Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki
Mlungu Woyambira January 10
Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Zilengezo zosankhidwa mu Utumiki Wathu wa Ufumu.
Mph. 15: “Kudziŵikitsa Dzina la Yehova M’dziko Lonse.” Kukambirana mwa mafunso ndi mayankho. Phatikizanipo ndemanga za m’buku la Olinganizidwa pa za kuchitira umboni mwamwayi, patsamba 93-4.
Mph. 20: Kusankha Mwalamulo Thandizo la Mankhwala Opanda Magazi. (Mac. 15:28, 29) Nkhani yokambidwa ndi mkulu woyeneretsedwa, kuchokera pa zomwe zalembedwa pa Khadi la Chidziŵitso kwa Dokotala/Chommasula ku Mlandu. Pamapeto pa msonkhano uno, Mboni zonse zobatizidwa zingalandire makadi atsopano a Chidziŵitso kwa Dokotala/Chommasula ku Mlandu, ndipo amene ali ndi ana osabatizidwa angalandire Khadi la Ana la mwana aliyense. Makadiwa asalembedwere panopa. Akalembedwere kunyumba bwinobwino koma OSAKAWASAINA. Makadi onse adzasainidwa, kuchitiridwa umboni, ndi kulembapo deti pamapeto pa Phunziro la Buku la Mpingo lotsatira. Ofuna kuthandizidwa, wochititsa phunziro la buku adzawathandiza. Musanasaine onetsetsani kuti makadiwo alembedwa bwinobwino monse. Amene adzasaina monga mboni ayenera kumuonadi mwiniwake wa khadilo akulisaina. Mwa kukonza mawu monga amene ali pakhadili kuti agwirizane ndi mikhalidwe komanso zikhulupiriro zawo, ofalitsa osabatizidwa angalembe makadi awoawo oti azigwiritsa ntchito iwo ndi ana awo. Ochititsa phunziro la buku atsimikizire kuti onse amene ali m’gulu lawo alandira chithandizo chimene akufuna polemba makadi a Chidziŵitso kwa Dokotala/Chommasula ku Mlandu.
Nyimbo Na. 155 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira January 17
Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Lipoti la maakaunti.
Mph. 15: Zosoŵa za pampingo.
Mph. 20: “Gwiritsani Ntchito Mabuku Athu Mwanzeru.” Kukambirana mwa mafunso ndi mayankho. Mukatha kukambirana ndime 7, onetsani zitsanzo ziŵiri kapena zitatu za ulaliki wachidule wofotokozedwa mu ndime 4-7.
Nyimbo Na. 57 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira January 24
Mph. 10: Zilengezo za pampingo ndi zokumana nazo za mu utumiki wakumunda.
Mph. 15: “Pendani Mawu a Yehova Tsiku Lililonse!” Nkhani komanso kukambirana ndi omvetsera. Limbikitsani onse kugwiritsa ntchito mwanzeru Kusanthula Malemba Tsiku ndi Tsiku—2000. Phatikizanipo ndemanga za m’kabuku kameneka zopezeka pa mawu oyamba, masamba 3-4. Pemphani ofalitsa kusimba mmene amachitira kuti apende lemba ndi ndemanga yake tsiku lililonse.
Mph. 20: “Ndidzabwezera Yehova Chiyani?” Kukambirana mwa mafunso ndi mayankho. Mukatha ndime yomaliza, onetsani chitsanzo cha kholo likuphunzitsa mwana kuti nayenso ali ndi udindo woika kangachepe mu bokosi la zopereka. Kapena, ngati mabokosi a zopereka sanapangidwe bwino, akulu aŵiri amene nkhaniyi yawakhudza mtima kwambiri angakambirane mwachidule zofunika kuchita.
Nyimbo Na. 157 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira January 31
Mph. 12: Zilengezo za pampingo. Kumbutsani onse kupereka malipoti awo a utumiki wakumunda a January. Tchulani mabuku ogaŵira mu February: Buku la Chimwemwe cha Banja. Sonyezani mmene mafunso atatu a m’bokosi la patsamba 12 angagwiritsidwire ntchito kuyamba kukambirana.
Mph. 15: Yankho la Funso la ‘Kuyang’anira.’ Nkhani yokambidwa ndi mkulu, kuchokera mu Nsanja ya Olonda ya July 15, 1999 masamba 29-31.
Mph. 18: Mmene Tingathandizire Ena Kudziŵa Chipembedzo Choona. Mtumiki wotumikira woyeneretsedwa akambirane ndi ofalitsa odziŵa bwino aŵiri kapena atatu za mmene anthu amachitira chidwi ndi Mboni za Yehova koma samvetsa bwinobwino mmene chipembedzo chathu chimasiyanira ndi zipembedzo zina. Pendani mfundo khumi za mu Galamukani! yachingelezi ya May 8, 1995 patsamba 20. Fotokozani mmene kudziŵa mfundo zimenezi kungathandizire munthu woongoka mtima kuona kusiyana pakati pa kulambira koona ndi konyenga ndiponso kufunika kophunzitsidwa ndi anthu a Yehova ndi kuyanjana nawo.
Nyimbo Na. 60 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira February 7
Mph. 5: Zilengezo za pampingo.
Mph. 20: Kuthandiza Ofalitsa Atsopano Kukwaniritsa Ziyeneretso. Nkhani yokambidwa ndi mkulu woyeneretsedwa kuchokera mu buku la Olinganizidwa Kutsiriza Uminisitala Wathu, kuyambira tsamba 97 ndime 2, mpaka tsamba 100 ndime 1. Chonde ŵerengani ndime 2, patsamba 98, ndi ndime 1, patsamba 99.
Mph. 20: Anasankha Mwanzeru. Nkhani yochokera mu Nsanja ya Olonda ya October 15, 1997 masamba 19-21, ndime 3-16. Simbani mawu olimbikitsa a apainiya, osonyeza chifukwa chake amaona kuti miyoyo yawo aigwiritsa ntchito m’njira yosangalatsa ndi yopindulitsa kwambiri. Limbikitsani omvetsera onse kulingalira zochita upainiya.
Nyimbo Na. 182 ndi pemphero lomaliza.