Anachita Chifuniro cha Yehova
Chitsanzo cha Kudzimana ndi Kukhulupirika
KWA mlimi wina wachinyamata wotchedwa Elisa, tsiku lolima limene linayamba monga mwa nthaŵi zonse linasintha kukhala tsiku lapadera kwambiri m’moyo wake. Pamene anali kulima m’munda, Elisa anachezeredwa mwadzidzidzi ndi Eliya, mneneri wamkulu wa Israyeli. ‘Kodi angafunenji kwa ine?’ Mwina Elisa anadzifunsa motero. Sipanapite nthaŵi yaitali asanapeze yankho. Eliya anaponya chofunda chake kwa Elisa, kusonyeza kuti tsiku lina Elisa adzaloŵa paulendo wakewo. Elisa sanatenge chiitanochi mopepuka. Nthaŵi yomweyo, anasiya munda wake nakhala mnyamata wa Eliya.—1 Mafumu 19:19-21.
Patapita zaka zisanu ndi chimodzi, nthaŵi inafika yoti Eliya achoke. Nkhani ya kuchoka kwake yatchedwa kuti “imodzi mwa nkhani zochititsa chidwi koposa” m’Malemba Achihebri.
Eliya Akonzekera Kuchoka
Eliya anafuna kukachezera Beteli, Yeriko, ndi Yordano nthaŵi yomaliza. Kuchezeraku kunali kudzaloŵetsamo kuyenda makilomita ambiri, nthaŵi zina kukwera mapiri ovuta. Atafika pamalo alionse paulendo wakewo, Eliya anali kulimbikitsa Elisa kuti atsale. Koma Elisa analimbikira kukhalabe ndi mbuye wake mpaka mapeto.—2 Mafumu 2:1, 2, 4, 6.
Pamene anali ku Beteli ndi ku Yeriko, “ana a aneneri,” anakaonana ndi Elisa.a “Kodi udziŵa kuti Yehova akuchotsera lero mbuye wako, mtsogoleri wako?” anamfunsa motero. “Inde ndidziŵa,” iye anayankha motero. “Khalani muli chete.”—2 Mafumu 2:3, 5.
Eliya ndi Elisa kenako anyamuka paulendo wopita ku Mtsinje wa Yordano. Atafika ku Yordano, Eliya anachita chozizwitsa ana a aneneri 50 akupenyerera potero. “Eliya anagwira chofunda chake, nachipindapinda napanda madzi, nagaŵanikana kwina ndi kwina; ndipo anaoloka iwo onse aŵiri pansi pouma.”—2 Mafumu 2:8.
Ataoloka, Eliya anati kwa Elisa: “Tapempha chimene ndikuchitire ndisanachotsedwe kwa iwe.” Elisa anapempha “magawo aŵiri” a mzimu wa Eliya—ndiko kuti, mbali ziŵiri zimene mwamwambo zimapatsidwa kwa mwana wamwamuna wachisamba. Ndithudi, Elisa analemekeza Eliya monga momwe mwana wamwamuna wachisamba angalemekezere atate wake. Ndiponso, anadzozedwa kukhala woloŵa malo wa Eliya monga mneneri wa Yehova m’Israyeli. Choncho pempho lake silinali lodzikonda kapenanso losayenera. Komabe, podziŵa kuti Yehova yekha ndiye angapereke chopemphedwacho, Eliya anayankha mofatsa kuti: “Wapempha chinthu chapatali.” Ndiyeno anawonjezera kuti: “Ukandipenya pamene ndichotsedwa kwa iwe, kudzatero nawe; koma ukapanda kundipenyapo, sikudzatero ayi.”—2 Mafumu 2:9, 10; Deuteronomo 21:17.
Mosakayikira, Elisa anatsimikiza mtima kuposa kale lonse kuti adzamamatira kwa mbuye wake. Kenako, “galeta wamoto ndi akavalo amoto” anaoneka. Elisa alikudzipenyera yekha modabwa, Eliya anatengedwa m’kavumvulu—kusamutsidwira kumalo ena mozizwitsa.b Elisa anatola chofunda cha Eliya ndi kubwerera kugombe la Mtsinje wa Yordano. Anapanda madziwo, nati: “Ali kuti Yehova Mulungu wa Eliya?” Madziwo anapatukana, kupereka umboni wokwana bwino wakuti Elisa anavomerezedwa ndi Mulungu monga woloŵa malo a Eliya.—2 Mafumu 2:11-14.
Maphunziro kwa Ife
Ataitanidwa ndi Eliya ku utumiki wapadera, Elisa nthaŵi yomweyo anasiya munda wake napita kukatumikira mneneri wamkulu wa Israyeli. Mwachionekere, ntchito zake zina zinali zapansi, popeza anadzadziŵika monga amene “anathira madzi m’manja a Eliya.”c (2 Mafumu 3:11) Komabe, Elisa anaona ntchito yake kukhala mwaŵi, ndipo mokhulupirika anamamatira ku mbali ya Eliya.
Atumiki ambiri a Mulungu lerolino amasonyeza mzimu wofananawo wodzimana. Ena asiya “minda” yawo, njira zawo zopezera ndalama, kuti akalalikire uthenga wabwino kumagawo akutali kapena kukatumikira monga mamembala a banja la Beteli. Ena apita ku maiko achilendo kukagwira ntchito kumene Sosaite ikumanga. Ambiri alandira zimene zingatchedwe ntchito zapansi. Komabe, palibe kapolo wa Yehova amene akuchita utumiki waung’ono. Yehova amayamikira onse amene amamtumikira mofunitsitsa, ndipo adzadalitsa mzimu wawo wodzimana.—Marko 10:29, 30.
Elisa anamamatira kwa Eliya mpaka mapeto. Anakana kusiya mneneri wokalambayo ngakhale atapatsidwa mwaŵi kuti atero. Mosakayikira, unansi woyandikana kwambiri umene anakulitsa ndi Eliya unapangitsa chikondi chokhulupirika chotero kukhala chokondweretsa. Lerolino, atumiki a Mulungu amayesetsa kulimbitsa unansi wawo ndi Mulungu ndi kuyandikana kwambiri ndi okhulupirira anzawo. Umodzi wathithithi udzadalitsidwa, popeza Baibulo limanena za Yehova kuti: “Kwa munthu wokhulupirika, inunso mudzakhala wokhulupirika.”—2 Samueli 22:26, NW.
[Mawu a M’munsi]
a Mawu akuti “ana a aneneri” angatanthauze sukulu yolangiza oitanidwa ku utumiki umenewu kapena chigwirizano cha aneneri.
b Patapita zaka zingapo Eliya analemba uthenga kwa Mfumu Yehoramu ya Yuda.—2 Mbiri 21:12-15.
c Unali mwambo kuti mnyamata wantchito azithira madzi m’manja a ambuye wake posamba, makamaka pambuyo pa kudya chakudya. Mwambo umenewu unali wofanana ndi kusambitsa mapazi, kumene kunali kusonyeza kuchereza alendo, ulemu, ndipo m’maunansi ena, kudzichepetsa.—Genesis 24:31, 32; Yohane 13:5.