Nyimbo 12
“Mulungu Akonda Wopereka Mokondwera”
1. Potumikira Tate, tiyenera kudziŵa
Kuti ngwokoma mtima ndi wachikondi.
Poti ali Wopatsa; anapatsa Mwana’ke,
Nafuna kuwonjola mitundu yonseyo.
2. Tingachite bwinodi kumtsanzira mkupatsa.
Tikapatsa mokondwa, tidzakondwera.
Nthaŵi yathu ndi chuma ziridi za Yehova.
Tikamupatsa iye, sitidzalakwanso.
3. Kupatsa mwachimwemwe kukondwetsa Yehova.
Kukonza chiphunzitso ndi chikondinso.
Nkofunika kwambiri kukachoka mumtima;
Kudzadzetsa chimwemwe ndi chisangalalo.
4. Motero Tiyamika M’lungu ndi Kristu Yesu,
Pokuza kulambira kwathu kowona.
Mtima utisonkheze tipereke mokondwa
Ndi kukondweretsa Ya pokhala ndi moyo.