Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 7/07 tsamba 3-4
  • Kugulitsa Malonda Pamisonkhano Yathu Yachigawo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kugulitsa Malonda Pamisonkhano Yathu Yachigawo
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2007
Utumiki Wathu wa Ufumu—2007
km 7/07 tsamba 3-4

Kugulitsa Malonda Pamisonkhano Yathu Yachigawo

1 Chaka chatha pamisonkhano yathu yachigawo yakuti “Chipulumutso Chayandikira,” zinali zolimbikitsa kuona abale ndi alongo, mabwenzi athu ndi anthu achidwi akucheza pa nthawi yopuma. Zimenezi zinali zotheka chifukwa ambiri anamvera malangizo oti abweretse chakudya m’malo mochoka pa malo a msonkhano kuti akagule chakudya. Tikukuyamikirani abale ndi alongo chifukwa chomvera malangizo amenewo.—Afil. 2:12, 13.

2 Popeza kuti misonkhano yachigawo ya chaka chino yakuti “Tsatirani Khristu!” yayandikira, tingachite bwino kuona mawu a mtumwi Petulo omwe ali pa 2 Petulo 1:12, 13, akuti: “Nthawi zonse ndizikukumbutsani zinthu zimenezi, ngakhale kuti mukuzidziwa kale ndipo ndinu okhazikika molimba m’choonadi chimene munachilandira. Chotero ndikuona kuti n’koyenera kumakugalamutsani mwa kukukumbutsani.” Ifenso tikusangalala kukukumbutsani zinthu zina zokhudza khalidwe lathu pamisonkhano imeneyi. Malingana ndi zimene zinachitika pa misonkhano ya m’mbuyomu, zikuoneka kuti abale ena amachokabe pa malo a msonkhano kuti akagule chakudya kwa ogulitsa zakudya m’mphepete mwa msewu kapena ku malesitilanti omwe ali pafupi. Nthawi zina anthu ena amachoka pa malo a msonkhano ngakhale kudya kumene, msonkhano uli m’kati. Kuchita zimenezi ndi kupanda ulemu.

3 Kumalo ena, anthu ogulitsa zakudya afika mpaka poumirira kuti apatsidwe malo ogulitsirapo malonda awo chapafupi ndi malo a msonkhanowo. Kulola zimenezi kungapangitse kuti pamisonkhano pazikhala anthu ambiri akunja amene angasokoneze bata lathu pamisonkhanoyi.

4 Pamisonkhano ina yachigawo, abale ena amakambirana nkhani zosiyanasiyana zamalonda. Ena amabweretsa malonda awo monga nzimbe, mbatata, chinangwa, mpunga, mandasi, zitumbuwa, nthochi, ndiwo zamasamba ndi zina zambiri, n’cholinga choti agulitse kwa Akhristu anzawo. Khalidwe limeneli si labwino konse. Tiyenera kupeweratu chilichonse chokhudza kapena cholimbikitsa malonda pamalo a misonkhano yachigawo. Zinthu zimenezi n’zosagwirizana n’komwe ndi cholinga chathu cha m’Malemba chosonkhanira pamodzi.—Aheb. 10:24, 25.

5 M’pofunika Kusamala: Aliyense amene apite ku msonkhano wachigawo wa chaka chino wakuti “Tsatirani Khristu!” akufunika kukumbukira zotsatirazi:

◼ Abale ndi alongo asadzabweretse zinthu zogulitsa pamalo a msonkhano wachigawo.

◼ Abale ndi alongo komanso anthu achidwi asadzagule kanthu kalikonse kwa aliyense wogulitsa chakudya amene angadzayale malonda ake pamalo a msonkhano. Kuti tipitirize kukhala audongo ndi adongosolo, m’pofunika kuti ogulitsa malonda asadzapezekepo n’komwe pamalo a msonkhano. Ngati abale akufuna kugula zinthu, agule zinthuzo kumsika kapena kusitolo, ndipo achite zimenezo msonkhano usanayambe kapena utatha.

◼ Msonkhano usanayambe, akalinde ayenera kuuza ogulitsa malonda onse mwaulemu kuti achoke pa malo athu olambirira. Ngati akufuna angakayale malonda awowo kutali ndi malo athu a msonkhano.—1 Pet. 1:12.

6 Ndife osangalala kwambiri kuti misonkhano yathu yachigawo yakuti “Tsatirani Khristu!” idzayamba posachedwapa. Tiyeni tonse tionetsetse kuti takonzekera kukakhala nawo pamsonkhano wonse, kuti tidzapindule kwambiri ndi phwando labwino lauzimu limene Yehova watikonzera kudzera m’gulu lake. Potero tidzakhala ‘okonzeka bwino lomwe kuchita ntchito iliyonse yabwino’ m’masiku otsatira.—2 Tim. 3:17.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena