Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g98 10/8 tsamba 22-24
  • Kodi Ndingatani Kuti Ndizimvetsera Mwachidwi?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Ndingatani Kuti Ndizimvetsera Mwachidwi?
  • Galamukani!—1998
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Chitani Nazo Chidwi
  • Aphunzitsi Amphwayi Amagwetsa Mphwayi
  • Kumvetsera ‘Mosamalitsadi’
  • Mmene Tingapindulire Zambiri Pamisonkhano
  • Khalani Mmvetseri Wabwino
    Buku Lolangiza la Sukulu ya Utumiki Wateokalase
  • ‘Samaliranidi’
    Nsanja ya Olonda—2002
  • N’chifukwa Chiyani Ndiyenera Kumapita ku Misonkhano ya Mpingo?
    Galamukani!—2012
  • “Yang’anirani Mamvedwe Anu”
    Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
Onani Zambiri
Galamukani!—1998
g98 10/8 tsamba 22-24

Achinyamata Akufunsa Kuti . . .

Kodi Ndingatani Kuti Ndizimvetsera Mwachidwi?

“Ndinatha zaka zambiri ndikupezeka pamisonkhano koma osapindula nayo kwenikweni. Maganizo anga ankangokhala kwina.”—Matthew.

KODI munayamba mwakhalapo m’kalasi kapena pamsonkhano wachikristu ndiyeno mwadzidzidzi nkupeza kuti simukukumbukira zimene zinali kukambidwapo? Chabwino, ngati maganizo anu amangoyendayenda nthaŵi zina, sindinu nokha. Monga momwe nkhani yoyamba ija inanenera, achinyamata ambiri samatha kumvetsera kwa nthaŵi yaitali.a Komabe, mwakuyesetsa ndi kuwongolera maganizo anu, mungaphunzire kutchera khutu ndithu.

Chitani Nazo Chidwi

Tangoganizani za munthu wazamaseŵero wophunzitsidwa bwino. Mtumwi Paulo anati: “Yense wakuyesetsana adzikanizira zonse.” Ngati munthu wothamanga alola chilichonse kumdodometsa ngakhale kwa mphindi imodzi, angalephere mpikisano. Kuti apambane, ayenera kuphunzira kuganizira chinthucho—kusamvetsera phokoso la khamu la anthu omchemerera, kunyalanyaza ululu wake ndi kutopa kwake, kuchotseratu maganizo akulephera. Koma kodi nchiyani chimawathandiza anthu othamanga kuchita khama longa limenelo? Malinga ndi Mtumwi Paulo, amachita zimenezo kuti “alandire korona wakuvunda.”—mphotho zimene opambanawo amapatsidwa.—1 Akorinto 9:25.

Momwemonso, mufunikira kukhala ncholinga chomvetsera! Buku la William H. Armstrong lakuti Study Is Hard Work, limati: “Wophunzirayo ayenera kuchita chidwi ndi zimene akuphunzirazo. Palibe wina amene angakuchitireni chidwicho, ndipo palibe aliyense amene angawonjezere chidwi chanu koma inu mwininu.” Chidziŵitso ndicho chingakuthandizeni kulidziŵa dziko limene mukukhalamo. Mukamadziŵa zambiri, mpamenenso mumaphunzira zambiri. Miyambo 14:6 imati: “Wozindikira saona vuto m’kuphunzira.” Simungakumbukire zinthu zonse zimene munaphunzira kusukulu, komabe pang’ono pokha, sukulu imakuthandizani kukulitsa maluso akuganiza. (Yerekezerani ndi Miyambo 1:4.) Mutaphunzitsa maganizo anu kuti muzitha kumvetsera mwa chidwi mungapindule kwa moyo wanu wonse.

Aphunzitsi Amphwayi Amagwetsa Mphwayi

Komabe, achinyamata ena amadandaula kuti ngakhale aphunzitsi awo amaoneka ngati kuti alibe chidwi. Wachinyamata wina wotchedwa Jesse anati: “Aphunzitsi amangoima kutsogolo, nkunena kanthu kena, nkukuuzani zochita, ndiye nkukuŵerutsani. Ndikuganiza kuti nawonso ngamphwayi. Aphunzitsiwo samasonyeza kuti nzofunika, ndiye nafenso sitimasamala.”

Kodi ndiye muyenera kuganiza kuti kumvetsera mwachidwi nkuwononga nthaŵi basi? Ayi ndithu. Aphunzitsi ambiri mwina amatanganidwa ndi ntchito. Wachinyamata wotchedwa Collin anati: “Palibe aliyense amene amawamvetsera aphunzitsi, ndiyeno aphunzitsiwo nawo amangoganiza kuti palibe wofuna kuphunzira. Ndiye samalimbikira kuphunzitsa mwachidwi.”

Kaya mukhulupirira kapena simukhulupirira, koma mungathandize kuthetsa zimenezo. Motani? Mwakungomvetsera basi. Mphunzitsi atangokhala ndi mwana mmodzi wochita chidwi, chokhacho chingampangitse kuyambanso kukonda ntchito yake. Chabe kuti aphunzitsi ena alibe luso lokopa chidwi cha ana awo kwa nthaŵi yaitali. Komabe musanayambe kulota masana, dzifunseni kuti, ‘Kodi akudziŵadi zimene akunena?’ Ngati akudziŵadi, tsimikizani kufuna kuphunzira kanthu kena kwa iye. Mvetserani bwino—chitani chidwi! Muzikambitsirana ndi ena m’kalasi. Funsani mafunso anzeru. Buku lakuti How to Study in High School limati: “Ophunzira ambiri amaona kuti nkothandiza kujambula zithunzi, mawu, matchati, ndi matanthauzo a mawu, ndiponso mfundo zazikulu zimene mphunzitsi amalemba pabolodi kapena zimene amanena motsimikiza.”

Kumvetsera ‘Mosamalitsadi’

Komabe, kutakhala kumvetsera pamisonkhano yachikristu, mungapindule zambiri kapena kuphonya zambirinso. Jesse anavomereza kuti: “Nthaŵi zina achinyamata samamvetsera zinthu zonga misonkhano chifukwa samadziŵa kuti misonkhanoyo njofunika.” Pa Ahebri 2:1 tikulamulidwa kuti “tiyenera kusamaliradi zimene tidazimvazi kuti kapena tingatengedwe ndi kusiyana nazo.” Mutangochoka pamsonkhano wampingo, kodi mumakumbukira kanthu kena kamene kanatchulidwa m’nkhani iliyonse? Kodi nthaŵi zina mumaona kuti simungakumbukire ngakhale omwe anakamba nkhanizo?

Panonso, yangokhala mfundo yakuona kufunika kwa zimene mukuphunzira. Potitu moyo wanu weniweniwo ukukhudzidwa! (Yohane 17:3) Mfundo ina yoyenera kuiganizira njakuti: Pamene mukuphunzira Baibulo, mukuphunzira kuganiza ngati Mulungu mwiniyo! (Yesaya 55:8, 9) Ndipo mukamagwiritsira ntchito zimene mukuphunzira, mukuvala chimene Baibulo limatcha kuti “umunthu watsopano.” (Akolose 3:9, 10, NW) Komanso, mukamalephera kumvetsera, simungasinthe moyo wanu monga momwe muyenera kusinthira; mudzingokhalabe choncho osakula mwauzimu. Yehova amadziŵa kuti tonsefe timakonda kulola maganizo athu kuyendayenda. Nchifukwa chake amatichonderera kuti: “Mverani Ine mosamalitsa, . . . Tcherani khutu lanu, mudze kwa Ine, imvani, mzimu wanu nudzakhala ndi moyo.”—Yesaya 55:2, 3.

Mmene Tingapindulire Zambiri Pamisonkhano

Ngakhale zili choncho, kumvetsera kwambiri pamisonkhano kungakhale kovuta poyamba. Koma ofufuza ena amatero kuti tikamayesera kutchera khutu kwambiri, ubongo wathu umazoloŵeranso kuichita ntchitoyo. Matthew, yemwe tinamgwira mawu kuchiyambi kwa nkhaniyi, maganizo ake anadzalekano kuyendayenda misonkhano ili mkati. Anati: “Ndinaona kuti ndiyenera kudziphunzitsa kumvetsera. Patapita kanthaŵi, zimakhala bwino, ndipo ungamamvetsere kwa nthaŵi yaitalidi.” Matthew anatchulanso mfundo imodzi yaikulu yomwe inapangitsa misonkhano kumsangalatsa. Anati: “Ndimaphunzira pasadakhale.” Wachinyamata wina wotchedwa Charese nayenso anati: “Ngati ndakonzekera, ndimaona kuti pamsonkhanopo ndimakhalapodi. Nkhani zake zimamveka bwino ndipo zimakhala zatanthauzo kwa ine.”

Nkofunikanso kukana malingaliro osokoneza. Nzoona kuti mungakhale ndi zinthu zingapo zoyeneradi kukudetsani nkhaŵa: mayeso omwe akubwera mlungu wamaŵa, kudandaula chifukwa chosemphana maganizo ndi munthu wina, ndalama zina zimene muyenera kulipira posachedwa. Koma Yesu anapereka uphungu uwu: “Ndani wa inu ndi kudera nkhaŵa angathe kuwonjezera pa msinkhu wake mkono umodzi? Chifukwa chake musadere nkhaŵa za maŵa; pakuti maŵa adzadzidera nkhaŵa iwo okha. Zikwanire tsiku zovuta zake.” (Mateyu 6:27, 34) Kutchera khutu pamisonkhano yachikristu sikuthetsa mavuto anu, komabe kungakutsitsimuleni mwauzimu kotero kuti mudzakhoza kuwasamala mavutowo bwino lomwe.—Yerekezerani ndi 2 Akorinto 4:16.

Kutchera khutu kungakuthandizeninso kusumika maganizo anu. Matthew anati: “Ndimayembekezera kumva zimene wokamba nkhani ati anene m’nkhani yake ndi kumva mmene aikambire.” Dzifunseni kuti, ‘Kodi mfundo zazikulu nziti m’nkhani imeneyi? Kodi zimene zikukambidwazi ndingazigwiritsire ntchito bwanji?’ Kuyembekezera zimene wokamba nkhani ati anene kungakuthandizeninso kumvetsera mwa chidwi. Tayesani kutsagana naye. Onani mfundo za m’Malemba zimene akugwiritsira ntchito. Lingalirani mfundo zakezo nkuzimanga pamodzi. Lembani manotsi achidule omveka bwino. Ngati nkhani ina njofuna kuti omvetsera ayankhepo, inunso yankhanipo! Mukamatero maganizo anu amakhazikika osayendayenda.

Koma nzoona kuti kumvetsera kungakhale kovuta makamaka ngati wolankhulayo nayenso alibe chidwi kapena ngati akulankhula mwamphwayi. Kumbukirani zimene Akristu a m’zaka za zana loyamba ankaganizira za luso lakulankhula la mtumwi Paulo: “Maonekedwe a thupi lake ngofooka, ndi mawu ake ngachabe.” (2 Akorinto 10:10) Koma Paulo anawayankha kuti: “Ndingakhale ndili wosaphunzira m’manenedwe, koma sinditero m’chidziŵitso.” (2 Akorinto 11:6) Inde, omvetsera akewo akanangosamala zimene Paulo anali kulankhula, bwenzi ataphunzira “zakuya za Mulungu.” (1 Akorinto 2:10) Momwemonso, ngati mungatchere khutu ndi kumvetsera, mungaphunzire ngakhale kwa wokamba nkhani “wamphwayi.” Ndani angadziŵe? Mwina angafotokoze mfundo ina kapena kutanthauzira lemba lina mwa njira imene simunayimvepo kale.

Mawu a Yesu pa Luka 8:18 ngomveka bwino, akuti: “Yang’anirani mamvedwe anu.” Nzoona kuti kuphunzira kutchera khutu—ndi kukhazikika maganizo—zimafuna khama ndi kuyesayesa. Koma potsirizira mudzapindula nazo. Kuphunzira kutchera khutu kudzatanthauza kukhoza kusukulu, ndiponso chofunika kwambiri, kukula mwauzimu!

[Mawu a M’munsi]

a Onani nkhani yakuti “Achinyamata Akufunsa Kuti . . . Nchifukwa Chiyani Sinditha Kumvetsera?” m’kope lathu la August 8, 1998.

[Chithunzi patsamba 24]

Kuchita chidwi ndi zimene mukumva ndiko kumathandiza kutchera khutu

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena