Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • mwbr22 March tsamba 1-11
  • Malifalensi a Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Malifalensi a Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu
  • Malifalensi a Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2022
  • Timitu
  • MARCH 7-13
  • MARCH 14-20
  • MARCH 21-27
  • MARCH 28–APRIL 3
  • APRIL 4-10
  • APRIL 18-24
  • APRIL 25–MAY 1
Malifalensi a Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2022
mwbr22 March tsamba 1-11

Malifalensi a Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu

MARCH 7-13

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 1 SAMUELI 12-13

“Kudzikuza Kumabweretsa Manyazi”

w00 8/1 13 ¶17

Kudzikuza Kumabweretsa Manyazi

17 Poyamba, zomwe Sauli anachitazo zingaoneke ngati zolondola. Ndipotu, anthu a Mulungu ‘zinawathina,’ “anali atapanikizika,” ndipo anali kunjenjemera chifukwa chakuti zinthu sizinali bwino. (1 Samueli 13:6, 7) Kunena zoona, si kulakwa kuchita zinthu mofulumira ngati tikufunika kutero. Koma kumbukirani kuti Yehova amaona zimene zili mumtima mwathu ndipo amadziwa zimene tikuganiza. (1 Samueli 16:7) Choncho, n’kutheka kuti iye anaona zinthu zina mwa Sauli zomwe sanazitchule mwachindunji mu nkhani ya m’Baibuloyi. Mwachitsanzo, n’kutheka kuti Yehova anaona kuti kudzikuza n’komwe kunachititsa kuti Sauli achite zinthu mopupuluma. Mwinamwake Sauli sanamve bwino mumtima kuti iye, wokhala mfumu ya Isiraeli yense, anafunikira kudikira winawake amene ankamuona ngati mneneri wokalamba ndi wozengereza. Mulimonse mmene zinalili, Sauli anaganiza kuti kuchedwa kwa Samueli kunam’patsa ufulu wochita zonse yekha komanso kusatsatira malangizo omveka bwino omwe anali atapatsidwa. Zotsatira zake? Samueli sanavomereze zimene Sauli anachitazi. M’malomwake, iye anamudzudzula Sauli kuti: “Ufumu wako sukhalitsa. . . . Chifukwa iwe sunasunge zimene Yehova anakulamula.” (1 Samueli 13:13, 14) Apanso, kudzikuza kunabweretsa manyazi.

w07 6/15 27 ¶8

Yehova Amakondwera Mukamamumvera

8 Nkhani ya m’Baibulo yonena za Mfumu Sauli imasonyeza kuti kumvera ndi kofunika kwambiri. Poyamba, Sauli anali mfumu yodzichepetsa ndipo anadziyesa ‘wamng’ono m’maso mwake.’ Koma patapita nthawi, anayamba kunyada ndi kukhala ndi maganizo olakwika pazochita zake. (1 Samueli 10:21, 22; 15:17) Nthawi ina, Sauli akukamenyana ndi Afilisti, Samueli anamuuza kuti amudikire kuti iye adzapereke nsembe kwa Yehova ndiponso kuti adzapatse mfumuyo malangizo ena. Koma Samueli anachedwa kubwera ndipo anthu anayamba kubalalika. Ataona zimenezo, Sauli “anapereka nsembe yopserezayo.” Zimenezi Yehova sanakondwere nazo. Samueli atabwera, mfumu inapereka zifukwa pofuna kulungamitsa kusamvera kwake. Inafotokoza kuti ‘inadzifulumiza’ ndi kupereka nsembe yopsereza kupembedzera Yehova chifukwa chakuti Samueli anachedwa. Mfumu Sauli anaona kuti kupereka nsembeyo kunali kofunika kwambiri kuposa kumvera malangizo oti adikire Samueli kudzapereka nsembe. Samueli anamuuza kuti: “Munachita kopusa; simunasunga lamulo la Yehova Mulungu wanu, limene iye anakulamulirani.” Mapeto ake, Sauli anataya ufumu wake chifukwa chosamvera Yehova.​—1 Samueli 10:8; 13:5-13.

Mfundo Zothandiza

w11 7/15 13 ¶15

Kodi Mukutsatira Malangizo Achikondi a Yehova?

15 Kodi Aisiraeli ankaganiza kuti munthu akhoza kukhala mfumu yeniyeni ndiponso yodalirika kuposa Yehova? Ngati ndi choncho, ndiye kuti anali kutsatira zinthu zopanda pake. Iwo anali pa ngozi yotsatira zinthu zinanso zopanda pake zochokera kwa Satana. Zikanakhala zosavuta kuti mafumu otere awachititse kulambira mafano. Anthu olambira mafano amaganiza kuti milungu yopangidwa kuchokera ku mitengo kapena miyala imakhala yeniyeni ndiponso yodalirika kuposa Yehova Mulungu wosaoneka amene analenga zinthu zonse. Koma malinga ndi zimene mtumwi Paulo ananena, mafano ndi ‘opanda pake.’ (1 Akor. 8:4) Sangaone, kumva, kulankhula kapena kuchita chilichonse. N’zotheka kuti muone ndiponso kukhudza mafanowo koma mukawalambira ndiye kuti mukutsatira chinthu chopanda pake, kapena kuti chinthu chimene si chenicheni, chomwe chingakuchititseni kukumana ndi zoopsa zokhazokha.​—Sal. 115:4-8.

MARCH 14-20

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 1 SAMUELI 14-15

“Kumvera Kumaposa Nsembe”

w07 6/15 26 ¶4

Yehova Amakondwera Mukamamumvera

Popeza kuti Yehova ndiye Mlengi, zinthu zonse zimene tili nazo ndi zake. Ndiyeno, kodi pali chilichonse chimene tingamuchitire? Inde, chilipo ndipo ndi chamtengo wapatali. Tingamuchitire chiyani? Tikupeza yankho pamalangizo otsatirawa akuti: “Mwananga, khala wanzeru, nukondweretse mtima wanga; kuti ndimuyankhe yemwe anditonza.” (Miyambo 27:11) Zimene tingamuchitire Mulungu ndi kumumvera basi. Ngakhale kuti tinabadwira kosiyanasiyana ndipo tili ndi moyo wosiyanasiyana, ifeyo mwa kumvera, tingatsutse bodza lamkunkhuniza la Satana Mdyerekezi lakuti anthufe sitingakhale okhulupirika kwa Mulungu poyesedwa. Ndithudi, Mulungu watilemekeza zedi potipatsa mwayi wotsutsa zimenezi!

it-2 521 ¶2

Kumvera

Palibe chilichonse chimene chingalowe m’malo mwa kumvera, ndipo munthu sangakondedwe ndi Mulungu ngati samvera. Samueli anauza Mfumu Sauli kuti: “Kodi Yehova amakondwera ndi nsembe zopsereza ndi nsembe zina kuposa kumvera mawu a Yehova? Taona! Kumvera kuposa nsembe, ndipo kumvetsera mosamala kuposa mafuta a nkhosa zamphongo.” (1Sa 15:22) Munthu wosamvera amakhala kuti akukana mawu a Yehova. Amasonyeza kuti sakudalira kapena kukhulupirira mawuwo komanso amene anawalankhula. Choncho munthu amene samvera amafanana ndi munthu amene amawombeza kapena kulambira mafano. (1Sa 15:23; yerekezerani ndi Aro 6:16) Kungonena ndi mawu okha kuti wamvera zinazake n’kopanda phindu ngati sukuchita zimene zikufunikazo. Kulephera kuchitapo kanthu kumasonyeza kuti sukhulupirira kapena kulemekeza amene akupereka malangizo. (Mt 21:28-32) Anthu amene amangokhutira ndi zimene amva komanso kungovomereza m’maganizo mokha, koma osachita zimene zikufunikira, amadzinyenga ndi maganizo onama ndipo salandira madalitso. (Yak 1:22-25) Mwana wa Mulungu ananena kuti anthu amene amachita zinthu zofanana ndi zimene analamula, koma amazichita moonekeratu kuti ndi m’njira yolakwika kapena kuti ali ndi zolinga zoipa, sadzalowa mu Ufumu ndiponso adzakanidwa kotheratu.​—Mt 7:15-23.

Mfundo Zothandiza

it-1 493

Chifundo

Kuyesetsa kuchitira ena chifundo koma mosemphana ndi zimene Mulungu amafuna, kukhoza kubweretsa mavuto aakulu. Izi zinaonekera pa zimene zinachitikira Mfumu Sauli. Nthawi inafika yoti Mulungu apereke chiweruzo kwa Aamaleki, mtundu womwe unali woyamba kuukira Aisiraeli atangochoka kumene ku Iguputo. Sauli analamulidwa kuti asakawachitire chifundo. Koma chifukwa choopa anthu, iye sanamvere zonse zimene Yehova anamulamula. Zimenezi zinachititsa kuti Yehova amukane kuti asakhalenso mfumu. (1Sa 15:2-24) Munthu akamayesetsa kutsatira njira zolungama za Yehova komanso kuona kuti kukhalabe wokhulupirika kwa iye n’kofunika kwambiri pa moyo wake, salakwitsa zinthu n’kukanidwa ndi Mulungu, ngati mmene Sauli anachitira.

MARCH 21-27

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 1 SAMUELI 16-17

“Yehova Ndiye Mwini Nkhondo”

wp16.5 11 ¶2-3

“Yehova Ndiye Mwini Nkhondo”

Davide anauza Sauli mmene anaphera mkango ndiponso chimbalangondo chija pofuna kusonyeza kuti akhoza kukamenyananso ndi Goliyati. Kodi Davide anauza Sauli zimenezi pongofuna kudzitama? Ayi. Tikutero chifukwa chakuti Davide ankadziwa chimene chinamuthandiza kupha zilombozo. Iye anati: “Yehova amene anandilanditsa m’kamwa mwa mkango ndi m’kamwa mwa chimbalangondo andilanditsanso m’manja mwa Mfilisiti ameneyu.” Sauli atamva zimenezi, anauza Davide kuti: “Pita, ndipo Yehova akhale nawe.”​—1 Samueli 17:37.

Kodi inunso mungakonde kukhala ndi chikhulupiriro ngati cha Davide? Sikuti iye ankangoganiza chabe kuti Mulungu akhoza kumuthandiza. Koma ankamukhulupirira ndi mtima wonse chifukwa chomudziwa bwino komanso chifukwa choti anali ataona kale Mulungu akumuthandiza. Ankadziwa kuti Yehova amateteza anthu ake mwachikondi komanso amakwaniritsa malonjezo ake. Kuti ifenso tikhale ndi chikhulupiriro cholimba, tiyenera kupitiriza kuphunzira za Mulungu. Tikamatsatira zimene timaphunzira, zinthu zidzatiyendera bwino ndipo zimenezi zidzalimbitsa chikhulupirira chathu.​—Aheberi 11:1.

wp16.5 11-12

“Yehova Ndiye Mwini Nkhondo”

Zimene Davide anayankha zimasonyeza kuti anali ndi chikhulupiriro cholimba. Taganizirani kuti mnyamata ngati ameneyu anauza Goliyati kuti: “Iwe ukubwera kwa ine ndi lupanga, mkondo ndi nthungo, koma ine ndikubwera kwa iwe m’dzina la Yehova wa makamu, Mulungu wa asilikali a Isiraeli, amene iweyo wam’tonza.” Davide ankadziwa kuti zilibe kanthu kuti Goliyati anali ndi mphamvu komanso zida zoopsa. Goliyati anali atanyoza Yehova Mulungu, ndipo Davide ankadziwa kuti Yehovayo achitapo kanthu. Iye ankadziwa kuti: “Yehova ndiye mwini nkhondo.”​—1 Samueli 17:45-47.

Sikuti Davide sankaona msinkhu wa Goliyati ndiponso zida zimene anali nazo. Kungoti sanalole kuti zinthu zimenezi zimuchititse mantha. Iye sanatengere chitsanzo choipa cha Sauli ndi asilikali ake omwe ankadziyerekezera ndi Goliyati. M’malomwake, Davide ankayerekezera Goliyati ndi Yehova. Goliyati anali wamtali pafupifupi mamita atatu ndipo ankapitirira anthu ena onse, koma msinkhu umenewu sunali kanthu pouyerekezera ndi Wolamulira Wamkulu wa chilengedwe chonse. Mofanana ndi anthu ena onse, tingati Goliyati anali ngati nyerere, yomwe singavute kuipha.

wp16.5 12 ¶4

“Yehova Ndiye Mwini Nkhondo”

Masiku ano, atumiki a Mulungu samenya nawo nkhondo. (Mateyu 26:52) Komabe tiyenera kutsanzira chikhulupiriro cha Davide. Nafenso tiyenera kumaona kuti Yehova yekha ndi amene tiyenera kumutumikira ndiponso kumuopa. Nthawi zina tikhoza kumaona kuti mavuto athu akutikulira, komabe tiyenera kukumbukira kuti mavutowo ndi aang’ono kwambiri tikawayerekezera ndi mphamvu zopanda malire za Yehova. Tikasankha kuti Yehova akhale Mulungu wathu ndiponso kumukhulupirira ngati mmene Davide anachitira, palibe vuto lililonse limene lingatichititse mantha. Zili choncho chifukwa palibe vuto limene Yehova angalephere kuligonjetsa.

Mfundo Zothandiza

it-2 871-872

Sauli

Panali pambuyo pa zimenezi komanso pambuyo poti Davide wadzozedwa monga mfumu yam’tsogolo ya Isiraeli, pamene mzimu wa Yehova unamuchokera Sauli. Kungoyambira pamenepo “mzimu woipa wochokera kwa Yehova unam’vutitsa.” Chifukwa chakuti Yehova anamuchotsera mzimu wake, anachititsa kuti mzimu woipa ukhale pa Sauli. Mzimu woipawo unachititsa kuti Sauli asakhale ndi mtendere wa m’maganizo komanso kuti mmene ankamvera mumtima mwake ndiponso maganizo ake, zizikhala zolakwika. Sauli atalephera kumvera Yehova, anasonyeza kuti maganizo komanso mtima wake zinali zoipa ndipo mzimu wa Mulungu sukanamuteteza kapena kumuthandiza kuti asachite zinthu zoipa. Ndiye popeza kuti Yehova analola kuti m’malo mwa mzimu wake, “mzimu woipa” ulowe mwa Sauli n’kumamuvutitsa, mzimu woipawu ukhoza kutchulidwa kuti “mzimu woipa wochokera kwa Yehova,” moti n’chifukwa chake atumiki a Sauli ankautchula kuti “mzimu woipa wa Mulungu.” Atalangizidwa ndi mtumiki wake, Sauli anapempha Davide kuti azimuimbira nyimbo kunyumba kwake n’cholinga choti azipeza bwino “mzimu woipa” ukayamba kumuvutitsa.​—1Sa 16:14-23; 17:15.

MARCH 28–APRIL 3

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 1 SAMUELI 18-19

“Tizidzichepetsa Zinthu Zikatiyendera”

w04 4/1 15 ¶4

Dalirani Mzimu wa Mulungu Zinthu Zikasintha pa Moyo Wanu

Posakhalitsa mbusa wachinyamata ameneyu anatchuka m’dziko lonselo. Anamuitana kuti azikatumikira mfumu ndi kumaiimbira nyimbo. Anapha Goliati yemwe anali katswiri wa nkhondo, chimphona, komanso woopsa moti ngakhale asilikali odziwa bwino nkhondo a Israyeli anaopa kulimbana naye. Atamusankha kuti atsogolere asilikaliwo, Davide anagonjetsa Afilisti. Anthu anamukonda kwambiri ndipo anapeka nyimbo zomutamanda. Izi zisanachitike, mlangizi wina wa Mfumu Sauli anafotokoza za Davide kuti anali ‘wanthetemya wodziwa kuimba’ zeze komanso kuti “wa mtima wolimba ndi woyenera nkhondo, ndiponso ali wochenjera manenedwe ake; ndiye munthu wokongola.”​—1 Samueli 16:18; 17:23, 24, 45-51; 18:5-7.

w18.01 28 ¶6-7

Tizikhala Osiyana ndi Anthu a M’dzikoli

6 Anthu ena amayamba kunyada chifukwa cha zinthu monga kuoneka bwino, kutchuka, luso loimba kapena udindo wapamwamba. Davide anali ndi zinthu zonsezi koma anakhala wodzichepetsa kwa moyo wake wonse. Iye atapha Goliyati, Mfumu Sauli anamupatsa mwana wake wamkazi kuti amukwatire. Koma Davide ananena kuti: “Ndine yani ine, ndipo abale anga, anthu a m’banja la bambo anga ndani mu Isiraeli monse muno kuti ndikhale mkamwini wa mfumu?” (1 Sam. 18:18) N’chiyani chinathandiza Davide kuti akhalebe wodzichepetsa? Iye ankadziwa kuti anali ndi makhalidwe abwino, maluso komanso udindo chifukwa choti Mulungu ‘anatsika m’munsi,’ kapena kuti anadzichepetsa, kuti amuthandize. (Sal. 113:5-8) Davide ankadziwanso kuti zinthu zonse zabwino zimene anali nazo anachita kuzilandira kuchokera kwa Yehova.​—Yerekezerani ndi 1 Akorinto 4:7.

7 Masiku ano, anthu a Yehova amayesetsa kukhala odzichepetsa ngati mmene ankachitira Davide. Timatsanzira Yehova, yemwe ndi Munthu wamkulu m’chilengedwe chonse, koma amadzichepetsa. (Sal. 18:35) Timatsatira malangizo a m’Baibulo akuti: “Valani chifundo chachikulu, kukoma mtima, kudzichepetsa, kufatsa, ndi kuleza mtima.” (Akol. 3:12) Timadziwanso kuti chikondi ‘sichidzitama ndiponso sichidzikuza.’ (1 Akor. 13:4) Ndipo tikamayesetsa kukhala odzichepetsa, anthu ena angafune kuyamba kuphunzira za Yehova ngati mmene amuna angakopekere ndi khalidwe labwino la akazi awo.​—1 Pet. 3:1.

Mfundo Zothandiza

it-2 695-696

Mneneri

Ngakhale kuti ankaikidwa ndi mzimu wa Yehova, sikuti nthawi zonse aneneri ankangolankhula mawu ouziridwa okhaokha. M’malomwake, mzimu wa Mulungu ‘unkawafikira’ pa nthawi zina, n’kuwaululira uthenga umene unkafunika kulengezedwa. (Eze 11:4, 5; Mik 3:8) Zimenezi zinkawapatsa mphamvu kuti alankhule. (1Sa 10:10; Yer 20:9; Amo 3:8) Sikuti ankangochita zinthu zachilendo zokha, koma kaonekedwe kawo ndi mmene ankachitira zinthu, zinalinso zachilendo. Mwa zina, zimenezi ndi zimene amatanthauza akamati anali “kuchita zinthu ngati aneneri.” (1Sa 10:6-11; 19:20-24; Yer 29:24-32; yerekezerani ndi Mac 2:4, 12-17; 6:15; 7:55.) Iwo ankaika maganizo awo onse pa ntchito yawo ndipo ankaigwira mwakhama komanso molimba mtima kwambiri. Zimenezi zinkachititsa kuti anthu aziona kuti akuchita zinthu mwachilendo kwambiri. Chitsanzo ndi mneneri amene anaonekera kwa akuluakulu a asilikali pamene ankadzoza Yehu. Ndipotu akuluakulu a asilikaliwo atazindikira kuti munthuyo anali mneneri, analandira uthenga wake ndi mtima wonse. (2Mf 9:1-13; yerekezerani ndi Mac 26:24, 25.) Pamene Sauli ankathamangitsa Davide, mzimu wa Mulungu unamuchititsa kuti ‘achite zinthu ngati mneneri,’ ndipo anang’amba zovala zake ndi kukhala “wosavala usana wonse ndi usiku wonse,” ndipo n’kutheka kuti imeneyo inali nthawi imene Davide anathawa. (1Sa 19:18–20:1) Komatu zimenezi sizikutanthauza kuti nthawi zambiri aneneri ankakhala osavala chifukwa si zomwe Baibulo limanena. Munkhani zina ziwiri zimene zili m’Baibulo, aneneri anakhala osavala pofuna kusonyeza mbali ina ya ulosi wawo. (Yes 20:2-4; Mik 1:8-11) Chifukwa chimene Sauli anakhalira wosavala, sichinatchulidwe. Kaya kunali kufuna kusonyeza kuti anali munthu basi, kapena kuti anavulidwa zovala zachifumu, kapena kuti analibe mphamvu poyerekezera ndi mphamvu komanso udindo wa Yehova, kapenanso mwina panali chifukwa china, palibe chinatchulidwa.

KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI

Nkhani

km 1/03 1

Ntchito Imene Imafunika Kudzichepetsa

1 Mawu a Mulungu amatilangiza kuti tikhale “odzichepetsa; osabwezera choipa ndi choipa, . . . koma . . . [kupereka, NW] madalitso.” (1 Pet. 3:8, 9) Mosakayikira, uphungu umenewu umagwira ntchito polalikira. Inde, utumiki wachikristu ungatiyese pa kudzichepetsa kwathu.

2 Khalidwe la kudzichepetsa limatithandiza kupirira zovuta zimene tingakumane nazo. Tikamalalikira, timapita tokha asanatiitane ndi kukalankhula ndi anthu osawadziwa, ndipo timadziwa kuti ena satilandira bwino. Kuti tilalikirebe tikakumana ndi anthu osatilandira bwinowa, m’pofunika kudzichepetsa. M’gawo lina louma kwambiri, alongo awiri omwe ndi apainiya anayenda khomo ndi khomo tsiku lililonse kwa zaka ziwiri popanda kulankhula ndi munthu wina aliyense! Koma analimbikira, ndipo lero kumeneko kuli mipingo iwiri.

3 Ngati Tichitiridwa Chipongwe: Ena akapanda kutikomera mtima kapena akatichitira chipongwe, kudzichepetsa kudzatithandiza kutsanzira Yesu. (1 Pet. 2:21-23) Panyumba ina, mlongo wina anatukwanidwa, koyamba ndi mkazi kenako ndi mwamuna wa mkaziyo amene anam’thamangitsa. Asanachoke, mlongoyo anangomwetulira ndipo anati adzalankhula nawo nthawi ina. Zimenezi zinadabwitsa kwambiri banjalo moti pamene wa Mboni wina anafika, iwo anamvetsera. Atawapempha kupita ku msonkhano ku Nyumba ya Ufumu, iwo anavomera. Mlongo anam’thamangitsa uja anali komweko ndipo anawapatsa moni ndi kuwalalikiranso. Ifenso tingafewetse mitima ya anthu osafuna kumva mwa kusonyeza “chifatso ndi mantha.”​—1 Pet. 3:15; Miy. 25:15.

4 Pewani Kudzitukumula: Kudziwa kwathu Baibulo sikutipatsa chifukwa choti tiziderera anthu ena kapena kuwanyoza. (Yoh. 7:49) M’malo mwake, Mawu a Mulungu amatilangiza ‘kusachitira mwano munthu aliyense.’ (Tito 3:2) Tikakhala a mtima wodzichepetsa ngati mmene Yesu analili, timapumulitsa ena. (Mat. 11:28, 29) Kukhala odzichepetsa kumathandiza kuti uthenga wathu ukhale wokopa anthu.

5 Inde, kudzichepetsa kumatithandiza kupirira m’gawo louma. Kungafewetse mitima ya anthu osafuna kumva, ndipo ena amakopeka nako n’kulandira uthenga wa Ufumu. Koposa zonse, kumasangalatsa Yehova, amene “apatsa chisomo kwa odzichepetsa.”​—1 Pet. 5:5.

APRIL 4-10

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU 1 SAMUELI 20-22

“Kodi Mungatani Kuti Mukhale Bwenzi Labwino?”

w19.11 7 ¶18

Pezani Anzanu Apamtima Mapeto Asanafike

18 Masiku ano, abale ndi alongo athu amakumana ndi mavuto osiyanasiyana. Mwachitsanzo, amakumana ndi ngozi zachilengedwe komanso zoyambitsidwa ndi anthu. Zimenezi zikachitika, mwina tingalolere kuti abale athuwo adzakhale kunyumba kwathu. Apo ayi, tingawathandize ndi ndalama. Koma aliyense angapemphe Yehova kuti azithandiza abale ndi alongowo. Tikamva kuti m’bale kapena mlongo wina akuvutika maganizo, tikhoza kusowa chonena kapena chochita. Koma mfundo ndi yakuti aliyense wa ife angathandize anzake m’njira inayake. Mwachitsanzo, tingapeze mpata wocheza nawo ndipo akamalankhula, tiziwamvetsera mwachifundo. Tingawauzenso malemba amene amatilimbikitsa kwambiri. (Yes. 50:4) Chofunika kwambiri ndi kukhala limodzi ndi anzathu pamene akukumana ndi mavuto.​—Werengani Miyambo 17:17.

w08 2/15 8 ¶7

Yendani M’njira za Yehova

7 Mulungu amafuna kuti tikhale mabwenzi odalirika. (Miy. 17:17) Jonatani mwana wa Mfumu Sauli anakhala bwenzi la Davide. Atamva kuti Davide anapha Goliati, “mtima wa Jonatani unalumikizika ndi mtima wa Davide, ndipo Jonatani anam’konda iye monga moyo wa iye yekha.” (1 Sam. 18:1, 3) Jonatani anachenjezanso Davide pamene Sauli anafuna kumupha. Davide atathawa, Jonatani anakakumana naye ndi kuchita pangano. Iye anatsala pang’ono kutaya moyo wake chifukwa cholankhula za Davide kwa Sauli. Ngakhale ndi choncho, anthu awiriwa anakumananso ndi kulimbitsa ubwenzi wawo. (1 Sam. 20:24-41) Ulendo womaliza umene anakumana, Jonatani analimbitsa dzanja la Davide “mwa Mulungu.”​—1 Sam. 23:16-18.

w09 10/15 19 ¶11

Mungathe Kukhalabe ndi Mabwenzi M’dziko Lopanda Chikondi Lino

11 Khalani okhulupirika. Solomo analemba kuti: “Bwenzi limakonda nthawi zonse; ndipo m’bale anabadwira kuti akuthandize pooneka tsoka.” (Miy. 17:17) Polemba mawu amenewo, mwina Solomo anali kuganiza za ubwenzi wa bambo ake Davide ndi Jonatani. (1 Sam. 18:1) Mfumu Sauli anali kufuna kuti mwana wake Jonatani adzakhale mfumu ya Isiraeli iye akadzamwalira. Koma Jonatani anazindikira kuti Yehova anasankha Davide kuti ndiye adzakhale ndi udindo umenewo. Mosiyana ndi Sauli, Jonatani sanachitire nsanje Davide. Iye sanaipidwe poona kuti anthu akutamanda Davide, ndiponso sanakhulupirire mabodza amene Sauli anali kufalitsa onena za Davide. (1 Sam. 20:24-34) Kodi ifeyo tili ngati Jonatani? Mabwenzi athu akapatsidwa maudindo, kodi timasangalala? Akakumana ndi mavuto, kodi timawatonthoza ndi kuwathandiza? Tikauzidwa miseche yonena za bwenzi lathu, kodi timafulumira kuikhulupirira? Kapena, mofanana ndi Jonatani, kodi timasonyeza kuti ndife okhulupirika kwa bwenzi lathulo poliikira kumbuyo?

Mfundo Zothandiza

w05 3/15 24 ¶4

Mfundo Zazikulu za M’buku la Samueli Woyamba

21:12, 13. Yehova amayembekezera kuti tizigwiritsa ntchito nzeru zathu ndi maluso athu pothana ndi mavuto m’moyo wathu. Watipatsa Mawu ake ouziridwa, omwe amatithandiza kukhala ochenjera, odziwa zinthu, ndiponso aluso la kulingalira. (Miyambo 1:4) Palinso akulu oikidwa achikristu omwe amatithandiza.

APRIL 18-24

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 1 SAMUELI 23–24

“Tiziyembekezera Yehova Moleza Mtima”

w04 4/1 16 ¶8

Dalirani Mzimu wa Mulungu Zinthu Zikasintha pa Moyo Wanu

8 Davide anakana kupha Sauli. Posonyeza chikhulupiriro ndi kuleza mtima, anaganiza zongosiya nkhaniyo m’manja mwa Yehova. Mfumuyo itachoka m’phangamo, Davide anaifuulira ndi kunena kuti: “Yehova aweruze pakati pa ine ndi inu; ndipo Yehova adzandibwezera chilango kwa inu; koma dzanja langa silidzakhala pa inu.” (1 Samueli 24:12) Ngakhale ankadziwa kuti Sauli anali kulakwitsa, Davide sanabwezere yekha, ndiponso sanalankhule kwa Sauli monyoza kapena kumunyoza pamaso pa anthu ena. Pa maulendo ena angapo, Davide anadziletsa kubwezera yekha choipa. M’malo mwake, anadalira Yehova kuti adzakonza zinthu.​—1 Samueli 25:32-34; 26:10, 11.

w04 6/1 22-23

Kodi Mavuto Amene Mumakumana Nawo Amalamulira Moyo Wanu?

Mfundo yachitatu imene tikuphunzirapo n’njakuti tiyenera kudikira Yehova m’malo mogwiritsa ntchito njira zosemphana ndi Malemba kuti tithetse mavuto athu. Wophunzira Yakobo analemba kuti: “Chipiriro chikhale nayo ntchito yake yangwiro, kuti mukakhale angwiro ndi opanda chilema, osasowa kanthu konse.” (Yakobo 1:4) Tiyenera kulola chipiriro ‘kukhala nayo ntchito yake yangwiro’ mwa kulola chiyeso kupitirira mpaka chonse chitatha popanda kutsatira njira zosemphana ndi Malemba kuti chiyesocho chithe msanga. Tikalola chiyesocho kupitirira, ndiye kuti chikhulupiriro chathu chidzayesedwa ndi kuyengedwa, ndipo mphamvu yake yolimbitsa munthu idzaonekera. Ndi mmene kupirira kwa Yosefe ndi Davide kunalili. Iwo sanayese kupeza njira zawozawo zothetsera mavuto awo zoti Yehova sakanakondwera nazo. Koma anayesetsa kuchita zimene akanatha ngakhale anali pamavuto. Iwo anadikira Yehova, ndipo analandira madalitso aakulu. Yehova anawagwiritsa ntchito onse awiri kulanditsa ndi kutsogolera anthu ake.​—Genesis 41:39-41; 45:5; 2 Samueli 5:4, 5.

Ifenso tingakumane ndi mavuto amene angatiyese kuchita zinthu zosemphana ndi Malemba pofuna kuwathetsa. Mwachitsanzo, kodi ndinu wokhumudwa chifukwa chakuti simunapezebe munthu woyenera kumanga naye banja? Ngati limeneli ndi vuto lanu, musayese ngakhale pang’ono kuswa lamulo la Yehova la kukwatira “mwa Ambuye.” (1 Akorinto 7:39) Kodi ukwati wanu uli pamavuto? M’malo motengera mzimu wa dziko umene umalimbikitsa anthu kupatukana ndi kusudzulana, yesetsani kuthandizana kuthetsa mavuto anuwo. (Malaki 2:16; Aefeso 5:21-33) Kodi zikukuvutani kusamalira banja lanu chifukwa cha vuto la zachuma? Kudikira Yehova kumatanthauzanso kuti mupewe kuchita ntchito zokayikitsa kapena zosaloleka pofuna kuti mupeze ndalama. (Salmo 37:25; Ahebri 13:18) Inde, tonsefe tiyenera kulimbikira kuchita zimene tingathe ngakhale tili pamavuto kuti Yehova apeze potidalitsira. Pamene tikutero, tisasiye kudikira Yehova kuti apereke njira yabwino yothetsera mavuto athuwo.​—Mika 7:7.

Mfundo Zothandiza

w17.11 27 ¶11

Musalole Kuti Chilichonse Chikulepheretseni Kulandira Mphoto

11 Tikamayesetsa kukhala achikondi ndiponso okoma mtima, sitidzachitira ena nsanje. Paja Baibulo limati: “Chikondi n’choleza mtima ndiponso n’chokoma mtima. Chikondi sichichita nsanje.” (1 Akor. 13:4) Kuti tisamachite nsanje tiyenera kuyesetsa kuona zinthu mmene Mulungu amazionera. Tiyenera kuona kuti ndife thupi limodzi ndi abale ndi alongo athu. Maganizo amenewa angatithandize kuti tizikondana mogwirizana ndi malangizo akuti: “Chiwalo chimodzi chikalemekezedwa, ziwalo zina zonse zimasangalalira nacho limodzi.” (1 Akor. 12:16-18, 26) Choncho m’malo mochita nsanje mnzathu akadalitsidwa, tiyenera kusangalala naye. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi mwana wa Mfumu Sauli dzina lake Yonatani. M’malo mochitira nsanje Davide atasankhidwa kuti alowe ufumu wa Sauli, anamulimbikitsa. (1 Sam. 23:16-18) Nafenso tiyenera kuyesetsa kukhala achikondi komanso okoma mtima ngati Yonatani.

KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI

Nkhani

w19.03 23-24 ¶12-15

Tizisonyeza Anthu Chifundo Tikakhala mu Utumiki

12 Chachitatu, tizileza mtima ndi anthu amene timawaphunzitsa. Tizikumbukira kuti anthuwo mwina sanaganizirepo mfundo za m’Baibulo zimene ifeyo timazidziwa bwino. Ndipo ambiri amakonda kwambiri mfundo zimene amakhulupirira. Mwina amaona kuti mfundo zimene amakhulupirirazo zimawathandiza kuti azigwirizana ndi achibale awo, anthu am’dera lawo kapena achikhalidwe chawo. Ndiye kodi tingawathandize bwanji?

13 Kuti timvetse nkhaniyi, tiyerekezere kuti mlatho ukutha ndipo pakufunika kukonza watsopano. Nthawi zambiri mlatho watsopano umayamba kukonzedwa wakalewo udakalipo komanso ukugwira ntchito. Watsopanowo ukatha m’pamene amagwetsa wakalewo. N’chimodzimodzi ndi ntchito yophunzitsa anthu mfundo za choonadi. Tisanawauze kuti asiye kukhulupirira mfundo zawo tiyenera kuwathandiza kuti amvetse bwino mfundo zatsopano zimene sakuzidziwa bwino. Akamvetsa zatsopanozo m’pamene angathe kusiya zimene ankakhulupirira poyamba. Ndiye kuti zimenezi zichitike pangadutse nthawi yambiri.​—Aroma 12:2.

14 Ngati ndife oleza mtima, sitidzayembekezera kuti anthu amvetse komanso kuvomereza mfundo za m’Baibulo pa ulendo woyamba. Mtima wachifundo ungatithandize kuti tizikambirana nawo Malemba kwa nthawi yaitali ndithu. Tiyerekeze kuti tikukambirana ndi munthu za moyo wosatha m’paradaiso padziko lapansi. Anthu ambiri amangodziwa zochepa pa nkhaniyi ndipo ena sadziwa chilichonse. Mwina amakhulupirira kuti munthu akafa zonse zimathera pomwepo. Apo ayi amakhulupirira kuti anthu abwino onse amapita kumwamba. Ndiye kodi tingawathandize bwanji?

15 M’bale wina anafotokoza zimene zimamuthandiza. Choyamba, amawerengera munthu lemba la Genesis 1:28. Kenako amamufunsa kuti, “Kodi Mulungu ankafuna kuti anthu azikhala kuti, nanga azikhala motani?” Ambiri amayankha kuti, “Padziko lapansi mosangalala.” Kenako m’baleyo amawerenga Yesaya 55:11 n’kufunsa munthuyo ngati cholinga cha Mulungu chinasintha. Nthawi zambiri anthu amayankha kuti sichinasinthe. Pomaliza, m’baleyo amawerenga Salimo 37:10, 11 n’kufunsa munthuyo kuti, “Malinga ndi vesili, kodi n’chiyani chidzachitike m’tsogolo?” Malemba ngati amenewa amathandiza anthu ambiri kumvetsa mfundo yoti Mulungu akufunabe kuti anthu akhale m’Paradaiso padziko lapansi.

APRIL 25–MAY 1

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 1 SAMUELI 25–26

“Kodi Mumachita Zinthu Mopupuluma?”

ia 78 ¶10-12

Anachita Zinthu Mwanzeru

10 Kodi asilikaliwa ankatani akakumana ndi abusawo? Zinali zosavuta kuti aziba nkhosa za Nabala, koma iwo sankachita zimenezi. M’malomwake, iwo ankateteza nkhosazo ndiponso abusawo. (Werengani 1 Samueli 25:15, 16.) Abusa pamodzi ndi nkhosa zawo ankakumana ndi mavuto ambirimbiri chifukwa kuderali kunkapezeka zilombo zambiri zolusa. Komanso derali linali pafupi kwambiri ndi malire akum’mwera a dziko la Isiraeli, moti akuba ochokera m’madera ena ankabwera kuderali pafupipafupi.

11 Davide ayenera kuti anali ndi udindo waukulu kwambiri wopezera chakudya anthu ake, omwe anali nawo m’chipululumo. Motero tsiku lina anatumiza anyamata ake 10 kuti akapemphe chakudya kwa Nabala. Nthawi imene Davide anatumiza anyamatawa inali yabwino chifukwa inali nthawi yometa ubweya wankhosa ndiponso yamadyerero. Pa nthawiyi anthu ankakonda kugawana zinthu. Komanso Davide anasankha bwino mawu oti anyamata ake akalankhule kwa Nabala ndipo anawauza kuti akalankhule naye mwaulemu kwambiri. Anawalangiza anyamatawo kukanena kuti ‘mwana wanu Davide’ ndi amene akupempha zinthuzi ndipo mwina anachita zimenezi posonyeza kuti ankazindikira zoti Nabala ndi munthu wamkulu. Koma kodi Nabala anatani?​—1 Sam. 25:5-8.

12 Iye anakwiya kwambiri moti mnyamata wake, yemwe watchulidwa kumayambiriro kwa nkhani ino, pouza Abigayeli za nkhaniyi ananena kuti “mbuyanga walalatira nthumwizo.” Nabala anali munthu womana kwambiri moti anauza anyamatawo kuti sangawononge nyama, madzi ndiponso mkate wake kupatsa Davide ndi anyamata ake. Iye ananyoza Davide ponena kuti anali wachabechabe ndiponso anali ngati kapolo amene wathawa mbuye wake. N’kutheka kuti Nabala ankaona Davide mofanana ndi mmene Sauli, yemwe ankadana ndi Davideyo, ankamuonera. Nabala ndi Sauli sankaona Davide ngati mmene Yehova ankamuonera. Mulungu ankakonda kwambiri Davide ndipo ankamuona kuti ndi mfumu ya m’tsogolo ya Isiraeli, osati ngati kapolo wothawa mbuye wake.​—1 Sam. 25:10, 11, 14.

ia 80 ¶18

Anachita Zinthu Mwanzeru

18 Abigayeli analankhula ngati kuti walakwitsa ndi iyeyo ndipo anapempha Davide kuti am’khululukire. Iye anavomereza kuti mwamuna wake anali wopanda nzeru, mogwirizana ndi tanthauzo la dzina lake. Choncho anapempha Davide, yemwe anali waulemu wake, kuti asalimbane ndi munthu wopanda nzeruyo. Iye analankhula mosonyeza kuti ankadziwa zoti Davide ndi mtumiki wa Yehova ndiponso kuti akumenya “nkhondo za Yehova.” Abigayeli anasonyezanso kuti ankadziwa zoti Yehova analonjeza Davide kuti adzamupatsa ufumu. Tikutero chifukwa polankhula ndi Davide, iye anati: “Yehova . . . adzakuikani kukhala mtsogoleri wa Isiraeli.” Kenako anapempha Davide kuti asachite chilichonse chimene chingam’chititse kuti akhale ndi mlandu wamagazi kapena zimene ‘zikanavutitsa chikumbumtima’ chake. (Werengani 1 Samueli 25:24-31.) Apa iye analankhuladi mokoma mtima ndiponso mogwira mtima.

Mfundo Zothandiza

ia 80 ¶16

Anachita Zinthu Mwanzeru

16 Kodi zimenezi zikutanthauza kuti Abigayeli sankagonjera mwamuna wake monga mutu wa banjalo? Ayi si choncho. Nabala anali atachita zinthu zoipa kwa mtumiki wodzozedwa wa Yehova ndipo zimenezi zikanaphetsa anthu ambiri osalakwa a panyumba pake. Komanso Abigayeli akanapanda kuchita chilichonse, akanakhala ngati akugwirizana ndi zimene mwamuna wake anachita. Choncho, iye anaona kuti anayenera kugonjera Mulungu m’malo mogwirizana ndi zinthu zoipa zimene mwamuna wake anachita.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena