Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • mwb20 February tsamba 5
  • Zimene Mwamuna ndi Mkazi Wake Angachite Kuti Alimbitse Chikondi M’banja Lawo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zimene Mwamuna ndi Mkazi Wake Angachite Kuti Alimbitse Chikondi M’banja Lawo
  • Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2020
  • Nkhani Yofanana
  • Tetezani Banja Lanu
    Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2021
  • Pambuyo pa Tsiku la Ukwati
    Kodi Mungatani Kuti Mulungu Azikukondani?
  • Ukwati Ndi Mphatso Yochokera kwa Mulungu
    Kodi Mungatani Kuti Mulungu Azikukondani?
  • Ukwati Ndi Mphatso Yochokera Kwa Mulungu Wachikondi
    Kodi Mungatani Kuti ‘Mulungu Apitirize Kukukondani’?
Onani Zambiri
Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2020
mwb20 February tsamba 5
Abulahamu ndi Sara akukonzekera kuchoka ku Uri. Abulahamu wanyamula thumba lalikulu ndipo akulimbikitsa Sara amene nayenso akuika zinthu mu basiketi.

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Kodi Mungatani Kuti Banja Lanu Liziyenda Bwino?

Abulahamu ndi Sara ndi chitsanzo chabwino kwa anthu okwatirana pa nkhani yokondana komanso kulemekezana. (Gen. 12:11-13; 1 Pet. 3:6) Komabe iwo sanali angwiro choncho ankafunika kupirira mayesero osiyanasiyana. Kodi anthu a pabanja angaphunzire chiyani pa chitsanzo cha Abulahamu ndi Sara?

Muzilankhulana bwino. Muziyankha modzichepetsa mwamuna kapena mkazi wanu akalankhula mawu enaake chifukwa chokhumudwa. (Gen. 16:5, 6) Muzipeza nthawi yochitira zinthu limodzi. Mawu komanso zochita zanu zizisonyeza kuti mumamukonda mnzanuyo. Koposa zonse, muzilola kuti Yehova azitsogolera banja lanu pophunzira mawu ake, kupemphera komanso kuchitira limodzi zinthu zokhudza kulambira. (Mlal. 4:12) Mabanja olimba amalemekezetsa Yehova, yemwe anayambitsa banja.

ONERANI VIDIYO YAKUTI ZIMENE MUNGACHITE KUTI MULIMBITSE CHIKONDI M’BANJA LANU, KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:

  • N’chiyani chikusonyeza kuti Shaan ndi Kiara sakukondananso ngati kale?

  • N’chifukwa chiyani kulankhulana momasuka kuli kofunika m’banja?

  • Kodi chitsanzo cha Abulahamu ndi Sara chinathandiza bwanji Shaan ndi Kiara?

  • Kodi Shaan ndi Kiara anachita chiyani kuti banja lawo liyambenso kuyenda bwino?

  • N’chifukwa chiyani anthu okwatirana sayenera kuyembekezera kuti azichita zinthu mosalakwitsa chilichonse?

Zithunzi: Mbali za muvidiyo yakuti ‘Zimene Mungachite Kuti Mulimbitse Chikondi M’banja Lanu.’ Zomwe Shaan ndi Kiara anachita kuti alimbitse banja lawo. 1. Akhala pampando ndipo aliyense wayang’ana kwina. 2. Agwirana manja. 3. Akusangalala kulalikira limodzi.

Banja lanu likhoza kumayenda bwino

Mfundo zina zothandiza kuti banja lanu liziyenda bwino, mungazipeze munkhani zomwe zimapezeka mu Galamukani! komanso pawebusaiti yathu ya jw.org®:

  • “Ana Akakula N’kuchoka Pakhomo”​—g17.4 10-11

  • “Mungatani Kuti Musamakangane Pokambirana Mavuto Anu?”​—g16.3 10-11

  • “Ngati Banja Lanu Silikuyenda Bwino”—g 3/14 14-15

  • “Kodi Mungatani Kuti Muzimvetsera Mwamuna Kapena Mkazi Wanu Akamalankhula?”—g 12/13 12-13

  • “Zimene Mungachite Kuti Musamakangane”—g 2/13 4-5

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena