Fufuzani Anthu Oyenerera
1. Kodi timasonyeza bwanji kuti tikuyamikira utumiki wathu?
1 Panthawi yomwe Yesu ankachita utumiki padziko lapansi, ankayesetsa kutonthoza anthu ofatsa powauza uthenga wabwino. (Yes. 61:1, 2) Ifenso masiku ano, monga akazembe ndi nthumwi zoimira Khristu, tiyenera kuyesetsa kutengera chitsanzo chake pofufuza mwakhama anthu oyenerera m’gawo lathu.—Mat. 10:11; 2 Akor. 5:20.
2. Kodi Paulo anasintha bwanji gawo lake, ndipo zotsatira zake zinali zotani?
2 Muzisintha: Mtumwi Paulo ankakonda kupita m’masunagoge kukalalikira kwa Ayuda ndi anthu otembenukira ku Chiyuda. (Mac. 14:1) Koma nthawi ina iye ndi Sila ali ku Filipi, anapita kukafufuza anthu ‘kumene anali kuganiza kuti kuli malo opempherera.’ Atapita kumeneko anayamba kulalikira gulu la amayi, ndipo mmodzi mwa iwo, dzina lake Lidiya, sanachedwe kukhulupirira choonadi.—Mac. 16:12-15.
3. Kuwonjezera pa ulaliki wa nyumba ndi nyumba, kodi ndi ulaliki winanso uti umene tingachite?
3 Kuwonjezera pa kulalikira nyumba ndi nyumba, mungathenso kulalikira m’malo okwerera basi ndi sitima, m’mapaki, m’maofesi, m’misewu, m’malo ochitira malonda, ndiponso m’masitolo a m’gawo lanu. Mwina mungathenso kulalikira m’nyumba zokhala ndi mipanda ndiponso malo ena amene salola anthu kufikako polemba kalata kapena kuimba foni. Kuyesetsa kudziwa zinthu zochitika m’gawo lanu komanso kusintha njira zolalikirira kungakuthandizeni kukhala ndi “zochita zochuluka m’ntchito ya Ambuye.”—1 Akor. 15:58.
4. Kodi tingathe kuchita chiyani ngati mpingo wathu uli ndi gawo laling’ono?
4 Ofalitsa ambiri awonjezera utumiki wawo posamukira ku mipingo kumene kukufunikira ofalitsa Ufumu ambiri. Ena amaphunzira chinenero china kuti athe kulalikira anthu ochokera m’mayiko ena.
5. Kodi tiyenera kuiona bwanji nthawi imene tikukhalayi, ndipo tiyenera kuyesetsa kuchita chiyani?
5 Tonse tiyenera kukumbukira kuti “munda ndiwo dziko.” (Mat. 9:37; 13:38) Popeza kuti mapeto a dongosolo la zinthu loipali ayandikira, aliyense ayenera kuganizira mozama mmene zinthu zilili pamoyo wake, luso lake ndi mipata imene ali nayo kuti aone ngati angathe kuwonjezera utumiki wake. Yehova amatitsimikizira kuti ngati tiika patsogolo ufumu wake, adzadalitsa khama lathu lowonjezera utumiki.—Mat. 6:33.