Nyimbo 214
Kulondola Njira ya Mulungu ya Moyo
1. Moyo mphatso ya mtengo wapatali,
Mwa Kristuyo! Tiusamalire.
Tivomereza, kwa inu Yehova:
Njira yanu itisangalatsa.
2. Moyenelera tiwopa inu Ya.
Tipeza chidziŵitso ndi nzeru.
Mulamulo lanu tisangalala;
Tiyenda nalo mwa umulungu.
3. Moyo ngwachifuno ndinu wabwino.
Mwa Mwana’nu taphunzira moyo.
Musakonde dziko ndi zinthu zake.
Mufunefune chisangalalo.
4. Tithandizeni kuphunzitsa moyo,
Popeza Ufumu wayandika.
Tilalikire kwa ofatsa m’dziko,
Mubwezeretsa kulambirako.