NYIMBO 31
Muziyenda Ndi Mulungu
Losindikizidwa
(Mika 6:8)
1. Muziyenda ndi Mulungu.
Musonyeze chikondi
Ndipo musachoke kwa Yehova,
Azikulimbitsani.
Muzimvera mawu akewo
Simudzasochera
Ndipo mukamamumvera
Akutsogolerani.
2. Muziyenda ndi Mulungu.
Muzipewa zoipa.
Mayesero angakule bwanji
Adzakuthandizani.
Zinthu zonse zotamandika
Ndiponso zoona
Muziziganizirabe.
M’lungu sakusiyani.
3. Muziyenda ndi Mulungu.
Mudzasangalaladi.
Muzimuthokoza pa zabwino
Zomwe amapereka.
Muimbireni M’lungu wathu,
Inde, mwachimwemwe.
Chimwemwecho ndi umboni
Woti ndinu a M’lungu.
(Onaninso Gen. 5:24; 6:9; Afil. 4:8; 1 Tim. 6:6-8.)