Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w99 10/1 tsamba 28-31
  • Olimba Pokana Kuchita Tchimo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Olimba Pokana Kuchita Tchimo
  • Nsanja ya Olonda—1999
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kukana N’kofunikadi Lerolino
  • Kuphunzira Kuchokera Kwa Mnyamata Yemwe Anakana
  • Kukana Chisonkhezero cha Mabwenzi
  • Kukana​—Ndi Nkhani ya Moyo ndi Imfa
  • ‘Ndingachitirenji Choipa Chachikulu N’kuchimwira Mulungu?’
    Nsanja ya Olonda—2014
  • Lingaliro Laumulungu la Khalidwe Loyera
    Nsanja ya Olonda—2000
  • Nkhondo ya Kuchita Chimene Chiri Chabwino
    Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi
  • Yehova Amatithandiza Kuti Zinthu Zizitiyendera Bwino
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2023
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1999
w99 10/1 tsamba 28-31

Olimba Pokana Kuchita Tchimo

“PAMENE ndinali wachinyamata, ndinkagwira ntchito m’sitolo,” akulongosola motero Timothy, “mnzanga wa kuntchito anandiitanira kunyumba kwake. Iye anandiuza kuti makolo ake achoka, ndipo kunyumba kwawoko kubwera atsikana, mwakuti tikakhala ndi mwayi wochita nawo zachiwerewere.” Achinyamata ambiri lerolino angakopeke msanga ndi kuvomera chiitano choterechi. Koma kodi Timothy anayankha kuti chiyani? “Ndinamuuziratu nthaŵi yomweyo kuti sindipita naye kwawoko. Ndinamuuzanso kuti chifukwa cha chikumbumtima changa cha Chikristu, sindikufuna kugonana ndi mkazi yemwe sin’nakwatirane naye.”

Mmene Timothy anali kunena zimenezo, sanadziwe kuti msungwana wina yemwe amagwira naye ntchito pomwepo anali kumvetsera. Msungwanayu anadabwa kwambiri ndi kukana kwakeko, moti msungwanayu anafuna kuti amuyese payekha, ndipo anatero mobwerezabwereza​—koma nthaŵi zonse Timothy anakanitsitsa, monga momwe tionere kutsogoloku.

Kukumana ndi mayesero, sikunayambe m’nthaŵi yathu ino ayi. Zaka 3,000 zapitazo, Mfumu Solomo inalemba kuti: “Mwananga, akakukopa ochimwa usalole. . . . Letsa phazi lako ku mayendedwe awo.” (Miyambo 1:10,15) Yehova mwiniyo analamula mtundu wa Israyeli kuti: “Usatsata unyinji wa anthu kuchita choipa.” (Eksodo 23:2) Inde, nthaŵi zina tiyenera kukana, kusalola mayesero omwe angatitsogolere kuchita tchimo, ngakhale kuti zomwe tikuyesedwa nazozo n’zoti ambiri sachita.

Kukana N’kofunikadi Lerolino

Kukana kuchita choipa kwakhala kovuta kwambiri, ndipo masiku ano kuvutako kukuwonjezeka, chifukwa tikukhala m’masiku omwe Baibulo likuwatcha “masiku otsiriza” a dongosolo lino la zinthu. Ulosi wa m’Baibulo n’ngwoona. Anthu ochuluka akhala “okonda zokondweretsa munthu” ndi chiwawa, zomwe sizimasonyeza mkhalidwe wauzimu ndi waumunthu. (2 Timoteo 3:1-5) Pulezidenti wina wa payunivesite, yemwenso ndi Mjezwiti ananena kuti: “Tinali ndi miyezo yachikhalidwe yomwe tsopano yatsutsidwa ndi kupezeka yosayenera kapenanso yachikale. Tsopano kukuoneka kuti kulibe m’pang’ono pomwe miyezo yolimbikitsira chikhalidwe chabwino.” M’lingaliro lofananalo, mkulu wa oweruza milandu anati: “Palibe kusiyana pakati pa chabwino ndi choipa tsopano. Zonse n’zosadziŵika bwino . . . Anthu ochepa chabe ndi amene amatha kusiyanitsa chabwino ndi choipa. Tchimo tsopano lafala kwambiri ndipo kulichita sikukuonekanso ngati n’kulakwa.”

Mtumwi Paulo analemba za anthu a malingaliro oterowo kuti: ‘Ngwodetsedwa m’nzeru zawo, oyesedwa alendo pa moyo wa Mulungu, chifukwa cha chipulukiro chili mwa iwo, chifukwa cha kuumitsa kwa mitima yawo; amenewo popeza sazindikiranso kanthu konse, anadzipereka okha kuti akhumbe zonyansa, kuti achite chidetso chonse mu umbombo.’ (Aefeso 4:18, 19) Koma iwo akuyembekeza kukumana ndi mavuto. Yesaya ananenetsa kuti: “Tsoka kwa iwo amene ayesa zoipa zabwino, ndi zabwino zoipa; amene aika mdima m’malo mwa kuyera, ndi kuyera m’malo mwa mdima.” (Yesaya 5:20) Kuwonjezera pa kututa zimene akufesa, posachedwa “tsoka” lidzawagweranso​—chiweruzo choopsa cha Yehova.​—Agalatiya 6:7.

“Pophuka oipa ngati msipu, ndi popindula ochita zopanda pake; chitero kuti adzawonongeke kosatha,” imatero Salmo 92:7. Mwa mawu ena, kututa zochuluka m’zoipa kumeneku sikudzapitirira kosatha, kukumachititsabe moyo kukhala wovuta kwa onse. Ndi iko komwe, Yesu ananena kuti “mbadwo” womwe ukuchirikiza kuipa konseku ndi umene Mulungu adzauwononge pa “chisautso chachikulu.” (Mateyu 24:3, 21, 34) Choncho ngati ife tikufuna kudzapulumuka chisautso chachikulu chimenecho, tiyenera kudziŵa kusiyanitsa chabwino ndi choipa mogwirizana ndi miyezo ya Mulungu; ndiponso, tifunika kukhala ndi mphamvu ya mikhalidwe yabwino kuti tithe kukana kulakwa m’njira iliyonse. Ngakhale kuti zimenezi sizofeŵa, Yehova watisonyeza zitsanzo zolimbikitsa kwambiri za m’nthaŵi ya m’Baibulo komanso zamakono.

Kuphunzira Kuchokera Kwa Mnyamata Yemwe Anakana

Kukana chisembwere ndi chigololo kukuoneka kukhala kovuta kwenikweni, ngakhale kwa ena m’mpingo wachikristu. Timothy, yemwe tam’tchula m’ndime zoyambirira, anakumbukira ndi kutsanzira chitsanzo chabwino cha mnyamata uja Yosefe, yemwe nkhani yake yalembedwa m’Malemba pa Genesis 39:1-12. Yosefe anasonyeza mphamvu ya mikhalidwe yabwino pamene mobwerezabwereza anaitanidwa ndi mkazi wa mdindo wa ku Igupto, Potifara, kuti agone naye. Malemba akulongosola kuti, Yosefe “anakana, nati . . . ‘ndikachita choipa chachikulu ichi bwanji ndi kuchimwira Mulungu?’”

Kodi Yosefe anapeza bwanji mphamvu ya mikhalidwe yabwinoyo yomwe inam’theketsa kukana zofuna za mkazi wa Potifara tsiku ndi tsiku? Choyamba, anaona ubwenzi wake ndi Yehova kukhala wamtengo wapatali kusiyana ndi zosangalatsa zakanthaŵi. Komanso, Yosefe anadziwa bwino za mapulinsipulo amikhalidwe yabwino, ngakhale kuti panthaŵiyo panalibe mpambo wa Malamulo a Mulungu (Chilamulo cha Mose kunalibe), Iye anadziŵa kuti kuchita chisembwere ndi mkazi wa Potifara wachimasomasoyo kunali kuchimwira osati mwamuna wake yekhayo komanso kuchimwira Mulungu.​—Genesis 39:8, 9.

Mwachionekere, Yosefe anazindikira kufunika kwa kusadzutsa ngakhale chilakolako chokha chomwe chingabutse kutenthedwa m’thupi kosalamulirika. N’kwanzeru kuti Mkristu atsatire chitsanzo cha Yosefechi. Nsanja ya Olonda yachingelezi ya July 1, 1957, inati: “Ayenera kudziŵa kufooka kwa umunthu wake, ndi kuti asaganize kuti angathe kutsata zikhumbo zamalingaliro ndi kuleka pamene waona kuti zayamba kupyola malire a Malemba. Ngakhale ngati angakwanitse kuchita zimenezo poyamba, pang’ono ndi pang’ono adzalumpha malire amenewo ndi kulowa mu tchimo. Zimenezi zingachitikedi, chifukwatu zilakolako zomwe zimakhalapo zimakhala zamphamvu ndipo zimazikika mwa munthu. Ndipo zikafika pamenepo kumadzakhala kovuta zedi kuti azichotse m’malingaliro mwake. Choncho njira yabwino yodzitetezera nayo, ndiyo kukaniza zilakolakozo pamene zangoyamba.”

Kukaniza zilakolakozo pamene zikuyamba kumene n’kosavuta, pamene tikukulitsa chikondi cha zinthu zabwino ndi chidani cha zinthu zoipa. (Salmo 37:27) Koma tifunikabe kugwirirapo ntchito, kuti chimenechi chikhale chizoloŵezi chathu. Ngati titero ndi chithandizo cha Yehova, kukonda kwathu chabwino ndi kunyansidwa nacho choipa kudzakhala kwamphamvu. Komabe pakali pano, tiyenera kukhalabe atcheru, monga momwe Yesu anasonyezera, kupitirizabe kupemphera kuti tisaloŵe m’kuyesedwa ndi kuti tipulumutsidwe kwa woipayo.​—Mateyu 6:13; 1 Atesalonika 5:17.

Kukana Chisonkhezero cha Mabwenzi

Mabwenzi nawonso angatisonkhezere kuchita tchimo. Wachinyamata wina anavomereza akumati: “Ndikukhala ndi moyo wa paŵiri​—umodzi wa kusukulu ndi wina wa kunyumba. Kusukulu ndimacheza kwambiri ndi anzanga omwe amalankhula zotukwana nthaŵi zonse. Ndipo inenso ndikuyamba kutengera malankhulidwe amenewo. Kodi ndichitenji pamenepa?” Chofunika ndicho kulimba mtima kuti mukhale osiyana nawo, ndipo njira imodzi yokhalira wolimba mtima ndiyo kuwerenga ndi kusinkhasinkha zolembedwa m’Baibulo, lomwe limatiuza za atumiki okhulupirika a Mulungu monga Yosefe. Zitsanzo zina zabwino ndi za Danieli, Sadrake, Misake, ndi Abedinego​—achinyamata anayi omwe analimba mtima kuchita zosiyana ndi mabwenzi awo.

Pamene ankaphunzitsidwa limodzi ndi achinyamata ena m’nyumba ya mfumu ya Babulo, Aisrayeli anayi ameneŵa ankayenera kudya “gawo la chakudya cha mfumu tsiku ndi tsiku.” Posafuna kuswa zomwe Chilamulo cha Mose chinanena pa nkhani ya zakudya, iwo anakana chakudya chimenecho. Kuchita zimenezo panafunika kulimba mtima​—makamaka chifukwa “chakudya cha mfumu,” chinalidi chosiririka kwabasi. Achinyamata ameneŵa anasonyezadi chitsanzo chabwino ndithu kwa Akristu amakono omwenso angayesedwe, ngakhale kukakamizidwa kumwetsa mowa, kapena kumwa mankhwala osokoneza bongo ndi kusuta fodya!​—Danieli 1:3-17.

Sadrake, Misake, ndi Abedinego anasonyeza zoona zenizeni m’zomwe Yesu Kristu ananena pambuyo pake kuti: “Iye amene akhulupirika m’chaching’onong’ono alinso wokhulupirika m’chachikulu.” (Luka 16:10) Kulimba mtima kwawo m’nkhani yaing’ono ya zakudya, kunawadzetsera zotsatira zabwino, Yehova sanakayikire kuwalimbitsa pamene m’tsogolo mwake anakumana ndi chiyeso chokulira. (Danieli 1:18-20) Chiyeso chimenechi chinawagweradi pamene anawalamula kulambira nawo fano, ndi kuti ngati salambira adzaponyedwa m’ng’anjo ya moto. Achinyamata atatu ameneŵa, molimba mtima, anakhalabe ofunitsitsa kulambira Yehova yekha, ndi kum’khulupirira ndi mtima wonse zivute zitani. Kachiŵirinso Yehova anawadalitsa chifukwa cha chikhulupiriro ndi kulimba mtima kwawo​—panthaŵi ino anawateteza mozizwitsa m’malawi a moto momwe anaponyedwa, m’ng’anjo yotentha kwambiri.​—Danieli 3:1-30.

M’mawu a Mulungu muli zitsanzo zina zambiri za ena amene anakana kuchita tchimo. Mose anakana “kutchedwa mwana wake wa mwana wamkazi wa Farao,” ngakhale kuti kumeneku kukanam’patsa mwayi ‘wokhala nazo zokondweretsa za zoipa kwa kanthaŵi’ mu Igupto. (Ahebri 11:24-26) Mneneri Samueli anakana kugwiritsa ntchito ulamuliro wake molakwa pamene anakana kulandira ziphuphu. (1 Samueli 12:3, 4) Atumwi a Yesu Kristu anakana mwamphamvu pamene analamulidwa kusiya kulalikira. (Machitidwe 5:27-29) Yesu mwiniyo anakana kuchita tchimo motsimikiza mtima​—m’maola otsirizira a moyo wake, pamene asilikali “anam’patsa vinyo wosanganiza ndi mure.” Kumwa vinyo panthaŵi imeneyo kukanafooketsa cholinga chake chomwe panthaŵi imeneyi chinafunika kwambiri.​—Marko 15:23; Mateyu 4:1-10.

Kukana​—Ndi Nkhani ya Moyo ndi Imfa

Yesu anati: “Loŵani pa chipata chopapatiza; chifukwa chipata chili chachikulu, ndi njira yakumuka nayo kukuwonongeka ili yotakata; ndipo ali ambiri amene aloŵa pa icho. Pakuti chipata chili chopapatiza, ndi ichepetsa njirayo yakumuka nayo kumoyo, ndimo akuchipeza chimenecho ali oŵerengeka.”​—Mateyu 7:13, 14.

Njira yotakata ambiri amaikonda chifukwa chakuti n’njosavuta kuyendamo. Oyendamo ake n’ngofuna kungodzikhutiritsa, kutsata zokhumba zathupi ndi njira zake, ndipo samafuna kukhala osiyana ndi ena, koma kukhala ogwirizana ndi dziko la Satana lino. Amaona malamulo ndi mapulinsipulo a Mulungu kukhala opanikiza kwa iwo. (Aefeso 4:17-19) Komabe, Yesu ananenetsa kuti njira yotakata imatsogolera “kukuwonongeka.”

Nanga n’chifukwa chiyani Yesu ananena kuti ochepa okha ndiwo asankha njira yopapatiza? Kwenikweni n’chifukwa chakuti ndi anthu ochepa amene amafuna kutsogozedwa ndi malamulo a Mulungu ndi mapulinsipulo ake kuti awathandize kupewa zokopa kapena mipata imene ingawakopere m’tchimo. Kuwonjezera pamenepo, ndi oŵerengeka okha amene amafuna kulimbana ndi zilakolako zoipa, kusonkhezeredwa ndi mabwenzi, ndi kuopa kunyozedwa chifukwa cha njira yomwe asankha kuyendamo.​—1 Petro 3:16; 4:4.

Ameneŵa amamvetsetsadi mmene mtumwi Paulo anamvera pamene amalongosola za nkhondo imene anamenya polimbana ndi tchimo. Mofanana ndi dziko lamakonoli, Roma ndi Girisi wa m’nthaŵi ya Paulo anapereka njira yotakata, mmene anthu sankawopa kuchita tchimo. Paulo analongosola kuti malingaliro ake, omwe anadziŵa chabwino, analandira mphotho chifukwa cha kulimbana ndi thupi lake, lomwe linali litatsata kuchita tchimo. (Aroma 7:21-24) Inde, Paulo anadziŵa kuti thupi lake linali mtumiki wabwino, koma mbuye woipa, choncho anaphunzira kukana zokhumba zake. Iye analemba kuti: “Ndipumphuntha thupi langa, ndipo ndiliyesa kapolo.” (1 Akorinto 9:27) Kodi anakwanitsa bwanji kuchita zimenezo mwaluso? Sanachite zimenezo ndi mphamvu yakeyake, yomwe inali yochepa zedi, koma chifukwa cha thandizo la mzimu wa Mulungu.​—Aroma 8:9-11.

Zotsatira zake zinali zakuti, Paulo, ngakhale anali wopanda ungwiro, anasungabe umphumphu wake kwa Yehova kufikira mapeto. Atatsala pang’ono kumwalira analemba kuti: “Ndalimbana nako kulimbana kwabwino, ndatsiriza njirayo, ndasunga chikhulupiriro: chotsalira wandiikira ine korona wa chilungamo.”​—2 Timoteo 4:7, 8.

Pamene tikulimbana ndi kupanda ungwiro kwathuku, taonani zitsanzo zabwino zomwe tiyenera kuzitsatira, osati za Paulo zokha ayi, komanso za awo amene anapereka zitsanzo zabwino kwa iyenso monga​—Yosefe, Mose, Danieli, Sadrake, Misake, Abedinego, ndi ena ambiri. Ngakhale kuti anali anthu opanda ungwiro, aliyense wa amuna okhulupirira ameneŵa anakana kuchimwa, osati chifukwa cha kuuma mtima, kapena kuti mitima yawo inali yaliuma, koma chifukwa chakuti anali ndi mphamvu ya makhalidwe abwino yopatsidwa kwa iwo mwa mzimu wa Yehova. (Agalatiya 5:22, 23) Anali amuna auzimu. Anamva njala ya mawu otuluka m’kamwa mwa Yehova. (Deuteronomo 8:3) Mawu ake ndiwo anali moyo wawo. (Deuteronomo 32:47) Choposa zonse, anakonda Yehova ndi kumuopa, ndipo ndi chithandizo chake, moleza mtima anakulitsa udani pa tchimo.​—Salmo 97:10; Miyambo 1:7.

Tiyeni tiwatsanzire. Ndithudi, kuti tipitirizebe kukana kuchita tchimo mwa njira iliyonse, tifunikira mzimu wa Yehova monga momwe iwo anachitira. Yehova amapereka mzimu wake moolowa manja ngati ife tim’pempha modzichepetsa, kuphunzira Mawu ake, ndi kusaphonya misonkhano yachikristu.​—Salmo 119:105; Luka 11:13; Ahebri 10:24, 25.

Timothy, yemwe tam’tchula m’ndime zoyamba zija, anali wachimwemwe chifukwa chakuti sananyalanyaze zofunika zazikulu zauzimu. Msungwana yemwe anamvetsera nawo makambirano a Timothy ndi mnzake wogwira naye ntchito uja, anakopeka ndi chiyero cha Timothy, ndipo pambuyo pake anaitanira Timothy kunyumba kwake pamene mwamuna wake anali atachoka. Timothy anakana kupitako. Anachitabe khama ngati mkazi wa Potifara, ndipo anabwereza kangapo kumuitanira kunyumba kwakeko. Motsimikiza mtima koma mwaulemu, Timothy anakana nthaŵi zonse zimene msungwanayo anayesa. Ndipo anam’patsanso mkaziyu umboni wochokera m’Mawu a Mulungu. Akuyamikira Yehova mozama chifukwa chomulimbitsira mikhalidwe yabwino kuti athe kukana. Tsopano Timothy akusangalala chifukwa anakwatira Mkristu mnzake wosangalatsa zedi. Ndithudi, Yehova adzadalitsa ndi kulimbitsa onse ofuna kusunga umphumphu wawo wachikristu mwa kukana kuchita tchimo.​—Salmo 1:1-3.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena