Nyimbo 186
Chimwemwe Chathu Chaumulungu
1. Tifunikira chimwemwe
Kuti tipilire.
Chimwemwechi chimafuna
Chikhulupiliro.
Simkhalidwe wakanthaŵi;
Ndiwanthaŵi zonse.
Nchifukwa timaŵerenga
Kuti “Kondwerani!”
2. Tikondwere kuti ndife
Odziŵa Mulungu;
Tiri ndi ulemu monga
Mboni muumodzi.
Tikondwa chifukwa M’lungu
Adzatamandidwa,
Akufawo adzauka
Nadzakhala m’dziko.
3. Kukulitsa chimwemwechi
Timvere Mulungu,
Titchinjirize mitima
Kupanda njirunso.
Tikhale amasobe ndi
Kutamanda M’lungu;
Nthaŵi zonse tiganize
Pazopindulitsa.
4. Nkana tiponderezedwa
Tipeza zambiri,
Chimwemwe ndi mphotho yathu
Pomtumikiradi.
Tiri mboni za Yehova
Kunena za iye.
Tidzazidwe ndi chimwemwe
Pamodzi ndi ena.