Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 9/00 tsamba 1
  • Madalitso a Yehova Amatilemeretsa

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Madalitso a Yehova Amatilemeretsa
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2000
  • Nkhani Yofanana
  • Sitinakhalepo ndi Zabwino Zotere Mwauzimu!
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1996
  • Kodi Ndinu “Wolemera kwa Mulungu”?
    Nsanja ya Olonda—2007
  • “Makhalidwe Amene Mzimu Woyera Umatulutsa” Amalemekeza Mulungu
    Nsanja ya Olonda—2011
  • Madalitso a Yehova Amatilemeretsa
    Nsanja ya Olonda—2001
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2000
km 9/00 tsamba 1

Madalitso a Yehova Amatilemeretsa

1 Nthaŵi zambiri anthu amaona kulemera kwa munthu malinga n’kuchuluka kwa ndalama zimene amalandira. N’chifukwa chake anthu ambiri amaona anthu a ndalama kukhala anthu achimwemwe kwambiri ndiponso amoyo wokhutiritsa zedi. Komabe, anthu amene amaganiza kuti ndalama zingagule chimwemwe amalakwitsa kwabasi. (Mlal. 5:12) Anthu ‘ofuna kukhala achuma’ mwakuthupi alibiretu chimwemwe chokhalitsa. (1 Tim. 6:9) Komano, atumiki a Yehova ndi achimwemwe kwabasi ndiponso ndi amene ali olemera kwambiri padziko lapansi. (Miy. 10:22; Chiv. 2:9) Motani?

2 Umboni wa Kulemera Kwathu: Tili ndi nzeru zauzimu zochuluka ndiponso chidziŵitso cha Mawu a Mulungu, Baibulo. Mwa gulu lake la padziko lapansi, Yehova akupitiriza kutiphunzitsa za iyemwini ndi Mwana wake, kuti tipindule kwamuyaya. Chidziŵitso cholondola chimatichititsa kuyandikana ndi Yehova ndiponso kukhala naye paunansi wolimba. (Yak. 4:8) Kusiyanitsa chabwino ndi choipa ndiponso kutsatira malamulo a Mulungu kumatitetezera kumatenda ena ndiponso ngozi zina. Tili ndi chikhulupiriro kuti Yehova adzatipatsa zinthu zimene zidzabweretsa chikhutiro chaumulungu ndi mtendere wa mumtima.—Mat. 6:33.

3 Timakhala mwamtendere ndi mogwirizana ndi abale athu auzimu chifukwa timakulitsa zipatso za mzimu wa Mulungu. Popeza kuti ndife ogwirizanitsidwa n’chikondi chimene chili chomangira cholimba, tikakumana ndi mavuto kapena masoka sitiyenera kuona kuti Mulungu kapena abale athu atisiya.—Agal. 6:10.

4 Miyoyo yathu ili ndi tanthauzo lenileni ndiponso cholinga chenicheni. Timauona kukhala mwayi wapamwamba zedi kuchita nawo ntchito yapadziko lonse yolalikira uthenga wabwino. Izi zimatipatsa chimwemwe chokhalitsa pamene tikuthandiza ena kukhala paunansi wabwino ndi Mulungu ndi kutumikira nafe mogwirizana m’kulambira koyera. Chuma chathu chamtengo wapatali zedi cha utumiki chimalemekeza Yehova ndipo chimatikhutiritsa kuti tathandiza nawo kuyeretsa dzina lake. Timakhalabe ndi maganizo abwino, popeza kuti chiyembekezo chathu cha m’tsogolo chidzakwaniritsidwa posachedwa.

5 Kusonyeza Kuyamikira Kwathu: Tiyeni nthaŵi zonse tisonyeze kuyamikira madalitso a Yehova, amene amatichititsa kukhaladi anthu olemera kwambiri padziko lapansi. (Miy. 22:4) Tsiku lililonse kukhala ndi nthaŵi yosinkhasinkha zimene tili nazo kumatisonkhezera kum’thokoza Yehova ndiponso kupitiriza kumulambira ndi mtima wathu wonse chifukwa cha chikondi chake chochuluka.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena