Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 6/04 tsamba 1
  • Angelo Akutithandiza

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Angelo Akutithandiza
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2004
  • Nkhani Yofanana
  • Angelo Ndiwo “Mizimu Yotumikira Anthu”
    Nsanja ya Olonda—2009
  • Mmene Angelo Angakuthandizireni
    Nsanja ya Olonda—1998
  • Angelo—Kodi Amayambukira Moyo Wanu?
    Nsanja ya Olonda—1987
  • Mmene Angelo Amatikhudzira
    Nsanja ya Olonda—2006
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2004
km 6/04 tsamba 1

Angelo Akutithandiza

1 “Onani, Ine ndili pamodzi ndi inu masiku onse, kufikira chimaliziro cha nthaŵi ya pansi pano.” Mawu ameneŵatu ndi olimbikitsa kwa anthu onse amene amamvera lamulo la Yesu lakuti: “Mukani, phunzitsani anthu a mitundu yonse.” (Mat. 28:18-20) Njira imodzi yofunika kwambiri imene Yesu amakhalira pamodzi ndi Akristu oona ndiyo kugwiritsa ntchito angelo ake. (Mat. 13:36-43) N’zosangalatsa kwambiri kulengeza “uthenga wabwino wosatha” pamodzi ndi zolengedwa zauzimu zokhulupirika zimenezi.—Chiv. 14:6, 7.

2 Mu Utumiki Wathu: Baibulo limafotokoza kuti angelo amatumizidwa ‘kuti atumikire iwo amene adzaloŵa chipulumutso.’ (Aheb. 1:14) M’zaka 100 zoyambirira, angelo anathandiza kulondolera otsatira a Yesu kwa anthu oyenerera. (Mac. 8:26) Masiku ano, atumiki a Mulungu akupitiriza kuona umboni woti angelo akuwathandiza. Eninyumba anenapo maulendo ambiri kuti anali akupemphera kuti athandizidwe pamene Mboni inabwera panyumba pawo. Timasangalala pamodzi ndi angelo, anthu oterowo akalandira uthenga wa Ufumu.—Luka 15:10.

3 Ena Akamatitsutsa: Danieli, Ahebri anzake atatu achinyamata, mtumwi Petro, ndi ena ambiri amene anakumana ndi mayesero aakulu anaona Yehova akuwathandiza pogwiritsa ntchito angelo kapena kuti amithenga, “a mphamvu zolimba.” (Sal. 103:20; Dan. 3:28; 6:21, 22; Mac. 12:11) Ngakhale kuti nthaŵi zina tingaone ngati tilibe pogwira ena akamatitsutsa, tingalimbikitsidwe ndi zimene mnyamata wa Elisa anaona pamene anazindikira kuti “okhala pamodzi ndi ife achuluka koposa aja okhala pamodzi ndi iwo.” (2 Maf. 6:15-17) Ngakhale atatisiyanitsa ndi abale athu achikristu motiumiriza, sitifunika kutaya mtima. Mawu a Mulungu amatitsimikizira kuti: “Mngelo wa Yehova azinga kuwachinjiriza iwo akuopa iye.”—Sal. 34:7.

4 Posachedwapa magulu ankhondo a angelo adzachita nkhondo kuti achotse onse amene amatsutsa ufumu wa Kristu. (Chiv. 19:11, 14, 15) Pamene tikuyembekezera nthaŵi imeneyo, tiyeni tipitirize kulemekeza Yehova molimba mtima, tikhulupirire ndi mtima wonse thandizo lamphamvu la ankhondo akumwamba olamulidwa ndi Kristu.—1 Pet. 3:22.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena