Achinyamata—Peŵani Moyo Wachiphamaso
1, 2. Kodi ndi chitsanzo chiti cha wachinyamata amene anali ndi moyo wachiphamaso?
1 Mnyamata wina analemba kuti: “Kuyambira ndili mwana ndinaleredwa m’Chikristu, pakati pa Mboni za Yehova. Komabe, moyo wanga, ngakhale kunyumba, unali wosiyana kwambiri ndi mfundo komanso maganizo a makolo anga. Mbali yaikulu, ndinali ndi moyo wotayirira, moyo wopulupudza wa m’dzikoli.”
2 Wachinyamatayu anapitiriza kufotokoza kuti: “Ngakhale ndisanakwanitse zaka khumi, ndimati kwinaku ndimakhala wa Mboni kwinaku ndimakhala m’kunja, ndinkachita zoti ndizikondedwa ndi kukhala ndi anzanga kusukulu komanso kwinaku makolo anga azisangalala nane. Kusukulu ndinkatsatira zochita ndi makhalidwe a kumeneko monga momwe ndikanathera . . . Koma kunyumba ndinalinso munthu wina. Ndinali Mkristu wa makhalidwe abwino amene makolo anga ankafuna.”
3. (a) Kodi tili ndi chikhulupiriro chotani, komabe tikudziŵa chiyani? (b) Kodi n’chiyani chachititsa kuti tiike maganizo athu onse pa achinyamata?
3 Tikudziŵa kuti ambiri mwa achinyamatanu mulibe makhalidwe onga wachinyamata ameneyu. Tikukhulupirira kuti ambiri mwa inu, ndinu oona mtima kwa makolo anu ndiponso kumpingo, ndipo zimenezi zimatisangalatsa. Komabe, tikudziŵa kuti ena amadzionetsa ngati ali ndi makhalidwe abwino, pamene akuyesetsa kubisira achikulire makhalidwe awo oipa. N’chifukwa chake tikukufunsani kuti: Kodi makhalidwe anu ndi amenedi timawaonaŵa, kapena muli ndi moyo wachiphamaso? Sitikufunsa zimenezi pofuna kukupezerani zifukwa, m’malo mwake, tikufunsa chifukwa chakuti timakukondani kwambiri ndipo tikufuna kukuthandizani kuti musangalale ndi unyamata wanu mwa kuchita zinthu zimene zingasangalatse Yehova.—Mlal. 11:9, 10; 12:14; 2 Akor. 5:10.
4. Kodi achikulire ena anasonyeza bwanji moyo wachiphamaso, koma posachedwapa paoneka zotani pakati pa achinyamata?
4 Komabe, mungafunse kuti: ‘N’chifukwa chiyani mukunena za ife achinyamata? Nanga achikulire?’ Inde, nawonso ayenera kupeŵa moyo wachiphamaso. Gehazi, mtumiki wa Elisa, anachita chinyengo, anayesetsa kubisa zoti analandira mphatso kwa Namani. (2 Maf. 5:20-26) Ndiponso Hananiya ndi Safira, omwe anali achikulire, ananama ponena kuti anapereka kwa atumwi mtengo wonse wa munda, kudzionetsera kuti ndi abwino, pamene anasunga ndalama zina kuti azigwiritse ntchito okha. (Mac. 5:1-4) Koma chifukwa chimene taikira maganizo athu pa achinyamatanu n’chakuti pakhala kuwonjezeka kwambiri kwa moyo wachiphamaso pakati pa inu.
5. (a) N’chifukwa chiyani achinyamata ena amakhala ndi moyo wachiphamaso? (b) Kodi achinyamata amene ali ndi moyo wabwino amachitiridwa zotani, ndiye chifukwa cha zimenezi ena amachita chiyani?
5 Chifukwa Chake Ena Ali ndi Moyo Wachiphamaso: N’chifukwa chiyani ena amakhala ndi moyo wachiphamaso? Wachinyamata wina anafotokoza chifukwa chachikulu pamene anati: “Sindinafune kuti ndikhale wopanda anzanga pochita zinthu zosiyana ndi iwowo.” N’zoona kuti kuchita zinthu zabwino zosiyana ndi ena, nthaŵi zambiri kumachititsa kuti munthu uzinyozedwa. (Yerekezani ndi 1 Petro 3:16; 4:4.) Pofuna kupeŵa zimenezi ndiponso kuti anzawo aziwakonda, achinyamata ena amatha ngakhale kuledzera kapena kuchita chiwerewere. Mtsikana wina wa zaka 13 yemwe si Mboni, amene m’kalasi ankakhoza bwino kwambiri maphunziro onse ndipo nthaŵi zonse ankakhala nawo pa zokambirana za m’kalasi, anadandaula kuti: “Anyamata safuna munthu amene amachita bwino ngati ine . . . Ndikuganiza zosiya kukhoza bwino m’kalasi kapena kuchita zinthu zina kuti azindikonda.”
6. Kodi zinakhala bwanji kuti Petro achite zolakwika, ndipo zimenezi ziyenera kukhudza bwanji mmene timawaonera achinyamata?
6 N’zochititsa chidwi kuti nayenso mtumwi Petro nthaŵi ina anaganizira kwambiri za mbiri yake, m’malo mochita zimene ankadziŵa kuti ndi zolondola. Akristu achiyuda a ku Yerusalemu atapita ku Antiokeya, Petro anasiya kucheza ndi Akristu omwe sanali Ayuda poopa kuti Ayuda amudzudzula chifukwa chocheza pamodzi ndi anthu omwe sanali Ayudaŵa. (Agal. 2:11-14) Motero, popeza ngakhale Akristu achikulire agonjapo pankhani yochita zimene anzawo akufuna, kodi zingadabwitse kuti achinyamata amene sakudziŵa zambiri angachitenso zimenezo?—Miy. 22:15.
7. N’chiyani chingakope achinyamata ena kukhala ndi moyo wachiphamaso?
7 Chifukwa china chogwirizana ndi chimenechi chimene chimachititsa achinyamata kukhala ndi moyo wachiphamaso n’chakuti amakhulupirira kuti akumanidwa zinthu zosangalatsa. Amamva achinyamata kusukulu akufotokoza zimene achita, mmene phwando linalili losangalatsa, nyimbo zapamwamba, kumwa, mankhwala osokoneza bongo, mmene analedzerera. Kapena angamve iwo akufotokoza mmene mnyamata kapena mtsikana wakuti amapsopsonera ndi mmene amachitira pogonana. Motero chilakolako chofuna kuchita nawo zimenezi chimayambika, ndipo zimenezi zimawachititsa achinyamatawo kuyesera kuchita zimene Baibulo limatcha ‘zokondweretsa zoipa zakanthaŵi.’—Aheb. 11:24, 25; 1 Akor. 10:6-8.
8. Kodi chifukwa chachikulu chimene achinyamata amakhalira ndi moyo wachiphamaso n’chiyani?
8 Komabe, chifukwa chachikulu chimene achinyamata ena amakhala ndi moyo wachiphamaso n’chakuti saona kuti Yehova ndi weniweni ndiponso saona kuti dziko latsopano likudzalo lidzakhalapodi. Sakhulupirira ndi mtima wonse malonjezo a Yehova kapena zimene amachenjeza kudzera m’Mawu ake ndi gulu lake looneka pankhani ya zotsatira za kusamvera Yehova. (Agal. 6:7, 8) Sakufanana ndi Mose amene Baibulo limafotokoza za iye kuti: ‘Anapenyerera chobwezera cha mphotho ya [Mulungu] . . . Anapirira molimbika monga ngati kuona Wosaonekayo.’ Mose ankaona kuti Yehova ndi weniweni ndiponso kuti malonjezo Ake adzakwaniritsidwa. Koma anthu amene amakhala ndi moyo wachiphamaso alibe chikhulupiriro chimenecho. Zomwe akuona n’zimene Satana amafuna kuti aone, zosangalatsa za dongosolo lake. Motero iwo amasangalala kwakanthaŵi pochita tchimo, komabe kwinaku akudzionetsera ngati anthu oyera.—Aheb. 11:26, 27.
9. (a) Kodi zingachitike bwanji kuti makolo n’kuchititsa kuti mwana wawo akhale ndi moyo wachiphamaso? (b) Kodi achikulire ayenera kuzindikira chiyani ndipo ayenera kukhala tcheru kuchita chiyani?
9 Makolo, Mungachititse Vutoli: Wachinyamata amene tamugwira mawu pachiyambi pa nkhani ino, anati: “Zinthu zimene zinkachititsa kuti anthu asamandikonde kusukulu, ndi zimene zinkachititsa kuti kunyumba azisangalala nane ndi kundikonda. Koma ndinkafuna zoposa zimenezi. Ndinkafuna munthu amene ndingamudalire, kulankhula naye, ndi kumuuza zakukhosi, ndipo makolo anga sanali otero.” Makolo, kodi mukusamala kuti musalimbikitse ana anu kukhala ndi moyo wachiphamaso? Kodi mumawaganizira mwapadera ndiponso kuwapatsa malangizo amene akufunikira? Achikulire ayenera kuzindikira mavuto aakulu ofooketsa chikhulupiriro amene achinyamata athu akukumana nawo kusukulu ndiponso kukhala tcheru kuchita zonse zimene angathe pofuna kuwalimbikitsa ndi kuwathandiza.—Sal. 73:2, 3; Aheb. 12:3, 12, 13.
10. (a) Kodi ndi nkhani iti imene ndi udindo wa makolo kuphunzitsa ana awo? (b) Kodi nthaŵi zambiri zotsatira zake zimakhala zotani ngati makolo sanapereke malangizo?
10 Nthaŵi zambiri achinyamata amakhala ndi mafunso ambiri okhudza ubwenzi wa pakati pa mnyamata ndi mtsikana, nkhani imene makolo ambiri amaipeŵa zomwe n’zomvetsa chisoni kwabasi. Wophunzira wina wokongola wa zaka 15 yemwe anali kuchita bwino kwambiri kusukulu anati: “Sitinalankhulanepo zochokera pansi pa mtima. Zonse zimene ndinadziŵa pankhani ya kugonana ndinaziphunzira pandekha . . . Ndinkachita manyazi kwambiri kuwafunsa ngakhale kuti panali zambiri zimene ndinafunika kudziŵa.” Kodi zotsatira zake zinali zotani? Iye anati: “Mgwirizano wanga ndi makolo anga unali kucheperachepera, ndipo ndinakhala mtsikana wolakalaka kudziŵa zambiri, wopusa ndiponso woti chilichonse choipa chikhoza kundichitikira.” Inde, zotsatira zake anagona ndi mnyamata wina amene anamunyengerera kuti agone naye, koma kodi mungati ndani amene anathandizira kuti iye achite zimenezi?—Miy. 22:3; 27:12.
11. (a) Kodi makolo angasonyeze bwanji kuti amakonda ana awo? (b) Kodi achinyamata adzachita bwanji chifukwa cha chikondi choterocho?
11 N’zofunika kwambiri kuti makolo aziwasonyeza ana awo kuti amawakonda kwambiri popatula nthaŵi yocheza nawo, kulankhula nawo zachinsinsi, ndi kuwapatsa malangizo. (Miy. 15:22; 20:18) Wachinyamata wina anati: “Ndikuganiza kuti akanakhala kuti ankandiganizira akanandipatsa malamulo ena ake.” Ngakhale kuti achinyamata angaipidwe ndi malamulo anu pakalipano, m’tsogolo adzawakumbukira ndipo adzakuyamikirani. Mtsikana wina anawalembera mayi ake kuti: “Ine monga mwana amene nthaŵi zonse ndinkafuna kuyesa kupyola malire, kufuna pozembera malamulo okhwima, ndikuyamikira kwambiri kuti munapitiriza kundilamulira.” Motero, sonyezani kuti mumawakonda ana anu pokonza zoti azitsatira malangizo anu. Ndiyetu musathandizire ana anu kukhala ndi moyo wachiphamaso polephera kulankhula nawo kapena polephera kukhala wokonzeka kuwathandiza akafuna kuti muwathandize.
12. Kodi ndi maganizo opanda nzeru ati amene makolo ena amakhala nawo omwe amathandizira kuti ana akhale ndi moyo wachiphamaso?
12 Pa Mlaliki 11:9, pamanena kuti: “Kondwera ndi unyamata wako, mnyamata iwe; . . . koma dziŵitsa kuti Mulungu adzanena nawe mlandu wa zonsezi.” Makolo angathandizirenso m’njira ina kuchititsa ana awo kukhala ndi moyo wachiphamaso. Zimene ananena woweruza wa khoti lalikulu ku New Jersery zikupereka chitsanzo pankhani imeneyi. Woweruzayo anati: “Aphunzitsi amayesetsa kulanga ana chifukwa chochita zolakwa komano makolo amadzudzula aphunzitsiwo m’malo mowathandiza.” Zikuoneka kuti makolo ena amaganiza molakwika kuti mwana wawo sangachite zolakwa. Ngakhale akulu achikristu kapena abale ena amene ali ndi udindo mumpingo akauza makolowo zoipa zimene ana awo akuchita, makolowo safuna kumva. Mwa kuchita zimenezo, amathandizira kuti ana awowo akhale ndi moyo wachiphamaso.
13. Kodi kukhala ndi moyo wachiphamaso kumatanthauza chiyani?
13 Tanthauzo la Moyo Wachiphamaso: Zimenezi n’zofunika kuzilingalira: Kukhala ndi moyo wachiphamaso kumatanthauza bodza, kukhala wachinyengo. (Sal. 12:2; 2 Tim. 3:13) Ndiko kukhala ngati Satana amene ‘amadzionetsera ngati mngelo wa kuunika.’ (2 Akor. 11:14, 15) Ndikonso kukhala ngati atsogoleri achipembedzo amene Yesu anafotokoza za iwo kuti: “Tsoka inu, alembi ndi Afarisi, onyenga! chifukwa mufanafana ndi manda opaka njereza, amene aonekera okoma kunja kwake koma adzala m’katimo ndi mafupa a anthu akufa ndi zonyansa zonse. Chomwecho inunso, muonekera olungama pamaso pa anthu, koma m’kati muli odzala ndi chinyengo ndi kusayeruzika.” (Mat. 23:27, 28) Mwachionekere, kukhala ndi moyo wachiphamaso ndi kulakwira Mulungu kwambiri.
14. N’chifukwa chiyani munthu ayenera kupeŵa moyo wachiphamaso?
14 Mfundo inanso yofunika kuiganizira kwambiri ndi iyi: N’zosatheka kubisa chinyengo mpaka kalekale. Baibulo limati: “Ngakhale mwana adziŵika ndi ntchito zake ngati ntchito yake ili yoyera ngakhale yolungama.” (Miy. 20:11; Luka 12:1-3) Inde, zimene mukuchita kaya n’zabwino kapena zoipa, m’kupita kwa nthaŵi zidzadziŵika. Ndipo Baibulo limasonyeza kuti Mulungu adzalanga kwambiri anthu amene amachita chinyengo. (Mat. 24:51) Kunena zoona, muyenera kupeŵa moyo wachiphamaso.
15. N’chiyani chingathandize achinyamata kupeŵa moyo wachiphamaso?
15 Mmene Mungapeŵere Moyo Wachiphamaso: Njira imodzi yopeŵera moyo wachiphamaso ndiyo kuganizira zimene moyo wachiphamaso umatanthauza ndiyeno mudzifunse kuti: Kodi mmenemu ndi mmene ndikufunira kuti anthu adzandikumbukire, monga munthu wachinyengo, wotsatira Satana ndi Afarisi? Mosakayika simungafune kuti mukhale wotero. Chinthu china chimene chingakuthandizeni kupeŵa moyo wachiphamaso ndicho kuganizira mmene mavuto ake a moyo wotero adzakupwetekerani mtima ndi kukusautsirani. Kumbukirani zimene zinachitikira Gehazi chifukwa cha bodza lake. Khate la Namani linamugwera iye ndipo anakhala wakhate kwa moyo wake wonse. Ndipo Hananiya ndi Safira anaphedwa ndi Mulungu chifukwa chonamizira kuti ndi ooloŵa manja pamene sanali otero.—2 Maf. 5:27; Mac. 5:5, 9, 10.
16. Kodi n’chiyani chinachitika kwa wachinyamata wina amene anatsatira moyo wa dzikoli?
16 Palinso zitsanzo za masiku ano. Wachinyamata wina ku United States anayamba kuphunzira Baibulo ndi kupezeka pa misonkhano pa Nyumba ya Ufumu. Komano anayamba kutsatira moyo wa dzikoli ndipo anasiya kusonkhana. Patapita zaka analemba kuti: “Miyezi pafupifupi iŵiri yapitayo ndinapempha Mulungu kuti anditumizire Mboni chifukwa ndinafuna kuti ndiyambirenso. Ndinayamba kuphunziranso pamene bomba linaphulika. Anandipeza mwezi wapitawo ndi mtundu wa kansa ya pakhungu, imene ndi mbali ina ya matenda atsopano osachiritsika a Edzi.” Iye anamaliza ponena kuti: “Ndikanatsatira ndi kumvera zimene Malemba amachenjeza zimenezi zisanachitike, sindikanakhala ndi vuto limeneli panopa.” Inde, mufunika kupeŵa mavuto omvetsa chisoni ngati ameneŵa. Dzikoli lilibe chabwino.—1 Yoh. 2:15-17.
17. Kodi n’kuganiziranso mfundo iti kumene kungathandize achinyamata kupeŵa moyo wachiphamaso?
17 Chinanso chimene chingakuthandizeni kupeŵa moyo wachiphamaso ndicho kuganizira mmene kuchita zimenezo kungakhudzire dzina la Yehova. Wachinyamata amene tamutchula poyambirira uja anati munthu wina amene anamuona akulandira ndudu ya fodya anati: “Sindinkadziŵa kuti Mboni za Yehova zimasuta. Kodi sindiwe wa Mboni?” Patapita nthaŵi iye ananena kuti funsolo linamupweteka kwambiri chifukwa zimene ankachita zinali kunyozetsa dzina la Yehova. Kodi mukufuna kuchita zimenezo? Kodi mumapeputsa kwambiri Mulungu wathu moti mungafune kuchititsa manyazi dzina lake monga mmene anachitira Aisrayeli akale osakhulupirika?—Sal. 78:36, 37, 41; Ezek. 36:22.
18. (a) Kodi makolo amachita bwanji akadziŵa kuti mwana wawo ali ndi moyo wachiphamaso? (b) N’chifukwa chiyani zimenezi ziyenera kuthandiza achinyamata kupeŵa moyo wachiphamaso?
18 Kuwonjezeranso pamenepo, ganizirani mbiri ya makolo anu ndi mmene angamvere. Mnyamata amene tamutchula kaleyu analemba kuti: “Tsiku lina makolo anga anadziŵa zimene ndinali kuchita. Zinawakhumudwitsa kwambiri. Ndipo kwa nthaŵi yoyamba pa moyo wanga, ndinaona bambo ndi mayi anga akulira. Zimene ndinachita zinawapweteka kwambiri.” Makolo anunso akhoza kulira ngati atadziŵa kuti muli ndi moyo wachiphamaso. Kodi zimenezo n’zimene mukufuna? Baibulo limati: “Mbiri yabwino ifunika kopambana chuma chambiri.” (Miy. 22:1) Mwa kukhala ndi moyo wachiphamaso, mumawononga mbiri yanu yabwino. Koma si zokhazi. Mumawononganso mbiri yabwino ya makolo anu ndi kuipaka matope, kuwachititsa manyazi.—Miy. 10:1; 17:21.
19. Kodi khalidwe loipa la ana aamuna a Yakobo linamukhudza bwanji Yakoboyo, ndipo tingaphunzirepo chiyani pamenepa?
19 Chitsanzo cha ana aamuna a Yakobo chimasonyeza bwino mmene ana angawonongere mbiri yabwino ya makolo awo. Mwana wamkazi wa Yakobo, Dina, ataipitsidwa, abale ake anapha amuna a m’mudziwo ndi kuwononga mudziwo, zimene zinachititsa Yakobo kudandaula kuti: ‘Mwandisautsa ndi kundinunkhitsa ine mwa anthu okhala m’dzikomu.’ Mulungu mpaka analangiza Yakobo kuti achoke m’deralo. (Gen. 34:30; 35:1) Inunso munganunkhitse mbiri ya bambo ndi mayi anu, kuwapangitsa kuchita manyazi akakumana ndi anthu amene amakhala nawo pafupi kapena anzawo. Inde, monga mmene Baibulo linanenera: “Mwana wopusa achititsa atate wake chisoni, namvetsa zowawa amake wom’bala.”—Miy. 17:25.
20. Kodi ndi mphatso yaikulu iti imene makolo achikristu apereka kwa ana awo?
20 Komabe, tikukhulupirira kuti simukufuna kuti makolo anu apwetekedwe mtima motero. Choncho, ganizirani mmene zochita zanu zingawakhudzire. Ndiponso, ngati muli ndi mwayi woti makolo anu ndi Akristu, ganizirani zimene akupatsani, osati moyo wokha, koma chinthu chinanso cha mtengo wapatali. Baibulo limafotokoza za Yehova kuti: “Pakuti chifundo chanu chiposa moyo makomedwe ake.” (Sal. 63:3) Chifukwa chakuti makolo anu akulererani m’choonadi, mwalandira chifundo cha Mulungu, chimene chakuthandizani kukhala naye paubwenzi. Kukhala ndi ubwenzi umenewu kukuposa moyo chifukwa ngakhale mumwalire, Mulungu adzakuukitsani kuti mukhale ndi moyo kosatha m’Paradaiso.
21. (a) Kodi achinyamata amene akudziŵa zoipa zimene achinyamata ena akuchita ali ndi udindo wotani? (b) Kodi ndi chitsanzo chabwino chiti chimene mtsikana wina wa zaka 13 anapereka?
21 Thandizani Ena Kupeŵa Moyo Wachiphamaso: Bwanji ngati mukudziŵa za wachinyamata wina amene ali ndi moyo wachiphamaso? Choyamba, mulimbikitseni kuonana ndi akulu. Nanga bwanji ngati akukana kuchita zimenezi? Inuyo muli ndi udindo wa m’Malemba wokauza akuluwo. (Lev. 5:1) Tikudziŵa kuti zimenezi sizingakhale zophweka, koma ndizo zoyenera kuchita. Baibulo limati: “Kulasa kwa bwenzi kuli kokhulupirika.” (Miy. 27:6) Mtsikana wina wa zaka 13, atamva nkhani yofotokoza udindo wake wa m’Malemba, anapita kwa mnzake amene iye ankadziŵa kuti ankachita zinthu zoipa ndipo anamuuza kuti akaulule kwa akulu. Mtsikanayu analemba kuti: “Ndinapitakonso kukaona ngati anakauza mkulu wina aliyense. Anali asanaulule. Motero ndinapita n’kukalankhula ndi mmodzi mwa akuluwo.” Mtsikanayu anafunsa kuti: “Kodi ndinachita bwino kukamunenera ‘mzanga wapamtima wakaleyu’”? Inde, anachita bwino. Ngakhale kuti zotsatira zake poyamba zingakhale zomvetsa chisoni, m’tsogolo zingakhale zosangalatsa, ngakhalenso zopulumutsa moyo wa munthu wolakwayo.—Aheb. 12:11.
22. Kodi achinyamata akulimbikitsidwa kuchita zinthu zanzeru ziti, ndipo zotsatira zake zidzakhala zotani?
22 Komabe, zonsezi zingapeŵedwe ngati poyamba pomwepo simunakhale ndi moyo wachiphamaso. Motero, khalani wanzeru. Khalani paubwenzi wolimba ndi Mulungu, monga mmene mungakhalire ndi mnzanu wapamtima. Chitani zimenezi mwa kupemphera kwa iye nthaŵi zonse, mwa kum’pempha kuti akuthandizeni, ndiponso mwa kuphunzira Mawu ake, Baibulo, mwakhama, kuti muthe kumvetsa makhalidwe ake. Achinyamata, mukatero mudzadalitsidwa ndipo mudzasangalatsa mtima wa makolo anu. Ndipo koposa zonse, mudzasangalatsa mtima wa Yehova.—Miy. 27:11.
Kodi Mungayankhe bwanji?
◼ N’chifukwa chiyani achinyamata ena ali ndi moyo wachiphamaso?
◼ Kodi makolo ena amathandizira bwanji kuti ana akhale ndi moyo wachiphamaso?
◼ Kodi kukhala ndi moyo wachiphamaso kumatanthauza chiyani?
◼ Kodi achinyamata angapeŵe bwanji kukhala ndi moyo wachiphamaso?
◼ Kodi achinyamata ali ndi udindo wotani akadziŵa kuti achinyamata ena achita tchimo lalikulu?