PHUNZIRO 32
Kulankhula Motsimikiza
PAMENE munthu alankhula motsimikiza, ena amaona kuti munthuyo amakhulupiriradi zimene akunenazo. Mofananamo, mtumwi Paulo pochita ulaliki wake, anthu anali kuona kuti anali wotsimikiza pa zimene anali kunena. Kwa amene anakhala okhulupirira ku Tesalonika, iye anawalembera kuti: “Uthenga wabwino wathu sunadza kwa inu m’mawu mokha, komatunso . . . ndi kutsimikiza kwamphamvu.” (1 Ates. 1:5, NW) Kutsimikiza kumeneko kunaonekeratu m’kalankhulidwe kake ndi m’moyo wake. Njira imene tikufotokozera mfundo za m’Baibulo iyenera kusonyezanso kuti tili otsimikiza kwambiri pankhaniyo.
Kulankhula motsimikiza kumasiyana ndi kungonena za m’mutu, kapena kukhala woumirira maganizo ako, kapena wosamva za ena. M’malo mwake, pamene munthu wolankhula motsimikiza afotokoza zinthu za m’Mawu a Mulungu, amatero m’njira yosonyeza chikhulupiriro champhamvu.—Aheb. 11:1.
Pamene Muyenera Kulankhula Motsimikiza. M’pofunika kulankhula motsimikiza pamene muli mu utumiki wa kumunda. Kaŵirikaŵiri, anthu amatha kuona kalankhulidwe kanu ngati mmene amaoneranso uthenga wanu. Amatha kuzindikira maganizo anu pa zimene mukunenazo. Kutsimikiza kwanu kumatha kusonyeza bwino koposa mawu anu, kuti muli ndi uthenga wa phindu lalikulu.
M’pofunikanso kukhala wotsimikiza polankhula kwa okhulupirira anzanu. Mtumwi Petro analemba kalata yake yoyamba youziridwa ‘podandaulira ndi kupereka umboni za chisomo choona cha Mulungu.’ Ndipo m’chisomo chimenecho analimbikitsa abale ake kuti: “Muimemo.” (1 Pet. 5:12) Polembera mpingo wa ku Roma, mtumwi Paulo anasonyeza kuti anali wotsimikiza ndipo zimenezo zinawapindulitsa. Analemba kuti: “Ndakopeka mtima [“ndatsimikiza,” NW] kuti ngakhale imfa, ngakhale moyo, ngakhale angelo, ngakhale maufumu, ngakhale zinthu zilipo, ngakhale zinthu zilinkudza, ngakhale zimphamvu, ngakhale utali, ngakhale kuya, ngakhale cholengedwa china chilichonse, sichingadzakhoze kutisiyanitsa ife ndi chikondi cha Mulungu, chimene chili mwa Kristu Yesu Ambuye wathu.” (Aroma 8:38, 39) Paulo analembanso mokopa mtima za kufunika kolalikira kwa ena, ndipo kukangalika kwake m’ntchito imeneyo kunaonetseratu kuti analidi wotsimikiza za kufunika kwa ntchitoyo. (Mac. 20:18-21; Aroma 10:9, 13-15) Momwemonso akulu achikristu lerolino ayenera kusonyeza kuti ndi otsimikiza akamaphunzitsa Mawu a Mulungu.
Pophunzira ndi ana awo komanso nthaŵi zina, makolo ayenera kulankhula motsimikiza pokambirana nkhani zauzimu. Kuti makolo achite zimenezo afunikira kukulitsa chikondi chawo pa Mulungu ndi njira zake. Akatero akhoza kulankhula motsimikiza mtima kwa ana awo, pakuti munthu “atulutsa zabwino m’chuma chokoma cha mtima wake.” (Luka 6:45; Deut. 6:5-7) Kukhala wotsimikiza motero kungalimbikitsenso makolo kupereka chitsanzo cha “chikhulupiriro chosanyenga.”—2 Tim. 1:5.
Kulankhula motsimikiza n’kofunika makamakanso chikhulupiriro chanu chikamayesedwa. Mnzanu wa kusukulu, mphunzitsi, kapena mnzanu wa kuntchito angadabwe poona kuti simukuchita nawo chikondwerero chinachake. Kuyankha kwanu motsindika ndi molingalira bwino kungam’chititse kulemekeza chikhulupiriro chanu cha m’Baibulo. Koma bwanji ngati munthu wina akuyesa kukunyengererani kuti muchite choipa—monga kunama, kumwa mankhwala osokoneza bongo, kapena chiwerewere? Muyenera kukana motsindika kuti simungayerekeze kuchita khalidwe limenelo ndipo palibe chimene chingasinthe maganizo anu. Zimenezi zimafuna kuti mulankhule motsimikiza pokana zimene akufunazo. Pamene Yosefe anakana mkazi wa Potifara, ananena motsindika kuti: “Ndikachita choipa chachikulu ichi bwanji ndi kuchimwira Mulungu?” Pamene mkaziyo anaumirira, Yosefe anangothaŵa ndi kutuluka m’nyumbamo.—Gen. 39:9, 12.
Mmene Mungalankhulire Motsimikiza. Mawu amene mukugwiritsa ntchito amatha kusonyeza kuti mukulankhula motsimikiza. Nthaŵi zambiri, Yesu ponena mawu ofunika kwambiri anayamba ndi mawu akuti: “Indetu, indetu, ndinena ndi iwe.” (Yoh. 3:3, 5, 11; 5:19, 24, 25) Paulo anasonyeza kutsimikiza mtima kwake m’mawu ngati akuti “ndakopeka mtima,” “ndidziŵa, ndipo ndakhazikika mtima mwa Ambuye Yesu,” ndi akuti “ndinena zoona, wosanama ine.” (Aroma 8:38; 14:14; 1 Tim. 2:7) Nthaŵi zina Yehova anauzira aneneri ake kuti anenere motsindika za kukwaniritsidwa kwa mawu ake; anati azinena mawu otsimikiza ngati akuti, “Afika ndithu, osazengereza.” (Hab. 2:3) Pamene mukunena za maulosi ameneŵa, inunso mungagwiritse ntchito mawu ofananako. Ngati m’malo modzidalira nokha mumadalira Yehova, ndiponso ngati mulankhula kwa anthu motsimikiza koma mwaulemu, iwo adzaona kuti muli ndi chikhulupiriro champhamvu.
Mungasonyezenso kutsimikiza koteroko mwa kulankhula moona mtima ndi mphamvu ya mawu anu. Nkhope yanu, manja, ndi thupi, zonse zimathandizana posonyeza kutsimikiza kwanu, ngakhale kuti zimachitika mosiyana kwa anthu osiyanasiyana. Ngakhale kuti mwachibadwa ndinu wamanyazi kapena wofatsa, ngati mwakhutira ndi mtima wonse kuti nkhani imene mukunena ndi yoona ndipo n’njofunika kuti ena aimve, kutsimikiza mtima kwanu kudzaonekera.
Komabe, mawu alionse otsimikiza amene tinganene ayenera kukhala enieni. Ngati anthu aona kuti zimene tikulankhula sizikuchokera mu mtima, amaganiza kuti tikungonena zinthu zopanda phindu lenileni. Choncho, chofunika n’chakuti muzilankhula mwachibadwa. Malinga ndi kuchuluka kwa omvera anu, nthaŵi zina mungafunikire kukweza mawu ndi kuwonjezera mphamvu ya mawu anu. Koma cholinga chanu chizikhala kulankhula moona mtima ndi mwachibadwa.
Zimene Zingakuthandizeni Kulankhula Motsimikiza. Popeza kuti kulankhula motsimikiza kumadaliranso mmene mukuionera nkhaniyo, kukonzekera n’kofunika kwambiri. Kungokopera mfundo kuchokera m’chofalitsa chinachake kenako n’kuzilankhula mongozibwereza n’kosakwanira. Muyenera kuzimvetsa mfundozo ndi kutha kuzifotokoza m’mawu anuanu. Muyenera kukhala wokhutira kwathunthu kuti ndi zoona ndipo zimene mukunenazo n’zopindulitsa kwa omvera anu. Izi zikutanthauza kuti pamene mukukonza nkhani yanu, muyenera kuganizira mikhalidwe yawo ndi zimene angakhale akuzidziŵa kale pankhaniyo kapena mmene angaionere.
Ngati tikulankhula mosadodoma, ena akhoza kuona mosavuta kuti tikulankhula motsimikiza. Choncho, kuwonjezera pa kusankha mfundo zabwino, konzekerani kalankhulidwe kosadodoma. Pokonzekera nkhani, samalani kwambiri mbali zozamirapo kotero kuti mukazilankhule bwino mosadalira kwambiri kuyang’ana manotsi. Kumbukiraninso kupemphera kwa Yehova kuti adalitse zoyesayesa zanu. Mwa njira imeneyi ‘mudzalimbika pakamwa mwa Mulungu’ kulankhula m’njira yosonyeza kutsimikiza kwanu za choonadi ndi kufunika kwa uthenga wanu.—1 Ates. 2:2.