Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki
Mlungu Woyambira June 14
Mph. 7: Zilengezo za pampingo. Sankhani zilengezo zina mu Utumiki Wathu wa Ufumu uno. Gwiritsani ntchito mfundo zimene zili patsamba 8 (ngati zikugwirizana ndi gawo lanu) posonyeza chitsanzo cha mmene tingagaŵire Nsanja ya Olonda ya June 15 ndi Galamukani! ya July 8. Mu ulaliki umodzi, sonyezani wofalitsa akulalikira m’gawo la malonda. Mungagwiritsenso ntchito maulaliki ena oti angachitikedi. (Ngati magazini ameneŵa sanafike pampingopo, gwiritsani ntchito chitsanzo cha ulaliki cha mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa mwezi watha.)
Mph. 15: “Yehova Amathandiza Anthu Amene Amamudalira.” Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Pokambirana ndime 4 phatikizanipo ndemanga ya mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa March 2000, tsamba 6, ndime 3-4, ndi buku la Sukulu ya Utumiki, tsamba 67, ndime 1.
Mph. 23: “Achinyamata—Peŵani Moyo Wachiphamaso.” (Ndime 1-11) Ikambidwe ndi mkulu woyenerera. Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Gwiritsani ntchito mafunso amene aperekedwawo. Malemba amene ali ndi mfundo zazikulu ayenera kuŵerengedwa ndi kuwafotokozera.
Nyimbo Na. 179 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira June 21
Mph. 5: Zilengezo za pampingo.
Mph. 15: “Angelo Akutithandiza.” Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Pemphani omvera kupereka ndemanga pa malemba amene sanagwidwe mawu ngati nthaŵi ilola.
Mph. 20: “Achinyamata—Peŵani Moyo Wachiphamaso.” (Ndime 12-22) Ikambidwe ndi mkulu woyenerera. Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Gwiritsani ntchito mafunso amene aperekedwawo. Malemba amene ali ndi mfundo zazikulu ayenera kuŵerengedwa ndi kuwafotokozera. Kambirananinso mafunso obwereza amene ali m’bokosilo.
Nyimbo Na. 53 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira June 28
Mph. 12: Zilengezo za pampingo. Lipoti la maakaunti. Kumbutsani ofalitsa kupereka malipoti awo a utumiki wakumunda a June. Mwa kugwiritsa ntchito mfundo zimene zili patsamba 8 (ngati zikugwirizana ndi gawo lanu), sonyezani zitsanzo za mmene tingagaŵire Nsanja ya Olonda ya July 1 ndi Galamukani! ya July 8. M’chitsanzo chilichonse, wofalitsayo ayambe ndi mawu aubwenzi achidule. Fotokozani kuti kuchita zimenezi kungathandize mwininyumbayo kukhala womasuka. (Ngati magazini ameneŵa sanafike pampingopo, gwiritsani ntchito chitsanzo cha ulaliki cha mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa mwezi watha.)
Mph. 15: Zosoŵa za pampingo.
Mph. 18: “Chifukwa Chake Phunziro la Buku la Mpingo N’lofunika.” Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Gwiritsani ntchito mafunso amene aperekedwawo. Phatikizanipo ndemanga za m’nkhani yakuti “Thandizani Woyang’anira Phunziro Lanu la Buku la Mpingo,” imene inatuluka mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa November 2002, patsamba 1.
Nyimbo Na. 20 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira July 5
Mph. 10: Zilengezo za pampingo.
Mph. 15: Kodi Mukanena Chiyani? Nkhani ndi kukambirana ndi omvera. M’miyezi ya July ndi August, tidzagaŵira mabulosha. Kodi ndi mabulosha ati amene ofalitsa aona kuti ndi ogwira mtima kwambiri m’gawolo? Pendani maulaliki amene anaperekedwa mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa July 1998, tsamba 8, kapena wina wakale. Tsindikani kuti ulaliki uliwonse uli ndi (1) funso, (2) lemba, ndi (3) mfundo yoti mukambirane ya m’buloshalo. Chitirani chitsanzo ulaliki umodzi kapena maulaliki aŵiri. Limbikitsani onse kugwiritsa ntchito Baibulo polalikira uthenga wabwino.
Mph. 20: Zimene Ana Amafuna kwa Makolo Awo. Nkhani ndi kukambirana ndi omvera pogwiritsa ntchito buku la Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso, masamba 6-7. N’zofunika kuti ana aphunzire mfundo za m’Baibulo za kulambira koona ndi kumvetsa ntchito yaikulu imene makolo amachita pophunzitsa ana. Kambiranani mfundo zimene zaperekedwa zophunzirira bukuli. Apempheni makolo kufotokoza mmene agwiritsira ntchito chida chophunzirira chimenechi. Konzani zoti mwana mmodzi kapena aŵiri afotokoze chifukwa chake amalikonda bukuli.
Nyimbo Na. 65 ndi pemphero lomaliza.