Kodi Pangakhale Vuto Lililonse ndi Kuchita za Matsenga ndi Ufiti?—Gawo 2
1. Kodi Satana amafuna kuti ife tikhulupirire chiyani, ndipo ndi fanizo lotani limene likusonyeza zimenezi?
1 Satana ndi katswiri ponyenga anthu. Amapusitsa anthu powachititsa kuganiza kuti iye ali ndi mphamvu kwambiri kusiyana ndi zimene ali nazo. Tifotokoze mwafanizo: Pankhondo yaposachedwapa m’dziko lina mu Africa muno, asilikali anagwiritsa ntchito zokuzira mawu poopseza adani awo. Asilikaliwo akafuna kuukira anzawo, anali kuliza kwambiri makaseti amene anajambulamo kulira kwa mizinga ndi mfuti. Pochita zimenezi iwo anali kufuna kupusitsa adani awo kuganiza kuti gulu limene likuwaukiralo lili ndi zida zambiri zoopsa. N’chimodzimodzinso ndi Satana. Iye amafuna kuti anthu azikhulupirira kuti ali ndi mphamvu zopanda malire. Cholinga chake n’chakuti aopseze anthu kuti achite zofuna zake m’malo mwa zofuna za Mulungu.
2. Kodi Baibulo limasonyeza bwanji kuti Satana si amene amachititsa mavuto onse?
2 Ngakhale kuti Satana ali ndi mphamvu yoyambitsa mavuto ena, n’kulakwa kuganiza kuti ali ndi mphamvu yoyambitsa mavuto onse. Baibulo limati: ‘Omwe athamanga msanga sapambana m’liwiro, ngakhale olimba sapambana m’nkhondo, ngakhale anzeru sapeza zakudya, ngakhale ozindikira bwino salemera, ngakhale odziwitsa sawakomera mtima; koma yense angoona zom’gwera m’nthawi yake.’ (Mlaliki 9:11) Pa mpikisano wothamanga, wina akhoza kukhala waliwiro kwambiri kuposa anzake onse, koma sangapambane. “Zochitika zosayembekezera” zingam’lepheretse. Zingachitike kuti pamene akuthamanga angapunthwe n’kugwa kapena angadwale kapena minofu ya m’miyendo ingakungane. Zimenezi zingachitike kwa wina aliyense. Sikuti Satana ndi amene amachititsa zimenezo kapena kuti zimachitika chifukwa cha ufiti ayi, ndi zinthu zoti zimangochitika basi.
3. Kodi okhulupirira zamatsenga amaphunzitsa kuti ufiti uli ndi phindu lanji?
3 Amene amakhulupirira zamatsenga amanena kuti pali matsenga abwino. Zitsanzo za matsenga amene amawatcha kuti matsenga abwinowa zimaphatikizapo kudziteteza mwa kuvala mphete zamatsenga kapena makoza amatsenga, kumwa mankhwala odziteteza, kapena kutemera mankhwala. Munthu akhoza kubisa zithumwa panyumba pokhulupirira kuti zili ndi mphamvu yoteteza, n’cholinga cholepheretsa mfiti kumulodza. Okhulupirira zamatsenga amanenanso kuti matsenga abwino akhoza kuteteza munthu pa mbali ina iliyonse. Mwachitsanzo, kudziteteza kuti mbava zisakubere, kuyeretsera panyumba pochotsa mphamvu zovulaza zomwe wina amene ankakhala pamalopo poyamba anazisiya, kupangitsa munthu kuti ukhale naye pachibwenzi, kuchiritsa ndi kuteteza kuti usamadwaledwale, kuteteza kuti asakuchotse ntchito, ndiponso kupezera ndalama. Chifukwa cha mphamvu zochuluka zimenezi zomwe akuti mfitizi zimakhala nazo, n’zosadabwitsa kuti ufiti wafala kwambiri.
4. Kodi Malemba amati chiyani pa zamatsenga?
4 Komabe, Malemba sasiyanitsa pakati pa matsenga omwe amati ndi abwino ndi matsenga oipa. Mu Chilamulo choperekedwa kwa Mose, Mulungu ananena momveka bwino mmene amaonera matsenga. Iye anati: “Musamachita nyanga.” (Levitiko 19:26) Timawerenganso kuti: ‘Asapezeke mwa inu munthu . . . wanyanga kapena wotsirika kapena wosamalira kulira kwa mbalame, kapena wobwebweta, kapena wopenduza, kapena wofunsira akufa.’—Deuteronomo 18:10, 11.
5. N’chifukwa chiyani Yehova amadana ndi mtundu uliwonse wa zamizimu?
5 Yehova Mulungu amadana ndi mitundu yonse ya zamizimu. Chifukwa chiyani? Anthu akale a Yehova anawachenjeza kuti: ‘Musamatembenukira kwa obwebweta, kapena anyanga; musawafuna, ndi kudetsedwa nawo.’ (Lev. 19:31; 20:6, 27) Buku la m’Baibulo la Chivumbulutso limapereka chenjezo lakuti: “Amene amachita zamatsenga,” (Chipangano Chatsopano mu Chichewa cha Lero) adzathera “m’nyanja yotentha ndi moto ndi sulfure; ndiyo imfa yachiwiri [yosatha.]” (Chiv. 21:8; 22:15) Chifukwa chochita zamizimu, ziwanda zingamativutitse kapenanso tingagwidwe ndi mizimu yoipa. N’chifukwa chake Mulungu amatichenjeza mwachikondi kuti tipewe kuchita chilichonse chokhudza mizimu. (Deut. 18:14; Agal. 5:19-21) Ndiponso, ngati tipitirizabe kuchita zamizimu pambuyo poti tadziwa mmene Yehova amazionera, tidzakhala tikugwirizana ndi mizimu yoipa ndipo tidzakhala adani a Mulungu.—1 Sam. 15:23; 1 Mbiri 10:13, 14; Sal. 5:4.
6. Kodi ndi chitsanzo chiti chimene chikusonyeza kuti Yehova ndi wamphamvu kwambiri kuposa Satana?
6 Malemba amasonyeza kuti Yehova ali ndi mphamvu zambirimbiri kuposa Satana ndi atumiki ake. Mwachitsanzo, Balamu ankafuna kutemberera anthu a Mulungu pogwiritsa ntchito matsenga. (Numeri 22:7, 20-35) Koma Yehova anapangitsa matsenga a Balamu kukhala opanda ntchito. Anasintha matemberero akewo kukhala madalitso. Ndipo Balamu anavomereza kuti: “Palibe nyanga [imene ingalodze] Yakobo, kapena ula [umene ungagwere] Israyeli.” (Numeri 23:23) Lemba la Miyambo 18:10 limati: “Dzina la Yehova ndilo linga lolimba; wolungama athamangiramo napulumuka.” Chotero tiyenera kuyang’ana kwa Yehova kuti atiteteze. Atumiki a Mulungu sakhulupirira kuti zithumwa kapena mankhwala zingawateteze ku zoipa zimene Satana ndi ziwanda zake amachita, ndipo saopa kuti mfiti zingawalodze. Atumiki a Mulungu amakhulupirira zimene Baibulo limanena kuti: “Pakuti maso a Yehova ayang’ana uko ndi uko m’dziko lonse lapansi, kudzionetsera wamphamvu kwa iwo amene mtima wawo uli wangwiro ndi Iye.”—2 Mbiri 16:9.
7. Kodi tingayembekeze kuti Yehova atichitira chiyani ngati timvera Iye?
7 Inunso mungakhale ndi chikhulupiriro chimenechi ngati mukutumikira Yehova. Yakobo 4:7 amati: “Mverani Mulungu; koma kanizani Mdyerekezi, ndipo adzakuthawani inu.” Kodi tingachite bwanji zimenezi? Mwa kuonetsetsa kuti sitikuchita chilichonse chokhudza zamizimu. Zimenezi zikuphatikizapo miyambo ya pamaliro. Mwachitsanzo, n’chibadwa munthu kulira ndi kumva chisoni kwambiri pamene munthu amene umam’konda wamwalira. Koma kulira mosagwirika kwinaku ukulankhula mokuwa zinayamba chifukwa chofuna kusangalatsa akufa. Ndiponso tifunika kusamala kwambiri tikamafuna mankhwala. Ambiri amene amati amadziwa mankhwala amachita zamizimu. Mwachitsanzo, taganizani za chizolowezi choveka khanda kachingwe. Kodi n’zoona kuti kachingweko kangateteze matenda? Kodi kachingweko kali ndi mphamvu yanji? Zinthu zimenezo n’zochokera ku zamizimu ndipo tiyenera kuzipewa kuti tikondweretse Mulungu. Ngati tikutumikira Mulungu woona ndi kumvera iye, Yehova adzatiteteza.
8. Kodi Malemba amatitsimikiziranso za chiyani?
8 Mtumwi Yohane anatsimikiziranso okhulupirira anzake kuti: “Chilichonse tipempha, tilandira kwa Iye [Mulungu] chifukwa tisunga malamulo ake, ndipo tichita zom’kondweretsa pamaso pake.” (1 Yoh. 3:22) Inde, “mngelo wa Yehova azinga kuwatchinjiriza iwo akuopa Iye, nawalanditsa iwo.” (Sal. 34:7) Ngati tikhulupirira Mulungu ndi kuvala zida zankhondo zauzimu zimene amapereka, Yehova adzagonjetsa aliyense amene angayesere kuchita zaufiti kuti ativulaze.—Aef. 6:10-18.