PHUNZIRO 50
Yesetsani Kuwafika Pamtima Anthu
KUWONJEZERA pa umboni umene mumapereka kwa anthu, muyeneranso kuyesetsa kuwafika pamtima. M’Baibulo, mtima kaŵirikaŵiri amaufotokoza kukhala wosiyana ndi maonekedwe a munthu akunja. Mtima wofanizira umaimira mmene munthu alili m’kati—mmene amalingalirira, maganizo ake onse, chimene chikum’khalitsa ndi maganizowo, ndi mmene maganizowo amalimbikitsira zochita zake. Mu mtima wofanizira umenewu, ndi mmene mbewu ya choonadi imabzalidwa. (Mat. 13:19) Ndiponso ndi mu mtima womwewonso mmene muyenera kuchokera kumvera Mulungu.—Miy. 3:1; Aroma 6:17.
Kuti kuphunzitsa kwanu kukhale kofika pamtima, ikani maganizo anu pa zinthu izi: (1) Dziŵani zimene zili m’mtima mwa womvera wanu. (2) Limbikitsani makhalidwe abwino, monga chikondi ndi kuopa Mulungu. (3) Limbikitsani womvera wanu kuti azifufuza zolinga zake kuti akathe kukondweretsa Yehova mokwanira.
Khalani Wozindikira. Zifukwa zimene anthu ambiri sanalandirire choonadi n’zosiyanasiyana. Pochititsa phunziro la Baibulo la panyumba, mufunikira kuchotsa maganizo olakwika amene munthuyo angakhale nawo mwa kufotokoza zenizeni. Dzifunseni kuti: ‘Kodi ameneyu akudziŵa kuti monga munthu ali ndi zosoŵa zauzimu? Kodi amakhulupirira zotani? Nanga ndi ziti zimene sakhulupirira? N’chifukwa chiyani ali ndi maganizo amenewo? Kodi afunikira kum’thandiza kuti agonjetse zilakolako zimene zingam’letse kulandira udindo umene umabwera ndi kudziŵa choonadi?’
Nthaŵi zina kumakhala kovuta kudziŵa chifukwa chimene anthu amakhulupirira zinthu zina. Lemba la Miyambo 20:5 limati: “Uphungu wa m’mtima mwa munthu ndiwo madzi akuya; koma munthu wozindikira adzatungapo.” Kuzindikira ndi luso la kumvetsa zinthu zobisika. Zimenezi zimafuna kuonetsetsa ndi kukhala wosamala.
Sikuti kulankhulana konse kumachitika mwa mawu. Kungomva nkhani kokha kungasinthe maonekedwe a nkhope kapena mawu a wophunzira wanu. Ngati ndinu kholo, mumadziŵa ndithu kuti mwana wanu akamaonetsa mkhalidwe wina wachilendo, ndiye kuti wayamba kutengera makhalidwe osayenera. Musanyalanyaze zizindikiro zimenezo. Zimaonetsa munthu wam’kati.
Mafunso osankhidwa bwino angachititse munthu winayo kulankhula zakukhosi kwake. Mungafunse kuti: “Kodi inuyo mukuganiza bwanji za . . . ?” “N’chiyani chinakupangitsani kukhala wotsimikiza za . . . ?” “Kodi mungachite chiyani ngati . . . ?” Komabe, samalani kuti musachite kuwapanikiza anthu ndi mafunso ngati kuti ndi mlandu. Pochita mwanzeru, mungayambe funso ndi mawu akuti, “Mwina ndifunseko kuti . . . ?” Kudziŵa zimene zili m’mtima wa munthu ndi ntchito yofuna kufatsa. Nthaŵi zambiri, pamafunika kuyamba mwakhulupirirana kwa kanthaŵi ndithu kuti munthu ayambe kuulula zakukhosi kwake. Ngakhale zitafika pamenepo, m’pofunika kusamalabe kuti munthuyo asaone ngati mukuloŵerera nkhani zake zosakukhudzani.—1 Pet. 4:15.
Mmene mungayankhire zimene mwamva m’pofunikiranso kuzindikira. Kumbukirani kuti cholinga chanu ndi kuwamvetsa anthu kuti mudziŵe mfundo za m’Baibulo zimene zingakhudze mitima yawo. Fulumirani kupondereza mtima wofuna kusonyeza kuti malingaliro awo n’ngolakwa. M’malo mwake, zindikirani msanga chimene chikuwanenetsa zimene akunenazo. Mukatero, mudzadziŵa mmene mungayankhire; ndipo wophunzira wanuyo, poona kuti mukumumvetsa, adzalingalira mozama zimene mukunena.—Miy. 16:23.
Mukhozanso kuwafika pamtima anthu ena ngakhale pamene mukulankhula pa gulu. Ngati mukuyesa kuyendera limodzi ndi omvera anu, mwa kuyang’ana maonekedwe a nkhope zawo, ndi kupereka mafunso opangitsa anthu kulingalira, mungazindikire mmene anthu akuonera zimene mukunena. Ngati omvera anu mukuwadziŵa bwino, sonyezani kuti mumaganizira miyoyo yawo. Lingaliraninso maganizo a mpingowo pamene mukukambirana nawo Mawu a Mulungu.—Agal. 6:18.
Limbikitsani Maganizo Opindulitsa. Mutamvetsa zimene munthu amakhulupirira, komanso zimene sakhulupirira, ndi zifukwa zake, mudzakhoza kupitiriza kuchokera pamenepo. Yesu ataukitsidwa, anawafika pamtima ophunzira ake mwa ‘kuwatsegulira malembo’ okhudza zinthu zimene zinangochitika kumene. (Luka 24:32) Inunso yesetsani kugwirizanitsa zimene munthuyo waona pamoyo wake, zimene akulakalaka, ndi zimene waona m’Mawu a Mulungu. Zimene munena zikhoza kugwira mtima wophunzirayo m’njira yopindulitsa pamene azindikira bwino lomwe kuti: “Ichi ndicho CHOONADI!”
Pamene mugogomeza ubwino wa Yehova, chikondi chake, kukoma mtima kwake kopambana, ndi kulungama kwa njira zake, mumathandiza anthu amene mumawaphunzitsa kukulitsa chikondi chawo pa Mulungu. Pamene muyesetsa kusonyeza omvera anu makhalidwe abwino amene Mulungu amaona mwa aliyense wa iwo payekha, amatha kuona kuti n’zotheka munthu kupalana ubwenzi ndi Mulungu. Mukhoza kuchita zimenezo mwa kukambirana malemba ngati Salmo 139:1-3, Luka 21:1-4, ndi Yohane 6:44, komanso mwa kuthandiza omvera anu kuzindikira mmene Yehova amawakondera atumiki ake okhulupirika. (Aroma 8:38, 39) Fotokozani kuti Yehova saona zolakwa zathu zokha. Amaona moyo wathu wonse; kukangalika kwathu pa kulambira koyera, ndi chikondi chathu pa dzina lake. (2 Mbiri 19:2, 3; Aheb. 6:10) Iye amakumbukira ngakhale mbali zochepetsetsa za umunthu wathu, ndipo m’njira yodabwitsa kwambiri, adzaukitsa “onse ali m’manda” okumbukika. (Yoh. 5:28, 29; Luka 12:6, 7) Pakuti anthu anapangidwa m’chifaniziro cha Mulungu, kukambirana makhalidwe ake kaŵirikaŵiri kumakhudza mtima wa munthu.—Gen. 1:27.
Munthu amakhudzidwanso mtima pamene aphunzira kuona anthu mmene Yehova amawaonera. N’zachidziŵikire kuti ngati Mulungu wathu amatisamala payekhapayekha, ndiye kuti amasamalanso anthu ena mofananamo; popanda kuyang’ana makulidwe awo, dziko lawo, kapena mtundu wawo. (Mac. 10:34, 35) Munthu akafika pa kuzindikira zimenezo, amakhala ndi maziko olimba a m’Malemba akuti achotse chidani ndi tsankhu m’mtima mwake. Akafika pamenepo amatha kuyanjana ndi ena pamene akuphunzira kuchita chifuniro cha Mulungu.
Mkhalidwe wina umene muyenera kuulimbikitsa mwa ena ndiwo kuopa Mulungu. (Sal. 111:10; Chiv. 14:6, 7) Mantha aulemu amenewo, kapena kuti kuopa Mulungu, amathandiza munthu kupeza zimene sangathe kuzipeza mwa nyonga yake. Mwa kukambirana zochita za Yehova zochititsa mantha ndi kukoma mtima kwake kopambana, mungathandize ena kukhala ndi mantha oyenera oopa kukwiyitsa Mulungu.—Sal. 66:5; Yer. 32:40.
Tsimikizani kuti omvera anu akuzindikira kuti khalidwe lawo n’lofunika kwambiri kwa Yehova. Iyenso amakhudzidwa mtima, ndipo mmene timalabadira malangizo ake, tikhoza kum’mvetsa chisoni kapena kum’kondweretsa. (Sal. 78:40-42) Asonyezeni anthu mmene khalidwe lawo lingamuyankhire Satana pa chitonzo chake kwa Mulungu.—Miy. 27:11.
Thandizani omvera anu kuona kuti kukwaniritsa zofuna za Mulungu ndi chinthu chowapindulitsa kwambiri. (Yes. 48:17) Njira imodzi yochitira zimenezo ndi kuwasonyeza zotsatira zosiyanasiyana za kukana nzeru ya Mulungu, ngakhale kwa kanthaŵi chabe. Fotokozani mmene uchimo umatitalikitsira ndi Mulungu, mmene umatsekera mwayi ena kuti asaphunzire choonadi kwa ife, ndi mmenenso umawalandira ufulu wawo. (1 Ates. 4:6) Thandizani omvera anu kuyamikira madalitso omwe akusangalala nawo kale chifukwa chosunga malamulo a Mulungu. Athandizeni kuzindikira kuti kuyenda m’njira zolungama za Yehova kwatipulumutsa ku masoka ambiri. Munthu akakhulupirira nzeru ya kuyenda m’njira za Mulungu, amanyansidwa ndi chilichonse chotsutsana ndi njirazo. (Sal. 119:104) Kwa iye, kumvera sikukhalanso mtolo wolemetsa, koma njira yosonyezera kudzipereka kwake kwa Yehova.
Thandizani Ena Kudzifufuza. Kuti anthu apitirize kukula mwauzimu, ayenera kuzindikira zimene zili m’mitima yawo. Fotokozani mmene Baibulo lingawathandizire kuchita zimenezo.
Thandizani omvera anu kuzindikira kuti Baibulo silili chabe ndi malamulo, uphungu, zochitika zakale, ndi maulosi. Limasonyezanso maganizo a Mulungu. Pa Yakobo 1:22-25, Mawu a Mulungu amawayerekeza ndi galasi lodziyang’anira. Malinga ndi mmene timalabadirira zimene limanena ndi njira imene Yehova amachitira chifuniro chake, uthenga wa Baibulo umavumbula zimene zili m’mtima mwathu. Inde, limavumbula mmene Mulungu, amene “ayesa mitima,” amationera. (Miy. 17:3) Limbikitsani omvera anu kumakumbukira zimenezi. Alimbikitseni kusinkhasinkha zimene Mulungu watiikira m’Baibulo komanso kusintha kumene ayenera kuchita pa moyo wawo kuti Mulungu akondwere nawo kwambiri. Athandizeni kuzindikira kuti kuŵerenga Baibulo ndiyo njira yodziŵira “zolingirira ndi zitsimikizo za mtima” zimene Yehova amafuna. Akatero adzasintha mbali zofunikira pa moyo wawo mogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu.—Aheb. 4:12; Aroma 15:4.
Ophunzira Baibulo ena angakhale ofunitsitsa kuchita zimene amaphunzira; koma amaopa zimene anthu ena angaganize. Mwina akulimbana ndi zilakolako zina za thupi. Kapena akudzikhululukira pambali zina kuti pamene akutumikira Mulungu azichitabe zinthu zina za dzikoli. Atchulireni kuopsa kwake kwa maganizo amenewo. (1 Maf. 18:21) Alimbikitseni kuti azipemphera kwa Mulungu kuti awathandize kufufuza ndi kuyeretsa mitima yawo.—Sal. 26:2; 139:23, 24.
Athandizeni kuona kuti Yehova amamvetsa nkhondo imene alipo ndi kuti Baibulo limalongosola zimene zikuchitikazo. (Aroma 7:22, 23) Athandizeni kukhala osamala kotero kuti zokhumba za mtima wopanda ungwiro zisakule mphamvu mwa iwo.—Miy. 3:5, 6; 28:26; Yer. 17:9, 10.
Limbikitsani aliyense kuti aziyang’anitsitsa zolinga zake pochita zinthu. Aphunzitseni kumadzifunsa kuti: ‘Ndikufuna kuchita zimenezi chifukwa chiyani? Kodi zidzasonyeza Yehova kuti ndimayamikira zonse zimene wandichitira?’ Yesetsani kulimbikitsa maganizo akuti kukhala paubwenzi ndi Yehova ndiko chuma chopambana chimene munthu angakhale nacho.
Thandizani omvera anu kuzindikira kufunika kotumikira Yehova ndi ‘mtima wawo wonse.’ (Luka 10:27) Zimenezi zikutanthauza kuti malingaliro awo onse, zokhumba zawo, ndi zolinga zawo ziyenera kugwirizana ndi njira za Yehova. Choncho, phunzitsani omvera anu kuonetsetsa bwino zimene amachita, mmene amaonera zimene Mulungu amafuna ndi zolinga zawo pomutumikira. (Sal. 37:4) Pamene ophunzira anu azindikira mbali zimene ayenera kusintha, alimbikitseni kupemphera kwa Yehova motere: “Muumbe mtima wanga ukhale umodzi kuti uliope dzina lanu.”—Sal. 86:11.
Pamene wophunzira apalana ubwenzi ndi Yehova, amamvera Mulungu chifukwa cha chikhulupiriro chake, osati chabe chifukwa chakuti inu mumamulimbikitsa. Akatero, aziyesetsa payekha kutsimikiza “chokondweretsa Ambuye n’chiyani.” (Aef. 5:10; Afil. 2:12) Kumvera kochokera pansi pa mtima ngati kumeneko n’kumene kumakondweretsa Yehova.—Miy. 23:15.
Kumbukirani kuti Yehova ndiye amayesa mitima ndi kukopa anthu kuti akhale mabwenzi ake. (Miy. 21:2; Yoh. 6:44) Ife timagwira ntchito ngati otumidwa. (1 Akor. 3:9) Zili ngati kuti ‘Mulungu alikudandaulira mwa ife.’ (2 Akor. 5:20; Mac. 16:14) Yehova saumiriza aliyense kuti alandire choonadi, koma pamene tikugwiritsa ntchito Malemba, amatha kuchititsa omverawo kuzindikira kuti zimene akumvazo ndiwo mayankho a mafunso awo—kapena a mapemphero awo. Mukapeza mpata wophunzitsa uliwonse, kumbukirani mfundo imeneyi, ndipo pemphani Yehova ndi mtima wonse kuti akutsogolereni ndi kukuthandizani.—1 Mbiri 29:18, 19; Aef. 1:16-18.