Kulambira Mulungu m’Choonadi
Kuti kulambira kukhale kololeka kwa Mulungu, kuyenera kuzikidwa pachoonadi. (Yohane 4:23) Baibulo limati olambira oona ali mu “Eklesia [“mpingo,” NW] wa Mulungu wamoyo, mzati ndi mchirikizo wa choonadi.” (1 Timoteo 3:15) Anthu amene amapanga mpingo wa Mulungu samangokhulupirira choonadi cha Mawu a Mulungu koma amachitsatiranso pamoyo wawo ndi kuchichirikiza, kuchilengeza padziko lonse lapansi.—Mateyu 24:14; Aroma 10:9-15.
MBONI ZA YEHOVA zimadziŵika bwino lomwe ndi ntchito yawo yophunzitsa Baibulo, imene tsopano zikuichita m’maiko oposa 200. Zimaphunzira Baibulo ndi kuliphunzitsa monga choonadi, popanda kuwonjezerapo mafilosofi a anthu amene amalisukulutsa. Kodi ziphunzitso zawo za m’Baibulo mumazidziŵa? Ambiri amakayikira kumvetsera Mboni za Yehova chifukwa cha nkhani zosasangalatsa zimene amamva zokhudza Mboni. Koma anthu oona mtima akupemphedwa kuti adzigamulire okha ngati Mboni zimaphunzitsa kapena sizimaphunzitsa choonadi. Chigamulo chachikulu chimenechi sichiyenera kuzikidwa pa manenanena. Ochuluka amene adzifufuzira okha ziphunzitso za Mboni za Yehova apindula kwambiri.
Kudziŵa Choonadi Kumachotsa Mantha
Mwachitsanzo, talingalirani zimene zinachitikira Eugenia. Iye analeredwa m’banja lachangu lachikatolika. Atate wake anali mmodzi mwa olinganiza ulendo wa papa wodzacheza ku Mexico mu 1979. Pochezera mabwenzi ake, Eugenia anakumana ndi Mboni za Yehova. Mothandizidwa ndi Mbonizo, iye anayamba kusanthula mosamalitsa zimene Baibulo limanena. Pokumbukira, iye anati: “Poyamba, mantha anandigwira. Ndinali nditapeza choonadi! Koma zimenezi zinatanthauza kuti zikhulupiriro zanga zambiri zoyambirira zinali zolakwika. Kunyumba, mabwenzi anga, anthu amene ndinali kuwakonda—onse anali ndi zikhulupiriro zolakwika. Ndinachita mantha. Ndinali kungoganizira mmene kunyumba adzaonera zinthu zatsopanozi zimene ndinali nditapeza. M’kupita kwa nthaŵi ndiponso mothandizidwa ndi Yehova, ndinayamba kuzoloŵera zinthu zachilendo zimenezi. Tsiku lina ndinaganiza zokalankhula ndi bwenzi la banja lathu, profesa wina wa maphunziro a zaumulungu. Ndinamuuza zonse za kufunitsitsa kwanga kupeza choonadi. Ndiyeno anati, ‘Ngati ukufuna kudziŵa choonadi, funafuna Mboni za Yehova.’”
Zomwe Eugenia ankaopa zinachitikadi. Anampitikitsa panyumba. Koma Mboni zinapitirizabe kumthandiza mwauzimu. Iye anati: “Zinandilimbitsa mtima kuima kumbali ya choonadi. Ndinazindikira kuti pafunikiradi kulimbikira. Mmene Mboni za Yehova zinandilandirira zinandithandiza kwambiri. Ndinadzimva kukhala wokondedwa mumpingo wachikristu. Kuyandikana ndi gulu la Mulungu kunandithandiza kuthetsa mantha akuti ndidzaima pandekha.”
Lingalirani chitsanzo china. Sabrina analeredwa ndi chizoloŵezi chokhala ndi makambitsirano a Baibulo apabanja nthaŵi zonse. Kwenikweni, iwo anakhala ndi ‘chipembedzo cha pabanja.’ Iye ankakonda kukambitsirana ndi anthu a zipembedzo zosiyanasiyana kuti avumbule zolakwa zawo. Pamene mmodzi wa Mboni za Yehova anampempha kuti azichita naye phunziro la Baibulo, Sabrina anavomera mosazengereza ncholinga chotsutsa zikhulupiriro zawo. Iye anakumbukira kuti: “Nditaphunzira kwa nthaŵi yoposa chaka chimodzi, ndinachita mantha kuti ndidzataya ‘choonadi changa’. Sindinavutike kuvumbula chinyengo cha zipembedzo za anthu ambiri amene ndinakambitsirana nawo, koma si mmene zinalili nthaŵiyi.”
Chifukwa cha mantha, Sabrina analekeza phunziro lake la Baibulo ndi Mboni za Yehova. Komano anamva njala yaikulu yauzimu. Anasankha kuyambanso kuphunzira ndipo m’kupita kwa nthaŵi analandira choonadi chatsopano chimenechi. Sabrina anapita patsogolo mpaka pofuna kuuzako ena zimene amaphunzira. Anapemphanso kutsagana ndi Mboni mu utumiki wawo wa kunyumba ndi nyumba. Sabrina anafotokoza kuti: “Asanandilole kulalikira pamodzi ndi Mboni za Yehova, ndinafunsidwa kuti: ‘Kodi ukufunadi kukhala mmodzi wa Mboni za Yehova?’ ‘Iyayi!’ ndinayankha motero. Mantha anandigwiranso.” Pomalizira pake, atapitiriza kupezeka pamisonkhano yonse ndi kuona zochita za anthu a Mulungu ndi mmene amatsatirira mapulinsipulo a Baibulo, Sabrina anafika potsimikiza kuti chimenechidi ndicho choonadi. Anabatizidwa ndipo tsopano ndi mlaliki wanthaŵi zonse.
Kodi Nchifukwa Chiyani Zili Zosiyana Kwambiri?
Wina angafunse kuti, ‘Kodi nchifukwa chiyani ziphunzitso za Mboni za Yehova zili zosiyana kwambiri ndi za zipembedzo zina?’ Kusanthula mwachidule zikhulupiriro za Mboni kudzakuthandizani kuona kuti iwo ndi Akristu oona mtima ndipo amaphunzira Baibulo mosamala. Tikukupemphani kuti malemba osonyezedwa pachidule chimene chili pamwambapo cha zikhulupiriro zawo zazikulu muwaŵerenge m’Baibulo lanu.
Mwa kusanthula mosamalitsa zikhulupiriro za Mboni za Yehova ndi mmene amagwiritsitsira zimene Baibulo limaphunzitsa, mungasangalale ndi ufulu umene choonadi chimapereka. (Yohane 17:17) Palibe chifukwa choopera choonadi. Kumbukirani lonjezo la Yesu: “Mudzazindikira choonadi, ndipo choonadi chidzakumasulani.”—Yohane 8:32.
[Bokosi patsamba 6]
ZIKHULUPIRIRO ZINA ZAZIKULU ZA MBONI ZA YEHOVA
◯ Yehova ndiye Mulungu wamphamvuyonse. Dzina lake limapezeka nthaŵi zoposa 7,000 m’mipukutu yoyambirira ya Baibulo.—Salmo 83:18.
◯ Yesu Kristu ndi Mwana wa Mulungu, ndipo anadza padziko lapansi kudzapereka moyo wake m’malo mwa mtundu wa anthu. (Yohane 3:16, 17) Mboni za Yehova zimatsatira ziphunzitso za Yesu Kristu monga momwe zilili m’Mauthenga Abwino.
◯ Dzina lakuti Mboni za Yehova linatengedwa pa Yesaya 43:10, pamene pamati: “Inu ndinu mboni zanga, ati Yehova.”
◯ Ufumu umene anthu amapempherera m’pemphero la “Atate wathu wa Kumwamba” ndi boma lakumwamba limene posachedwapa lidzachotsapo kuvutika konse ndi zopweteka zonse padziko lapansi kuti pakhale Paradaiso amene Baibulo limalonjeza.—Yesaya 9:6, 7; Danieli 2:44; Mateyu 6:9, 10; Chivumbulutso 21:3, 4.
◯ Aliyense amene akuchita chifuniro cha Mulungu adzakhala ndi madalitso a Ufumu kosatha.—Yohane 17:3; 1 Yohane 2:17.
◯ Khalidwe la Akristu liyenera kutsatira zimene Baibulo limanena. Iwo ayenera kuyesetsa kukhala oona mtima, kukhala ndi moyo wachiyero, ndi kusonyeza chikondi kwa anansi awo.—Mateyu 22:39; Yohane 13:35; 1 Akorinto 6:9, 10.
[Chithunzi patsamba 5]
Mboni za Yehova zikulengeza choonadi cha Baibulo m’maiko oposa 200