Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki
Dziwani Izi: M’miyezi ikubwerayi Utumiki Wathu wa Ufumu uzikhalabe ndi ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki ya mlungu uliwonse. Mipingo ingasinthe ndandanda moyenera kuti ikapezeke pa Msonkhano Wachigawo wakuti “Tsatirani Khristu!” Ngati n’koyenera, gwiritsani ntchito mphindi 15 pa Msonkhano wa Utumiki womaliza musanapite ku msonkhano wachigawo kuti muonenso malangizo oyenera ndi zikumbutso za mu mphatika ya Utumiki Wathu wa Ufumu uno zimene zikukhudza mpingo wanu. Pakadutsa mwezi umodzi kapena iwiri utatha msonkhano wachigawo, gwiritsani ntchito mphindi 15 mpaka 20 za mu Msonkhano wa Utumiki (mwina mungagwiritse ntchito chigawo cha zosowa za pampingo) kuti mubwereze mfundo za msonkhano wachigawo zimene ofalitsa aona kuti n’zothandiza muutumiki. Woyang’anira utumiki asamalire mbali imeneyi. Pemphani omvera kufotokoza mmene akugwiritsira ntchito mfundozo muutumiki wawo.
Mlungu Woyambira July 9
Mph.10: Zilengezo za pampingo. Gwiritsani ntchito mfundo zimene zili pa tsamba 8 kapena mfundo zina zothandiza m’gawo lanu, posonyeza zitsanzo za mmene tingagawirire Nsanja ya Olonda ya July 15 ndi Galamukani! ya July. (Ngati mpingo wanu sunalandire magazini tatchulawa gwiritsirani ntchito zitsanzo za mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa mwezi watha.)
Mph.15: “Kusintha Kosangalatsa kwa Nsanja ya Olonda.”*
Mph.20: Bokosi la Mafunso. Ikambidwe ndi mkulu. Werengani ndi kukambirana nkhani yonse. Phatikizanipo ndemanga zofotokoza mfundo za mu Galamukani! ya June 8, 2005, masamba 29 ndi 30, pa kamutu kakuti, “Kuopsa kwa Chinyengo ndi Kuchita Zinthu Mwakabisira” ndiponso kakuti, “Munthu Womuona Ali Bwino Kusiyana ndi Wongom’dziwira pa Intaneti.”
Nyimbo Na. 91 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira July 16
Mph.5: Zilengezo za pampingo.
Mph.25: “Tsatirani Khristu Podzisungira Ulemu.” Ikambidwe ndi mlembi wa mpingo. Tchulani msonkhano wachigawo umene mpingo wanu uyenera kupezeka. Mukambirane bokosi lakuti, “Zofunika Kukumbukira pa Msonkhano Wachigawo.”
Mph.15: “Kugulitsa Malonda Pamisonkhano Yathu Yachigawo.”a Tsindikani kufunika koti anthu abweretse chakudya m’malo mochoka pa malo amsonkhano ndi kukagula chakudya kwa ogulitsa zakudya m’mphepete mwa msewu kapena ku malesitilanti omwe ali pafupi.
Nyimbo Na. 189 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira July 23
Mph.10: Zilengezo za pampingo. Werengani lipoti la maakaunti ndi mawu oyamikira zopereka olembedwa pa sitetimenti. Gwiritsani ntchito mfundo zimene zili pa tsamba 8 kapena mfundo zina zothandiza m’gawo lanu, posonyeza zitsanzo za mmene tingagawirire Nsanja ya Olonda ya August 1 ndi Galamukani! ya August. (Ngati mpingo wanu sunalandire magazini tatchulawa gwiritsirani ntchito zitsanzo za mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa mwezi watha.)
Mph.20: Mucherezane Wina ndi Mnzake. Nkhani yochokera mu Nsanja ya Olonda ya January 15, 2005, masamba 21 mpaka 23. Mwachidule funsani wofalitsa mmodzi kapena awiri omwe amadziwika kuti ndi ochereza. Kodi achita chiyani kuti azichereza anthu ena? Kodi iwo limodzi ndi mabanja awo akhala ndi madalitso chifukwa chokhala ochereza?
Mph.15: Kodi N’chiyani Chimachititsa Anthu Kukhala ndi Chimwemwe Chenicheni? Nkhani yokambirana ndi omvetsera yochokera mu Nsanja ya Olonda ya May 15, 2006, masamba 28 ndi 29, ndime 11 ndi 12. Mwachidule funsani munthu yemwe wasankha utumiki kukhala ntchito yake yofunika m’malo mwa zosangalatsa kapena ntchito ina. N’chifukwa chiyani anasankha zolinga zauzimu? Kodi zimenezi zam’bweretsera motani chimwemwe?
Nyimbo Na. 61 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira July 30
Mph.10: Zilengezo za pampingo. Kumbutsani ofalitsa kuti apereke malipoti awo a utumiki wa kumunda a mwezi wa July.
Mph.15: Yehova Amadalitsa Anthu Odzimana. Nkhani yochokera mu Nsanja ya Olonda ya November 15, 2005, masamba 8 ndi 9.
Mph.20: “Ali Wosangalala Munthu Wopirira Mayesero.”b Pokambirana ndime 3, pemphani omvetsera kupereka ndemanga za mmene chikhulupiriro cholimba chinawathandizira pamene mayesero anayamba mwadzidzidzi. Mungakonzekeretseretu munthu mmodzi kapena awiri kuti adzapereke ndemanga.
Nyimbo Na. 13 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira August 6
Mph.5: Zilengezo za pampingo. Zilengezo zina musankhe mu Utumiki Wathu wa Ufumu uno.
Mph.20: Kusunga Mtendere ndi Chiyero cha Mpingo. Nkhani yokambirana ndi omvetsera yochokera m’buku la Gulu Lochita Chifuniro cha Yehova kuyambira pa tsamba 144 kukalekezera pa kamutu ka patsamba 150.
Mph.20: “Chifukwa Chake Timapita Mobwerezabwereza.”c Pokambirana ndime 5, pemphani omvetsera kuti afotokoze chifukwa chake anafuna kuphunzira zowonjezereka ngakhale kuti poyamba ankatsutsa kapena analibe chidwi.
Nyimbo Na. 211 ndi pemphero lomaliza.
[Mawu a M’munsi]
a Mawu oyamba asapitirire mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho.
b Mawu oyamba asapitirire mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho.
c Mawu oyamba asapitirire mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho.