Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 7/02 tsamba 5
  • Khutiritsani Zosoŵa Zanu Zauzimu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Khutiritsani Zosoŵa Zanu Zauzimu
  • Utumiki wathu wa Ufumu—2002
  • Nkhani Yofanana
  • ‘Mvetserani Ndipo Wonjezerani Kuphunzira’
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2001
  • Mvetserani ndi Kuphunzira
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2013
  • Misonkhano Yachigawo ya 1999 ya “Mawu Aulosi a Mulungu”
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1999
  • Msonkhano Wachigawo wa mboni za Yehova wa “Amithenga a Mtendere Waumulungu” wa 1996
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1996
Onani Zambiri
Utumiki wathu wa Ufumu—2002
km 7/02 tsamba 5

Khutiritsani Zosoŵa Zanu Zauzimu

1 Msonkhano wathu Wachigawo womwe ukubwerawu, wakuti “Olengeza Ufumu Achangu” udzatipatsa mwayi wapadera wokhutiritsa zosoŵa zathu zauzimu. Mofanana ndi chakudya chabwino chakuthupi, pulogalamuyi idzatipatsadi thanzi mwauzimu “m’mawuwo a chikhulupiriro.” (1 Tim. 4:6) Idzatithandiza kuyandikana kwambiri ndi Yehova. Ndipo tikuyembekeza kukalangizidwa ndi kukalimbikitsidwa kuti tithe kupirira ziyeso zimene timakumana nazo pamoyo wathu. Yehova akutitsimikizira kuti: “Ine ndidzakulangiza ndi kuphunzitsa iwe za njira ukayendayo; ndidzakupangira ndi diso langa la kuyang’ana iwe.” (Sal. 32:8) Ndife odala kwabasi kuti Yehova amatsogolera moyo wathu mwachikondi. Onani zina mwa zimene tingachite kuti tikapindule kwambiri ndi msonkhanowu.

2 Tifunika Kukonzekeretsa Mtima Wathu: Aliyense ali ndi udindo wotchinjiriza mtima wake wophiphiritsira. (Miy. 4:23) Zimenezi zimafuna kuti tikhale odziletsa ndiponso tipende maganizo athu moona mtima. Nthaŵi ya msonkhano ndi nthaŵi yosinkhasinkha za unansi wathu ndi Yehova, komanso ‘yopenya m’lamulo langwiro, ndilo laufulu.’ Kuti tikonzekeretse mtima wathu ‘kulandira mawu ookedwa mwa ife,’ tifunika kupempha Yehova kuti atipende, n’kuona ngati tili nawo “mayendedwe oipa” ofunika kusintha, ndiponso kuti atitsogolere pa “njira yosatha.”—Yak. 1:21, 25; Sal. 139:23, 24.

3 Mvetserani Ndipo Sinkhasinkhani: Yesu poyamikira Mariya chifukwa chomvetsera mwatcheru zimene anali kunena, anati: “Mariya anasankha dera lokoma limene silidzachotsedwa kwa iye.” (Luka 10:39, 42) Tikakhala ndi maganizo ngati ameneŵa, tidzapeŵa kudodometsedwa ndi zinthu za zii. Tidzaonetsetsa kuti takhala pansi ndi kumamvetsera mwatcheru nthaŵi yonse ya pulogalamu. Tidzapeŵa kulankhulalankhula ndi kuyendayenda popanda zifukwa zenizeni ndipo tidzayesetsa kuti tisadodometse anthu ena ndi matelefoni a m’manja ndiponso makamera.

4 Pomvetsera nkhani, ndi bwino kulemba notsi zachidule zotithandiza kuona momwe nkhaniyo akuifotokozera. Tizigwirizanitsa zimene tikumvazo ndi zimene timadziŵa kale. Zimenezi zidzathandiza kuti timvetsetse nkhaniyo ndiponso kuti tiziikumbukira. Pobwerera mu manotsi athu, tizikhala ndi maganizo ofuna kugwiritsa ntchito zimenezo. Ndi bwino kuti aliyense azidzifunsa kuti: ‘Kodi zimenezi zikukhudza motani unansi wanga ndi Yehova? Kodi ndi zinthu ziti zimene ndikufunika kusintha pamoyo wanga? Kodi ndi motani mmene ndingagwiritsire ntchito zimenezi pochita zinthu ndi anthu ena? Kodi ndingazigwiritse ntchito motani mu utumiki wanga?’ Kambiranani ndi anthu ena mfundo zimene zakusangalatsani kwambiri. Kuchita zimenezi kudzatithandiza kusunga mawu a Yehova ‘m’kati mwa mtima wathu.’—Miy. 4:20, 21.

5 Tiyeni Tigwiritse Ntchito Zimene Taphunzira: Munthu wina atabwerako ku msonkhano wachigawo, anati: “Msonkhanowo unali wokhudza kwambiri munthu aliyense, wolimbikitsa munthu kuona zimene zili mu mtima wake ndi m’mitima ya achibale ake, ndi kuwathandiza achibale akewo mwachikondi pogwiritsa ntchito Malemba pamene akufunika kutero. Wandithandiza kuona udindo wanga wakuti ndizithandiza kwambiri mpingo.” Ndithudi ambirife tinaonanso chimodzimodzi. Komano pagona nkhani si kubwerako kumsonkhano titalimbikitsidwa ndi kutsitsimulidwa, pakuti Yesu anati: ‘Ngati mudziŵa izi, odala inu ngati muzichita.’ (Yoh. 13:17) Tiyesetse kugwiritsira ntchito mfundo zimene zikutikhudza kwambiri. (Afil. 4:9) Imeneyi ndiyo njira yokhutiritsira kwambiri zosoŵa zathu zauzimu.

[Bokosi patsamba 5]

Sinkhasinkhani Zimene Mwamva:

■ Kodi zikukhudza motani unansi wanga ndi Yehova?

■ Kodi zikukhudza motani zimene ndimachitira anthu ena?

■ Kodi zimenezi ndingazigwiritse ntchito motani pamoyo wanga ndiponso mu utumiki wanga?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena