Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
◼ Kodi tiyenera kulingalira kuchokera pa Mateyu 7:13, 14 ndi Luka 13:24 kuti ngakhale m’chiukiriro, anthu ambiri adzakana kulambira kowona?
Ayi, mavesiwa samachirikiza lingaliro limenelo. Mmalomwake, iwo amaloza makamaka kukupeza moyo mu Ufumu wakumwamba.
Mawu a Yesu pa Mateyu 7:13, 14 ali mbali ya Ulaliki wa pa Phiri. Iye ananena kuti: “Loŵani pa chipata chopapatiza; chifukwa chipata chiri chachikulu, ndi njira yakumuka nayo kukuonongeka iri yotakata; ndipo ali ambiri amene aloŵa pa icho. Pakuti chipata chiri chopapatiza, ndi ichepetsa njirayo yakumuka nayo kumoyo, ndimo akuchipeza chimenecho ali oŵerengeka.”
Zambiri zimene Yesu ananena pa chochitikachi zinasonya makamaka ku Ufumu wakumwamba. Mwachitsanzo, iye anayamba ndi mawu akuti: “Achimwemwe ali awo ozindikira kusowa kwawo kwauzimu, popeza kuti ufumu wa kumwamba uli wawo.” Iye anati oyera mu mtima “adzaona Mulungu” ndikuti “ufumu wa kumwamba” uli wa awo amene “azunzidwa kaamba ka chifukwa cha chilungamo.” (Mateyu 5:3, 8, 10, NW) Pambuyo pake m’nkhani imodzimodziyo, Yesu analankhula za njira yotakata yotsogoza ku chionongeko ndi njira yopapatiza yotsogoza ku moyo. Mwambali, iye anawonjezera kuti: “Si yense wakunena kwa ine, Ambuye, Ambuye, adzaloŵa mu Ufumu wa Kumwamba; koma wakuchitayo chifuniro cha Atate wanga wa Kumwamba.”—Mateyu 7:13, 14, 21.
Tanthauzo la Luka 13:24 nlofanana, monga kwasonyezedwa ndi mawu ozungulira lemba. Yesu anapereka mafanizo aŵiri onena za “ufumu wa Mulungu.” Pambuyo pake, anafunsidwa kuti: “Ambuye, akupulumutsidwa ndiwo oŵerengeka kodi?” Yesu anayankha nati: “Yesetsani kuloŵa pa khomo lopapatiza; chifukwa anthu ambiri, ndikuuzani, adzafunafuna kuloŵamo, koma sadzakhoza.” “Ambiri” pano akulozera kwa anthu amene anapempha kuloledwa kuloŵa pambuyo pakuti chitseko chinatsekedwa ndi kukhomedwa. Iwowa anali “akuchita chosalungama” amene sanayeneretsedwe kukhala ndi “Abrahamu, ndi Isake, ndi Yakobo, ndi aneneri onse, mu Ufumu wa Mulungu.” “Ambiri” amenewa analingalira kuti akakhala oyamba “mu Ufumu wa Mulungu,” koma iwo kwenikweni akakhala akuthungo, mowonekeratu kutanthauza kuti sadzakhalamo mpang’ono ponse.—Luka 13:18-30.
Mawu ozungulira lemba akusonyeza kuti Yesu ankachita ndi kuloŵa mu Ufumu wa kumwamba wa Mulungu. Atsogoleri Achiyuda kalelo anasangalala kwa nthaŵi yaitali kukhala m’malo a mwaŵi, okhala ndi Mawu a Mulungu. Iwo anadzimva kuti anali olemera mwauzimu ndikuti anali olungama pamaso pa Mulungu, mosiyana ndi anthu wamba, amene anawonedwa otsika kwa iwo. (Yohane 9:24-34) Komabe, Yesu ananena kuti osonkhetsa msonkho ndi akazi achigololo amene akalandira uthenga wake ndi kulapa akakhala ndi chivomerezo cha Mulungu.—Yerekezerani ndi Mateyu 21:23-32; Luka 16:14-31.
Anthu wamba amene anakhala ophunzira a Yesu anali pa mzera wolandiridwa monga ana auzimu pamene chiitano chakumwamba chinatseguka pa Pentekoste wa 33 C.E. (Ahebri 10:19, 20) Ngakhale kuti makamu aakulu anamumva Yesu, awo amene anamlandira ndipo pambuyo pake napeza chiyembekezo chakumwamba anali oŵerengeka. Koma kagulu kankhosa ka anthu obadwa ndi mzimu kolandira mphothoyo kakanayerekezedwa ndi Yakobo akumaseyama pa gome kumwamba ndi Yehova (Abrahamu Wamkulu) ndi Mwana wake (wochitiridwa chithunzi ndi Isake). Zimenezo zinalidi zoyenerera kuyesetsa mwamphamvu, koma ambiri amene anamumva Yesu sanachite choncho.
Motero, tingawone kuchokera ku mawu ozungulira lembalo m’zochitika zonse ziŵiri kuti ndemanga za Yesu (ponena za oŵerengeka okhala pa njira yopapatiza yotsogoza ku moyo ndi kupulumutsidwa) zikusonya choyambirira ku kukhala ndi chivomerezo cha Mulungu pa nthaŵi yomwe ija pamene Iye ankapereka chiyembekezo cha moyo wakumwamba. Oŵerengeka amene anamva uthenga wa chowonadi ndi kuphunzira zimene zinafunikira ndiwo amene anavomereza ndi kutsimikizira kukhala okhulupirika.—Mateyu 22:14; 24:13; Yohane 6:60-66.
Nzosangalatsa kuti ngakhale lerolino, pamene Baibulo lathunthu liripo ndipo pali kukwaniritsidwa kochuluka kwa maulosi aumulungu onena za masiku otsiriza, oŵerengeka okha ndiwo amene akuvomereza ku uthenga Wachikristu ndi kupitirizabe kutumikira Yehova. Izi nzogwirizana ndi fanizo la Yesu lonena za nthaka zosiyanasiyana. Iye adati ena adzamva “mawu a Ufumu,” koma Satana adzatsomphola zimene zinabzalidwa. Enanso adzalandira mawuwo ndi chisangalalo koma m’kupita kwa nthaŵi adzalephera chifukwa cha nsautso kapena chizunzo. Ndiponso ena adzakhala osakhulupirika chifukwa cha “kulabadira kwa dziko lapansi, ndi chinyengo cha chuma.”—Mateyu 13:18-23.
Tingakhale otsimikizira kuti chidzakhala chosiyana kwambiri pamene mamiliyoni amamiliyoni adzaukitsidwa m’Tsiku Lachiweruzo. Ndiyeno Satana sadzakhoza kutsomphola mbewu za chowonadi zobzalidwa m’mitima yawo. Iwo sadzafunikira kuchita ndi chizunzo kapena nkhaŵa za dongosolo iri loipa. Iwo adzaphunzitsidwira mumkhalidwe wolungama, wozingidwa ndi ntchito yozizwitsa ya Mulungu, kuphatikizapo chiukiriro cha akufa ndi kuchiritsa mitundu. Kusapita mbali, ena sadzavomereza ngakhale pa nthaŵiyo. (Yerekezerani ndi Yohane 11:45-53.) Koma pali chifukwa chabwino cholingalirira kuti ambiri adzamvetsetsa mawuwo, kuwavomereza, ndi kupulumutsidwa.