Kum’patsa Yehova Zabwino Koposa
1 Chilamulo cha Yehova kwa Israyeli chinanena momveka bwino kuti nsembe za nyama zoperekedwa kwa iye zizikhala ‘zopanda chilema.’ Nyama yachilema inali yosayenera. (Lev. 22:18-20; Mal. 1:6-9) Komanso, popereka nsembe, mafuta onse—omwe anali mbali yabwino koposa—anali a Yehova. (Lev. 3:14-16) Popeza Yehova anali Atate ndi Mbuye wa Israyeli, iye anafunika zabwino koposa.
2 Monga mmene zinalili kale, masiku anonso Mulungu ali ndi chidwi choona mmene nsembe zathu zilili. Utumiki wathu uyenera kusonyeza kuti timam’patsa Yehova ulemu womuyenera. N’zoona kuti anthufe tili ndi moyo wosiyanasiyana. Komabe, tili ndi chifukwa chomveka chodzipendera kuti titsimikizire kuti tikum’patsa zabwino koposa.—Aef. 5:10.
3 Kutumikira ndi Mtima Wonse: Kuti utumiki wathu ulemekeze Yehova ndi kuwafika pamtima omvera athu, suyenera kuchitika mwachizoloŵezi chabe. Zimene timanena zokhudza Mulungu wathu ndi zolinga zake zazikulu zizichokera mu mtima woyamikira. (Sal. 145:7) Zimenezi zikutsindika kufunika kokhalabe ndi ndondomeko yabwino yoŵerenga ndi kuphunzira Baibulo patokha.—Miy. 15:28.
4 Kum’patsa Yehova zabwino koposa kumaphatikizaponso kutsanzira kukonda kwake anthu. (Aef. 5:1, 2) Kukonda anthu kudzatipangitsa kuyesetsa kufikira anthu ambiri mmene tingathere ndi uthenga wopatsa moyo wa choonadi. (Marko 6:34) Kumatilimbikitsa kusonyeza chidwi kwa anthu amene timalankhula nawo. Kumatipangitsa kuti tiziwaganizirabe tikachoka panyumba yawo paulendo woyamba ndipo kumatilimbikitsa kubwererakonso. Kumatilimbikitsa kuchita zonse zimene tingathe kuti tiwathandize kupita patsogolo mwauzimu.—Mac. 20:24; 26:28, 29.
5 “Nsembe Yakuyamika”: Njira ina imene timam’patsira Yehova zabwino koposa ndiyo kuchita khama mu utumiki. Ngati tili adongosolo ndiponso ngati tiika maganizo pantchito imene tapatsidwa, tingachite zambiri m’nthaŵi imene tili nayo. (1 Tim. 4:10) Kukonzekera bwino kumatithandiza kulankhula zomveka ndiponso mwachidaliro, zimene zimathandiza kuti anthu alabadire uthenga wathu. (Miy. 16:21) Pouza ena uthenga wabwino, zimene timalankhula kuchokera pansi pamtima zingatchedwedi kuti “nsembe yakuyamika.”—Aheb. 13:15.