Kuthandiza Ana Athu Kukhalabe M’choonadi—Mbali Yoyamba: N’kotheka
1 N’zosangalatsa kuona m’zaka zaposachedwapa chiŵerengero cha ofalitsa chimene tinali nacho Malaŵi muno chikukwera kwambiri. N’zoonekeratu kuti Yehova akudalitsa ntchitoyi, monga ananenera Paulo pa 1 Akorinto 3:6 kuti: “Ndinawoka ine, anathirira Apolo; koma Mulungu anakulitsa.” Popeza chaka chatsopano chautumiki chikuyamba mwezi uno wa September, tiika maganizo athu pa kuthandiza ana athu kukhalabe m’choonadi monga cholinga cha dziko lathu lino.
2 Kuphatikiza pa munda umene timalalikira, tili ndi munda wina waukulu woti tipezemo ofalitsa Ufumu—ana athu! Ana ambiri akukulira m’mabanja achikristu. Kodi tikugwiritsa ntchito mokwanira mwayi waukulu umenewu? Zikuoneka kuti sitikutero.
3 Kalembera wa Ana: M’kalembera amene anachitidwa m’mipingo 650 m’Malaŵi muno, anapeza kuti ana (a abale) 16,700 a zaka pakati pa 10 ndi 20 sanakhalebe ofalitsa. Mwa ana ameneŵa, ana 1,291 anali ana a akulu ndi atumiki otumikira. Izi zikusonyeza kuti m’mipingo 680 ya m’Malaŵi muno mutha kupezeka ana ambiri kuposa 16,700 a misinkhu yoti n’kukhala ofalitsa amene pakalipano sali ofalitsa. Akanakhala kuti onseŵa anali achangu muutumiki wakumunda, bwenzi tsopano tili ndi ofalitsa oposa 60,000.
4 Chokhumudwitsa kwambiri n’choti ambiri mwa ana ameneŵa ndi ana a akulu ndi atumiki otumikira. China cha ziyeneretso za atumiki otumikira chalembedwa pa 1 Timoteo 3:12 kuti: “Atumiki akhale . . . akuweruza bwino ana awo, ndi iwo a m’nyumba yawo ya iwo okha.” Mkulu, malinga ndi kunena kwa vesi 4 ayenera kukhala mwamuna “woweruza bwino nyumba yake ya iye yekha, wakukhala nawo ana ake omvera iye ndi kulemekezeka konse.” Ndithudi, amuna ameneŵa ayenera kukhala chitsanzo pophunzitsa ndi kulangiza ana awo kukhala atumiki a Yehova. Kodi mkulu kapena mtumiki wotumikira angakhale bwanji chitsanzo chabwino kwa ena ngati ana ake saloŵa muutumiki? Choncho, akulu ndi atumiki otumikira inu, ngati ana anu sanayambebe kufalitsa, lingalirani nkhaniyi mozama ndiponso mwapemphero!
5 Sachita Maphunziro a Baibulo: Chomvetsa chisoni china chimene apeza m’kalemberayu n’chakuti makolo ambiri sachita n’komwe maphunziro a Baibulo ndi ana awo. Mwa ana 16,700 amene si ofalitsa azaka pakati pa 10 mpaka 20, ana 5,906 sanali kuchititsidwa phunziro ndipo ana 5,333 anali kuchita maphunziro a Baibulo a banja osakhazikika. Mwachidule, ambiri mwa ana 16,700 ameneŵa sachita phunziro la Baibulo lokhazikika lowathandiza kupita patsogolo m’choonadi. N’zomvetsadi chisoni bwanji! Mpake kuti anaŵa sanayambebe ntchito yolalikira!
6 Ndithu makolo afunika kulimbikira zedi, makamaka akulu ndi atumiki otumikira. Lerolino, Satana ndi dziko lake akupondereza kwambiri achinyamata, ndipo ambiri aloŵerera m’dziko. Tikuthandiza atsopano kuloŵera pakhomo la kumaso kwa Nyumba ya Ufumu, pomwe ana athu ambiri akutulukira ku khomo la kumbuyo.
7 Tikukupemphani makolonu, inde, kukuchondererani kulingalira mozama zimene mukuchita kuti muthandize ana anu panjira ya kumoyo. (Deut. 6:6, 7; Mat. 7:13, 14) Ngati simunayambebe kuphunzira nawo, yambani lero. Ngati sanayambebe kupereka malipoti, lingalirani zimene mungachite kuti muwathandize kuyamba mwamsanga. M’nkhani zotsatira za nkhani zoterezi, tidzafotokoza zinthu zimene tingachite kuti tithandize ana athu kukhalabe m’choonadi.