulupirika. Mwa kumvera mosamalitsa uphungu wake, akhala osiyana ndi dziko ndipo akhala paunansi wathithithi ndi olambira anzawo. (Eks. 34:11-16; 2 Akor. 6:14-18) Makamaka m’masiku omaliza ano tikulimbikitsidwa kusonkhana nthaŵi zonse, osati kokha kukaphunzitsidwa ndi Yehova komanso kukalimbikitsana ndi kufulumizana wina ndi mnzake ku chikondano ndi ntchito zabwino.—Aroma 1:11, 12; Aheb. 10:23-25.

2 Kuyambira m’zaka za zana loyamba mpaka lerolino Akristu polambira akhala akusonkhana m’nyumba zawo ndi m’mabwalo. (Mac. 2:42, 46; 12:12) Koma makamaka kuyambira 1935, pamene analengeza kuti malo olambirira omwe anali kumanga ku Hawaii adzatchedwa Nyumba ya Ufumu, kulikonse mipingo ya Mboni za Yehova yayesetsa kukhala ndi malo awo olambiriramo ndipo amadziŵika ndi dzina lomweli. M’malo mwake, Nyumba za Ufumu zikupezeka padziko lonse, ndipo chaka chilichonse nyumba zambiri zikumangidwa kapena kuzisandutsa malo ampingo osonkhanirapo.

3 M’dera lililonse nyumba yofunika kwambiri kwa Mboni za Yehova ndi Nyumba ya Ufumu. Itha kukhala yokongola m’kamangidwe, koma ngakhale itakhala yosakongola kwenikweni m’maonekedwe ake akunja, m’deralo imadziŵika kwambiri monga pachimake pa kulambira koona ndi ntchito zateokalase. Imapereka umboni wakuti m’deralo uthenga wabwino wa Ufumu ukulalikidwa. Ndi malo amene amatsitsimuladi mwauzimu ndi kupereka malangizo kwa onse amene amazindikira kusoŵa kwawo kwauzimu.—Mat. 5:3.

4 Kuwonjezeka kwa Anthu Kwawonjezeranso Kufunika kwa Nyumba za Ufumu: Malipoti akumunda akuonetsa kuti Yehova akupitirizabe ‘kufulumiza’ ntchito yosonkhanitsa pamene mapeto a dongosolo la zinthu lino akufulumira kudza. Zachitikadi monga momwe ananenera mwa mneneri Yesaya kuti “wamng’ono adzasanduka chikwi, ndi wochepa adzasanduka mtundu wamphamvu.” (Yes. 60:22) Chiŵerengero chachikulu chimenechi chayambitsa mipingo yatsopano mazanamazana, ndipo zimenezi zikutanthauza kuti mazanamazana a Nyumba za Ufumu akufunika. Koma kwakhala kovuta kwa mipingo yathu kumanga Nyumba za Ufumu mogwirizana ndi chiwonjezeko chimenechi. M’kupita kwa nthaŵi vutoli likukula kwambiri pamene ntchito yosonkhanitsa ikuwonjezekabe.

5 M’kope lino la Utumiki Wathu wa Ufumu, tili okondwa kulengeza za makonzedwe atsopano ofulumiza kumanga Nyumba za Ufumu kapena kugula malo ena owonjezereka m’Malawi, komanso kuthandiza mipingo yomwe ikufuna kukulitsa kapena kukonza Nyumba za Ufumu zomwe zilipo kale. Nazi zina mwa njira zomwe zingathandize abale onse kulikonse komwe ali kumvetsa bwino mmene makonzedwe atsopano ameneŵa agwirire ntchito ndi zimene aliyense angachite posonyeza umodzi wathu wachikristu.

6 Kufunika Kwake: Buku la Olinganizidwa Kutsiriza Uminisitala Wathu limati patsamba 61: “Nyumba ya Ufumu, monga malo olambirira, siyenera kukhala nyumba yodabwitsa yolinganizidwira kuchititsa kaso ena, ayi. Pamene kuli kwakuti kumangidwa kwake kungasiyanesiyane malo ndi malo, chifuno chake ndicho chamisonkhano. (Yerekezerani ndi Machitidwe 17:24.) Iyenera kukhala malo abwino ndi oyenera ochitira misonkhano yachikristu imene imatithandiza kukula mwauzimu ndi kuphunzira ponena za Yehova, ndi imene imatilimbikitsa kukhala ndi phande mu utumiki wake wa Ufumu.” Monga pachimake pa maphunziro a Baibulo m’mzinda, Nyumba ya Ufumu imathandizira mwachindunji kulalikidwa kwa uthenga wabwino m’gawo lathu lampingo.

7 Pamene mpingo ulibe Nyumba ya Ufumu, anthu ena, makamaka achatsopano, amachita ulesi ndipo nthaŵi zambiri sapezeka pamisonkhano. Akulu ndi atumiki otumikira zimawavuta kwambiri kusamalira zosoŵa za abale ndi alongo aliyense payekha. Pamene Nyumba ya Ufumu ikugwiritsidwa ntchito ndi mipingo itatu kapena kuposerapo, akulu amachedwa kuvomereza kuti pakhale mpingo watsopano chifukwa mpingo watsopanowo udzasoŵa kosonkhana.

8 Pamene mipingo yoposa iŵiri igwiritsa ntchito Nyumba ya Ufumu imodzi, kumakhala kovuta kwa iwo kupanga makonzedwe a zochitika zapadera monga kuchezetsa kwa woyang’anira dera kapena phwando lapachaka la Chikumbutso cha Imfa ya Kristu. Komanso, kwa mipingo yokhudzidwayo pangakhale zolepheretsa popanga makonzedwe a utumiki wakumunda. Ngati zinthu ndi mmene zilili kuti Nyumba ya Ufumu imodzi imagwiritsidwa ntchito tsiku lililonse, pamakhala mavuto ena okhudza kukonza. Nthaŵi zina, kugwiritsa ntchito Nyumba ya Ufumu kaŵirikaŵiri kwadzetsa mavuto ndi anansi athu chifukwa cha phokoso losalekeza kapena mavuto ofanana nawo omwe angayambe chifukwa cha kuchuluka kwa anthu. Kuyenda mtunda wautali popita ku msonkhano kumapangitsa kufika ku misonkhano kukhala kovutirapo, ndipo zimenezi zimabwezera m’mbuyo chiwonjezeko.

9 Kwenikweni Vuto ndi Ndalama: Koma n’chifukwa chiyani kumanga Nyumba za Ufumu sikukuyendera limodzi ndi chiwonjezeko cha ofalitsa a Ufumu ndi kuyambika kwa mipingo yatsopano? Kwenikweni vuto ndi ndalama. Kuwonjezeka m’madera akutali kwakhala kovuta kwambiri kapenanso kosatheka chifukwa abale alephera kumanga kapena kupeza Nyumba za Ufumu zabwino m’madera ameneŵa. Komabe, pakali pano vuto limene gulu lakumana nalo makamaka ndi la m’mizinda, kumene mitengo ya malo yakwera kwambiri kwakuti mpingo uliwonse pawokha, kuphatikizapo ikuluikulu, yalephera kugula ngakhale malo okha oti amangepo Nyumba ya Ufumu.

10 Sosaite ili yokondwa kunena njira yothetsera mavuto ameneŵa, kuti abale onse apindule nalandire madalitso. Makonzedwe ameneŵa apereka mpata wina ku mipingo yonse ya Mboni za Yehova m’dziko lathu lino wosonyezera kuti tilidi ogwirizana.

11 Zoyenera Kuchita: Monga mukudziŵa, kuyambira kale Sosaite yakhala ikulimbikitsa kumanga Nyumba za Ufumu ndipo yakonza kuti ithandize mipingo mwa kupereka ngongole kuchokera pa ndalama zomwe zilipo. Zimenezi zachititsa mipingo ina kupempha ngongole ya Nyumba ya Ufumu. Ndipo Sosaite imakhala yosangalala kwambiri kuona mipingo yonse ikusonkhana mogwirizana ndi mosavuta m’Nyumba za Ufumu. Tonse tikudziŵa kufunika kofulumiza zinthu. Chotero, taganizira kwambiri zosoŵa za mipingo zomwe zilipo, ndipo takonza makonzedwe atsopano opereka thandizo loyenera mwa njira imene ili yabwino kwa tonse popanda kuika mtolo pa abale onse. Ndithudi, pulinsipulo la Baibulo lomwe ligwire ntchito pamakonzedwe ameneŵa ndi limene linanenedwa ndi mtumwi Paulo pa 2 Akorinto 8:14, 15. Anali wodera nkhaŵa zosoŵa zakuthupi za abale ake a ku Palestina ndipo anapereka malingaliro abwino a mmene mipingo ya ku Asia Minor ikanaperekera thandizo.

12 Mtumwiyo anasonya ku makonzedwe achikondi a Yehova osamalira zosoŵa za Aisrayeli pamene anali m’chipululu paulendo wawo wa zaka 40. Anati: “Mwa kulingana kuchuluka kwanu kukwanire kusoŵa kwawo nthaŵi ya makono ano, kutinso kuchuluka kwawo kukwanire kusoŵa kwanu. Kuti pakhale chilingano; monga kwalembedwa, Wosonkhetsa chambiri sichinam’tsalira; ndi iye wosonkhetsa pang’ono sichinam’soŵa.” (Yerekezerani ndi Eksodo 16:18.) Koma kodi kusoŵa kwa Nyumba za Ufumu zatsopano kumene kulipoku kusamalidwe motani?

THUMBA LA SOSAITE LA NDALAMA ZA NYUMBA ZA UFUMU —MMENE LIGWIRIRE NTCHITO

13 Tikufunikira kuchita mwanzeru kwambiri. Pakhala mapemphero ochuluka ndi kulingalira mosamalitsa za mmene timangire Nyumba za Ufumu zambiri. Kuti tichite zimenezi ndi cholinga cha kulambira Yehova mogwirizana, Sosaite ikuyamba pologalamu yatsopano kuyambira mwezi wamaŵa. Cholinga cha pologalamuyi ndi kusonkhanitsa ndalama zomangira Nyumba za Ufumu kapena kukuza maholo omwe alipo kale. Tikukhulupirira kuti zitheka kuchita zochuluka pokhala takhazikitsa Thumba la Ndalama za Nyumba za Ufumu ku ofesi ya nthambi ya Sosaite ku Lilongwe.

14 Makonzedwe a Thumba la Sosaite la Ndalama za Nyumba za Ufumu adzayamba kugwira ntchito pa April 1, 1999. Mipingo ya m’Malawi idzikhala ndi bokosi la zopereka lapadera pamalo awo osonkhanira lolembedwa “Thumba la Sosaite la Ndalama za Nyumba za Ufumu.” Makonzedwe ameneŵa adzachititsa aliyense mumpingo yemwe akufuna, kupereka chopereka chodzifunira nthaŵi iliyonse. Kapenanso, bungwe la akulu lingagamule ndalama zomwe azitapa pa ndalama za mpingo zoti zithandize kulikonse komwe akumanga Nyumba za Ufumu komano apemphe chivomerezo cha mpingo chakuti azitumiza ndalamazo ku Sosaite. Zopereka zimenezi adzizitumiza kumapeto kwa mwezi uliwonse ku ofesi ya Sosaite ndipo zidzagwiritsidwa ntchito kokha pothandiza mipingo yomwe ikusoŵa ndalama zomangira Nyumba ya Ufumu. Sosaite idzakudziŵitsani kuti yalandira zopereka zonse ndipo ikuthokoza, kenako idzaika ndalamazo m’Thumba la Sosaite la Ndalama za Nyumba za Ufumu.—Yerekezerani ndi 2 Mafumu 12:9-16.

15 Komanso, mipingo yomwe pakali pano ikusonkhetsa ndalama zoti imangire Nyumba ya Ufumu yawo ndipo ili ndi bokosi la zopereka zomangira nyumbayo ayenera kupitiriza kugwiritsa ntchito bokosi lapadera la cholinga chimenecho. Ngati akufunanso kuthandiza mipingo ina, angaike bokosi lina la zopereka za m’Thumba la Sosaite la Ndalama za Nyumba za Ufumu.

16 Mipingo yosoŵa ndalama zomangira Nyumba za Ufumu, ndalama zogulira nyumba zoti azikonze ngakhale zokonzetsera ndi kukulitsa Nyumba yawo ya Ufumu angapemphe ngongole ku Thumba la Sosaite la Ndalama za Nyumba za Ufumu. Ngongole zimenezi zidzabwezedwa ndi mpingo kapena mipingo yomwe ikugwiritsa ntchito Nyumba ya Ufumuyo. Tidzapitiriza kufuna kachiwongola dzanja kochepa pandalama zobwerekedwazo kuti tidzakhale okhoza kulipirira zinthu zowonongedwa posamalira zinthu zimenezi ndiponso kuti ndalamazo ziwonjezeke.

17 Mipingo Yomwe Ilibe Ngongole ya Nyumba ya Ufumu: Mipingo ina ili nazo kale Nyumba za Ufumu, ndipo ingakhale ilibiretu ngongole. Pamakonzedwe atsopano ameneŵa, mipingo imeneyi ingafune kupereka zopereka ku Thumba la Sosaite la Ndalama za Nyumba za Ufumu kuti athandize mipingo ina kukhala ndi maholo abwino. Monga tanenera pamwambapa, angafune kupatula ndalama zoti azipereka mwezi uliwonse ku Thumba la Sosaite la Ndalama za Nyumba za Ufumu. Ngati zili choncho, akulu ayenera kuuza mpingo zimene agamula pankhaniyi ndipo mpingo unene malingaliro ake ofuna kuthandiza mwanjira imeneyi.

18 Mmene Muzitumizira Ndalama ku Sosaite: Potumiza ndalama pamwezi ku Sosaite za Thumba la Sosaite la Ndalama za Nyumba za Ufumu, alembi adzagwiritsa ntchito fomu yotumizira ndalama (S-20). Chonde lembani pamwamba pa S-20 imeneyi kuti: “Thumba la Sosaite la Ndalama za Nyumba za Ufumu,” ndipo pamzera wachiŵiri wa Zopereka lembanipo chiŵerengero cha ndalamazo musanalembe Chiwonkhetso Chonse. Pamene mukutumiza ndalama za Thumba la Sosaite la Ndalama za Nyumba za Ufumu, ndipo mukugwiritsa ntchito cheke, ndi bwino kulemba cheke chapadera chopita ku: Watch Tower Bible and Tract Society. Komanso, aliyense payekha angatumize zopereka ku Thumba la Sosaite la Ndalama za Nyumba za Ufumu. Ngati mbale kapena mlongo akufuna kutero, sadzafunikira fomu ya S-20 koma adzafunikira kulemba kalata yachidule yonena kuti ndalamazo zipite ku Thumba la Sosaite la Ndalama za Nyumba za Ufumu. Monga tanena poyamba paja, zopereka zonse zotumizidwa ku Thumba la Sosaite la Ndalama za Nyumba za Ufumu zidzagwiritsidwa ntchito pa cholinga chake.

19 Sosaite Idzapenda Zosoŵa za Kumaloko: Koyambirira kwa mphatika ino tinanena za kufunika kofulumiza kumanga Nyumba za Ufumu m’Malawi muno. Tanenanso chifukwa chake pakufunika kuti mipingo yonse igwirizane kuti tithetse vuto lilipoli ndi kutinso tionetsetse kuti m’tsogolomu kusoŵa kwa malo okwanira osonkhanira sikukubwezera m’mbuyo chiwonjezeko m’dziko lonseli. Mogwirizana ndi akulu akwanuko, kupendako kudzachitika ndi kutsirizidwa panthaŵi yochepa.

20 Zitsanzo za Kugwirizana Zaposachedwapa: Miyezi ingapo yapitayo, Sosaite yamanga Nyumba ya Ufumu yoyamba kumpingo wa Nafisi ku Lilongwe. Makomiti a Chigawo Omanga akonzedwa m’dziko muno kuti apereke thandizo lofunikira pantchito yomanga Nyumba za Ufumu. Makonzedwe ameneŵa adzakhala othandiza kwambiri pomanga Nyumba za Ufumu. Mipingo imene ikulingalira zomanga Nyumba za Ufumu choyamba iyenera kufunsira malangizo ku Ofesi ya Nyumba za Ufumu ku Sosaite onena za mmene angapezere malo, zofunika kuboma, njira zomangira, ndi nkhani zina. Komiti ya Chigawo Yomanga yomwe muli nayo pafupi idzadziŵitsidwa chifuno cha mpingo chofuna kumanga.

21 Kusonyeza Umodzi Wachikristu: Mwa makonzedwe ameneŵa, lerolino tikuona madalitso ochuluka a Yehova pa anthu ake ogwirizana. Ndithudi, tili monga mmene Mika ananenera kuti, “ngati nkhosa za ku Bozira; ngati zoweta pakati pa busa pawo.” Yehova ‘watiika pamodzi’ ndipo chisangalalo chomwe tili nacho m’gululi panopo chikufotokozedwa bwino m’mawu akuti, “adzachita phokoso chifukwa cha kuchuluka anthu.”—Mika 2:12.

22 Abale athu m’mipingo yambiri ayenera kuthokozedwa pokhala oyambirira kumanga Nyumba ya Ufumu. Tikukhulupiria kuti kugwirizana kwa anthu akwanuko ndi m’zigawozigawo kudzapangitsa Nyumba za Ufumu zambiri kumangidwa m’Malawi. M’madera osiyanasiyana nyumba zimenezi sizidzakwaniritsa zosoŵa za mipingo zokha komanso zidzapereka umboni kwa onse oziona wakuti anthu a dzina la Yehova ali achangu m’deralo. Kuphatikiza apo, pamene akuthandiza ndi ndalama zomangira ndi zoyendetsera ntchito, abale adzapitiriza kupereka mooloŵa manja popititsa patsogolo ntchito ya Ufumu ya padziko lonse.

23 Makonzedwe a Thumba la Sosaite la Ndalama za Nyumba za Ufumu atipatsa mwayi wina wosonyezera kuti ndifedi anthu ogwirizana pochita zinthu, olambira Yehova mu umodzi wachikristu monga gulu limodzi. Polingalira zosoŵa za mpingo wathu zomwe zilipo, tiyeneranso kulingalira za abale athu kumadera ena a m’dzikoli amene ali osoŵa kwambiri thandizo la ndalama zomangira Nyumba za Ufumu. Zimenezi zidzatithandiza kwambiri kukhala ogwirizana pamodzi pamene tilingalira zosoŵa za “abale [athu] ali m’dziko,” pa chomwe aliyense payekha ndi monga mpingo angachite kuthandiza kuthetsa vuto limeneli.—1 Pet. 5:9.

24 Mawu Omaliza: Makonzedwe ameneŵa akhaletu nkhani yofunika kuisamalira mwachangu ndi yofuna pemphero lochokera pansi pa mtima nthaŵi zonse. Tiyeni tipitirize kufunafuna njira yochitira mogwirizana ndi mapemphero athu kuti chosoŵa chimenechi cha Nyumba za Ufumu zochuluka chikwaniritsidwe. Yehova akupitiriza kutsegula njira kwa “nkhosa zina” zambiri kuti zisonkhanitsidwe m’gulu limodzi la alambiri ogwirizana. Aonensotu kuti tili ndi nyumba zokwanira zothandizira achatsopano onse kukhala okhazikika m’choonadi ndi kukula msinkhu mwauzimu. Zoona chimwemwe chathu tsopano chikukula ndipo chidzapitirira kuwonjezeka m’tsogolomu chifukwa cha madalitso ochuluka a Yehova pa kulambira kogwirizana kwa Mulungu yekha woona.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena