Nyimbo 155
‘Landiranani’!
1. O landiranani monga anachita Kristu!
Poti Kristu anafera mbale m’landireni.
Chotero amphamvu athandize ofooka,
Kuwathandiza kuteteza chiyembekezo.
Zinthu zolembedwa ndi aneneri akale
Zingathe kukulitsa chiyembekezo chathu.
Chotero tisadzikondweretse ife tokha,
Koma kuwona zokonda zawo monga zathu.
2. Ya akusonkhanitsa anthu osamenyana.
Nthaŵi yadzera Mwana’ke kudzetsa mtendere.
Akutenga anthu m’mitundu ndi malirime,
M’mitima mwawo muli kukonda malamulo.
Polemekeza M’lungu tilandirabe ena
Timayanjana ndi onse popanda kusankha.
Ndimwaŵi waukulu kutsanzira Mulungu.
Monga otsanza Mwanayo, tikuze mitima.
3. Tilimbikitse anthu kutamanda Yehova,
Kukondwa ndi mtundu wake, ndi kumutamanda.
Tilengezebe panyumba ndi pamakwalala,
Mbiri yake ndi dzina kwa okumana nawo.
Ulemuwu wa kutamanda Ya sudzadzanso.
Ndiwo masiku otsiriza kwa olungama.
Tikonde abale M’lungu akhale wowona;
Inde mulandiranedi Mawuwo atero.