Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 1/00 tsamba 1
  • Ndidzabwezera Yehova Chiyani?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Ndidzabwezera Yehova Chiyani?
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2000
Utumiki Wathu wa Ufumu—2000
km 1/00 tsamba 1

Ndidzabwezera Yehova Chiyani?

1 “Ndidzabwezera Yehova chiyani chifukwa cha zokoma zake zonse anandichitira?” anafunsa motero wamasalmo pa Salmo 116:12. Kodi Yehova amafunadi kuti tim’patse kanthu? Inde, Yehova amayembekezera alambiri ake kusonyeza chikondi chawo pa iye mwa kuchirikiza kulambira kwake koyera ndi zopereka zaufulu. Amuna onse mu Israyeli anayenera kupita ku kachisi wa ku Yerusalemu katatu pachaka. Onse analamulidwa kutenga kanthu kokachirikizira kulambira koona kuti “asaoneke pamaso pa Yehova opanda kanthu.”—Deut. 16:16b.

2 Kupereka zothandizira kusamalira kachisi wa ku Yerusalemu kunapitirira mpaka m’nthaŵi ya Yesu. Marko 12:41 amanena kuti Yesu “anakhala pansi pandunji pa mosungiramo zopereka.” Ayuda amati panali mabokosi a zopereka okwanira 13. Bokosi lililonse linali lolemba m’Chihebri ntchito imene ndalama za mmenemo zikagwire. Panali a ndalama zogulira zinthu, nsembe, nkhuni zowotchera nsembe, zofukiza, ndi zina zotero. Izi zikutiphunzitsa kuti nsembe ndi zopereka zinali mbali zofunika kwambiri pa kulambira kwa Aisrayeli.

3 Kodi lerolino zopereka zaufulu zili mbali ya kulambira koona? Inde! Maofesi a nthambi akumangidwa m’mayiko ambiri, monga nthambi yathu yatsopano ku Lilongwe. Zimenezi zimafuna makwacha ambiri kwabasi. M’chaka chautumiki cha 1998, Watch Tower Society inawononga ndalama zokwanira $64,414,274.00 posamalira apainiya apadera, amishonale, ndi oyang’anira oyendayenda pantchito zawo zautumiki wakumunda padziko lonse. Kodi ndalama zolipirira zinthu zonsezi zimachokera kuti?

4 Mofanana ndi Aisrayeli komanso Akristu oyambirira, uli udindo wa wolambira aliyense kuchirikiza kulambira koyera. (Agal. 6:5) Mtumwi Paulo analangiza kuti “tsiku loyamba la sabata yense wa inu asunge yekha, monga momwe anapindula.” Langizolo linachokera kwa Yehova.—1 Akor. 16:2.

5 Baibulo limanena momveka bwino kuti Yehova “akonda wopereka mokondwerera.” (2 Akor. 9:7) Safuna kuti wina achite kukakamizidwa kapena kulamulidwa kuti apereke. Pachifukwa chimenechi, Nyumba ya Ufumu iliyonse iyenera kukhala ndi mabokosi a zopereka angapo. Ena a mabokosi ameneŵa angalembedwe kuti: “Zopereka za Ntchito ya Sosaite ya Padziko Lonse—Mateyu 24:14,” “Thumba la Sosaite la Ndalama za Nyumba za Ufumu,” “Makonzedwe Othandiza pa Nyumba za Ufumu,” ndi “Thumba la Chithandizo.” Ameneŵa ndi mabokosi apadera kuwonjezera pa bokosi la zopereka zothandizira pa zosoŵa za pampingo, monga zofunika pa Nyumba ya Ufumu yanu, komanso ulendo wa woyang’anira dera, ndi zina zotero. Komanso, bokosi lina limene ofalitsa onse a mumpingo ayenera kuponyamo malipoti awo a mu utumiki wakumunda (S-4) liyenera kukhalaponso pa Nyumba ya Ufumu. Pangakhalenso mabokosi a zopereka ena ngati pangakhale zosoŵa zina.

6 Chotero, kodi tingam’bwezere Yehova ubwino wonse umene amatichitira? Inde, koma sitingam’bwezere zonse. Mwa kumvera kwathu malangizo ake, kuchita nawo ntchito yolalikira ndi kuphunzitsa, ndiponso mwa zopereka zathu zaufulu. Zonsezi zidzathandiza kwambiri kusonyeza chikondi chathu ndi kuyamikira kwathu ubwino umene Yehova amatichitira.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena