Ntchito Imene Imafunika Kudzichepetsa
1 Mawu a Mulungu amatilangiza kuti tikhale “odzichepetsa; osabwezera choipa ndi choipa, . . . koma . . . [kupereka, NW] madalitso.” (1 Pet. 3:8, 9) Mosakayikira, uphungu umenewu umagwira ntchito polalikira. Inde, utumiki wachikristu ungatiyese pa kudzichepetsa kwathu.
2 Khalidwe la kudzichepetsa limatithandiza kupirira zovuta zimene tingakumane nazo. Tikamalalikira, timapita tokha asanatiitane ndi kukalankhula ndi anthu osawadziŵa, ndipo timadziŵa kuti ena satilandira bwino. Kuti tilalikirebe tikakumana ndi anthu osatilandira bwinoŵa, m’pofunika kudzichepetsa. M’gawo lina louma kwambiri, alongo aŵiri omwe ndi apainiya anayenda khomo ndi khomo tsiku lililonse kwa zaka ziŵiri popanda kulankhula ndi munthu wina aliyense! Koma analimbikira, ndipo lero kumeneko kuli mipingo iŵiri.
3 Ngati Tichitiridwa Chipongwe: Ena akapanda kutikomera mtima kapena akatichitira chipongwe, kudzichepetsa kudzatithandiza kutsanzira Yesu. (1 Pet. 2:21-23) Panyumba ina, mlongo wina anatukwanidwa, koyamba ndi mkazi kenako ndi mwamuna wa mkaziyo amene anam’thamangitsa. Asanachoke, mlongoyo anangomwetulira ndipo anati adzalankhula nawo nthaŵi ina. Zimenezi zinadabwitsa kwambiri banjalo moti pamene wa Mboni wina anafika, iwo anamvetsera. Atawapempha kupita ku msonkhano ku Nyumba ya Ufumu, iwo anavomera. Mlongo anam’thamangitsa uja anali komweko ndipo anawapatsa moni ndi kuwalalikiranso. Ifenso tingafeŵetse mitima ya anthu osafuna kumva mwa kusonyeza “chifatso ndi mantha.”—1 Pet. 3:15; Miy. 25:15.
4 Peŵani Kudzitukumula: Kudziŵa kwathu Baibulo sikutipatsa chifukwa choti tiziderera anthu ena kapena kuwanyoza. (Yoh. 7:49) M’malo mwake, Mawu a Mulungu amatilangiza ‘kusachitira mwano munthu aliyense.’ (Tito 3:2) Tikakhala a mtima wodzichepetsa ngati mmene Yesu analili, timapumulitsa ena. (Mat. 11:28, 29) Kukhala odzichepetsa kumathandiza kuti uthenga wathu ukhale wokopa anthu.
5 Inde, kudzichepetsa kumatithandiza kupirira m’gawo louma. Kungafeŵetse mitima ya anthu osafuna kumva, ndipo ena amakopeka nako n’kulandira uthenga wa Ufumu. Koposa zonse, kumasangalatsa Yehova, amene “apatsa chisomo kwa odzichepetsa.”—1 Pet. 5:5.