Chimwemwe Chenicheni—Kodi Mfungulo Yake Nchiyani?
ANTHU analengedwa kuti akhale nchimwemwe. Nchifukwa ninji tili otsimikiza zimenezo? Chabwino, lingalirani za chiyambi cha munthu.
Yehova Mulungu analenga anthu aŵiri oyamba kuti azitha kukhala ndi chimwemwe. Adamu ndi Hava anaikidwa m’paradaiso, munda wosangalatsa wotchedwa Edene. Mlengi anawapatsa zofunika zonse zakuthupi za m’moyo. Mundawo unali ndi “mitengo yonse yokoma m’maso ndi yabwino kudya.” (Genesis 2:9) Adamu ndi Hava anali ndi thanzi labwino, amphamvu, ndi okongola—anali angwiro ndipo achimwemwedi.
Komabe, kodi mfungulo ya chimwemwe chawo inali chiyani? Kodi inali mudzi wawo waparadaiso kapena ungwiro wawo wakuthupi? Mphatso zochokera kwa Mulungu zimenezi zinawathandiziradi kusangalala ndi moyo. Koma chimwemwe chawo sichinali kudalira pa zinthu zakuthupi zimenezo. Munda wa Edene sunali chabe paki yokongola. Unali malo opatulika, malo olambiriramo Mulungu. Mfungulo ya chimwemwe chawo chosatha inali kukhoza kwawo kukhala paunansi wachikondi ndi Mlengi wawo ndi kuusungabe. Kuti akhale ndi chimwemwe, choyamba anayenera kukhala ndi mkhalidwe wauzimu.—Yerekezerani ndi Mateyu 5:3.
Mkhalidwe Wauzimu Umatsogolera ku Chimwemwe
Adamu poyamba anali paunansi wauzimu ndi Mulungu. Unali unansi wachikondi ndipo wapafupi kwambiri monga uja wa mwana ndi atate wake. (Luka 3:38) M’munda wa Edene, Adamu ndi Hava anali pamikhalidwe yabwino kwambiri yomwe inawalola kukhutiritsa chikhumbo chawo cha kulambira. Mwa kumvera kwawo Yehova mofunitsitsa ndiponso mwachikondi, akanadzetsa ulemu ndi ulemerero waukulu kwambiri kwa Mulungu kuposa umene nyama zinadzetsa. Akanatha kutamanda Mulungu mwaluntha chifukwa cha mikhalidwe yake yodabwitsa ndipo akanatha kuchirikiza uchifumu wake. Akanapitirizanso kulandira chisamaliro cha Yehova chachikulu ndiponso chachikondi.
Ubwenzi wathithithi umenewu ndi Mlengi ndi kumvera malamulo ake kunadzetsa chimwemwe chenicheni kwa makolo athu oyamba. (Luka 11:28) Adamu ndi Hava sanafunikire kukhala moyo zaka zambirimbiri akumayesayesa kupeza mfungulo ya chimwemwe. Iwo anali achimwemwe kuyambira panthaŵi ya kulengedwa kwawo. Kukhala pamtendere ndi Mulungu ndiponso kugonjera ulamuliro wake kunawapatsa chimwemwe.
Komabe, chimwemwe chimenecho chinatha nthaŵi imene sanamvere Mulungu. Mwa kupanduka, Adamu ndi Hava anadula unansi wawo ndi Yehova. Iwo sanalinso mabwenzi a Mulungu. (Genesis 3:17-19) Zikuoneka kuti kuyambira tsiku limene anathamangitsidwa m’mundawo, Yehova analeka kulankhula nawo. Iwo anataya ungwiro wawo, chiyembekezo cha kukhala ndi moyo kosatha, ndi mudzi wawo wamunda wamaluŵa. (Genesis 3:23) Koma chachikulu kwambiri nchakuti, popeza kuti anataya unansi wawo ndi Mulungu, iwo anataya mfungulo ya chimwemwe.
Ufulu Wathu wa Kusankha
Adamu ndi Hava asanafe, iwo anapatsira mbadwa zawo mikhalidwe yawo yaumunthu, chikumbumtima chawo chachibadwa, ndi kukhoza kwawo kwa kukhala ndi mkhalidwe wauzimu. Banja la anthu silinatsitsidwe kufikira pakulingana ndi nyama. Ifeyo tingayanjidwenso ndi Mlengi. (2 Akorinto 5:18) Monga zolengedwa zaluntha, anthu amapitirizabe kukhala ndi ufulu wosankha kumvera kapena kusamvera Mulungu. Zimenezi zinasonyezedwa patapita zaka mazana ambiri pamene Yehova anapatsa mtundu wopangidwa chatsopanowo wa Israyeli mwaŵi wa kusankha moyo kapena imfa. Mwa womlankhulira wake Mose, Mulungu anati: “Ndaika pamaso panu lerolino moyo ndi zokoma, imfa ndi zoipa.”—Deuteronomo 30:15-18.
Ngakhale tsopano, zaka zikwi zambiri kuchokera pamene Paradaiso woyambayo anatayika, anthufe tikhozabe kupanga chosankha chabwino. Tili ndi chikumbutima chogwira ntchito ndipo tikhoza kumvera malamulo a Mulungu. Baibulo limanena za ‘munthu wa mkati mwathu’ ndi za munthu “wa mkati.” (2 Akorinto 4:16; Aroma 7:22) Mawu ameneŵa amanena za kukhoza kwachibadwa kosonyeza umunthu wa Mulungu, kuganiza momwe amaganizira, ndi kukhala ndi mkhalidwe wauzimu, komwe tonsefe tili nako.
Ponena za chibadwa cha khalidwe lathu ndi chikumbumtima chathu, mtumwi Paulo analemba kuti: “Pamene anthu a mitundu akukhala opanda lamulo, amachita mwa okha za lamulo, omwewo angakhale alibe lamulo, adzikhalira okha ngati lamulo; popeza iwo aonetsa ntchito ya lamulo yolembedwa m’mitima yawo, ndipo chikumbumtima chawo chichitiranso umboni pamodzi nawo, ndipo maganizo awo wina ndi mnzake anenezana kapena akanirana.”—Aroma 2:14, 15.
Nzeru Yaumulungu ndi Kumvera—Mfungulo Yake
Komano wina angafunse kuti, ‘Ngati tonsefe mwachibadwa timafuna kulambira Mulungu ndipo, kenako, kukhala ndi chimwemwe chenicheni, kodi nchifukwa ninji anthu ambirimbiri chonchi akusoŵa chimwemwe?’ Nchifukwa chakuti aliyense wa ife, kuti akhale wachimwemwe, ayenera kukulitsa mkhalidwe wauzimu. Ngakhale kuti poyamba munthu analengedwa m’chifanizo cha Mulungu, iye wapatukana ndi Mlengi wake. (Aefeso 4:17, 18) Choncho, aliyense wa ife ayenera kuchitapo kanthu motsimikiza kuti ayambitsenso unansi wauzimu ndi Mulungu ndi kuusunga. Unansi umenewo sungakule wokha.
Yesu analongosola mapulinsipulo aŵiri ofunika pokulitsa mkhalidwe wauzimu. Loyamba ndilo kukhala ndi chidziŵitso cholongosoka chonena za Mulungu, ndipo lina ndilo kugonjera chifuniro chake momvera. (Yohane 17:3) Mwa kugwira mawu Mawu a Mulungu, Yesu anati: “Kwalembedwa, Munthu sadzakhala ndi moyo ndi mkate wokha, koma ndi mawu onse akutuluka mkamwa mwa Mulungu.” (Mateyu 4:4) Panthaŵi inanso, Yesu anati: “Chakudya changa ndicho kuti ndichite chifuniro cha Iye amene anandituma Ine, ndi kutsiriza ntchito yake.” (Yohane 4:34) Sitifunikira kutha zaka makumi ambiri tikufunafuna chimwemwe. Kudziŵa zinthu zambiri sindiko mfungulo ya chimwemwe. Komabe, nzeru yaumulungu ndiponso kumvera Mlengi wathu ndizo zokha zomwe zingatichititse kukhala ndi chimwemwe chenicheni m’moyo.—Salmo 19:7, 8; Mlaliki 12:13.
Ndithudi, chimwemwe chimene chimadza mwa kutsatira nzeru yaumulungu ndi kukhala ndi kaimidwe kabwino pamaso pa Mulungu tingachipeze. (Machitidwe 17:26, 27) Aliyense angathe kupeza chidziŵitso chonena za Yehova ndi chifuno chake. Pokhala ndi makope miyandamiyanda m’zinenero zambiri, Baibulo likupitirizabe kukhala buku lofalitsidwa kopambana padziko lonse lapansi. Baibulo lingakuthandizeni kukhala bwenzi la Mulungu ndi kukhala ndi chimwemwe chenicheni, popeza Malemba amatiuza kuti “odala [“achimwemwe,” NW] anthu amene Mulungu wawo ndi Yehova.”—Salmo 144:15.
[Bokosi patsamba 6]
Masitepe Opezera Chimwemwe
1. Zindikirani ndi kukulitsa mkhalidwe wauzimu. Yesu anati: “Odala [“Achimwemwe,” NW] iwo akumva mawu a Mulungu, nawasunga.”—Luka 11:28.
2. Zindikirani kuti chiyanjo cha Mulungu ndicho chofunika kwambiri kuposa chuma kapena zosangalatsa. Paulo analemba kuti: “Koma chipembedzo pamodzi ndi kudekha chipindulitsa kwakukulu; . . . pokhala nazo zakudya ndi zofunda, zimenezi zitikwanire.”—1 Timoteo 6:6-8.
3. Yesetsani kukulitsa chikumbumtima chophunzitsidwa ndi Baibulo ndi kuchimvera.—Aroma 2:14, 15.
4. Tsimikizani mtima kuti mudzamvera Yehova Mulungu, nimuyenerere kukhala mmodzi wa anthu ake. Davide wakale analemba kuti: “Odala [“Achimwemwe,” NW] anthu amene Mulungu wawo ndi Yehova.”—Salmo 144:15.
[Chithunzi patsamba 7]
“Achimwemwe ali awo ozindikira kusoŵa kwawo kwauzimu.”—Mateyu 5:3, NW