Nyimbo 174
Dzukani, Chirimikani, Khalani Wamphamvu
1. Dzukani, muchirimike
Munkhondo yoyenera.
Chitanitu mwachamuna,
Chilakiko chafika.
Pansi pa Gideoni ’Mkulu,
Tazinga msasa wa Midyani.
Mfu’ yankhondo iperekedwa,
Kupirikitsa mdani.
2. Dzukani, mukhale maso,
Achire mukumvera.
Yense alabadiretu
Zomwe Yesu anena.
Mwachitsanzo chake tidziŵa
Kupeza chiyanjo cha M’lungu.
Monga gulu titumikire,
Mokhulupirikabe.
3. Dzukani, ndi kupilira;
Yembekezani pa Ya.
Alamula zinthu zonse;
Sadzachita mochedwa.
Monga ’muna a Gideoni,
Mkuluyo adzatilamula.
Potero mverani lamulo.
Lidzatamanda dzina.
4. Dzukani, mugwirizane
Potchinjiriza mbiri.
M’njira ya teokratiki
Njofunika kwambiri.
Tifuule ndi anthu a Ya:
“Lupanga la Ya n’Gideoni!”
Dzukani m’chirimike m’khondo!
Kufikira mapeto!