Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w98 6/15 tsamba 30-31
  • Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
  • Nsanja ya Olonda—1998
  • Nkhani Yofanana
  • Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
    Nsanja ya Olonda​—1990
  • Zimene Zinachitika Pamene Yesu Ankalalikira ku Pereya
    Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
  • Kodi Tiyenera Kuchitanji Kuti Tipulumutsidwe?
    Nsanja ya Olonda—1996
  • Kodi Mwalandira “Mzimu wa Choonadi”?
    Nsanja ya Olonda—2002
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1998
w98 6/15 tsamba 30-31

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Yesu anapereka uphungu wakuti: “Yesetsani kuloŵa pakhomo lopapatiza; chifukwa anthu ambiri, ndikuuzani, adzafunafuna kuloŵamo, koma sadzakhoza.” (Luka 13:24) Kodi iye anatanthauzanji, ndipo kodi uphunguwu umagwira ntchito motani lerolino?

Tingazindikire bwino tanthauzo la nkhani yosangalatsa imeneyi mwa kulingalira zomwe zinali kuchitika panthaŵiyo. Patakhala miyezi isanu ndi umodzi kuti iye aphedwe, Yesu anali m’Yerusalemu pamwambo wopatuliranso kachisi. Iye anafotokoza kuti anali mbusa wa nkhosa za Mulungu koma Ayuda ambiri sanali pakati pa nkhosa zimenezo chifukwa chakuti anakana kumvetsera. Pamene ananena kuti iye ndi Atate wake anali “amodzi,” Ayuda anatenga miyala kuti amponye nayo. Iye anathaŵira ku Pereya kutsidya lina la Yordano.​—Yohane 10:1-40.

Ali kumeneko, munthu wina anamfunsa kuti: “Ambuye, akupulumutsidwa ndiwo oŵerengeka kodi?” (Luka 13:23) Munthu ameneyu anayeneradi kufunsa funso limeneli, popeza kuti Ayuda a panthaŵiyo anali kukhulupirira kuti anthu oŵerengeka chabe ndiwo anali ofunikira chipulumutso. Malinga ndi khalidwe limene iwo anasonyeza, nkosavuta kuzindikira amene iwo anawalingalira kuti adzakhala pakati pa oŵerengekawo. Iwo analingalira molakwa chotani nanga, popeza zochitika zamtsogolo mwake zinasemphana ndi zimenezo!

Kwa zaka ziŵiri, Yesu anali pakati pawo, kuphunzitsa, kuchita zozizwitsa, ndi kulalikira za chiyembekezo chakuti iwo angakhale oloŵa nyumba a Ufumu wakumwamba. Kodi chotsatirapo chake chinali chotani? Iwo, ndi atsogoleri awo makamaka, anali kunyadira kuti anali mbadwa za Abrahamu ndipo anapatsidwa Chilamulo cha Mulungu. (Mateyu 23:2; Yohane 8:31-44) Koma iwo sanamvetsere ndi kuvomera chiitano cha Mbusa Wabwino. Zinakhala monga kuti patsogolo pawo panali chitseko chotseguka, ndipo aliyense woloŵamo anali kuyembekezera kulandira mphotho yokhala mmodzi wa mu Ufumu, koma iwo anakana. Oŵerengeka chabe, kwenikweni onyozeka, ndiwo amene anamvetsera uthenga wa Yesu wa choonadi, kuvomera, ndi kumamatirana naye.​—Luka 22:28-30; Yohane 7:47-49.

Patsiku la Pentekoste wa 33 C.E., anali onyozeka ameneŵa omwe anali m’gulu la amene anadzozedwa ndi mzimu. (Machitidwe 2:1-38) Iwo sanali pakati pa akuchita chosalungama amene anatchulidwa ndi Yesu kuti anali kudzalira ndi kukukuta mano chifukwa cholephera kugwiritsira ntchito mwayi umene iwo anapatsidwa.​—Luka 13:27, 28.

Chotsatirapo chake, m’zaka za zana loyamba ‘ambiriwo’ kwenikweni anali Ayuda, ndipo makamaka atsogoleri achipembedzo. Ameneŵa anasonyeza kuti anali kufuna chiyanjo cha Mulungu​—komatu mogwirizana ndi zofuna zawo ndi njira zawo, osati za Mulungu. Mosiyana ndi zimenezo, “oŵerengeka” amene anavomera mofunitsitsadi kukhala mbali ya Ufumu anakhala pakati pa odzozedwa a mumpingo wachikristu.

Tsopano tiyeni tilingalirepo mmene mawuwo akugwirira ntchito mowonjezereka m’tsiku lathu. Anthu ambirimbiri omwe amapita kumatchalitchi a m’Dziko Lachikristu amaphunzitsidwa kuti adzapita kumwamba. Komabe, chiphunzitso chimenechi nchosazikidwa pa ziphunzitso zolongosoka za m’Malemba. Mofanana ndi Ayuda akalewo, anthu ameneŵa amafuna chiyanjo cha Mulungu m’njira yawoyawo.

Komabe, pali oŵerengeka m’nthaŵi yathu amene avomera uthenga wa Ufumu modzichepetsa, kudzipatulira kwa Yehova, ndi kukhala pakati pa anthu olandira chiyanjo chake. Zimenezi zawapangitsa kukhala “ana a Ufumu.” (Mateyu 13:38) “Ana” odzozedwa ameneŵa anayamba kuitanidwa pa Pentekoste wa 33 C.E. Mboni za Yehova zakhala zikukhulupirira kuti umboni wa zimene Mulungu amachita kwa anthu ake umasonyeza kuti ambiri a m’gulu la kumwamba aitanidwa kale. Choncho, amene aphunzira choonadi cha Baibulo m’zaka zaposachedwapa azindikira kuti chiyembekezo cha moyo wosatha padziko lapansi la paradaiso tsopano chikuperekedwa. Chiŵerengero cha ameneŵa tsopano chapitirira chiŵerengero chomwe chikutsika cha Akristu odzozedwa otsalira, amene ali ndi chiyembekezo chopitadi kumwamba. Luka 13:24 sagwira ntchito kwenikweni kwa anthu amene alibe chiyembekezo chopita kumwamba, koma mawuwo ali ndi uphungu wothandiza kwambiri kwa iwo.

Mwa kutilangiza kuti tiyesetse, Yesu sanali kutanthauza kuti iye kapena Atate wake amadzetsa zopinga kuti zitilepheretse ayi. Koma tikudziŵa kuchokera pa Luka 13:24 kuti Mulungu safuna osayenerera. Mawu akuti “Yesetsani” akusonyeza kuti tiyenera kuchita khama, kulimbikira. Choncho, tingadzifunse kuti, ‘Kodi ndikulimbikira?’ M’njira ina, mawu a pa Luka 13:24 tingawalembe kuti, ‘Ndifunikira kuyesetsa kuloŵa pakhomo lopapatiza chifukwa chakuti ambiri adzafunafuna kuloŵamo koma sadzakhoza. Choncho, kodi ndikuyesetsadi? Kodi ndili monga wochita mpikisano wothamanga m’bwalo lakale lamaseŵero yemwe amadzipereka kotheratu kuti apate mphotho? Wothamanga wotero sangakhale wokayikira kapena wamphwayi ayi. Kodi ndikuyesetsa?’

Mawu ameneŵa a Yesu akusonyeza kuti mwina ena angafune ‘kuloŵa pakhomopo’ monga mmene angafunire, angayende mosatekeseka monga momwe akufunira. Mzimu umenewu ungakhudze a Mboni ena. Ena angalingalire kuti, ‘Ndikudziŵa Akristu odzipereka amene anatumikira mokangalika kwa zaka zambiri, anadzimana zambiri; komatu iwo anafa, ndipo mapeto a dongosolo lino sanafikebe. Choncho, mwina kuli bwino kuti ndichepetseko changu changa, ndizingokhala monga momwe ena onse amakhalira.’

Kungakhaledi kosavuta kulingalira motero, koma kodi nkulingalira kwanzeru? Mwachitsanzo, kodi atumwi analingalira motero? Ndithudi iwo sanalingalire motero. Anachita kulambira koona ndi mtima wawo wonse​—kufikira imfa yawo. Mwachitsanzo, Paulo anati: “[Kristu] amene timlalikira ife . . . kuchita ichi ndidzivutitsa ndi kuyesetsa monga mwa machitidwe ake akuchita mwa ine ndi mphamvu.” Pambuyo pake analemba kuti: “Kukalingako tigwiritsa ntchito ndi kuyesetsa, chifukwa chiyembekezo chathu tili nacho pa Mulungu wamoyo, amene ali Mpulumutsi wa anthu onse, makamaka wa okhulupirira.”​—Akolose 1:28, 29; 1 Timoteo 4:10.

Tikudziŵa kuti Paulo anachita chinthu chabwino kwambiri pamene anayesetsa. Aliyense wa ife angakhaledi wokondwa ngati anena mofanana ndi momwe ananenera Paulo kuti: “Ndalimbana nako kulimbana kwabwino, ndatsiriza njirayo, ndasunga chikhulupiriro.” (2 Timoteo 4:7) Choncho, mogwirizana ndi mawu a Yesu olembedwa pa Luka 13:24, aliyense wa ife angadzifunse kuti, ‘Kodi ndikuyesetsa mwakhama ndi mokangalika? Inde, kodi ndimapereka umboni wokwanira komanso woŵirikiza wakuti ndikutsatira uphungu wa Yesu wakuti: “Yesetsani kuloŵa pakhomo lopapatiza”?’

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena