Nyimbo 80
Tizichita Zinthu Zabwino
Losindikizidwa
1. N’zosangalatsa kudziwa
Ubwino wa Yehova.
Monga Tate wakumwamba
Amachita zabwino.
Amasonyeza chifundo
Ndipo amatikonda.
N’ngoyenera kum’lambira
Ndi kumutumikira.
2. M’chifaniziro cha M’lungu
Anatilenga ife,
Kuti makhalidwe ake
Inde, tiwasonyeze.
Ubwino wathu ukule
Mulungu tim’tsanzire,
Chipatso cha mzimu wake
Tifuna tisonyeze.
3. Makamaka ’bale athu
Tiwakomere mtima,
Komanso kwa anthu onse
Tisonyeze ubwino.
Pomwe tikulalikira
Uthenga wa Ufumu
Tikhale opanda tsankho
Abwino m’zinthu zonse.
(Onaninso Sal. 103:10; Maliko 10:18; Agal. 5:22; Aef. 5:9.)