CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | MLALIKI 1-6
Muzisangalala Chifukwa Chogwira Ntchito Mwakhama
Yehova amafuna kuti tizisangalala ndi ntchito yathu ndipo amatiphunzitsa mmene tingachitire zimenezi. Munthu akhoza kumasangalala ndi ntchito yake ngati amaigwira ndi maganizo oyenera.
Mukhoza kumasangalala ndi ntchito yanu . . .
mukamaona ntchitoyo moyenera
mukamaganizira mmene ntchitoyo imathandizira anthu ena
mukamaigwira mwakhama, komabe mukaweruka muziyesetsa kuika maganizo pa banja lanu ndiponso kutumikira Yehova